Ndadalitsidwa Moyo Wanga Wonse Chifukwa Chosankha Bwino Zochita
Mbiri ya Moyo Wanga
Ndadalitsidwa Moyo Wanga Wonse Chifukwa Chosankha Bwino Zochita
Yosimbidwa ndi Paul Kushnir
M’CHAKA cha 1897 agogo anga aakazi ndi aamuna anasamuka ku Ukraine n’kupita ku Canada ndipo anakakhala pafupi ndi tawuni ya Yorkton m’chigawo cha Saskatchewan. Anafika ndi ana anayi, anyamata atatu ndi mtsikana mmodzi. Mu 1923, mtsikanayo, dzina lake Marinka, anabereka ineyo, ndipo ndinali mwana wake wa nambala 7. Masiku amenewo moyo unali wosalira zambiri koma wamtendere. Tinali ndi chakudya chabwino ndi zovala zabwino zamphepo, ndipo boma linkatithandiza pa zosowa za pa moyo wathu. Komanso, anthu okhala moyandikana ankathandizana akamagwira ntchito inayake yaikulu. M’nyengo yozizira m’chaka cha 1925, mmodzi wa Ophunzira Baibulo, omwe panopa amatchedwa Mboni za Yehova, anabwera kudzatichezera kunyumba kwathu. Ulendo umenewo unatichititsa kusankha zochita zimene ndimayamikirabe mpaka pano.
Banja Lathu Linaphunzira Choonadi
Amayi analandira timabuku tingapo kwa Wophunzira Baibuloyo ndipo nthawi yomweyo anazindikira kuti chinali choonadi. Anapita patsogolo msanga mwauzimu ndipo anabatizidwa mu 1926. Amayi atakhala Ophunzira Baibulo, banja lathu linasintha kwambiri. Nyumba yathu inasanduka malo ocherezera alendo. Oyang’anira oyendayenda ndi Ophunzira Baibulo ena nthawi zambiri ankakhala kunyumba kwathu. Mu 1928 woyang’anira woyendayenda wina anationetsa “Sewero la Eureka,” lomwe kwenikweni linali ngati chidule cha sewero la “Photo-Drama of Creation.” Anabwereka chidole chathu chokhala ngati chule chomwe chinkalira chikafinyidwa. Akafinya chidolecho ndiye kuti nthawi yosintha chithunzi yakwana. Anafe tinasangalala kwambiri popeza anagwiritsira ntchito chidole chathu.
Woyang’anira woyendayenda wina dzina lake Emil Zarysky nthawi zambiri ankabwera kudzatichezera pa galimoto yake yomwe inali ndi kalavani yogonamo. Nthawi zina ankabwera limodzi ndi mwana wake wamwamuna wamkulu, yemwe ankatilimbikitsa anafe kuti tiganizire zodzakhala atumiki a nthawi zonse, kapena kuti apainiya. Apainiya 1 Petulo 4:8, 9.
