Omaliza Maphunziro a Gileadi Anapatsidwa Malangizo Okhudza Mtima
Omaliza Maphunziro a Gileadi Anapatsidwa Malangizo Okhudza Mtima
PA SEPTEMBER 9, 2006, ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, mu mzinda wa New York, kunali mwambo womaliza maphunziro wa kalasi ya nambala 121 ya Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Unali mwambo wolimbikitsa kwambiri.
Geoffrey Jackson, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, potsegulira mwambowo anayamba n’kulandira anthu 56 omaliza maphunzirowo ndi omvera ena okwana 6,366 ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Anafotokoza lemba la Salmo 86:11, limene limati: “Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’choonadi chanu: muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.” M’bale Jackson anatchula zinthu zitatu zimene zagogomezeredwa m’vesi limenelo. Anati: “Mbali yoyambirirayo ikutchula za malangizo; yachiwiri ikutchula za kuwagwiritsa ntchito, ndipo yotsirizayo ikutchula za kulimbikitsidwa kuchitapo kanthu. Zinthu zitatu zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka kwa inu amishonale pamene mukupita ku magawo kwanu.” Kenaka anaitana anthu angapo amene anafunsa mafunso ndi kukamba nkhani zomwe zinagogomezera zinthu zitatu zonsezi.
Malangizo Olimbikitsa
William Malenfant, mmodzi wa anthu ogwira ntchito ku likulu, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Moyo Wabwino Kuposa Wina Uliwonse.” Anatchula za chitsanzo cha Mariya, m’bale wake wa Marita. Pa nthawi inayake Yesu atapita kunyumba kwawo, Mariya anasankha kukhala pa mapazi ake kuti amumvetsere, ndipo anaona kuti kuchita zimenezi ndiko kunali kofunika kwambiri. Yesu anauza Marita kuti: “Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri, ndipo sadzalandidwa chimenecho.” (Luka 10:38-42) Kenaka wokamba nkhaniyo anati: “Tangoganizirani zimenezo. Kwa umuyaya wonse, Mariya adzakumbukira kuti anakhala pa mapazi a Yesu n’kumumvetsera pamaso m’pamaso akufotokoza mfundo zabwino kwambiri za choonadi, ndipo zonsezi zinachitika chifukwa anasankha bwino zinthu.” Atawayamikira omaliza maphunzirowo chifukwa chosankha bwino zinthu, anati: “Zosankha zanu zakubweretserani moyo wabwino kuposa wina uliwonse.”
Kenaka Anthony Morris, wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Valani Ambuye Yesu Khristu,” wochokera pa Aroma 13:14. Kodi tingachite bwanji zimenezi? M’bale Morris anafotokoza kuti ‘kuvala Ambuye Yesu Khristu’ kumaphatikizapo kutsanzira makhalidwe a Ambuye. Choncho zimenezi zimatanthauza kutengera chitsanzo cha Yesu komanso mtima wake. Wokamba nkhaniyo anati: “Yesu ankachititsa anthu kumasuka naye, chifukwa ankakhala nawo chidwi chenicheni, ndipo anthuwo ankatha kuona zimenezo.” Kenaka wokamba nkhaniyo anafotokoza kuti ophunzirawo anadziwa zinthu zambiri pa maphunziro awo a Gileadi ndi ‘cholinga chakuti athe kudziwa bwino lomwe m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama’ kwa choonadi, monga momwe lemba la Aefeso 3:18 limanenera. Koma anawakumbutsa za vesi 19, lomwe limati: “Ndi kuti mudziwe chikondi cha Khristu chimene chiposa kudziwa zinthu konse.” M’bale Morris analimbikitsa ophunzirawo kuti: “Pochita phunziro lanu laumwini, ganizirani momwe mungatsanzirire chifundo ndi chikondi cha Khristu kuti ‘muvaledi Ambuye Yesu Khristu.’”
