Thandizani Anthu Kumvera Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Thandizani Anthu Kumvera Zimene Baibulo Limaphunzitsa
“Komano zogwera panthaka yabwino, ndizo anthu amene pambuyo pomva mawu ndi mtima woona komanso wabwino, amawasunga ndi kubereka zipatso mwa kupirira.”—LUKA 8:15.
1, 2. (a) Kodi buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? linapangidwa n’cholinga chotani? (b) M’zaka zaposachedwapa, kodi Yehova wadalitsa bwanji khama la anthu ake popanga ophunzira?
“BUKULI n’labwino kwabasi. Ophunzira anga amalikonda kwambiri. Inenso ndimalikonda zedi. Pogwiritsa ntchito buku limeneli, tingathe kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi anthu titangolankhula nawo mawu ochepa.” Mawuwa ananena ndi mtumiki wa nthawi zonse, kapena kuti mpainiya wa Mboni za Yehova pofotokoza buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? * Ponena za buku lomweli, wofalitsa Ufumu wina wachikulire anati: “Ndathandiza anthu ambiri kudziwa Yehova pa zaka 50 zimene ndakhala ndikulalikira. Koma ndikuona kuti buku limeneli n’labwino koposa. Mafanizo ndi zithunzi zokongola za m’bukuli zimasangalatsa kwambiri.” Kodi inunso mumaliona choncho buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? Buku lophunzirira Baibulo limeneli linapangidwa n’cholinga choti likuthandizeni kukwaniritsa lamulo la Yesu loti: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse. . . . Kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”—Mateyo 28:19, 20.
2 N’zachidziwikire kuti mtima wa Yehova umasangalala akamaona Mboni zake zoposa mamiliyoni 6 zikumvera modzipereka lamulo la Yesu loti tipange ophunzira. (Miyambo 27:11) Zikuchita kuonekeratu kuti Yehova akudalitsa khama lawo. Mwachitsanzo, mu 2005 uthenga wabwino unalalikidwa m’mayiko 235, ndipo maphunziro a Baibulo okwana pafupifupi 6,061,500 anachititsidwa. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri ‘analandira mawu a Mulungu amene anamva kwa ife, ndipo sanawalandire monga mawu a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu.’ (1 Atesalonika 2:13) Pa zaka ziwiri zapitazi, ophunzira atsopano oposa 500,000 atsatira miyezo ya Yehova pamoyo wawo ndipo adzipereka kwa Mulungu.
3. Kodi mu nkhani ino tikambirana mafunso ati okhudza kagwiritsidwe ntchito ka buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?
3 Kodi inuyo posachedwapa mwakhalapo ndi mwayi wosangalatsa wophunzira Baibulo ndi munthu wina? Pa dziko lonse lapansi pakadali anthu amene ali “ndi mtima woona komanso wabwino” amene akadzamva mawu a Mulungu ‘adzawasunga ndi kubereka zipatso mwa kupirira.’ (Luka 8:11-15) Tiyeni tione momwe mungagwiritsire ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pa ntchito yopanga ophunzira. Tikambirana mafunso atatu awa: (1) Kodi mungayambitse bwanji phunziro la Baibulo? (2) Kodi njira zophunzitsira zabwino kwambiri n’ziti? (3) Kodi mungathandize bwanji munthu kuti asangokhala wophunzira chabe, koma akhalenso mphunzitsi wa Mawu a Mulungu, Baibulo?
Mmene Mungayambitsire Phunziro la Baibulo
4. N’chifukwa chiyani anthu ena angakane kuphunzira Baibulo, ndipo mungawathandize bwanji kuti avomere?
4 Ngati atakupemphani kuti mudumphe mtsinje waukulu kamodzi n’kamodzi, mwina mukhoza kukana. Koma ngati ataika miyala yowolokera, mwina simungakane kuwoloka mtsinjewo. Mofanana ndi zimenezi, munthu wotanganidwa akhoza kukana kuphunzira Baibulo. Mwininyumba angaganize kuti zimatenga nthawi yambiri ndiponso zimafuna khama. Kodi mungamuthandize bwanji kuti avomere? Mukhoza kugwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kuti muzikambirana naye mwachidule mfundo zofunika, n’cholinga choti ayambe kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse. Mukamakonzekera bwino, ulendo wobwereza uliwonse umene mungapange ndi munthuyo, ungakhale ngati mwala wowolokera popanga ubwenzi wabwino ndi Yehova.