ambiri ankakhalanso kunyumba kwathu nthawi zina. Pa nthawi inayake amayi anabwereka mpainiya wina shati kuti amusokere shati yake. Mosadziwa, iye anatenga shati anam’patsa amayi ija pamene ankachoka. Patapita nthawi yaitali, anaitumiza n’kupepesa chifukwa choibweza mochedwa. Analemba kuti: “Pepani kuti ndinalibe ndalama zokwana masenti 10 zopositira shatiyi.” Tinamva chisoni ndipo tinaona kuti zikanakhala bwino akanangotenga shatiyo. Ndinkalakalaka kuti tsiku lina ndidzatengere chitsanzo cha apainiya odzipereka ngati amenewo. Ndimathokoza mtima wochereza alendo wa amayi, umene unatichititsa kukhala ndi moyo wosangalatsa ndi kukulitsa chikondi chathu pa abale.—Abambo sanakhale Wophunzira Baibulo, koma sankatitsutsa. Ndipo mu 1930 analoleza kuti abale achitire msonkhano wa tsiku limodzi m’chishedi chawo chachikulu. Ngakhale kuti ndinali ndi zaka 7 zokha, msonkhanowo unandikhudza kwambiri chifukwa unali wosangalatsa ndi wabata. Abambo anamwalira mu 1933. Amayi, omwe panthawiyo anali mayi wamasiye wa ana 8, sanasinthe ngakhale pang’ono cholinga chawo choti tikhalebe pa njira ya kulambira koona. Ankaonetsetsa kuti ndikupita nawo limodzi kumisonkhano. Panthawiyo, misonkhanoyo inkaoneka yaitali kwambiri kwa ine, ndipo ndinkalakalaka n’takhala limodzi ndi ana ena, omwe makolo awo ankawalola kuti azingosewera panja. Koma chifukwa chowapatsa ulemu amayi, ndinkakhalabe pamisonkhanoyo. Amayi akamaphika, nthawi zambiri ankalakatula lemba n’kundifunsa kuti ndinene pomwe limapezeka m’Baibulo. Mu 1933 tinakolola zinthu zambiri ndipo amayi anagula galimoto ndi ndalama zomwe tinapeza. Anthu ena apafupi anawanena amayi kuti akuwononga ndalama, koma amayi ankaona kuti galimotoyo itithandiza pa ntchito zathu zotumikira Mulungu. Ndipotu sanalakwitse ayi.
Anthu Ena Anandithandiza Kusankha Bwino Zochita
Nthawi imafika yoti wachinyamata asankhe zinthu zokhudza tsogolo lake. Nthawi imeneyo itawakwanira alongo anga aakulu, Helen ndi Kay, anayamba kuchita upainiya. Mpainiya wina amene tinam’landirapo kunyumba kwathu anali John Jazewsky, ndipo anali mnyamata wa makhalidwe abwino. Amayi anamupempha John kuti akhale kunyumba kwakanthawi kuti atithandize ntchito za pafamu. Patsogolo pake, John anakwatira Kay, ndipo anayamba kuchita upainiya kufupi ndi kunyumba kwathu. Ndili ndi zaka 12, anandipempha kuti ndizipita nawo mu utumiki wa kumunda pa nthawi imene ndinali patchuthi kusukulu. Zimenezo zinandipatsa mpata wolawako moyo waupainiya.
Patapita nthawi, ine ndi mkulu wanga John tinkayendetsa tokha pafupifupi ntchito zonse za pa famu yathu. Zimenezi zinawapatsa amayi mpata woti mu July ndi August azichita nawo ntchito imene panopa imatchedwa upainiya wothandiza. Ankagwiritsira ntchito ngolo ya matayala awiri yokokedwa ndi kavalo wokalamba. Kavalayo, bambo anam’patsa dzina loti Sauli chifukwa anali wamakani, koma amayi ankawamvera ndipo ankatha kumulamulira bwinobwino. Ine ndi John tinkakonda famu yathuyo, koma nthawi iliyonse amayi akabwera kunyumba kuchokera ku utumiki wa kumunda n’kumatiuza zomwe anakumana nazo, zinkachititsa kuti pang’ono ndi pang’ono chikondi chathu cha pa famuyo chizichepa n’kuyamba kukonda kwambiri utumiki wa upainiya. Mu 1938, ndinayamba kuchita zambiri mu utumiki wanga wa kumunda, ndipo pa February 9, 1940, ndinabatizidwa.
