Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musafooke Mwana Wanu Akapanduka

Musafooke Mwana Wanu Akapanduka

Musafooke Mwana Wanu Akapanduka

MAYI wina wachikhristu amene timutche Joy anayesetsa kulera mwana wake m’njira yoti azikonda Yehova Mulungu. Koma mwanayo atatsala pang’ono kukwanitsa zaka 20, anapanduka n’kuchoka panyumba. Joy anati: “Zimenezi zinandipweteka kwambiri kuposa chinthu china chilichonse. Mwanayo anandigwiritsa fuwa lamoto n’kundikhumudwitsa, ndipo ndinasweka mtima. M’mutu mwanga munangodzaza maganizo oipa okhaokha.”

Mwina nanunso mwayesetsa kulera ana anu m’njira yoti azikonda Mulungu ndi kumutumikira, koma kenaka mmodzi kapena angapo anasiya kutumikira Mulungu. Kodi mungatani kuti mupirire mukakhumudwitsidwa kwambiri choncho? N’chiyani chingakuthandizeni kuti musafooke pa utumiki wanu kwa Yehova?

Ana a Yehova Atapanduka

Choyamba, muyenera kuzindikira kuti Yehova akudziwa ndendende mmene mukumvera. Pa Yesaya 49:15 timawerenga kuti: “Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wom’bala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.” Zoonadi, Yehova amamva mofanana ndi mmene atate ndi amayi amamvera. Choncho tangoganizani mmene anasangalalira panthawi imene angelo onse, omwe ndi ana ake, anali kumutamanda ndi kumutumikira. Poyankha munthu wakale Yobu “m’kavumvulu,” Yehova anakumbukira nthawi yomwe ankasangalala limodzi ndi banja lake la zolengedwa zauzimu. Iye anati: “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? . . . Muja nyenyezi za m’mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?”​—Yobu 38:1, 4, 7.

M’kupita kwa nthawi, Mulungu woona anaona mwana wake mmodzi wangwiro, yemwe anali mngelo, akumupandukira n’kukhala Satana, kutanthauza “Wotsutsa.” Yehova anaonanso mwana wake woyamba waumunthu, Adamu, ndi mkazi wake wangwiro, Hava, nawonso akupanduka. (Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9) Kenaka ana ena omwe anali angelo “anasiya malo awo okhala” n’kupandukira Mulungu.​—Yuda 6.

Malemba satiuza mmene Yehova anamvera pamene ana ake ena angwiro nawonso anapanduka. Komabe, Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha. Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anavutika m’mtima mwake.” (Genesis 6:5, 6) Kupanduka kwa anthu osankhidwa a Yehova, Aisiraeli, nakonso ‘kunam’mvetsa chisoni’ ndi kumupweteka kwambiri.​—Salmo 78:40, 41.

N’zosakayikitsa kuti Yehova amawamvetsa makolo amene amamva ululu ndi chisoni chifukwa cha khalidwe la ana opanduka. M’Mawu ake, Baibulo, iye wapereka malangizo othandiza ndi mfundo zolimbikitsa kuti athandize makolo oterowo kupirira mavuto awo. Mulungu amawalimbikitsa kuti amutulire nkhawa zawo, adzichepetse, ndiponso alimbane ndi Satana Mdyerekezi. Tiyeni tione mmene kutsatira malangizo amenewa kungakuthandizireni kuti musafooke mwana wanu akapanduka.

Tulirani Yehova Nkhawa Zanu

Yehova amadziwa kuti makolo amada nkhawa kwambiri akaona kuti ana awo ali pangozi yoti akhoza kudzivulaza kapena kuvulazidwa ndi anthu ena. Mtumwi Petulo anatchula njira imodzi yolimbanirana ndi nkhawa imeneyi komanso nkhawa zina. Analemba kuti: ‘Mum’tulire [Yehova] nkhawa zanu zonse, pakuti amasamala za inu.’ (1 Petulo 5:7) Kodi mawu olimbikitsa ndi otsitsimula amenewa angathandize bwanji makamaka makolo amene mwana wawo wapanduka?

Pamene mwana wanu anali wamng’ono, munkayesetsa kumuteteza ku zinthu zoipa, ndipo mosakayikira mwanayo ankamvera malangizo achikondi amene munkam’patsa. Koma pamene anali kukula, mwina simunafunike kumuchitira zambiri pomuteteza, ngakhale kuti mtima wanu wofuna kumuteteza ku zinthu zoipa unalipobe. Ndipotu, mwina unakula kwambiri.