5. N’chifukwa chiyani muyenera kuwerenga buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?
5 Komabe, musanathandize munthu wina kuti apindule ndi buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, inuyo muyenera kulidziwa bwino kwambiri. Kodi mwawerenga bukuli kuyambira koyambirira mpaka kumapeto? Mwamuna wina ndi mkazi wake anatenga bukuli popita kutchuthi ndipo anayamba kuliwerenga akupuma pa gombe lanyanja. Mayi wina wa kuderalo wogulitsa malonda kwa alendo atawayandikira, anaona mutu wakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Anauza banjalo kuti panali patangodutsa maola ochepa chabe kuchokera pamene anapemphera kwa Mulungu za funso limenelo, n’kumufunsa kuti amuuze yankho lake. Mokondwera, banjalo linamupatsa mayiyo bukulo. Kodi ‘mwadziwombolera nthawi’ kuti muwerenge bukuli koyamba kapena kachiwiri, panthawi imene mukudikira kuti muonane ndi munthu wina kapena popuma kuntchito kapena kusukulu? (Aefeso 5:15, 16) Ngati mutatero, mudzalidziwa bwino buku lophunzirira Baibulo limeneli ndiponso mukhoza kutsegula mipata yolankhula ndi anthu ena za nkhani zomwe zili m’bukuli.
6, 7. Kodi mungagwiritsire ntchito bwanji buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani poyambitsa maphunziro a Baibulo?
6 Pogawira bukuli kwa anthu mu ulaliki, gwiritsirani bwino ntchito mafunso, malemba, ndi zithunzi za pa tsamba 4, 5, ndi 6. Mwachitsanzo, mukhoza kuyamba kucheza ndi munthu pomufunsa kuti, “Poona mavuto onse amene anthu akukumana nawo masiku ano, kodi mukuganiza kuti malangizo odalirika tingawapeze kuti?” Mukamvetsera mosamala yankho la munthuyo, werengani 2 Timoteyo 3:16, 17, ndiyeno fotokozani kuti Baibulo limatiuza njira yabwino yothetsera mavuto a anthu. Kenaka muonetseni mwininyumbayo tsamba 4 ndi 5, ndipo m’funseni kuti: “Pa mavuto onse omwe asonyezedwa pa masamba amenewa, ndi vuto liti limene limakuipirani kwambiri?” Mwininyumbayo akaloza vuto limodzi, muuzeni kuti agwire bukulo pamene inuyo mukuwerenga lemba logwirizana ndi vutolo m’Baibulo lanu. Kenaka, werengani tsamba 6, ndipo m’funseni mwininyumbayo kuti, “Pa mafunso 6 amene atchulidwa m’munsi mwa tsamba lino, ndi funso liti limene mungakonde kudziwa yankho lake?” Munthuyo akasankha funso limodzi, muonetseni mutu umene ukuyankha funsolo, musiyireni bukulo, ndipo mupangane naye kuti mudzakumanenso n’cholinga choti mudzayankhe funsolo.
7 Ulaliki umene tafotokozawu ungatenge mwina mphindi zisanu. Koma mu mphindi zochepa zimenezo, mudzakhala mutadziwa zimene zimadetsa nkhawa mwininyumbayo, mutawerenga ndi kum’fotokozera malemba awiri, ndiponso mutayala maziko a ulendo wobwereza. Kukambirana mwachidule kumeneku ndi mwininyumbayo mwina kungakhale chinthu cholimbikitsa ndi chotonthoza kwambiri chomwe sichinamuchitikirepo kwa nthawi yaitali. Chifukwa cha zimenezi, ngakhale munthu wotanganidwa angamalakelake kudzacheza nanunso kwa mphindi zochepa pamene mukumuthandiza kudziwa zinthu zinanso zimene ayenera kuchita kuti afike pa ‘msewu wolowera kumoyo.’ (Mateyo 7:14) Nthawi ikamapita, chidwi cha mwininyumbayo n’kumakula, muyenera kuyamba kuchita phunzirolo kwa nthawi yotalikirapo. Mungachite zimenezi mwakumupempha ngati angalole kuti muphunzire naye kwa nthawi yotalika mwakutimwakuti.