Patapita kanthawi ndinaikidwa kukhala mtumiki mumpingo. Ndinkasamalira mafaelo a mpingo ndipo ndinkasangalala nthawi iliyonse yomwe panali kuwonjezeka. Ndinali ndi gawo langalanga lolalikira pa mtunda wa mamailo pafupifupi 10 kuchokera kunyumba. M’nyengo yozizira, ndinkayenda pansi kupita kugawoko mlungu uliwonse ndipo tsiku limodzi kapena awiri ndinkagona m’kachipinda kapamwamba ka nyumba ya banja lina lomwe linkachita chidwi ndi Baibulo. Nthawi ina ndinakambirana ndi m’busa wa tchalitchi cha Lutheran, ndipo sindinalankhule mosamala kwenikweni, moti anandiopseza kuti aitana apolisi ndikapanda kusiya nkhosa
zake. Koma zimenezo zinangondilimbitsa mtima kuti ndipitirizebe.Mu 1942, mlongo wanga Kay, ndi mwamuna wake, John, anakonza zopita ku msonkhano ku Cleveland, ku Ohio, m’dziko la United States. Ndinasangalala kwambiri atandiuza kuti ndipite nawo. Msonkhano umenewo ndi chimodzi mwa zinthu zabwino kwambiri zimene zinandichitikirapo. Unalimbitsa zolinga zanga za m’tsogolo. M’bale Nathan Knorr, amene panthawiyo ankatsogolera ntchito yapadziko lonse, atapempha mochokera pansi pamtima kuti pakufunika apainiya 10,000, ndinasankha nthawi yomweyo kuti ndikufuna kukhala mmodzi wa iwo!
Mu January 1943, Henry, amene anali woyang’anira woyendayenda, anadzachezera mpingo wathu. Anakamba nkhani yokhudza mtima kwambiri imene inatilimbikitsa kwabasi. Atakamba nkhaniyo, tsiku lotsatira kunja kunazizira madigiri seshasi –40, ndipo mphepo yamphamvu yochokera kumpoto chakumadzulo inakokomeza mphamvu ya kuzizirako. Nthawi zambiri kukazizira choncho tinkakhala m’nyumba, koma Henry ankafunitsitsa kupita mu utumiki. Iye ndi anthu ena anakwera ngolo yotseka pamwamba yokokedwa ndi kavalo, yoyenda m’chipale chofewa. M’ngolomo munali sitovu yophikira nkhuni, ndipo anapita nayo ku mudzi wina womwe unali pa mtunda wa makilomita 11. Ine ndinapita ndekha kukayendera banja lina lomwe linali ndi ana aamuna asanu. Anawo anavomera n’tawapempha kuti ndiziphunzira nawo Baibulo, ndipo m’kupita kwa nthawi anaphunzira choonadi.
Kulalikira Ataletsa Ntchitoyi
Pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, ntchito ya Ufumu inaletsedwa ku Canada. Tinafunikira kubisa mabuku athu ofotokoza za m’Baibulo, ndipo pa famu yathu panali malo ambiri obisako mabukuwa. Apolisi ankabwerabwera kudzafuna mabukuwa, koma sanapeze chilichonse. Tinkalalikira ndi Baibulo lokha basi. Tinkakumana m’magulu ang’onoang’ono, ndipo ine ndi mkulu wanga John tinasankhidwa kuti tizigwira ntchito yonyamula mabuku mwakabisira kupita nawo ku malo osiyanasiyana.
Pa nthawi ya nkhondoyo, mpingo wathu unagwira nawo ntchito yogawa kabuku ka End of Nazism m’dziko lonselo. Tinapita kokagawa timabukuto pakati pausiku. Ndinkachita mantha kwambiri tikamayandikira nyumba iliyonse tikuyenda monyang’ama n’kusiya kabuku pakhomo. Sindinachitepo chinthu china chilichonse chochititsa mantha kuposa pamenepa. Mtima wanga unakhala m’malo pamene tinagawira kabuku komaliza. Kenaka tinabwerera mwamsanga kumene tinaimitsa galimoto n’kuwerengana, kenaka n’kunyamuka pagalimotoyo kunja kuli chimdima.
