Zimene Mungachite Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino
Zimene Mungachite Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino
MONGA mmene makolo amasamalira ana, Atate wathu wa kumwamba amatisamalira ndipo amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino. Amasonyeza zimenezi potiuza mfundo zambiri zokhudza kuyenda bwino kapena kusayenda bwino kwa zinthu. Ponena za munthu amene amamvera zomwe Mulungu amanena, Baibulo limanena motsindika kuti: “Zonse azichita apindula nazo.”—Salmo 1:3.
Ngati zili choncho, n’chifukwa chiyani anthu ambiri sizikuwayendera bwino ndipo sakukhala moyo wosangalatsa ndiponso wokhutiritsa? Kumvetsetsa zimene salmo limeneli limanena kungatipatse yankho ndipo kungatisonyeze zomwe ifenso tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino.
“Uphungu wa Oipa”
Wamasalmo anachenjeza za kuyenda mu “uphungu wa oipa.” (Salmo 1:1) ‘Woipa’ wamkulu ndi Satana Mdyerekezi. (Mateyo 6:13) Malemba amatiuza kuti iye ndi “wolamulira wa dziko lino” ndiponso kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (Yohane 16:11; 1 Yohane 5:19) Choncho n’zosadabwitsa kuti malangizo ambiri amene timawamva m’dzikoli amasonyeza maganizo a woipayo.
Ndi malangizo otani amene anthu oipa amapereka? Nthawi zambiri oipa ‘amanyoza Mulungu.’ (Salmo 10:13) Malangizo awo ochititsa kuti tizinyalanyaza kapena kunyoza Mulungu, amapezeka ponseponse. Dzikoli masiku ano limalimbikitsa “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pamoyo wake.” (1 Yohane 2:16) Mawailesi, manyuzipepala ndi zina zotero, zimalimbikitsa maganizo akuti tiyenera kupeza “chilichonse chapamwamba chomwe tingathe kupeza pamoyo wathu.” Padziko lonse, makampani amawononga ndalama zopitirira madola 500 biliyoni chaka ndi chaka potsatsa malonda, kuti anthu agule malondawo, kaya anthuwo akufunikiradi kukhala ndi zinthuzo kapena ayi. Kutsatsa malonda kotereku sikuti kwangosintha maganizo a anthu pa nkhani yogula katundu. Kwasinthanso maganizo a anthu a m’dzikoli okhudza zinthu zimene amaona mwa munthu kuti adziwe kuti zikumuyendera bwino.
Chifukwa cha zimenezi, anthu akungolakalakabe atakhala ndi zinthu zochuluka, ngakhale kuti ali ndi zinthu zomwe m’mbuyomu ankangolota atakhala nazo. Amaganiza zoti munthu sangakhale wosangalala ngati alibe zinthu zimenezi. Maganizo amenewa ndi abodza ndipo ‘sachokera kwa Atate, koma ku dziko.’—1 Yohane 2:16.
Mlengi wathu amadziwa zimene zingapangitse kuti zinthu zizitiyenderadi bwino. Malangizo ake ndi osiyana ndi “uphungu wa oipa.” Choncho, kuyesetsa kuti tiyanjidwe ndi Mulungu pamene tikuyesa kutsatira njira ya dzikoli yoti zinthu zizitiyendera bwino, kuli ngati kuyesa kuyenda pamisewu Aroma 12:2.
iwiri panthawi imodzi. Zimenezi n’zosatheka n’komwe. N’chifukwa chaketu Baibulo limatichenjeza kuti: “Musamatengere nzeru za dongosolo lino la zinthu.”—Musatengeke ndi Dzikoli
Dziko lolamulidwa ndi Satanali, limaoneka ngati likukufunirani zabwino. Koma tisamale. Kumbukirani kuti Satana ananyengerera mkazi woyamba, Hava, kuti akwaniritse zofuna zadyera za Satanayo. Kenako anam’gwiritsa ntchito kunamiza Adamu kuti atsatire njira yauchimo. Masiku anonso Satana akugwiritsa ntchito anthu popereka malangizo ake oipa.
