Samueli Analimbikitsa Kulambira Koona
Samueli Analimbikitsa Kulambira Koona
MNENERI wina anadzudzula okhulupirira anzake amene anapempha munthu woti akhale mfumu yawo ndipo anawalimbikitsa kuti amvere Mulungu. Kuti asonyeze udindo wake, anapempha Yehova kuti abweretse mvula yamabingu monga chizindikiro. Ku Isiraeli sikunkagwa mvula yamabingu m’nyengo imeneyo, yomwe inali nyengo yokolola tirigu. Komabe, Mulungu anatumiza mabingu ndi mvula. Chifukwa cha zimenezi, anthuwo anayamba kuopa kwambiri Yehova ndi womuimira wake, Samueli.—1 Samueli 12:11-19.
Mneneri Samueli analinso wolemba. Analemba nkhani za m’mbiri zosangalatsa. N’zokhudza nyengo yokwana zaka pafupifupi 330 ndipo zimafotokozanso ntchito zapadera za Oweruza a ku Isiraeli. Mwachitsanzo, nkhani yomwe inachitikadi ya Samsoni, munthu wamphamvu kwambiri amene anakhalapo, yagwiritsidwa ntchito m’ndakatulo ndi m’masewero ochita kuimba komanso m’masewero ena ndi m’mafilimu. (Oweruza, machaputala 13-16) Samueli analembanso za Rute ndi apongozi ake, Naomi. Akazi awiri onsewa anali amasiye komanso osauka. Nkhani yoona imeneyi ili ndi mathero abwino, ndipo imasangalatsa kwambiri kuiwerenga.—Rute, machaputala 1-4.
Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera ku zimene Samueli analemba ndiponso kuchokera ku moyo wake? Kodi analimbikitsa motani kulambira koona?
Ali Mwana
Bambo ake a Samueli, a Elikana, anali wolambira Yehova ndipo anali mwamuna wachikondi. Mkazi wa Elikana, Hana, anali wolimba mwauzimu. Hana anali wosabereka, ndipo ali ku nyumba ya Yehova ku Silo, anapemphera mochokera pansi pamtima n’kulumbira kuti: “Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.” (1 Samueli 1:1-11) Zimenezi zinatanthauza kuti mwanayo adzapatulidwa kuti azitumikira Yehova.
Hana anapemphera mosatulutsa mawu. Nkhaniyo imati: “Hana ananena mu mtima.” Mkulu wa Ansembe Eli anaganiza molakwa kuti Hana anali ataledzera ndipo anam’dzudzula. Koma Hana anafotokoza mwaulemu mmene zinthu zinalili, ndipo Eli anati: “Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Isiraeli akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye.” Yehova anaterodi, chifukwa nkhaniyo imapitiriza kuti: “Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samueli, nati, Chifukwa ndinam’pempha kwa Yehova.” (1 Samueli 1:12-20)
Samueli analeredwa ‘m’malango ndi kalingaliridwe ka Yehova.’ (Aefeso 6:4) Atangomusiyitsa kumene kuyamwa, Hana anapita naye ku nyumba ya Mulungu ku Silo n’kukamupereka kwa Eli, Mkulu wa Ansembe. Ndi chisamaliro cha Eli, mnyamatayo ‘anatumikira Yehova.’ Chimwemwe chachikulu cha Hana chinaonekera m’mawu ake oyamikira okhudza mtima kwambiri amene anadzalembedwa ndi Samueli mwana wakeyo.—1 Samueli 2:1-11.
Ngati ndinu kholo, kodi mukulimbikitsa ana anu kuti ntchito yawo idzakhale yotumikira Yehova? Kulimbikitsa kulambira koona ndiyo ntchito yabwino kwambiri imene munthu angagwire.
Samueli sanavutike kuzolowera moyo wa pa malo opatulika. “Anakula pamaso pa Yehova” ndipo “Yehova ndi anthu omwe anam’komera mtima.” Anali ndi makhalidwe oopa Mulungu amene anachititsa anthu ena kumukonda.—1 Samueli 2:21, 26.
Koma Hofeni ndi Pinehasi, ana a Eli, anali osiyana 1 Samueli 2:12, 15-17, 22-25, 27, 30-34) Yehova anadzagwiritsiranso ntchito Samueli kupereka uthenga wina wa chiweruzo.
ndi Samueli. Iwo anali oipa ndipo ‘sanadziwe Yehova.’ Ankachita chiwerewere ndipo ankatenga mbali zabwino kwambiri za nsembe zimene anthu ankabweretsa ku malo opatulika. Mulungu anali atatumiza kale mneneri kudzalengeza chilango chimene Eli akanayembekezera, chomwe chinaphatikizapo imfa ya ana ake awiri. (Samueli Anali Mneneri
Mulungu anauza Samueli kuti auze Eli kuti: “Ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletsa.” Umenewu sunali uthenga wophweka kupereka, ndipo Eli anamuuzitsa Samueli kuti asam’bisire mawu alionse a uthengawo. Choncho Samueli anamuuza zonse zimene Yehova ananena. Anafunika kulimba mtima kwabasi kuti achite zimenezo!—1 Samueli 3:10-18.
Pamene Samueli anali kukula, Aisiraeli onse anafika podziwa kuti anali mneneri wa Mulungu. (1 Samueli 3:19, 20) Chiweruzo chimene Samueli ananeneratu chinayamba pamene Aisiraeli anasakazidwa kwambiri ndi Afilisti. Hofeni ndi Pinehasi anafa pankhondoyo, ndipo Afilistiwo analanda likasa la chipangano la Yehova. Eli atamva za imfa ya ana ake ndi kulandidwa kwa Likasa, anagwa cham’mbuyo pa mpando wake, ndipo anathyoka khosi n’kufa.—1 Samueli 4:1-18.
Patadutsa zaka 20, Samueli analimbikitsa Aisiraeli kuti asiye kulambira konyenga. Iwo atamva zimenezi anachotsa mafano awo, anasala kudya, ndipo anaulula machimo awo. Samueli anawapempherera n’kuwaperekera nsembe yopsereza. Kodi kenako chinachitika n’chiyani? Afilisti atawaukiranso, Mulungu anawasokoneza ndipo Aisiraeli anagonjetsa adani awowo. Moyo wa Aisiraeli unasintha kwambiri ndi madalitso a Yehova, ndipo anatenganso malo amene Afilisti anawalanda.—1 Samueli 7:3-14.
Samueli analimbikitsadi kulambira koona. Mwachitsanzo, anaonetsetsa kuti zinthu zina zimene anafunkha kunkhondo zigwiritsidwe ntchito kukonza chihema. Anathandizanso kukonza madyerero a Pasika ndi utumiki wa Alevi odikira kuzipata. (1 Mbiri 9:22; 26:27, 28; 2 Mbiri 35:18) Chaka chilichonse, Samueli ankachoka kunyumba kwake ku Rama kupita m’mizinda yosiyanasiyana kukaweruza anthu. Anadziwika monga munthu wachilungamo ndi wopanda tsankho. Chifukwa choti anthu ankamulemekeza, anatha kuwathandiza mwauzimu. (1 Samueli 7:15-17; 9:6-14; 12:2-5) Mosakayikira anthu ambiri analimbikitsidwa kutengera chitsanzo chake chifukwa anali munthu wachilungamo ndi wokonda zinthu zauzimu. Kodi chitsanzo cha Samueli chimakukhudzani motero nanunso?
Aisiraeli Anapempha Mfumu
Samueli atakalamba anaika ana ake, Yoeli ndi Abiya, kukhala oweruza. Anawo “sanatsanza makhalidwe ake, koma anapambukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.” Khalidwe lawolo linachititsa akulu a Isiraeli kupempha mfumu. (1 Samueli 8:1-5) Zimenezi sizinamukondweretse Samueli. Koma atapempherera nkhaniyi, Yehova anamuuza kuti: “Sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yawo.” (1 Samueli 8:6, 7) Mulungu anauza Samueli kuti awachitire anthuwo zimene anali kufuna koma awachenjeze kuti akamadzalamulidwa ndi mfumu, ufulu wawo udzachepa. Anthuwo ataumirira, Yehova anakonza zoti Samueli adzoze Sauli kuti akhale mfumu.—1 Samueli 8:6-22; 9:15-17; 10:1.
Samueli anagwirizana ndi dongosololi ngakhale kuti sankasangalala nalo kwenikweni. 1 Samueli 10:17-24; 11:11-15) Samueli anafotokoza mbiri ya Aisiraeli ndipo analimbikitsa mfumuyo ndi anthuwo kuti amvere Yehova. Mulungu anayankha pemphero la Samueli pobweretsa mvula yamabingu yomwe yatchulidwa koyambirira ija, ngakhale kuti sinali nyengo yake. Mvula yamabinguyo inachititsa anthuwo kuvomereza kulakwa kwawo pokana Yehova. Atamupempha Samueli kuti awapempherere, iye anayankha kuti: “Kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.” Anasonyezadi chitsanzo chabwino kwambiri chokonda Yehova ndi anthu ake mokhulupirika! (1 Samueli 12:6-24) Kodi nanunso mumakhala ofunitsitsa choncho kuchita zinthu zogwirizana ndi dongosolo la Mulungu ndi kupempherera okhulupirira anzanu?
Aisiraeli atagonjetsa Aamoni, iye anasonkhanitsa anthuwo ku Giligala kuti adzaone Sauli akulongedwa ufumu. (Anthu Awiri Oyamba Kukhala Mafumu a Isiraeli
Sauli anali munthu wodzichepetsa wovomerezeka pamaso pa Mulungu. (1 Samueli 9:21; 11:6) Koma m’kupita kwa nthawi, anasiya kumvera malangizo a Mulungu. Mwachitsanzo, Samueli anamudzudzula chifukwa chopupuluma kupereka nsembe m’malo modikira, monga momwe anamuuzira. (1 Samueli 13:10-14) Sauli atalephera kumvera zimene anauzidwa n’kumusiya ndi moyo Agagi, Mfumu ya Aamaleki, Samueli anamuuza kuti: “Yehova anang’amba ufumu wa Isiraeli lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.” Kenaka Samueliyo payekha anapha Agagi n’kuyamba kumulira Sauli.—1 Samueli 15:1-35.
Patapita nthawi Yehova anauza Samueli kuti: “Iwe ukuti ulire chifukwa cha Sauli nthawi yotani, popeza Ine ndinam’kana kuti asakhale mfumu ya Isiraeli.” Atatero, Yehova anatuma Samueli ku Betelehemu kuti akadzoze mwana wa Jese kuti akhale mfumu. Samueli anayang’ana ana a Jese mmodzi ndi mmodzi mpaka pamene Yehova anavomereza Davide, wamng’ono pa onse, kuti adzozedwe. Tsiku limenelo, Samueli anaphunzira mfundo yofunika, yakuti: “Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.”—1 Samueli 16:1-13.
Popeza kusamvera kwa Sauli kunam’pweteka mumtima Samueli, ziyenera kuti zinam’pweteka kwambiri pamene Sauli anayamba kudana kwambiri ndi Davide mpaka kufuna kumupha. Ngakhale anakumana ndi mayesero ngati amenewo, Samueli anachitabe zinthu zambiri paukalamba wake ndipo ankachita zonse zomwe akanatha potumikira Yehova.—1 Samueli 19:18-20.
Mbiri Imene Samueli Anasiya
Samueli atamwalira, Aisiraeli anamulira mneneri wodzichepetsa ndi wolimba mtima ameneyu, amene zochita zake zinakhudza miyoyo ya anthu ambiri. (1 Samueli 25:1) Samueli anali wopanda ungwiro, ndipo nthawi zina ankaganiza molakwika. Ngakhale anali ndi zolephera zake, Samueli anadzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse ndipo anagwira ntchito mwakhama pothandiza ena kuti achite chimodzimodzi.
Zinthu zambiri zasintha kuchokera pa nthawi ya Samueli, koma tikhoza kuphunzira zinthu zambiri zothandiza poona mbiri ya moyo wake. Koposa zonse, Samueli ankatsatira ndi kulimbikitsa kulambira koona kwa Yehova. Kodi inunso mukuchita zimenezo?
[Bokosi patsamba 16]
GANIZIRANI MOYO WA SAMUELI
• Monga momwe makolo a Samueli anam’phunzitsira mawu a Mulungu, lerani ana anu “m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.”—Aefeso 6:4.
• Limbikitsani ana anu kuti ntchito yawo idzakhale yotumikira Yehova, ngati Samueli.
• Makhalidwe oopa Mulungu a Samueli anachititsa anthu ena kumukonda, ndipo chimenechi n’chitsanzo chabwino kwa ife.
• Samueli anachita zonse zomwe akanatha kuti alimbikitse kulambira koona, ndipo nafenso tiyenera kutero.
[Chithunzi patsamba 15]
Samueli analimbikitsa kulambira koona ndipo modzipereka anathandiza anthu ena mwauzimu