Upainiya, Ndende, ndi Misonkhano Ikuluikulu
Pa May 1, 1943, ndinatsanzikana ndi amayi. Ndinanyamuka kupita ku gawo langa loyamba lochitirako upainiya ndili ndi madola 20 m’thumba mwanga ndi sutikesi yaing’ono. Mbale Tom Troop ndi banja lake lachikondi anandilandira mwansangala m’tawuni ya Quill Lake, ku Saskatchewan. Chaka chotsatira, ndinapita ku gawo lakutali m’tawuni ya Weyburn, ku Saskatchewan. Ndikuchita ulaliki wa mumsewu pa December 24, 1944, ndinamangidwa. Nditakhala kwakanthawi m’ndende kumeneko, anandisamutsira ku malo ena ogwirira ukaidi m’tawuni ya Jasper, ku Alberta. Kumeneko kunalinso Mboni zina ndipo tinazunguliridwa ndi mapiri a Rockies a ku Canada, omwe ali chilengedwe chodabwitsadi cha Yehova. Kumayambiriro kwa 1945, anthu oyang’anira malowa anatilola kupita ku msonkhano ku Edmonton, ku Alberta. M’bale Knorr anapereka lipoti losangalatsa kwambiri la mmene ntchito inali kupitira patsogolo pa dziko lonse lapansi. Tinkalakalaka tsiku limene ukaidi wathu udzathe kuti tidzayambenso kuchita nawo utumiki mokwanira.
Nditatulutsidwa, ndinayambiranso kuchita upainiya. Patapita nthawi yochepa, analengeza kuti msonkhano wa “All Nations Expansion” [“Kufutukuka kwa Mitundu Yonse”] udzachitikira ku Los Angeles, ku California. M’bale wina m’gawo langa latsopano lochitira upainiya anakhoma mabenchi m’galimoto yake kuti muthe kukwera anthu okwana 20. Pa August 1, 1947, tinanyamuka ulendo wosaiwalika, umene tinayenda makilomita 7,200 kudutsa m’zigwa, zipululu, ndi malo okongola kwambiri, kuphatikizapo malo osungirako zachilengedwe a Yellowstone ndi Yosemite. Ulendo wonsewo unatitengera masiku 27, ndipo unali wosangalatsa kwambiri!
Msonkhanowo paokha unali dalitso losaiwalika. Kuti ndipindule nawo mokwanira, ndinkatumikira monga kalinde masana ndi mlonda usiku. Pambuyo Yesaya 6:8.
pokhala nawo pa msonkhano wa anthu ofuna utumiki wa umishonale, ndinalemba fomu yofunsira utumikiwu koma ndinalibe chiyembekezo chachikulu choti anganditenge. Pa nthawi yomweyi mu 1948, ndinavomera pempho loti apainiya tipite kukatumikira m’chigawo cha ku Canada cha Quebec.—Kupita ku Gileadi Ndiponso Pambuyo Pake
Mu 1949 ndinasangalala kwambiri kulandira kalata yondiitana kuti ndikaphunzire nawo kalasi ya nambala 14 ya Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Maphunziro amenewo analimbitsa chikhulupiriro changa ndipo anandithandiza kuyandikira kwambiri kwa Yehova. John ndi Kay anali atamaliza kale maphunziro a kalasi ya nambala 11 ndipo anali kutumikira monga amishonale ku Northern Rhodesia (panopa ndi ku Zambia). Mkulu wanga John anamaliza maphunziro a Gileadi mu 1956. Iye anatumikira limodzi ndi mkazi wake Frieda ku Brazil kwa zaka 32 mpaka imfa yake.
Pa tsiku lomaliza maphunziro anga mu February 1950, ndinalimbikitsidwa kwambiri ndi matelegalamu awiri omwe ndinalandira, imodzi yochokera kwa amayi ndi ina yochokera ku banja la a Troop a ku Quill Lake. Telegalamu yochokera ku banja la a Troop, yomwe inali ndi mutu wakuti “Malangizo kwa Womaliza Maphunziro,” inati: “Ili ndi tsiku lapadera kwambiri kwa iwe. Ndi tsiku lomwe udzalikumbukire moyo wako wonse, ndipo tikukufunira zabwino zonse ndi chimwemwe pamoyo wako.”