N’chifukwa chake, mwana wanu akapanduka n’kuvulazidwa mwauzimu, m’maganizo, kapena m’thupi, mungaganize kuti ndi inuyo amene mwachititsa zimenezi. Joy, amene tinamutchula kale uja, anamva choncho. Iye anati: “Tsiku lililonse, chifukwa chodziona kuti ndine wolephera, ndinkangokhalira kuganizira zinthu zimene zinachitika kale kuti ndione pamene ndinalakwitsa.” Makamaka panthawi ngati zimenezi m’pamene Yehova amafuna kuti ‘mum’tulire nkhawa zanu zonse.’ Mukatero, adzakuthandizani. Wamasalmo anati: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Joy analimbikitsidwa m’njira imeneyi. Anafotokoza kuti: “Ndinkamuuza Yehova zonse zomwe ndinkamva mumtima mwanga. Ndinkamutsanulira maganizo anga onse, ndipo ndinkamva bwino kwambiri pambuyo pake.”

Popeza ndinu kholo lopanda ungwiro, mwina munalakwitsa zinthu zina ndi zina polera mwana wanu. Koma kodi pali chifukwa chomangokhalira kuganiza za zimenezi? Zikuoneka kuti Yehova samangokhalira kuganiza za zolakwa zathu, chifukwa wamasalmo pouziridwa anaimba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chiriri ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Ngakhale mukadapanda kulakwitsa chilichonse, mwana wanu mwina akanapandukabe. Choncho muuzeni Yehova momwe mukumvera, ndipo adzakuthandizani kupirira. Komabe, kuti inuyo panokha musafooke potumikira Yehova ndipo mupewe kugwera mu msampha wa Satana, mufunika kuchita zambiri kuposa zimenezi.

Dzichepetseni

Petulo analemba kuti: “Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti m’nthawi yake akakukwezeni.” (1 Petulo 5:6) N’chifukwa chiyani pamafunika kudzichepetsa mwana wanu akapanduka? Kuwonjezera pa kukuchititsani kumva ululu komanso kumva kuti ndinu wolakwa, kukhala ndi mwana wopanduka kukhozanso kukuchititsani manyazi. Mukhoza kumada nkhawa kuti zochita za mwana wanu zawononga mbiri ya banja lanu, makamaka ngati anachotsedwa mumpingo. Kudziimba mlandu ndi kuchita manyazi kukhoza kukuchititsani kuti musamafune kupita ku misonkhano yachikhristu.

Mukamalimbana ndi vuto limeneli, muyenera kuchita zinthu mwanzeru. Lemba la Miyambo 18:1 limati wodzipatula “afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.” Mukamapita ku misonkhano yachikhristu nthawi zonse ngakhale muli ndi chisoni, mudzalandira malangizo ndi chilimbikitso chofunika kwambiri. Joy anavomereza kuti: “Poyamba, sindinkafuna kuonana ndi munthu aliyense. Koma ndinadzikumbutsa za kufunika kosasintha chizolowezi changa chochita zinthu zauzimu. Komanso ndikanakhala kunyumba, mwina bwenzi ndikungodandaula za mavuto angawo. Misonkhano inandithandiza kuganizira kwambiri zinthu zauzimu zolimbikitsa. Ndimayamikira kwambiri kuti sindinadzipatule n’kutaya mwayi wolimbikitsidwa mwachikondi ndi abale ndi alongo anga.”​—Aheberi 10:24, 25.

Kumbukiraninso kuti munthu aliyense m’banja “ayenera kunyamula katundu wakewake” monga Mkhristu. (Agalatiya 6:5) Yehova amayembekezera makolo kukonda ana awo ndi kuwalanga. Amayembekezeranso ana kumvera ndi kulemekeza makolo awo. Makolo akayesetsa kwambiri kulera ana awo “m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake,” makolowo amakhala ndi mbiri yabwino kwa Mulungu. (Aefeso 6:1-4) Mwana akapandukira malangizo achikondi a makolo, mbiri ya mwanayo ndi imene imawonongeka. Lemba la Miyambo 20:11 limati: “Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.” Mwachitsanzo, kupanduka kwa Satana sikunawononge mbiri ya Yehova kwa anthu amene amaimvetsa bwino nkhaniyo.

