Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupita Patsogolo kwa Ntchito Yopanga Mabaibulo a Zinenero za mu Africa

Kupita Patsogolo kwa Ntchito Yopanga Mabaibulo a Zinenero za mu Africa

Kupita Patsogolo kwa Ntchito Yopanga Mabaibulo a Zinenero za mu Africa

ANTHU okonda kuwerenga Baibulo ochokera ku Ulaya ndi ku North America anazindikira kalekale kuti n’kofunika kuti anthu a ku Africa athe kuwerenga Mawu a Mulungu m’zinenero zawo. Kuti akwaniritse cholingacho, anthu ambiri anapita ku Africa kuti akaphunzire zinenero za kumeneko. Anthu ena anayambitsa kalembedwe ka zinenerozo ndipo anapanganso mabuku otanthauzira mawu. Atachita zimenezi, anayamba kumasulira Baibulo m’zinenero zambiri za mu Africa. Imeneyi sinali ntchito yophweka ayi. Buku la The Cambridge History of the Bible limati: “Mwina munthu ayenera kufufuza zaka zambiri kuti apeze mawu abwino ofotokoza ngakhale mfundo zosavuta kwambiri zikuluzikulu zachikhristu.”

M’chaka cha 1857 Atswana anali oyamba kukhala ndi Baibulo lonse, ndipo chinenero chawo chinali chimodzi mwa zinenero za mu Africa zomwe zinali zisanayambe kulembedwa. * Baibulolo linasindikizidwa m’mabuku aang’onoang’ono osati m’buku limodzi lalikulu. M’kupita kwa nthawi, Mabaibulo anayambanso kutulutsidwa m’zinenero zina za mu Africa. Ambiri a Mabaibulo amenewa anali ndi dzina la Mulungu, Yehova, m’Malemba Achiheberi, kapena kuti “Chipangano Chakale,” ndi m’Malemba Achigiriki Achikristu, kapena kuti “Chipangano Chatsopano.” Komabe, Mabaibulo atsopano ankamasuliridwa ndi kusinthidwanso ndi anthu omwe sankalemekeza dzina loyera la Mlembi wa Baibulo, Yehova. Iwowo ankatsatira mwambo wachiyuda wochotsa dzina la Mulungu n’kuika m’malo mwake mayina aulemu monga ngati Mulungu kapena Ambuye. Choncho, panafunika kuti anthu okonda Mulungu mu Africa akhale ndi Baibulo lomwe labwezeretsa dzina la Mulungu.

Kuyambira m’zaka za m’ma 1980, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lakhala likuyesetsa kuti Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu limasuliridwe m’zinenero zikuluzikulu zambiri za mu Africa. N’chifukwa chake masiku ano, anthu ambiri okonda Baibulo mu Africa amatha kuwerenga Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenero zawo. Panopa, Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu kapena mbali zake likupezeka m’zinenero 17 za mu Africa.

Anthu owerenga Mabaibulo amenewa a zinenero za mu Africa amasangalala kwambiri kukhala ndi Baibulo limene limagwiritsa ntchito dzina lolemekezeka la Mulungu, lakuti Yehova. Mwachitsanzo, pamene Yesu anaimirira m’sunagoge ku Nazarete, analengeza ntchito yake mwa kuwerenga mu mpukutu wa Yesaya, mmene dzina la Atate wake limapezeka. (Yesaya 61:1, 2) Malinga ndi Uthenga Wabwino wa Luka monga mmene unamasuliridwira mu Baibulo la Dziko Latsopano, Yesu anawerenga kuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi za kuchiritsidwa kwa akhungu. Inde, kudzamasula oponderezedwa kuti apite monga mfulu, kudzalalikira chaka chokomera Yehova.”​Luka 4:18, 19.

Zinthu zina zosangalatsa pa ntchito yopanga Mabaibulo a zinenero za mu Africa zinachitika m’mwezi wa August 2005. M’mwezi umenewu, Mabaibulo okwanira 76,000 a Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenero za mu Africa anasindikizidwa ku nthambi ya Mboni za Yehova ya ku South Africa. Pa Mabaibulo amenewa, 30,000 anali a Chishona. Baibulo la Chishonali linatulutsidwa ku Zimbabwe pa Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova yakuti “Kumvera Mulungu.”

M’mwezi wosaiwalikawu, alendo obwera kudzaona nthambi ya ku South Africa anasangalala kwabasi kuona Mabaibulo a zinenero za mu Africa akusindikizidwa. Mbale wina dzina lake Nhlanhla yemwe amagwira ntchito yomata mabuku ku Beteli ananena kuti: “Ndinkasangalala ndi kukondwera kwambiri kukhala ndi mwayi wothandiza kupanga Baibulo la Dziko Latsopano m’Chishona ndi m’zinenero zina za mu Africa.” Ndipotu, iye anafotokoza bwino lomwe mmene onse a m’banja la Beteli la ku South Africa anali kumvera.

Panopa Mabaibulo atsopano adzafikira anthu a mu Africa mwamsanga ndi mopanda kuwononga ndalama zambiri kuposa pamene anali kusindikizidwa kunja kwa Africa n’kumatumizidwa kuchokera kumeneko. Koma chofunika kwambiri n’choti anthu a mu Africa tsopano angapeze mosavuta Baibulo lomasuliridwa molondola lomwe limagwiritsa ntchito dzina loyera la Mlembi wamkulu wa Baibulo, Yehova Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Pofika m’chaka cha 1835, Baibulo linali litamasuliridwa m’chinenero cha ku Madagascar chotchedwa Chimalagase, ndipo pofika m’chaka cha 1840, m’chinenero cha ku Ethiopia chotchedwa Chiamuhariki. Koma Baibulo lisanamasuliridwe, zinthu zina zinali zitalembedwapo kalekale m’zinenerozi.

[Chithunzi patsamba 12]

Dzina la Mulungu m’Baibulo la Chitswana lomwe linapangidwa mu 1840.

[Mawu a Chithunzi]

Harold Strange Library of African Studies

[Chithunzi patsamba 13]

Alendo ochokera ku Swaziland akuona Mabaibulo atsopano akupangidwa ku nthambi ya ku South Africa