Ndinauzidwa kuti ndizikatumikira mu mzinda wa Quebec, koma kwakanthawi ndinakhalabe pa Kingdom Farm, ku New York State, kumene kunali sukulu ya Gileadi masiku amenewo. Tsiku lina, M’bale Knorr anandifunsa ngati ndingakonde kupita ku Belgium. Koma patatha masiku ochepa, anandifunsa ngati ndingavomere kukatumikira ku Netherlands. Nditalandira kalata yondiuza za ntchito yanga, inanena kuti “ndizikagwira ntchito ya mtumiki wa nthambi.” Ndinaona kuti ndachepa nayo kwabasi ntchito imeneyi.
Pa August 24, 1950, ndinanyamuka pa ulendo wa masiku 11 wopita ku Netherlands. Imeneyi inali nthawi yokwanira kuti ndiwerenge n’kumaliza Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu lachingelezi lomwe linali litangotulutsidwa kumene. Ndinafika ku Rotterdam pa September 5, 1950, kumene ndinalandiridwa ndi manja awiri ndi banja la Beteli. Ngakhale kuti nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inali itawononga zinthu zambiri, abale anayesetsa kuyambitsanso ntchito zachikhristu. Ndikumvetsera nkhani zawo za momwe anakhalirabe okhulupirika akuzunzidwa kwambiri, ndinaganiza kuti zingawavute kwambiri abale amenewo kutumikira motsogozedwa ndi mtumiki wa nthambi wachinyamata wongoyamba kumene ntchito yake. Koma pasanapite nthawi yaitali zinaoneka kuti panalibe chifukwa chilichonse choti ndizidera nkhawa.
Komabe, zinthu zina zinafunika kukonza. Ndinafika msonkhano wachigawo utangotsala pang’ono kuchitika ndipo ndinagoma kuona anthu masauzande ambiri obwera ku msonkhano akugona pa malo a msonkhanowo. Ndinapereka maganizo oti pa msonkhano wotsatira, anthu obwera kumsonkhano adzagone m’nyumba za anthu. Abalewo anaona kuti amenewo ndi maganizo abwino, koma sangathandize m’dziko lawolo. Titakambirana nkhaniyo, tinagonjerana, ndipo tinagwirizana zoti theka la anthu obwera ku msonkhano
adzagona pa malo a msonkhano ndipo theka linalo adzagona m’nyumba za anthu omwe si Mboni mu mzinda wochitira msonkhanowo. Ndinamutchulira zimenezi M’bale Knorr monyadira ndithu pamene anabwera pamsonkhanowo. Koma maganizo alionse amene ndinali nawo oti ndachita zinthu bwino anatheratu pamene ndinadzawerenga lipoti la msonkhano wathu mu Nsanja ya Olonda. Lipotilo linati: “Tikukhulupirira kuti ulendo wotsatira abale adzakhala ndi chikhulupiriro chokwanira n’kuyesetsa kuti anthu obwera ku msonkhano adzagone m’malo abwino kwambiri kuchitirako umboni, omwe ndi makomo a anthu.” Zimenezo n’zimene tinachitadi “ulendo wotsatira”!Mu July 1961, nthumwi ziwiri za ofesi yathu ya nthambi zinaitanidwa ku msonkhano ku London limodzi ndi nthumwi za nthambi zina. M’bale Knorr analengeza kuti Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu lidzatulutsidwa m’zinenero zina, kuphatikizapo Chidatchi. Nkhani imeneyo inali yosangalatsa kwabasi! Ubwino wake unali woti sitinkadziwa kuti ntchito yotulutsa Baibulolo idzakhala yaikulu bwanji. Patatha zaka ziwiri, mu 1963, ndinali ndi mwayi wokhala nawo pa pulogalamu pa msonkhano ku New York pamene Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa m’Chidatchi.
Kusankha Zochita ndi Kupatsidwa Utumiki Wosiyanasiyana
Mu August 1961, ndinakwatira Leida Wamelink. Banja lawo lonse linaphunzira choonadi mu 1942 panthawi ya chizunzo cha chipani cha a Nazi. Leida anayamba kuchita upainiya mu 1950 ndipo anapita ku Beteli mu 1953. Mmene ankagwirira ntchito pa Beteli ndi mumpingo zinandisonyeza kuti akhoza kumandithandiza mokhulupirika pa utumiki wanga.
