Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwamuna ndi Mkazi Anapangidwa Kuti Azithandizana

Mwamuna ndi Mkazi Anapangidwa Kuti Azithandizana

Mwamuna ndi Mkazi Anapangidwa Kuti Azithandizana

KUYAMBIRA kale mwamuna ndi mkazi akhala akulakalaka kukhala limodzi. Mulungu ndiye anayambitsa zimenezi. Yehova anaona kuti sikunali kwabwino kuti mwamuna woyamba, Adamu, akhale yekha. Choncho Mulungu anam’pangira “wom’thangatira iye.”

Yehova anagonetsa Adamu tulo tatikulu, kenako anatenga nthiti yake imodzi ndipo “anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu.” Iye anasangalala kwambiri ataona cholengedwa cha Mulungu chokongola chimenechi moti ananena kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga.” Mkazi wangwiro ameneyu dzina lake linali Hava ndipo chifukwa cha makhalidwe ake achikazi, anali wokondedwa kwambiri. Adamu analinso wangwiro ndipo monga mwamuna anali wofunika kumulemekeza. Awiriwa anapangidwa kuti azithandizana. Baibulo limanena kuti: “Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.”​—Genesis 2:18-24.

Koma, masiku ano, mabanja akutha, ndipo mgwirizano wa mwamuna ndi mkazi nthawi zambiri umakhala wankhanza ndipo onse amachita zinthu modzikonda. Mtima wampikisano wachititsa kuti mwamuna ndi mkazi asamagwirizane. Zonsezi n’zosemphana ndi cholinga cha Mulungu chokhudza mwamuna ndi mkazi. Mwamuna anapangidwa kuti akwaniritse udindo wofunika kwambiri pa dziko lapansi. Mkazi anapangidwa kuti akhale ndi udindo wapadera ndi wolemekezeka wothandiza mwamuna wake. Onse anapangidwa kuti azigwira ntchito limodzi mogwirizana. Kuyambira chiyambi cha anthu, amuna ndi akazi omvera Mulungu akhala akuyesayesa mokhulupirika kukwaniritsa udindo womwe Yehova anawapatsa, ndipo kuchita zimenezi kwawathandiza kukhala achimwemwe ndi okhutira pa moyo wawo. Kodi udindo umenewu ndi wotani ndipo tingaukwaniritse motani?

[Chithunzi patsamba 3]

Mwamuna ndi mkazi anapangidwa kuti akhale ndi udindo wolemekezeka m’dongosolo la Mulungu