Njira Zabwino Kwambiri Zophunzitsira
8, 9. (a) Kodi mungamukonzekeretse bwanji wophunzira Baibulo wanu kuti adzathe kupirira zopinga ndi mayesero amene mosakayikira adzakumana nawo? (b) Kodi zinthu zomangira chikhulupiriro cholimba zomwe sizingapse ndi moto zingapezeke kuti?
8 Munthu akayamba kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa, mosakayikira adzakumana ndi zopinga zomwe zingam’bweze m’mbuyo. Mtumwi Paulo anati: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Timoteyo 3:12) Paulo anayerekezera mayesero amenewa ndi moto womwe ungawononge zomangira zosalimba koma sungawononge zomangira ngati golide, siliva, ndi miyala yamtengo wapatali. (1 Akorinto 3:10-13; 1 Petulo 1:6, 7) Kuti muthandize wophunzira Baibulo wanu kukhala ndi makhalidwe ofunika kuti athe kupirira mayesero amene angakumane nawo, muyenera kumuthandiza mwa kumanga ndi zomangira zomwe sizingapse ndi moto.
9 Wamasalmo anayerekezera “mawu a Yehova” ndi “siliva woyenga m’ng’anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.” (Salmo 12:6) Zoonadi, m’Baibulo muli zofunika zonse zamtengo wapatali zimene zingagwiritsidwe ntchito pomanga chikhulupiriro cholimba. (Salmo 19:7-11; Miyambo 2:1-6) Ndipo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani limakusonyezani momwe mungagwiritsire ntchito Malemba mogwira mtima.
10. Kodi mungagogomezere bwanji Baibulo kwa wophunzira?
10 Pochita phunziro, gogomezerani kwa wophunzirayo malemba omwe ali m’mutu uliwonse womwe mukukambirana. Gwiritsirani ntchito mafunso kuti muthandize wophunzirayo kumvetsa mavesi ofunika a m’Baibulo n’kuona momwe angawagwiritsire ntchito pa moyo wake. Samalani kuti musamuuze zochita. M’malo mwake, tsanzirani Yesu. Mwamuna wina wodziwa bwino Chilamulo atam’funsa funso, Yesu anayankha kuti: “Kodi m’Chilamulo analembamo chiyani? Umawerengamo zotani?” Mwamunayo anayankha zochokera m’Malemba, ndipo Yesu anamuthandiza kuona momwe angagwiritsire ntchito mfundoyo pamoyo wake. Pogwiritsa ntchito fanizo, Yesu anamuthandizanso munthuyo kuona momwe mfundo yomwe anaphunzirayo iyenera kumukhudzira. (Luka 10:25-37) M’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani muli zitsanzo zambiri zosavuta kumva zimene mungagwiritse ntchito pothandiza wophunzira kuti atsatire mfundo za m’Malemba pa moyo wake.
11. Kodi muyenera kuphunzira zinthu zochuluka bwanji ulendo uliwonse?
11 Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani limafotokoza Mawu a Mulungu m’mawu osavuta kumva ndi achindunji, mofanana ndi momwe Yesu anaphunzitsira zinthu zovuta m’mawu osavuta kumva. (Mateyo 7:28, 29) Tsatirani chitsanzo chake. Fotokozani zinthu mosavuta kumva, mwachindunji, ndi molondola. Musafulumire kwambiri pophunzitsa. M’malo mwake, muziona nzeru za wophunzirayo ndi mmene zinthu zilili pa moyo wake kuti mudziwe kuti mukambirane ndime zingati ulendo uliwonse. Yesu ankadziwa zinthu zimene ophunzira ake sangathe kukwanitsa ndipo sanawalemetse powauza zinthu zambiri kuposa zomwe ankafunikira kudziwa panthawiyo.—Yohane 16:12.
12. Kodi za kumapeto ziyenera kugwiritsidwa ntchito bwanji?
12 M’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani muli za kumapeto zomwe zili ndi mitu 14. Poona zosowa za wophunzira wanu, inuyo monga mphunzitsi
muyenera kudziwa njira yabwino kwambiri yogwiritsira ntchito mitu imeneyi. Mwachitsanzo, ngati wophunzira akuvutika kumvetsetsa nkhani inayake kapena ali ndi mafunso pa zinthu zinazake chifukwa cha zimene ankakhulupirira kale, mwina zikhoza kukhala zokwanira kungomusonyeza pomwe nkhaniyo yafotokozedwa m’za kumapeto n’kumuuza kuti awerenge zimenezo payekha. Komabe, mwina mungafunike kuwerengera naye limodzi nkhaniyo malinga ndi zosowa za wophunzirayo. M’za kumapeto muli nkhani zofunika za m’Malemba, monga “Kodi Anthu Alidi ndi Mzimu Wosafa?” ndiponso “Kodi ‘Babulo Wamkulu’ N’chiyani?” Mungafunikire kukambirana mitu imeneyi ndi wophunzira wanu. Popeza nkhani za kumapeto zilibe mafunso, muyenera kuzidziwa bwino nkhanizo kuti muthe kufunsa mafunso abwino.13. Kodi pemphero limathandiza bwanji kulimbitsa chikhulupiriro?
13 Lemba la Salmo 127:1 limati: “Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.” Choncho mukamakonzekera kukachititsa phunziro la Baibulo, pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni. Mapemphero amene mumanena poyamba ndi pomaliza phunziro lililonse ayenera kusonyeza ubwenzi wabwino umene muli nawo ndi Yehova. Limbikitsani wophunzirayo kuti azipemphera kwa Yehova kuti am’patse nzeru zofunika kuti amvetsetse Mawu Ake ndi mphamvu zofunika kuti awagwiritsire ntchito pamoyo wake. (Yakobe 1:5) Akachita zimenezi, wophunzirayo adzalimbikitsidwa kuti athe kupirira mayesero ndipo adzapitiriza kukula molimba m’chikhulupiriro.
Thandizani Ophunzira Baibulo Kukhala Aphunzitsi
14. Kodi ophunzira Baibulo ayenera kupita patsogolo n’kufika pati?
14 Kuti ophunzira Baibulo athu athe kutsatira “zinthu zonse” zimene Yesu analamulira ophunzira ake, ayenera kupita patsogolo kuchoka pa kungokhala ophunzira a Mawu a Mulungu n’kufika pokhala aphunzitsi a Mawuwo. (Mateyo 28:19, 20; Machitidwe 1:6-8) Kodi mungachite chiyani kuti muthandize wophunzira kupita patsogolo choncho mwauzimu?
15. N’chifukwa chiyani muyenera kulimbikitsa wophunzira Baibulo wanu kupita ku misonkhano yachikhristu?
15 Kuyambira pachiyambi, pemphani wophunzirayo kuti azipita ku misonkhano kukasonkhana nanu limodzi. M’fotokozereni kuti kumisonkhano n’kumene mumaphunzitsidwa kuti mukhale mphunzitsi wa Mawu a Mulungu. Kwa milungu ingapo, muzipatula mphindi zingapo pamapeto pa phunziro la Baibulo lililonse kuti mum’fotokozere maphunziro auzimu amene mumalandira pa misonkhano yosiyanasiyana yampingo ndi pa misonkhano ikuluikulu. Lankhulani mwansangala za phindu limene mumapeza pa misonkhano imeneyi. (Aheberi 10:24, 25) Wophunzirayo akayamba kupita kumisonkhano nthawi zonse, mosakayikira adzakhala mphunzitsi wa Mawu a Mulungu.
16, 17. Kodi zolinga zina zimene wophunzira Baibulo angakhale nazo n’kuzikwaniritsa n’ziti?
16 Thandizani wophunzira Baibuloyo kukhala ndi zolinga zomwe angathe kuzikwaniritsa. Mwachitsanzo, mulimbikitseni kuuza anzake kapena achibale ake zinthu zimene akuphunzira. Mulimbikitseninso kukhala ndi cholinga chowerenga Baibulo lonse lathunthu. Mukamuthandiza kukhala ndi chizolowezi chowerenga Baibulo nthawi zonse, chizolowezichi chidzamuthandiza kwa nthawi yaitali ngakhale pambuyo pa ubatizo wake. Kuwonjezera apo, bwanji osamuuza wophunzirayo kuti akhale n’cholinga chokumbukira lemba limodzi la m’Baibulo kapena malemba angapo omwe akuyankha funso lofunika m’mutu uliwonse wa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? 2 Timoteyo 2:15.
