Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu Amene Ankakonda Moyo Ndiponso Anthu

Munthu Amene Ankakonda Moyo Ndiponso Anthu

Munthu Amene Ankakonda Moyo Ndiponso Anthu

DANIEL SYDLIK, munthu yemwe anatumikira m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova kwa nthawi yaitali, anamaliza moyo wake wa padziko lapansi, Lachiwiri, pa April 18, 2006. Anali ndi zaka 87 ndipo anatumikira m’banja la Beteli ku Brooklyn, mu mzinda wa New York, kwa zaka pafupifupi 60.

Anzake ankangomutchula kuti M’bale Dan, ndipo iyeyu anapita ku Beteli mu 1946. Asanapite ku Beteli, anatumikirapo monga mpainiya wapadera ku California ndiponso anakhalapo m’ndende pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse chifukwa chotsatira mfundo zachikhristu zosalowerera m’zochitika zadziko. Zochita zake za panthawiyo zafotokozedwa bwino m’mbiri ya moyo wake, yomwe ili mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya June 1, 1985 ya mutu wakuti “How Priceless Your Friendship, O God!”

M’bale Sydlik ankadziwika kuti anali munthu wosadzikweza, ndiponso wochezeka. Akamatsogoza kulambira kwa m’mawa kwa banja la Beteli, mawu oyamba amene ankakonda kunena ankasonyeza khalidwe lake labwino ndiponso ankasonyeza kuti amakonda moyo. Mawuwo anali akuti: “N’kokomatu kukhala ndi moyo ndi kumatumikira Mulungu woona ndi wamoyo.” Monga wokamba nkhani pagulu, ankalimbikitsa mfundo imeneyi kwa ena pokamba nkhani za mitu monga yakuti, “Odala Anthu Amene Mulungu Wawo ndi Yehova,” “Kusonyeza Chimwemwe cha Yehova,” “Musazimitse Mzimu wa Mulungu,” ndiponso “Zabwino Zili M’tsogolo.”

Mu 1970, M’bale Sydlik anakwatira Marina Hodson, wa ku England, amene anamutchula kuti anali “thandizo lochokera kwa Mulungu.” Anatumikira Yehova ali limodzi kwa zaka zoposa 35.

Kwa zaka zimene wakhala pa Beteli, M’bale Sydlik anatumikira m’madipatimenti osiyanasiyana, kuphatikizapo kosindikizira mabuku ndi ku Dipatimenti Yolemba. Anagwiraponso ntchito pa wailesi ya WBBR. Kenaka, mu November 1974, anaikidwa m’Bungwe Lolamulira ndipo patapita nthawi anayamba kutumikira m’Komiti ya Ogwira Ntchito ndiponso Komiti Yolemba.

Kwa zaka zoposa 30, ntchito yomwe M’bale Sydlik ankagwira ndi Komiti ya Ogwira Ntchito ankaichita mosonyeza kwambiri chikondi chake kwa anthu. Ndi mawu ake amphamvu, ankalimbikitsa anthu, ndipo nthawi zonse ankatsindika za mwayi wamtengo wapatali womwe tili nawo wotumikira Yehova. Nthawi zonse ankatsindika mfundo yakuti chimwemwe chenicheni sichidalira pa zinthu za m’dzikoli, koma chimadalira pa ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso zimene timachita pa moyo wathu.

Ngakhale kuti banja la Beteli likudandaula kwambiri kuti M’bale Sydlik salinso limodzi naye, chitsanzo chake monga munthu yemwe ankakonda moyo ndiponso anthu chidzapitiriza kupindulitsa banjali kwa nthawi yaitali. Sitikukayika kuti iye ndi mmodzi wa anthu amene atchulidwa pa Chivumbulutso 14:13 kuti: “Osangalala ali akufawo amene akufa mwa Ambuye kuyambira panthawi ino kupita m’tsogolo. Inde, mzimu ukuti, alekeni akapumule ku ntchito zawo za thukuta, pakuti zimene anachita zipita nawo limodzi.”