Mwamuna ndi Mkazi Onse Ali ndi Udindo Wolemekezeka
Mwamuna ndi Mkazi Onse Ali ndi Udindo Wolemekezeka
YEHOVA MULUNGU anayamba n’kulenga Adamu, kenako Hava. Hava asanalengedwe, Adamu anaphunzira zambiri pamoyo. Pa nthawi imeneyi, Yehova anam’patsa malangizo. (Genesis 2:15-20) Popeza kuti Mulungu ankalankhula ndi Adamu, Adamuyo anayenera kuuza mkazi wake malangizowo. Choncho, n’zoonekeratu kuti iyeyo ndiye anayenera kutsogolera pa zonse zokhudza kulambira.
Mu mpingo wachikhristu muli makonzedwe ofanana ndi amenewa ndipo tingapindule mwa kuwaonanso bwino. Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Sindivomereza kuti mkazi . . . azikhala ndi ulamuliro pa mwamuna, koma azikhala chete. Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa, kenako Hava.’ (1 Timoteyo 2:12, 13) Izi sizikutanthauza kuti akazi azingokhala chete pa msonkhano wa mpingo wachikhristu ayi. Koma, azikhala chete mwa kusakangana ndi mwamuna. Sayenera kunyoza udindo wake woikidwa kapena kuchita zinthu zofuna kuphunzitsa mpingo. Amuna ndi amene apatsidwa ntchito yoyang’anira ndi kuphunzitsa mpingo, koma akazi amachita zambiri pa misonkhano yachikhristu mwa kutenga nawo mbali m’njira zosiyanasiyana.
Potithandiza kumvetsa udindo wa amuna ndi wa akazi m’makonzedwe a Mulungu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwamuna sanachokere kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna . . . Ndiponso, mwa Ambuye mkazi sakhalapo popanda mwamuna kapena mwamuna popanda mkazi [aliyense sadziimira payekha]. Pakuti monga mkazi ali wochokera kwa mwamuna, mwamunanso amakhalapo kudzera mwa mkazi; koma zinthu zonse ndi zochokera kwa Mulungu.”—1 Akorinto 11:8-12.
Udindo Wosiyanasiyana wa Akazi
M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Isiraeli, akazi anali ndi udindo wosiyanasiyana ndipo anali ndi ufulu wogwiritsa ntchito nzeru zawo. Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 31:10-31 limanena za “mkazi wangwiro” yemwe amagula nsalu zapamwamba kuti apangire banja lake zovala zabwino. Ndipo, “asoka malaya abafuta, nawagulitsa.” (Mavesi 13, 21-24) Mofanana ndi “zombo za malonda,” mkazi wangwiroyu amakapeza chakudya chabwino, ngakhale ngati atafunikira kupita kutali kuti akachipeze. (Vesi 14) “Asinkhasinkha za munda, naugula,” ndipo ‘aoka mipesa.’ (Vesi 16) Popeza kuti amachita malonda mwanzeru, ‘amam’pindulira.’ (Vesi 18) Kuwonjezera pa ‘kuyang’anira mayendedwe a banja lake,’ mkazi woopa Yehovayu amathandizanso anthu ena modzipereka. (Mavesi 20, 27) Choncho m’pake kuti amatamandidwa.—Vesi 31.
Malamulo a Yehova omwe anapereka kudzera kwa Mose anapatsa akazi mwayi waukulu woti akule mwauzimu. Mwachitsanzo, pa Yoswa 8:35, timawerenga kuti: “Panalibe mawu amodzi a zonse adazilamulira Mose osawerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Isiraeli, ndi akazi ndi ang’ono, ndi alendo akuyenda pakati pawo.” Baibulo limanena za Ezara wansembe kuti: “Anabwera nacho chilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri. Nawerenga m’menemo pa khwalala lili ku chipata cha kumadzi kuyambira mbanda kucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.” (Nehemiya 8:2, 3) Akazi anapindula ndi kuwerenga kwa Chilamulo kotere. Anachitanso nawo mapwando achipembedzo. (Deuteronomo 12:12, 18; 16:11, 14) Chofunika kwambiri n’chakuti, akazi mu Isiraeli wakale anatha kukhala paubwenzi ndi Yehova Mulungu ndipo aliyense anatha kupemphera kwa iye.—1 Samueli 1:10.