Patangotha chaka chimodzi titakwatirana, ndinaitanidwa ku Brooklyn kuti ndikachite maphunziro ena kwa miyezi 10. Panalibe makonzedwe oti akazi azitsagana ndi amuna awo. Ngakhale kuti Leida sanali bwino, mwachikondi analola kuti ndipite. Kenaka, matenda a Leida anakula. Tinayesera kutumikirabe pa Beteli, koma kenaka tinaona kuti zingakhale bwino kuti tikapitirize utumiki wathu wa nthawi zonse m’munda. Choncho tinayamba kutumikira mu utumiki woyendayenda. Patangodutsa nthawi yochepa, mkazi wanga anachitidwa opaleshoni yaikulu. Chifukwa chothandizidwa mwachikondi ndi anzathu, tinathana ndi vuto limeneli, ndipo patatha chaka chimodzi tinatha kuvomera kuti tizitumikira mu ntchito ya chigawo.
Tinasangalala kwa zaka 7 ndi ntchito yolimbikitsa yoyendayenda. Kenaka, ndinafunikiranso kusankha pa nkhani yaikulu pamene anandipempha kuti ndizikaphunzitsa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Beteli. Tinavomera, ngakhale kuti zinativuta kusintha moyo wathu popeza tinkakonda utumiki woyendayenda. Makalasi 47 a sukuluyi, iliyonse yotha milungu iwiri, anandipatsa mpata wabwino wogawana madalitso auzimu ndi akulu a mipingo.
Panthawi imeneyo, ndinali ndikukonzekera kukaona mayi anga mu 1978. Koma mwadzidzidzi, pa April 29, 1977, tinalandira telegalamu yotiuza kuti amayi amwalira. Ndinamva chisoni kwambiri pozindikira kuti sindidzamvanso mawu awo achikondi kapena kuwauzanso momwe ndimayamikirira zinthu zonse zomwe anandichitira.
Sukulu ya Utumiki wa Ufumu itatha, anatipempha kuti tikhale m’banja la Beteli. Pa zaka zotsatira, ndinatumikira kwa zaka 10 monga mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi. Patapita nthawi, Bungwe Lolamulira linasankha mgwirizanitsi watsopano, amene anali wokhoza bwino kusamalira udindo umenewu kuposa ineyo. Ndimayamikira kwambiri zimenezo.
Kutumikirabe Paukalamba
Ine ndi Leida tsopano tonse tili ndi zaka 83. Ndatumikira mosangalala kwa zaka 60 mu utumiki wa nthawi zonse, ndipo zaka 45 zomalizazo ndatumikira limodzi ndi mkazi wanga wokhulupirika. Iye amaona kuti kundithandiza kwake mu utumiki wosiyanasiyana wonse womwe tachita ndi mbali ya utumiki wake wodzipereka kwa Yehova. Panopa, timachita zomwe tingathe pa Beteli ndi mumpingo.—Yesaya 46:4.
Nthawi ndi nthawi, timasangalala kukumbukira zinthu zikuluzikulu zimene zatichitikira pa moyo wathu. Sitinong’oneza bondo poganizira zimene tachita mu utumiki wa Yehova, ndipo sitikayika ngakhale pang’ono kuti zimene tinasankha kuchita tidakali aang’ono ndi zinthu zabwino kwambiri zimene munthu angasankhe kuchita pamoyo. Ndife ofunitsitsa kupitiriza kutumikira ndi kulemekeza Yehova ndi mphamvu zathu zonse.
[Chithunzi patsamba 13]
Ndili ndi mkulu wanga Bill, ndi kavalo wathu Sauli
[Chithunzi patsamba 15]
Pa tsiku la ukwati wathu, mu August 1961
[Chithunzi patsamba 15]
Ndili ndi Leida panopo