Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaona Chiyani Kuti Mudziwe Kuti Munthu Zikumuyendera Bwino?

Kodi Mumaona Chiyani Kuti Mudziwe Kuti Munthu Zikumuyendera Bwino?

Kodi Mumaona Chiyani Kuti Mudziwe Kuti Munthu Zikumuyendera Bwino?

JESSE LIVERMORE anali munthu yemwe ambiri ankamuona kuti anali katswiri pa nkhani yogulitsa magawo a makampani ku msika wogulitsirako makampani wa Wall Street komanso anali munthu wodziwa kuyendetsa bwino bizinesi. Chifukwa cha zimenezi, anapeza chuma chochuluka. Ankavala masuti abwino kwambiri osokedwa pamanja, ankakhala m’chinyumba chachikulu cha zipinda 29, ndiponso ankayenda pa galimoto yodula ya mtundu wa Rolls-Royce, mochita kuyendetsedwa ndi dalaivala.

Munthu winanso, dzina lake David * ankafuna atadzapeza chuma chochuluka. Popeza anali wachiwiri kwa bwana wamkulu komanso anali manijala wamkulu wa kampani yokonza zithunzi pakompyuta, anatsala pang’ono kukhala bwana wamkulu wa chigawo china cha kumene kunali makampani awo. Chuma ndi kutchuka zinamukopa kwambiri. Komabe, David anaganiza zosiya ntchito. David anati: “Ndikudziwa kuti sindidzakhalanso ndi mwayi wogwira ntchito ina yapamwamba.” Kodi mukuganiza kuti David analakwitsa?

Anthu ambiri amaganiza kuti, zinthu zimakuyendera bwino ukakhala ndi chuma, kapena ukakhala wotchuka. Komabe, amene ali ndi chuma chambiri akhoza kukhala osakhutira m’moyo wawo komanso akhoza kumaona kuti moyo wawo ulibe cholinga chenicheni. Zimenezi n’zimene zinawachitikira a Livermore. Ngakhale kuti anali ndi chuma, ankakhala moyo wamavuto. Anali ovutika maganizo, sankakhalitsa pabanja, ndiponso sankagwirizana ndi ana awo. Ndiyeno tsiku lina, chuma chawo chambiri chitatha, a Livermore anakhala pa malo ogulitsira mowa mu hotela inayake yapamwamba n’kumadandaula za chuma chawocho. Anaitanitsa mowa, n’kutulutsa kabuku kawo ka chikuto chachikopa, n’kulemba mawu otsanzikana ndi mkazi wawo. Atamaliza kumwa mowawo, anakalowa m’chipinda china momwe munali kamdima, ndipo n’zachisoni kuti atatero anadziwombera.

N’zoona kuti pali zifukwa zambiri zimene anthu amadziphera, koma nkhaniyi ikungotsimikizira zomwe Baibulo limanena kuti: “Anthu ofunitsitsa kulemera, . . . adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.”​—1 Timoteyo 6:9, 10.

Kodi n’zotheka kuti maganizo oti munthu amene zikumuyendera bwino ndi amene ali ndi chuma, udindo ndiponso amene ali wotchuka n’ngolakwika? Kodi inuyo mukuganiza kuti zinthu zikukuyenderani bwino? N’chifukwa chiyani mukuganiza choncho? Kodi ndi mfundo zotani zimene zikukuchititsani kuganiza choncho? Kodi ndi zinthu zotani zimene zimakuchititsani kuona kuti munthu zikumuyendera bwino? Nkhani yotsatirayi ikufotokoza malangizo omwe kwa nthawi yaitali akhala akuthandiza anthu mamiliyoni ambiri kuti zinthu ziziwayendera bwino. Tiyeni tikambirane zimene inunso mungachite kuti zinthu zizikuyenderani bwino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Dzinali talisintha.