M’nthawi ya atumwi, akazi oopa Mulungu anali ndi mwayi wotumikira Yesu. (Luka 8:1-3) Mkazi wina anathira mafuta pa mutu ndi mapazi a Yesu pamene anali kudya chakudya chamadzulo ku Betaniya. (Mateyo 26:6-13; Yohane 12:1-7) Ndipo ena mwa anthu omwe Yesu anawaonekera ataukitsidwa anali akazi. (Mateyo 28:1-10; Yohane 20:1-18) Yesu atapita kumwamba, gulu la anthu pafupifupi 120 lomwe linasonkhana limodzi linaphatikizapo “azimayi ena komanso Mariya mayi wa Yesu.” (Machitidwe 1:3-15) Mosakayikira, ambiri kapena onse a azimayi amenewa anali m’chipinda cha m’mwamba ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekosite 33 C.E., pamene mzimu woyera unatumizidwa ndipo ophunzira a Yesu mozizwitsa analankhula m’zinenero zambiri.—Machitidwe 2:1-12.
Amuna ndi akazi omwe anali pakati pa anthu amene anaona kukwaniritsidwa kwa lemba la Yoweli 2:28, 29, lomwe analigwira mawu mtumwi Petulo pa tsiku la Pentekosite ponena kuti: “[Ine Yehova] ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyanasiyana. Pamenepo ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera. . . . Ndidzatsanuliranso mbali ya mzimu wanga ngakhale pa akapolo ndi adzakazi anga m’masiku amenewo.” (Machitidwe 2:13-18) Kwa kanthawi ndithu pambuyo pa Pentekosite 33 C.E., akazi achikhristu analandira mphatso za mzimu. Analankhula ndi kunenera mu zinenero zina. Mwina sananeneretu za m’tsogolo kwenikweni koma analankhula mfundo zoona za m’Malemba.
M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma, mtumwi Paulo analankhula mwachikondi za “mlongo wathu Febe” pofuna kuwadziwitsa za iye. Anatchulanso za Turufena ndi Turufosa ndipo ananena kuti anali “akazi ogwira ntchito mwakhama potumikira Ambuye.” (Aroma 16:1, 2, 12) Ngakhale kuti akaziwa analibe udindo woikidwa m’mpingo woyambirira wachikhristu, iwo pamodzi ndi akazi ena ambiri anali ndi dalitso lokhala osankhidwa ndi Mulungu kuti akakhale limodzi ndi Mwana wake, Yesu Khristu, mu Ufumu wa kumwamba.—Aroma 8:16, 17; Agalatiya 3:28, 29.
Akazi omvera Mulungu masiku ano ali ndi udindo wabwino kwambiri. Lemba la Salmo 68:11 limati: “Ambuye anapatsa mawu: akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.” Akazi otere ayenera kuyamikiridwa. Mwachitsanzo, popeza amaphunzitsa mwaluso pa maphunziro a Baibulo, akuthandiza anthu ambiri kuvomereza ziphunzitso zoona zomwe zimakondweretsa Mulungu. Akazi okwatiwa achikhristu omwe amathandiza ana awo kukhala okhulupirira ndipo amathandiza amuna awo amene ali ndi ntchito zambiri mu mpingo, amafunikanso kutamandidwa. (Miyambo 31:10-12, 28) Akazi osakwatiwa alinso ndi udindo wolemekezeka m’makonzedwe a Mulungu, ndipo amuna achikhristu amalimbikitsidwa ‘kudandaulira . . . akazi achikulire monga amayi awo, akazi achitsikana monga alongo awo, ndi chiyero chonse.’—1 Timoteyo 5:1, 2.
Ntchito Zosiyanasiyana za Amuna
Mwamuna wachikhristu ali ndi udindo wopatsidwa ndi Mulungu ndipo ayenera kuukwaniritsa. Paulo anati: “Ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna; ndi mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Mwamunanso ali ndi mutu, yemwe ndi Khristu. Ndipotu, mwamuna adzayankha mlandu kwa Khristu, ndipo makamaka kwa Mulungu. Ndipo Mulungu amayembekezera kuti mwamuna azichita umutu wake mwachikondi. (Aefeso 5:25) Zimenezi zakhala choncho kuyambira pamene anthu analengedwa.
Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anapatsa mwamuna ntchito zogwirizana ndi udindo wake monga mutu. Mwachitsanzo, Yehova anauza Nowa kumanga chingalawa chopulumukiramo pa nthawi ya Chigumula. (Genesis 6:9–7:24) Abulahamu analonjezedwa kuti kudzera m’mbewu yake, mabanja ndi mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa. Mbali yaikulu ya mbewuyo ndi Khristu Yesu. (Genesis 12:3; 22:18; Agalatiya 3:8-16) Mulungu anaika Mose kuti atsogolere Aisiraeli kuchoka mu Iguputo. (Eksodo 3:9, 10, 12, 18) Yehova anagwiritsanso ntchito Mose kupereka malamulo otchedwa pangano la Chilamulo, kapena kuti Chilamulo cha Mose. (Eksodo 24:1-18) Ndiponso, olemba Baibulo onse anali amuna okhaokha.