Akamachita zimenezo, adzakhala “wantchito wopanda chochita nacho manyazi, wowalondoloza bwino mawu a choonadi.”—17 M’malo mouza wophunzira kuti azingoloweza malemba kapena azinena mfundo yake yaikulu, m’limbikitseni kuti azigwiritsira ntchito mavesi a m’Baibulo poyankha aliyense wofuna kudziwa chifukwa cha chikhulupiriro chimene ali nacho. Zikhoza kukhala zothandiza mutamakhala ndi chitsanzo chachifupi choyeserera, inuyo kukhala wachibale kapena wogwira naye ntchito amene wamufunsa wophunzirayo kuti afotokoze chikhulupiriro chake. Wophunzirayo akamayankha, m’sonyezeni momwe angayankhire “ndi mtima wofatsa ndi mwa ulemu waukulu.”—1 Petulo 3:15.
18. Wophunzira Baibulo akavomerezedwa kukhala wofalitsa wosabatizidwa, kodi mungam’thandize m’njira zinanso ziti?
18 M’kupita kwa nthawi, wophunzirayo akhoza kuyenerera kuti ayambe kuchita nawo utumiki wa kumunda. Mugogomezereni kuti ndi mwayi waukulu kuloledwa kugwira nawo ntchito imeneyi. (2 Akorinto 4:1, 7) Akulu akanena kuti wophunzirayo wavomerezedwa kukhala wofalitsa wosabatizidwa, m’thandizeni kukonza ulaliki wosavuta kenaka pitirani naye limodzi mu utumiki wa kumunda. Pitirizani kugwira naye ntchito limodzi nthawi zonse mu ulaliki wosiyanasiyana, ndipo m’phunzitseni momwe angakonzekerere maulendo obwereza ogwira mtima ndi momwe angawachitire. Chitsanzo chanu chabwino chingamuthandize kwambiri.—Luka 6:40.
‘Dzipulumutseni Inu Eni ndi Aja Okumverani Inu’
19, 20. Kodi tiyenera kukhala n’cholinga chotani, ndipo tiyenera kukhala nacho chifukwa chiyani?
19 Mosakayikira, pamafunika kugwira ntchito mwakhama kuti muthandize munthu kukhala ‘wodziwa choonadi molondola.’ (1 Timoteyo 2:4) Komabe, ndi zinthu zochepa zokha m’moyo zimene zingapatse munthu chimwemwe chofanana n’chimene munthu amakhala nacho akathandiza munthu wina kumvera zimene Baibulo limaphunzitsa. (1 Atesalonika 2:19, 20) Zoonadi, ndi mwayi waukulu kukhala “antchito anzake a Mulungu” pa ntchito yapadziko lonse yophunzitsa anthu imeneyi!—1 Akorinto 3:9.
20 Pogwiritsa ntchito Yesu Khristu ndi angelo amphamvu, Yehova posachedwapa adzapereka chiweruzo kwa anthu “osadziwa Mulungu ndi kwa osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:6-8) Miyoyo ya anthu ili pangozi. Kodi mungakhale ndi cholinga chochititsako phunziro la Baibulo lapanyumba m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mukamagwira ntchito imeneyi, mumakhala ndi mwayi ‘wodzipulumutsa inu mwini ndi aja okumverani inu.’ (1 Timoteyo 4:16) Panopa, kuposa pa nthawi ina iliyonse, tikufunika kuthandiza anthu mwachangu kuti amvere zimene Baibulo limaphunzitsa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 1 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mwaphunzira Chiyani?
• Kodi buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani analipanga n’cholinga chotani?
• Kodi mungayambitse bwanji maphunziro a Baibulo m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?
• Kodi njira zophunzitsira zabwino kwambiri n’ziti?
• Kodi mungathandize bwanji wophunzira kukhala mphunzitsi wa Mawu a Mulungu?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 26]
Kodi mukugwiritsira bwino ntchito bukuli?
[Chithunzi patsamba 27]
Kukambirana mwachidule kukhoza kum’patsa munthu chidwi chofuna kudziwa za m’Baibulo
[Chithunzi patsamba 29]
Kodi mungagogomezere bwanji Baibulo kwa wophunzira wanu?
[Chithunzi patsamba 30]
Thandizani wophunzira Baibulo kupita patsogolo