Mwachitsanzo, David yemwe tamutchula m’nkhani yapitayi, ankafunika kuti azigwira ntchito kwa maola owonjezera komanso kumayenda pafupipafupi maulendo opita kukagwira ntchito. David anati: “Ndinkanyamuka Lolemba m’mamawa n’kubwerako Lachinayi madzulo.” Poganiza kuti kudzipereka koteroko kunali kofunika kuti zinthu zizimuyendera bwino malinga ndi mmene anthu m’dzikoli amaonera, anzake apamtima, abale ake, ndiponso anzake akuntchito ankamulimbikitsa kuti “azichita zimenezi n’cholinga choti athandize banja lake.” Ankaona kuti achita zimenezi kwa zaka zochepa chabe mpaka adzafike pokhazikika. David anafotokoza kuti: “Iwo ankaganiza kuti zimenezi zingathandize banja langa, chifukwa choti ndikanatha kuwabweretsera ndalama zochuluka ndipo zinthu zikanatha kumandiyendera bwino. Ngakhale kuti nthawi zambiri sindinkakhala ndi banja langa, anzanga ankalimbikira kunena kuti ndinali kulisamalira bwino.” Pali anthu ambiri onga David, amene akugwira ntchito molimbika kuti apeze chilichonse chomwe akuganiza kuti banja lawo likuchifuna. Koma kodi kutsatira malangizo oterewa kumachititsadi kuti zinthu zizikuyenderani bwino? Kodi n’chiyani kwenikweni chimene banja lanu limafunikiradi?
David anadziwa chomwe banja lake linkafunikira pamene anali paulendo wokagwira ntchito. Iye anati: “Ndinkalankhula pa foni ndi mwana wanga wamkazi Angelica, amene anandifunsa kuti: ‘Ababa, kodi n’chifukwa chiyani simufuna kumakhala nafe panyumba?’ Zimenezi zinandikhudza kwambiri.” Zomwe mwana wakeyo ananena zinam’limbikitsa kulemba kalata yosiyira ntchito. David anaganiza zoti ayambe kumakhala ndi banja lake n’kumacheza nalo nthawi zambiri, chifukwa zimenezo n’zimene banjalo linkasowa.
Zinthu Zimatiyendera Bwino Tikamatsatira Malangizo a Mulungu
Kodi mungalimbane bwanji ndi maganizo olakwika ofala a m’dzikoli? Wamasalmo amatiuza kuti munthu amene zikumuyendera bwino ndiponso wachimwemwe ndi amene “m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.”—Salmo 1:2.
Mulungu atamusankha Yoswa kuti akhale mtsogoleri wa mtundu wa Isiraeli, anamuuza kuti: “Ulingiriremo [m’mawu a Mulungu] usana ndi usiku.” Inde, kuwerenga ndi kulingirira kunali kofunika, koma Yoswa anafunikanso kuti ‘asamalire kuchita monga mwa zonse zomwe zinalembedwamo.’ Ndi zoona kuti kuwerenga Baibulo pakokha sikungapangitse kuti zinthu zizikuyenderani bwino. M’pofunika kugwiritsa ntchito zimene mukuwerenga. Yoswa anauzidwa kuti: “Ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.”—Yoswa 1:8.
Taganizani za kamwana komwe kakhala pamiyendo ya kholo lake n’kumawerenga limodzi kankhani kosangalatsa. Ngakhale atakhala kuti anawerengapo kale nkhaniyo maulendo ambirimbiri, amasangalala nthawi iliyonse imene akuchita zimenezi. N’chimodzimodzinso ndi munthu yemwe amakonda Mulungu. Amaona kuti kuwerenga Baibulo n’kosangalatsa, ndipo amaona kuti imeneyi ndi nthawi yosangalatsa zedi yocheza ndi Atate wake wakumwamba. Munthu akamatsatira malangizo a Yehova n’kumatsogozedwa naye, amakhala ngati “mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.”—Mtengo umene wamasalmo akutchula sikuti unangomera wokha. Unadzalidwa bwinobwino m’mphepete mwa madzi ndipo umasamalidwa ndi mlimi. Chimodzimodzinso, Atate wathu wakumwamba amawongola ndiponso kukonza maganizo athu kudzera m’malangizo opezeka m’Malemba. Zikatero, timasonyeza zipatso zaumulungu.
Komabe, “oipa satero ayi.” Ndi zoona kuti angaoneke ngati zinthu zikuwayendera bwino kwa kanthawi, koma m’kupita kwa nthawi zinthu zimadzawatembenukira. “Oipa sadzaimirira pa mlanduwo.” M’malo mwake, “mayendedwe a oipa adzatayika.”—Salmo 1:4-6.
Choncho musalole kuti dzikoli lizikukakamizani kusankha zochita molakwika. Ngakhale mutakhala ndi luso loti mukhoza kufika penapake m’dzikoli, samalani ndi mmene mumagwiritsira ntchito luso lanulo kapena ndi mmene mumalolera kuti dzikoli ligwiritsire ntchito lusolo. Kufunafuna zinthu zakuthupi zopanda phindu kungachititse munthu ‘kufota.’ Mosiyana ndi zimenezi, kukhala ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu kumachititsa kuti zinthu zizikuyenderani bwinodi komanso kuti mukhale ndi chimwemwe chenicheni.
Zimene Mungachite Kuti Zizikuyenderani Bwino
N’chifukwa chiyani munthu akamatsatira malangizo a Mulungu, zonse zimene amachita amapindula nazo, kapena kuti zimamuyendera bwino? Wamasalmo sankanena za kupindula kwa m’dzikoli. Kupindula kwa munthu woopa Mulungu n’kogwirizana ndi kuchita kwake chifuniro cha Mulungu, ndipo chifuniro cha Mulungu nthawi zonse chimayenda bwino. Tiyeni tione mmene kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo kungakuthandizireni kuti zinthu zizikuyenderani bwino.
M’banja: Malemba amalimbikitsa amuna kuti “akonde akazi awo monga matupi awoawo” ndipo mkazi wachikhristu akulangizidwa kuti “akhale ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.” (Aefeso 5:28, 33) Makolo amalimbikitsidwa kucheza ndi ana awo, kuseka nawo, ndiponso kuwaphunzitsa zinthu zofunika m’moyo. (Deuteronomo 6:6, 7; Mlaliki 3:4) Mawu a Mulungu amalangizanso makolo kuti: “Musamapsetse mtima ana anu.” Malangizo amenewa akamagwiritsidwa ntchito, n’kosavuta kwa ana kuti ‘azimvera makolo awo’ ndiponso ‘kulemekeza atate awo ndi amayi awo.’ (Aefeso 6:1-4) Kutsatira malangizo ouziridwa amenewa kungachititse kuti banja lanu liziyenda bwino.
Mabwenzi: Anthu ambiri amafuna kukhala ndi mabwenzi. Timalakalaka kuti tizikonda anthu ena komanso kuti anthu ena azitikonda. Yesu anauza ophunzira ake kuti ‘azikondana.’ (Yohane 13:34, 35) Pakati pa ophunzira amenewa timapezapo mabwenzi amene tingawakonde komanso kuwakhulupirira, ngakhale kuwauza zakukhosi kwathu. (Miyambo 18:24) Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti, tikamagwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo, tikhoza ‘kuyandikira kwa Mulungu’ ndipo monga Abulahamu tingatchedwe “bwenzi la Yehova.”—Yakobe 2:23; 4:8.
Kukhala ndi Cholinga Pamoyo: M’malo momangokhala moyo wopanda cholinga, anthu omwe zikuwayenderadi bwino, amapeza cholinga chenicheni cha moyo. Moyo wawo sudalira zinthu zopanda tsogolo zomwe zili m’dzikoli. Chifukwa chakuti zolinga zawo zimakhala zogwirizana kwambiri ndi moyo weniweni, zimawabweretsera chisangalalo chenicheni ndiponso chokhalitsa. Kodi n’chiyani chomwe chingam’chititse munthu kukhala ndi cholinga m’moyo? “Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.” (Mlaliki 12:13)
Chiyembekezo: Mulungu akakhala Bwenzi lathu, timakhala ndi chiyembekezo cham’tsogolo. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti “asadalire chuma chosadalirika, koma adalire Mulungu.” Mwakuchita zimenezi, akanatha “kudzisungira okha maziko abwino a tsogolo lawo, kuti akagwire zolimba moyo weniweniwo.” (1 Timoteyo 6:17-19) Moyo weniweni umenewu udzabwera posachedwapa pamene Ufumu wakumwamba wa Mulungu udzabwezeretsa Paradaiso padziko lino.—Luka 23:43.
Mukamagwiritsa ntchito malangizo a Baibulo, sindiye kuti simudzakumana ndi mavuto, koma mudzatha kupewa mavuto osiyanasiyana komanso kuwawidwa mtima komwe oipa amadzibweretsera okha. David, yemwe tam’tchula poyamba uja, ndiponso anthu ena mamiliyoni ambiri onga iye aphunzira phindu la kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo m’moyo wawo. Atapeza ntchito yomwe inatha kum’patsa mpata, David anati: “Ndine wokondwa chifukwa cha ubwenzi womwe ndili nawo ndi mkazi wanga ndi ana anga komanso mwayi womwe ndili nawo wotumikira Yehova Mulungu monga mkulu mu mpingo.” N’chifukwa chake salmo limanena za munthu amene amamvera malangizo a Mulungu kuti: “Zonse azichita apindula nazo”!
[Tchati patsamba 6]
MFUNDO ZISANU ZOMWE ZINGAKUTHANDIZENI KUTI ZINTHU ZIZIKUYENDERANI BWINO
1 Pewani kutengeka ndi zolinga za dzikoli.
2 Werengani ndi kusinkhasinkha za Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku.
3 Gwiritsani ntchito malangizo a m’Baibulo m’moyo wanu.
4 Pangani ubwenzi ndi Mulungu.
5 Opani Mulungu woona ndipo sungani malamulo ake.
[Zithunzi patsamba 7]
Kodi mukutsatira mfundo zomwe zingakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino?