Mungathe Kupirira Mavuto
Mungathe Kupirira Mavuto
M’MASIKU ovuta ano, anthu ambiri akupirira mavuto ochuluka. Koma kumvera Mulungu ndi kusunga malamulo ake n’kumene kumathandiza Akhristu kupirira. Kodi kumawathandiza bwanji? Yankho lake tingalipeze mu fanizo lomwe Yesu Khristu ananena. Iye anafanizira ophunzira ake okhulupirika ndi “munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.” Yesu anati: “Kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika ndi kuwomba nyumbayo, koma sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo.”—Mateyo 7:24, 25.
Onani kuti ngakhale munthu wa m’fanizoli anali wochenjera, anakumanabe ndi mavuto ngati chimvula champhamvu, madzi osefukira ndiponso chimphepo chowononga. Yesu, sanasonyeze kuti ophunzira akewo adzapewa masoka onse n’kumakhala moyo wopanda mavuto, wamtendere wokhawokha. (Salmo 34:19; Yakobe 4:13-15) M’malo mwake, iye anasonyeza kuti atumiki okhulupirika a Mulungu angathe kukonzekera kukumana komanso kuthana ndi mavuto osiyanasiyana.
Yesu anayamba fanizo lake ndi mawu akuti: “Aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.” N’zoona kuti Yesu sanali kunena za kumanga nyumba zenizeni, koma anali kunena za kukhala ndi zolinga ndiponso kuchita ntchito zabwino zachikhristu. Anthu amene amamvera mawu a Khristu amalingalira mozama ndi kusankha zochita mwanzeru. Zolinga komanso zochita zawo zimakhala zozikidwa pa thanthwe lolimba, lomwe ndi zinthu zimene Khristu amaphunzitsa, ndipo kuti zitero iwo amagwiritsira ntchito zomwe aphunzitsidwazo. Onani kuti thanthwe lophiphiritsira lotchulidwa m’fanizoli silinali pamwamba panthaka. Munthu wam’fanizoli anayenera ‘kukumba mozama’ kuti alipeze. (Luka 6:48) Chimodzimodzinso, ophunzira a Yesu amayesetsa kuti asonyezebe makhalidwe abwino amene amawachititsa kuti ayandikire kwa Mulungu.—Mateyo 5:5-7; 6:33.
Kodi chimachitika n’chiyani mavuto okhala ngati mphepo yamkuntho akamayesa maziko a chikhulupiriro chachikhristu cha otsatira a Yesu? Kumvera mofunitsitsa ziphunzitso za Khristu ndiponso makhalidwe achikhristu amene ali nawo ndi zimene zimawapatsa mphamvu pa nthawi ya mavuto oterewa, ndiponso ndi zimene zidzawalimbitse pa mkuntho womwe ukubwera wa Armagedo. (Mateyo 5:10-12; Chivumbulutso 16:15, 16) Inde, mwa kutsatira ziphunzitso za Khristu, anthu ambiri akupirira mavuto okhala ngati mphepo yamkuntho. Inunso mukhoza kutero.—1 Petulo 2:21-23.