Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi kusindikiza chisindikizo kotchulidwa pa Chivumbulutso 7:3 n’kutani?

Lemba la Chivumbulutso 7:1-3 limati: “Ndinaona angelo anayi ataimirira ku ngodya zinayi za dziko lapansi, atagwira zolimba mphepo zinayi za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko lapansi, pa nyanja, kapena pa mtengo uliwonse. Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa, ali ndi chosindikizira cha Mulungu wamoyo. Mokweza mawu, iye anafuula kwa angelo anayiwo, amene anapatsidwa mphamvu zowononga dziko lapansi ndi nyanja. Amvekere: ‘Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titasindikiza akapolo a Mulungu wathu chisindikizo pamphumi pawo.’”

“Mphepo zinayi” zikadzamasulidwa, padzachitika “chisautso chachikulu,” chomwe chili chiwonongeko cha zipembedzo zonyenga ndiponso dziko lonse loipali. (Chivumbulutso 7:14) “Akapolo a Mulungu wathu” ndi abale odzozedwa a Khristu padziko lapansi. (1 Petulo 2:9, 16) Motero, ulosi umenewu ukusonyeza kuti kuika chisindikizo abale a Khristu kudzakhala kutatha chisautso chachikulu chikamadzayamba. Komabe, mavesi ena m’Baibulo amasonyeza kuti pali kuikidwa chisindikizo koyamba kwa odzozedwa. Motero, nthawi zina timatchula za kuikidwa chisindikizo koyamba ndiponso kuikidwa chisindikizo komaliza. Kodi kuika chisindikizo kuwiriku n’kosiyana bwanji?

Taganizirani momwe zikalata zinkaikidwira chisindikizo kalelo, ndiponso chifukwa chomwe ankachitira zimenezi. Ankagwiritsa ntchito kachida kenakake kuti adinde dongo lomwe amatira chikalata. Chidindo cha padongolo chinkasonyeza mphamvu za wodindayo kapena kuti ndiye mwiniwake wa chikalatacho.​—1 Mafumu 21:8; Yobu 14:17.

Paulo anayerekezera mzimu woyera ndi chisindikizo ponena kuti: “Amene amatitsimikizira kuti inuyo ndi ife tili a Khristu, amenenso anatidzoza, ndiye Mulungu. Iye watiikanso chisindikizo chake chotitsimikizira ndipo watipatsa m’mitima mwathu chikole cha zinthu zam’tsogolo, ndicho mzimu.” (2 Akorinto 1:21, 22) Motero, Yehova amadzoza Akhristu amenewa ndi mzimu wake woyera posonyeza kuti iwowa ndi ake.

Komano, odzozedwa amasindikizidwa chisindikizo nthawi ziwiri. Kuikidwa chisindikizo koyamba kumasiyana ndi kuikidwa chisindikizo komaliza m’njira ziwiri izi: (1) cholinga chake (2) nthawi yake. Kuikidwa chisindikizo koyambako kumakhala kusankha munthu watsopano woti akhale nawo m’gulu la Akhristu odzozedwa. Kuikidwa chisindikizo komaliza kumatsimikizira kuti munthu anasankhidwa n’kuikidwa chisindikizo uja wasonyeza kukhulupirika kwake mokwanira. Ndi pa kuikidwa chisindikizo chomaliza kumeneku pamene chisindikizocho chimaikidwa kosatha “pamphumi” pa wodzozedwayo, kuti adziwike mopanda kukayikira kulikonse kuti ndi ‘kapolo wa Mulungu wathu,’ yemwe wayesedwa ndipo wakhulupirika. Kuikidwa chisindikizo komwe kunatchulidwa mu Chivumbulutso chaputala 7 kumanena za mbali yotsirizayi ya kusindikiza chisindikizo.​—Chivumbulutso 7:3.

Ponena za nthawi imene kusindikiza koyamba kumachitika, mtumwi Paulo analemba mawu otsatirawa kwa Akhristu odzozedwa: “Inunso munakhala ndi chiyembekezo mwa iye mutamva mawu a choonadi, uthenga wabwino wonena za chipulumutso chanu. Kudzeranso mwa iye, mutakhulupirira, munaikidwa chisindikizo cha mzimu woyera wolonjezedwawo.” (Aefeso 1:13, 14) Nthawi zambiri, Baibulo limasonyeza kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi anaikidwa chisindikizo patangodutsa kanthawi kochepa atamva uthenga wabwino n’kuyamba kukhulupirira Khristu. (Machitidwe 8:15-17; 10:44) Kuikidwa chisindikizo kumeneku kunasonyeza kuti Mulungu wawavomereza. Koma sikunasonyeze kuti Mulungu wawavomerezeratu mpaka kalekale. N’chifukwa chiyani sizinali choncho?

Paulo ananena kuti Akhristu odzozedwa ‘amaikidwa chisindikizo cha patsiku limene adzamasulidwa.’ (Aefeso 4:30) Zimenezi zikusonyeza kuti pamatenga nthawi, kawirikawiri zaka zambiri, kuchokera pamene anawaika chisindikizo choyambirira. Akhristu odzozedwa ayenera kukhalabe okhulupirika kuyambira tsiku limene aikidwa chisindikizo ndi mzimu woyera mpaka kufika pa ‘tsiku limene adzamasulidwe’ ku matupi awo aumunthu, kapena kuti mpaka kufika tsiku la kufa kwawo. (Aroma 8:23; Afilipi 1:23; 2 Petulo 1:10) Motero, Paulo atafika pa mapeto a moyo wake m’pamene anatha kunena kuti: “Ndamenya nkhondo yabwino, ndathamanga panjirayo mpaka pomalizira pake, ndasunga chikhulupiriro. Kuyambira tsopano kumka m’tsogolo, andisungira kolona wa chilungamo.” (2 Timoteyo 4:6-8) Komanso, Yesu ananena izi ku mpingo wa Akhristu odzozedwa: “Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa, ndipo ndidzakupatsa kolona wa moyo.”​—Chivumbulutso 2:10; 17:14.

Mawu akuti “kolona” akuikiranso umboni mfundo yakuti pamapita nthawi ndithu kuchokera pa kuikidwa chisindikizo koyamba ndi kuikidwa chisindikizo komaliza. N’chifukwa chiyani tikutero? Kale ankapereka kolona kwa wothamanga amene wawina pampikisano. Kulowa nawo mpikisano wothamanga pakokha sikunali kokwanira kuti munthu alandire kolona. Munthuyo anayenera kuthamanga mpaka kukafika pothera mpikisanowo. N’chimodzimodzinso ndi Akhristu odzozedwa. Kuti akalandire kolona wa moyo wosafa kumwamba, ayenera kupirira mpaka pamapeto, kutanthauza kuchokera pa kuikidwa chisindikizo koyamba kufika pa kuikidwa chisindikizo komaliza.​—Mateyo 10:22; Yakobe 1:12.

Kodi otsalira a Akhristu odzozedwa omwe anaikidwa chisindikizo choyamba adzaikidwa liti chisindikizo chomaliza? Chisautso chachikulu chisanayambe, odzozedwa onse amene adzatsale padziko adzaikidwa chisindikizo “pamphumi pawo.” Mphepo zinayi za chisautso zikadzamasulidwa, Aisiraeli auzimu onse adzakhala ataikidwa chisindikizo chomaliza, ngakhale kuti ochepa adzakhala adakali ndi matupi aumunthu padziko pano ndipo adzakhala asanamalize moyo wawo padziko lapansi.