Yesu, pokhala Mutu wa mpingo wachikhristu, “anapereka mphatso za amuna.” (Aefeso 1:22; 4:7-13) Paulo ankanena za amuna pamene anandandalitsa ziyeneretso za oyang’anira. (1 Timoteyo 3:1-7; Tito 1:5-9) N’chifukwa chake m’mipingo ya Mboni za Yehova, ndi amuna amene amatumikira monga oyang’anira, kapena akulu, ndiponso amuna oikidwa kukhala atumiki othandiza. Ndi amuna okha amene ayenera kutumikira monga abusa mu mpingo wachikhristu. (1 Petulo 5:1-4) Komabe, monga momwe taonera kale, akazi ali ndi udindo wofunika wosiyanasiyana wopatsidwa ndi Mulungu.
Amasangalala ndi Udindo Wawo
Onse, amuna ndi akazi, akamakwaniritsa udindo wawo wopatsidwa ndi Mulungu, amapeza chimwemwe. Ndiponso, amuna ndi akazi awo amakhala ndi chimwemwe m’banja akamatsatira chitsanzo cha Khristu ndi mpingo wake. Paulo analemba kuti: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo . . . Aliyense wa inu akonde mkazi wake monga adzikonda iye mwini.” (Aefeso 5:25-33) Choncho, amuna ayenera kuchita umutu wawo mwachikondi ndi mosadzikonda. Ngakhale kuti mu Mpingo wa Khristu mulibe anthu angwiro, Yesu amaukondabe ndi kuusamalira. Mofanana ndi zimenezo, mwamuna wachikhristu ayenera kukonda ndi kusamalira mkazi wake.
Mkazi wachikhristu “akhale ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Pochita zimenezi, angatengere chitsanzo cha mpingo. Lemba la Aefeso 5:21-24 limati: “Gonjeranani wina ndi mnzake poopa Khristu. Akazi agonjere amuna awo monga kugonjera Ambuye, chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso Khristu alili mutu wa mpingo, pokhala iye mpulumutsi wa thupilo. Ndipotu, monga mpingo umagonjera Khristu, akazinso agonjere amuna awo m’chilichonse.” Ngakhale kuti nthawi zina mkazi zingamuvute kugonjera mwamuna wake, kuchita zimenezi “ndicho choyenera mwa Ambuye.” (Akolose 3:18) Kugonjera mwamuna wake kungakhale kosavuta akamakumbukira kuti kutero kumakondweretsa Ambuye Yesu Khristu.
Ngakhale mwamuna wake atakhala kuti si wokhulupirira mnzake, mkazi wachikhristu ayenera kugonjerabe umutu wake. Mtumwi Petulo anati: “Inu akazi, muzigonjera amuna anu, kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.” (1 Petulo 3:1, 2) Sara, yemwe analemekeza mwamuna wake Abulahamu, anapatsidwa mwayi wobereka Isake n’kudzakhala kholo la Yesu Khristu. (Aheberi 11:11, 12; 1 Petulo 3:5, 6) Akazi omwe amachita ngati Sara, mosakayikira adzadalitsidwa ndi Mulungu.
Amuna ndi akazi akamakwaniritsa udindo wawo wopatsidwa ndi Mulungu amakhala mwamtendere ndi mogwirizana. Ndipo zimenezi zimawakhutiritsa n’kuwapatsa chimwemwe. Komanso, kutsatira malangizo a m’Malemba kumapangitsa munthu kukhala wolemekezeka ndipo zimenezi n’zogwirizana ndi udindo wapadera womwe ali nawo m’makonzedwe a Mulungu.
[Bokosi patsamba 7]
Mmene Amaonera Udindo Wawo Wopatsidwa ndi Mulungu
Mkazi wina dzina lake Susan anati: “Mwamuna wanga amachita umutu wake mwachikondi ndi mokoma mtima. Nthawi zambiri, pakafunika kusankha zochita, timakambirana, ndipo akasankha zoti tichite, ndimadziwa kuti wasankha zokomera tonsefe. Kutsatira makonzedwe amene Yehova waikira akazi achikhristu, kumandipatsa chimwemwe ndipo kumalimbitsa ukwati wathu. Tili ndi ubwenzi wabwino ndipo timagwira ntchito limodzi kuti tikwaniritse zolinga zathu zauzimu.”
Mkazi wina dzina lake Mindy anati: “Udindo womwe Yehova anapatsa atumiki ake aakazi umatitsimikizira kuti amatikonda. Ndimaona kuti kulemekeza mwamuna wanga ndi kum’patsa ulemu ndiponso kumuthandiza ntchito zake mu mpingo, ndi njira yosonyezera kuti ndimayamikira makonzedwe a Yehova amenewa.”
[Zithunzi patsamba 5]
Mogwirizana ndi udindo wa mwamuna monga mutu, Mulungu anapatsa Nowa, Abulahamu, ndi Mose ntchito zosiyanasiyana
[Chithunzi patsamba 7]
“Akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu”