Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi mlaliki anapeza “mwamuna mmodzi mwa chikwi” koma sanapeze “mkazitu mwa onsewo” m’lingaliro lotani?—Mlaliki 7:28.
Kuti mawu ouziridwawa tiwamve molondola, choyamba tiyenera kudziwa mmene Mulungu amaonera akazi. Baibulo limafotokoza kuti Rute, mpongozi wa mkazi wamasiye Naomi, anali “mkazi wabwino kwambiri.” (Rute 3:11, NW) Malinga ndi lemba la Miyambo 31:10, mkazi wabwino “mtengo wake uposa ngale.” Choncho, kodi Mfumu Solomo ya ku Isiraeli inatanthauza chiyani pamene inati: “Ndapeza . . . mwamuna weniweni mmodzi pa amuna 1000, koma mkazi weniweni sindinam’peze”?—Moffatt.
Nkhaniyo imasonyeza kuti akazi ambiri m’nthawi ya Solomo analibe makhalidwe abwino. (Mlaliki 7:26) Mwina zimenezi zinachitika makamaka chifukwa chotengera chitsanzo cha akazi achilendo amene ankalambira Baala. Ngakhalenso Mfumu Solomo inagonjera akazi ake ambirimbiri achilendo. Baibulo limati: “Anali nawo akazi mazana asanu ndi awiri, ana aakazi a mafumu, ndi akazi achabe mazana atatu; ndipo akazi ake anapambutsa mtima wake.” (1 Mafumu 11:1-4) Khalidwe la amuna nalonso silinali labwino. Kupeza mwamuna wolungama mmodzi pa amuna 1000 zikutanthauzanso kuti amuna abwino anali osowa, kapena tingangoti kunalibe. Choncho Solomo anamaliza ndi mawu akuti: “Ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu.” (Mlaliki 7:29) Ponena mawu amenewa anali kufotokoza za anthu, kutanthauza mtundu wonse wa anthu, osati poyerekezera amuna ndi akazi. Choncho mawu opezeka pa Mlaliki 7:28 tiyenera kuwaona kuti ndi mawu onena za khalidwe la anthu m’nthawi ya Solomo.
Komabe, vesi limeneli likhozanso kukhala ndi tanthauzo lina. Likhoza kukhala ulosi, chifukwa palibe mkazi amene anamverapo Yehova mwangwiro. Koma pali mwamuna mmodzi amene anachitapo zimenezi. Mwamuna ameneyu ndi Yesu Khristu.—Aroma 5:15-17.
[Chithunzi patsamba 31]
“Mwamuna mmodzi mwa chikwi”