Malangizo Omaliza Ochokera kwa Alangizi a Gileadi
Nkhani yotsatira inakambidwa ndi mlangizi wa Gileadi Wallace Liverance, ndipo mutu wake unachokera pa Miyambo 4:7. Iye anati ngakhale kuti nzeru za Mulungu n’zofunika, tiyeneranso ‘kupeza luntha,’ kapena kuti kuzindikira, komwe kumatanthauza kusonkhanitsa mfundo zosiyanasiyana n’kuona momwe zikugwirizanirana n’cholinga choti tithe kumvetsa bwino nkhani yonse. Wokamba nkhaniyo anasonyeza kuti kuzindikira kumabweretsa chimwemwe. Mwachitsanzo, mu nthawi ya Nehemiya, Alevi ‘anatanthauzira chilamulo’ ndi ‘kuwazindikiritsa’ anthu. Kenaka, anthuwo ‘anasekerera kwakukulu; popeza anazindikira mawu amene adawafotokozera.’ (Nehemiya 8:7, 8, 12) M’bale Liverance anamaliza ndi mawu akuti: “Chimwemwe chimabwera chifukwa chozindikira bwino Mawu a Mulungu ouziridwa ndi mzimu.”
Mutu wa nkhani imene anakamba Mark Noumair, mlangizi wina wa Gileadi, unali wakuti “Kodi Mdani Wanu Weniweni Ndani?” Pankhondo, asilikali ambiri amaphedwa chifukwa chowomberedwa ndi asilikali a m’gulu lawo lomwe. Ndiye m’baleyu anafunsa kuti “Nanga bwanji pa nkhondo yauzimu imene tikumenya? Ngati sitisamala, tikhoza kusokonezeka n’kulephera kudziwa mdani wathu weniweni, kenaka n’kuvulaza asilikali a m’gulu lathu lomwe.” Ena angasokonezeke chifukwa cha nsanje. Nsanje inachititsa Mfumu Sauli kufuna kupha Davide, wolambira mnzake, pamene adani ake enieni anali Afilisti. (1 Samueli 18:7-9; 23:27, 28) Kenaka wokamba nkhaniyo anapitiriza n’kuti: “Bwanji ngati mukutumikira limodzi ndi mmishonale amene amachita bwino zinthu zambiri? Kodi mudzam’vulaza msilikali mnzanuyo pomunenera zinthu zoipa, kapena kodi mudzavomereza mfundo yoti anthu ena angathe kukuposani m’njira zina? Kuganizira kwambiri za kupanda ungwiro kwa ena kukhoza kungotisokoneza kuti tisadziwe bwino mdani wathu weniweni. Muzilimbana ndi mdani wathu weniweni, Satana.”
Zokumana Nazo Zosangalatsa ndi Mafunso Ophunzitsa
Nkhani yotsatira, yakuti “Gwira Ntchito ya Mlaliki,” inakambidwa ndi mlangizi wa Gileadi Lawrence Bowen ndipo inalinso ndi mbali ya kufunsa mafunso ndi kunena zokumana nazo. Anafotokoza kuti “ntchito yaikulu ya mmishonale wophunzitsidwa ku Gileadi ndi yofalitsa uthenga wabwino, ndipo anthu a m’kalasi ino anali kuchita zimenezo kulikonse komwe akanatha kupeza anthu.” Kenaka panali zitsanzo zabwino zedi zosonyeza zokumana nazo zina.
Pambuyo pake panabwera nkhani ziwiri. Imodzi inakambidwa ndi M’bale Michael Burnett, ndipo inayo inakambidwa ndi M’bale Scott Shoffner. Abale awiriwa ndi a m’banja la Beteli. Anafunsa mafunso anthu a m’Makomiti a Nthambi a ku Australia, Barbados, Korea, ndi ku Uganda. Mawu a anthu a m’makomiti a nthambiwa anasonyeza kuti amayesetsa kwambiri kusamalira amishonale, kuphatikizapo kuwapezera nyumba zabwino ndi kuwapititsa ku zipatala zomwe angapezeko chithandizo chabwino. Anthu a m’makomitiwo anagogomezera mfundo yoti amishonale amene zinthu zimawayendera bwino amakhala ofunitsitsa kusintha kuti agwirizane ndi zochitika za kumalo kumene ali.
Mawu Omaliza Olimbikitsa ndi Okhudza Mtima
Nkhani yaikulu pamwambowu inali ya mutu wakuti “Opani Mulungu ndi Kum’patsa Ulemerero,” yomwe inakambidwa ndi John E. Barr, amene wakhala nthawi yaitali m’Bungwe Lolamulira. Anafotokoza lemba la Chivumbulutso 14:6, 7, lomwe limati: “Ndinaona mngelo winanso akuuluka mu mlengalenga chapafupi. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa okhala padziko lapansi, ndi ku dziko lililonse, fuko, lilime, ndi mtundu uliwonse. Mofuula anali kunena kuti: ‘Opani Mulungu ndi kum’patsa ulemerero, chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika.’”
M’bale Barr analimbikitsa ophunzirawo kuti aganizire zinthu zitatu zokhudza mngelo ameneyo. Choyamba, anafunika kulengeza uthenga wabwino woti panopa Khristu akulamulira ndi mphamvu zonse za Ufumu. Wokamba nkhaniyo anati: “Sitikukayika ngakhale pang’ono kuti anaikidwa paufumu mu 1914. Choncho uthenga wabwino umenewu uyenera kulengezedwa pa dziko lonse lapansi.” Chachiwiri, mngeloyo anati: “Opani Mulungu.” Wokamba nkhaniyo anafotokoza kuti omaliza maphunzirowo ayenera kuthandiza ophunzira Baibulo awo kuti aziopa Mulungu kwambiri. Akatero sangachite chilichonse chomwe chingam’khumudwitse. Chachitatu, mngeloyo analamula kuti: ‘Patsani Mulungu ulemerero.’ Ophunzirawo analimbikitsidwa kuti: “Musamaiwale kuti timatumikira n’cholinga choti ulemerero upite kwa Mulungu, osati kwa ifeyo.” Kenaka, pofotokoza za “ola lakuti apereke chiweruzo,” M’bale Barr anati: “Nthawi yoti chiweruzo chomaliza chiperekedwe ikuyandikira kwambiri. Anthu ambiri m’magawo athu akufunikirabe kumva uthenga wabwino nthawi isanathe.”
Akuganizirabe za mawu amenewa, omaliza maphunziro 56 amenewo anapatsidwa madipuloma n’kutumizidwa ku malekezero a dziko. Omaliza maphunzirowo ndi ena onse omwe analipo anakhudzidwa mtima kwambiri ndi malangizo olimbikitsa amene anapatsidwa pa tsiku losangalatsalo.
[Bokosi patsamba 17]
ZA OPHUNZIRAWO
Chiwerengero cha mayiko amene ophunzira anachokera: 6
Chiwerengero cha mayiko amene anawatumiza: 25
Chiwerengero cha ophunzira: 56
Avereji ya zaka zakubadwa: 35.1
Avereji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 18.3
Avereji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 13.9
[Chithunzi patsamba 18]
Kalasi ya Nambala 121 ya Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo
Pa m’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliwonse.
(1) Fox, Y.; Kunicki, D.; Wilkinson, S.; Kawamoto, S.; Consolandi, G.; Mayen, C. (2) Santiago, N.; Clancy, R.; Fischer, M.; de Abreu, L.; Davis, E. (3) Hwang, J.; Hoffman, D.; Wridgway, L.; Ibrahim, J.; Dabelstein, A.; Bakabak, M. (4) Peters, M.; Jones, C.; Ford, S.; Parra, S.; Rothrock, D.; Tatlot, M.; Perez, E. (5) de Abreu, F.; Kawamoto, S.; Ives, S.; Burdo, J.; Hwang, J.; Wilkinson, D. (6) Fox, A.; Bakabak, J.; Cichowski, P.; Forier, C.; Mayen, S.; Consolandi, E.; Wridgway, W. (7) Parra, B.; Perez, B.; Tatlot, P.; Santiago, M.; Ibrahim, Y.; Kunicki, C. (8) Burdo, C.; Cichowski, B.; Ives, K.; Ford, A.; Rothrock, J.; Hoffman, D.; Davis, M. (9) Peters, C.; Dabelstein, C.; Jones, K.; Clancy, S.; Fischer, J.; Forier, S.