Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amosi Kodi Anali Wotchera Nkhuyu Kapena Wobaya Nkhuyu?

Amosi Kodi Anali Wotchera Nkhuyu Kapena Wobaya Nkhuyu?

Amosi Kodi Anali Wotchera Nkhuyu Kapena Wobaya Nkhuyu?

M’ZAKA za m’ma 800 B.C.E., Amaziya, yemwe anali wansembe woipa wopembedza mwana wa ng’ombe, analamula mneneri Amosi kuti asiye kulosera mu Isiraeli. Amosi anakana ndipo anati: “Ndinali woweta ng’ombe, ndi wakutchera [“wobaya,” NW] nkhuyu; ndipo Yehova ananditenga ndili kutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Isiraeli.” (Amosi 7:14, 15) Inde, Yehova ndiye anatumiza Amosi monga mneneri; sanadziike yekha ayi. Koma kodi Amosi ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti anali “wobaya” nkhuyu?

Mawu a Chiheberi omwe anawatanthauzira motere amangopezeka kamodzi kokhaka m’Baibulo la Dziko latsopano. Mabaibulo ena anamasulira mawuwa kuti “wotchera,” “wolima,” “wosamalira,” kapena “wodzala,” m’malo monena kuti “wobaya,” nkhuyu. Komabe, magazini ya Economic Botany inati kamasuliridwe kabwino ka mawu amenewa kakanakhala “wobaya,” chifukwa mawu amenewa amasonyeza ntchito yapadera imene mlimi wa nkhuyu amachita.

Kubaya, kapena kuti, kubowola timabowo pa nkhuyu, kwakhala kodziwika bwino ku Iguputo ndi ku Cyprus kuyambira kalekale. Kubaya nkhuyu sikuchitikanso ku Isiraeli chifukwa masiku ano amalimako nkhuyu za mtundu wina. Komabe, Aisiraeli a m’nthawi ya Amosi ankabaya nkhuyu, popeza nkhuyu zimene ankalima panthawi imeneyo zinali zochokera ku Iguputo.

Zikukhala ngati kuti, kubaya nkhuyu kumachititsa kuti nkhuyuzo ziyamwe madzi n’kukhala ndi madzi ambiri. Komanso kumawonjezera mpweya winawake mu nkhuyuzo, womwe umathandiza kuti zipse mwachangu, ndipo zimakhala zikuluzikulu ndiponso zotsekemera. Kuphatikiza apo, mavu sawononga zipatsozo chifukwa zimapsa mwamsanga.

Ngakhale kuti Amosi anali munthu wamba woweta ziweto ndiponso wobaya nkhuyu, sanaope adani ake. M’malo mwake, analengeza molimba mtima uthenga wachiweruzo wa Yehova kwa Isiraeli. Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwa atumiki a Mulungu masiku ano, amene mofanana ndi Amosi, ayenera kulengeza uthenga umene anthu ambiri sasangalala nawo.​—Mateyo 5:11, 12; 10:22.