Mulimbane Naye Mdyerekezi

Petulo anachenjeza kuti: “Sungani maganizo anu, khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.” (1 Petulo 5:8) Mofanana ndi mkango, Mdyerekezi nthawi zambiri amazembera ana ndi anthu osadziwa zinthu zambiri. Kale, mikango inkayendayenda ku Isiraeli ndipo inkaopseza ziweto zapakhomo. Mwana wa nkhosa akasochera n’kuchoka pa gulu la nkhosa zinzake, ankatha kugwidwa mosavuta. Nkhosa yaikazi inkatha kuika moyo wake pachiswe kuti iteteze mwana wake. Komabe, ngakhale nkhosa yaikulu singathe kulimbana ndi mkango. Choncho pankafunika abusa olimba mtima kuti ateteze nkhosazo.​—1 Samueli 17:34, 35.

Kuti ateteze nkhosa zake zophiphiritsira kwa “mkango wobangula,” Yehova wakonza zoti abusa auzimu azisamalira nkhosa motsogozedwa ndi “m’busa wamkulu,” Yesu Khristu. (1 Petulo 5:4) Petulo analimbikitsa amuna oikidwa paudindo oterowo kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe anakuikizani, osati mokakamizika, koma mwaufulu; osatinso chifukwa chofuna kupindulapo, koma ndi mtima wonse.” (1 Petulo 5:1, 2) Makolonu mukagwirizana nawo, abusa amenewa akhoza kuthandiza wachinyamata kuti asinthe khalidwe lake.

Abusa achikhristu akafuna kum’patsa uphungu mwana wanu wopanduka, mwina mungafune kumuteteza ku chilangocho. Koma kuchita zimenezo kungakhale kulakwitsa kwambiri. Petulo anati: “Mulimbane naye [Mdyerekezi],” osati abusa auzimu.​—1 Petulo 5:9.

Chilango Chikakhala Chokhwima

Ngati mwana wanu sakulapa ndipo ndi Mkhristu wobatizidwa, akhoza kupatsidwa chilango chokhwima kuposa zonse, chomwe ndi kuchotsedwa mumpingo. Zikatero, kuchuluka kwa nthawi imene mungamakhalire naye limodzi kudzadalira msinkhu wake ndi zochitika zina.

Ngati mwanayo ndi wamng’ono ndipo mukukhala naye panyumba, mwachidziwikire mudzapitirizabe kumusamalira. Amafunikanso kumuphunzitsa ndi kumulangiza, ndipo inuyo muli ndi udindo womuchitira zimenezi. (Miyambo 1:8-18; 6:20-22; 29:17) Mwina mukhoza kumachita naye phunziro la Baibulo, iyeyo n’kumayankhapo. Mukhoza kumusonyeza malemba osiyanasiyana ndi mabuku a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyo 24:45) Mukhozanso kumapita ndi mwanayo ku misonkhano yachikhristu n’kumakhala naye pamodzi. Mukhoza kuchita zonsezi n’chiyembekezo choti mwina adzamvera malangizo a m’Malemba.

Koma n’zosiyana ngati wochotsedwayo ndi wachikulire amene akukhala kwayekha. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kale ku Korinto kuti: “Muleke kuyanjana ndi aliyense wotchedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, wolalata, chidakwa, kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi.” (1 Akorinto 5:11) Ngakhale kuti mungafunike kumaonana naye nthawi zina kuti mukambirane zinthu zokhudza banja lanu, kholo lachikhristu liyenera kuyesetsa kupewa kucheza naye popanda chifukwa chomveka.

Mwana amene walakwa akalangidwa ndi abusa achikhristu, sichingakhale chinthu chanzeru kuti mukane kapena kupeputsa chigamulo chawo chozikidwa pa Baibulo. Kumuikira kumbuyo mwana wanu wopandukayo sikungamuteteze kwa Mdyerekezi. M’malo mwake, kukhoza kuikanso pangozi moyo wanu wauzimu. Koma mukagwirizana ndi zoyesayesa za abusawo, mudzakhalabe “olimba m’chikhulupiriro” ndipo mudzam’teteza mwana wanuyo m’njira yabwino koposa.​—1 Petulo 5:9.

Yehova Adzakugwirizizani

Mwana wanu akapanduka, kumbukirani kuti simuli nokha. Makolo ena achikhristu akumanapo ndi zimenezo. Kaya tikumane ndi mayeso otani, Yehova angathe kutigwiriziza.​—Salmo 68:19.

Dalirani Yehova mwapemphero. Muzisonkhana nthawi zonse ndi mpingo. Gwirizanani ndi chilango cha abusa a mumpingo. Mukachita zimenezi, simudzafooka. Ndipo chitsanzo chanu chabwino chikhoza kumuthandiza mwanayo kuti avomere pamene Yehova akumuitana mwachikondi kuti abwerere kwa iye.​—Malaki 3:6, 7.

[Zithunzi patsamba 18]

Pezani mphamvu m’pemphero ndi mu mpingo wachikhristu