Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chifukwa Chimene Ndimasangalalira Kupanga Ophunzira

Chifukwa Chimene Ndimasangalalira Kupanga Ophunzira

Mbiri ya Moyo Wanga

Chifukwa Chimene Ndimasangalalira Kupanga Ophunzira

Yosimbidwa ndi Pamela Moseley

Mu 1941, ku England kunali nkhondo ndipo panthawi imeneyi mayi anga ananditengera ku msonkhano wa Mboni za Yehova womwe unkachitikira ku Leicester. Joseph Rutherford anakamba nkhani yapadera yokhudza ana. Pamene ine ndi amayi tinabatizidwa pamsonkhanowo, ndinaona kuti anthu amene anatithandiza kukula mwauzimu anali osangalala kwambiri. Panthawiyo, sindinkadziwa za chimwemwe chimene munthu amakhala nacho chifukwa chopanga ophunzira a Yesu Khristu.

M’CHAKA cha 1940 ndi pamene tinayamba kupita patsogolo kuti tikhale ophunzira. Ndimakumbukirabe tsiku loopsa limene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba mu September 1939. Ndinaona misozi ikutsika m’masaya a amayi pamene ankafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani padzikoli palibe mtendere?” Makolo anga anagwirapo ntchito yausilikali panthawi yankhondo yoyamba ya padziko lonse ndipo anaona kuipa kwake. Amayi anapita kukafunsa funso lawolo kwa m’busa wa tchalitchi cha Angilikani ku Bristol. Anangowauza kuti: “Nkhondo zakhala zikuchitika kuyambira kalekale ndipo zidzakhala zikuchitikabe.”

Patangopita nthawi pang’ono, mayi wina wachikulire anafika panyumba pathu. Mayiyo anali wa Mboni za Yehova. Amayi anamufunsa funso lomwe lija lakuti: “N’chifukwa chiyani padzikoli palibe mtendere?” Mboniyo inafotokoza kuti nkhondo ndi mbali ya chizindikiro chakuti tikukhala kumapeto kwa dongosolo lazinthu lachiwawali. (Mateyo 24:3-14) Posakhalitsa, mwana wawo wa mkazi anayamba kuphunzira nafe Baibulo. Iye ndi amayi akewo anali ena mwa anthu amene anasangalala kuonerera ubatizo wathu. N’chifukwa chiyani kupanga ophunzira kumapatsa anthu chimwemwe chachikulu? Patapita nthawi ndinadziwa chifukwa chake. Ndiloleni ndikuuzeni zina mwa zimene ndaphunzira pa zaka zoposa zaka 65 zomwe ndakhala ndikupanga ophunzira.

Kupeza Chimwemwe Chifukwa Chophunzitsa Ena

Ndinayamba kugwira nawo ntchito yolalikira za Ufumu ku Bristol pamene ndinali ndi zaka 11. M’bale wina anandipatsa galamafoni ndi khadi laumboni n’kundiuza kuti: “Tsopano pita ku nyumba zonse zomwe zili mbali iyo ya msewu.” Choncho ndinapita ndekhandekha, ndipo n’zoona kuti ndinkachita mantha. Ndinkaika lekodi ya nkhani ya m’Baibulo pa galamafoni kenako n’kumuonetsa mwininyumba khadi laumboni, lomwe linkawauza anthu kuti alandire mabuku ofotokoza za m’Baibulo.

Kuyambira m’zaka za m’ma 1950, tinayamba kulimbikitsidwa kuti tiziwerenga Baibulo pamene tikuyenda khomo ndi khomo. Poyamba, kulankhula ndi anthu achilendo ndiponso kufotokoza ndime za m’Baibulo kunkandivuta chifukwa cha manyazi. Koma kenako ndinalimba mtima. Panthawiyi ndi pomwe ndinayamba kusangalaladi ndi utumiki. Anthu ena poyamba ankationa ngati anthu ongogulitsa mabuku, koma pamene tinkawerenga ndi kuwafotokozera malemba a m’Baibulo, anazindikira kuti ndife aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Ndinkasangalala kwambiri kuchita zimenezi moti ndinkalakalaka nditamakhala ndi nthawi yambiri yochita zimenezi. Choncho mu September 1955, ndinayamba utumiki wa nthawi zonse monga mpainiya.

Kulimbikira Kumapindulitsa

Chinthu chimodzi chomwe ndinaphunzira ndi choti kulimbikira mokoma mtima kumapindulitsa. Nthawi ina ndinapereka Nsanja ya Olonda kwa mayi wina, dzina lake Violet Morice. Nditapitanso kuti ndikamuone, anatsekula kwambiri chitseko n’kupinda manja, ndi kumamvetsera mwachidwi pamene ndinkamufotokozera Malemba. Nthawi zonse ndikapita kukamuyendera, anali kusonyeza chidwi chachikulu. Komabe, nditamufunsa ngati angakonde kuti ndiziphunzira naye Baibulo nthawi zonse, anayankha kuti: “Ayi. Ana anga akadzakula, ndidzaphunzira.” Ndinakhumudwa kwabasi! Baibulo limanena za “mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika.” (Mlaliki 3:6) Ndinaganiza zoti ndisaleme.

Patatha mwezi umodzi, ndinapitanso kukakambirana malemba ena ndi Violet. Sipanapite nthawi yaitali, Violet anayamba kuphunzira Baibulo mwachidule pakhomo la nyumba yake, ndipo kenako anati: “Bwanji tilowe m’nyumba?” Violet anakhala wokhulupilira mnzanga ndiponso bwenzi langa lenileni! Inde, Violet anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

Tsiku lina Violet anadzidzimuka kumva kuti mwamuna wake wagulitsa nyumba yawo iye asakudziwa ndiponso kuti wamusiya. Koma n’zosangalatsa kuti atathandizidwa ndi Mboni inzake, anapeza nyumba ina tsiku lomwelo masana ndipo anali wokondwa zedi. Pothokoza Yehova, iye anasankha zochita upainiya moyo wake wonse. Nditaona kuti mzimu wa Yehova wam’thandiza kukhala wachangu pa kulambira koona, ndinazindikira chifukwa chake kupanga ophunzira kumabweretsa chimwemwe chochuluka. Inde, ndinatsimikiza zogwira ntchito imeneyi kwa moyo wanga wonse.

Mu 1957, ine ndi Mary Robinson anatitumiza kukachita upainiya ku dera lina la malonda la Rutherglen ku Glasgow, m’dziko la Scotland. Tinkalalikira kuli chifunga, mvula ndiponso chipale chofewa, koma zinali zopindulitsa. Tsiku lina ndinakumana ndi Jesse, ndipo ndinasangalala kuphunzira naye Baibulo. Mwamuna wake Wally, anali wachikomyunizimu ndipo poyamba sankafuna kulankhula nane. Ataphunzira Baibulo n’kuzindikira kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha womwe udzabweretse makhalidwe abwino kwa anthu, anasangalala kwambiri. Kenako onse awiri anakhala opanga ophunzira.

Zochita za Munthu Poyamba Zingapereke Chithunzi Cholakwika

Kenako anatipatsa utumiki watsopano mu mzinda wa Paisley, ku Scotland. Tsiku lina ndikulalikira kumeneko, mayi wina anakana kumvetsera n’kutseka chitseko mwamwano kuti ndisalankhule naye. Pasanapite nthawi, anabwera kudzandifunafuna kuti andipepese. Nditapitanso sabata lotsatira, mayiyo anati: “Ndinamva ngati kuti ndatseka chitseko kuti ndisalankhulane ndi Mulungu. Sindikanachitira mwina koma kukakufunafunani basi.” Mayiyu dzina lake linali Pearl. Anandiuza kuti anzake ndiponso achibale ake anam’khumudwitsa kwambiri moti anapemphera kwa Mulungu kuti am’patse bwenzi lenileni. Iye anati: “Kenako ndi pamene munkabwera pakhomo paja, ndipo tsopano ndazindikira kuti inu ndinu bwenzi lenileni limenelo.”

Kukhala mnzake wa Pearl si kunali kophweka. Ankakhala pamwamba pa phiri lotsetsereka, ndipo ndinkakwera phirilo wapansi. Nditapita kukam’tenga kuti tipite ku misonkhano ulendo woyamba, pang’onong’ono ndikanagwa chifukwa cha mphepo ndi mvula. Ambulera wanga anang’ambika ndipo ndinamutaya. Patangotha miyezi 6 kuchokera pomwe anatseka mwamwano chitseko chija, Pearl anasonyeza kudzipereka kwake kwa Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi.

Posakhalitsa, mwamuna wake anaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo, ndipo pasanapite nthawi, anapita nane limodzi ku ulaliki wa khomo ndi khomo. Mwachizolowezi, kunali kugwa mvula. Iye anati: “Osadandaula. Ndimaima pamvula kuti ndionerere mpira, choncho ndikhozanso kuima pamvula kuti nditumikire Yehova.” Ndimasirira kwambiri khama la anthu a ku Scotland.

Nditabwereranso pambuyo pazaka zambiri ndinalimbikitsidwa kwambiri kuona kuti anthu ambiri amene ndinaphunzira nawo akadali kupilira mwachikhulupiriro. Chimenecho ndiye chimwemwe chimene munthu amakhala nacho chifukwa chopanga ophunzira. (1 Atesalonika 2:17-20) Nditachita upainiya ku Scotland kwa zaka zoposa 8, mu 1966 ndinaitanidwa ku Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo kuti ndikaphunzitsidwe umishonale.

M’munda wa Kudziko Lina

Ananditumiza ku Bolivia, m’tawuni ina yotentha yotchedwa Santa Cruz, kumene kunali mpingo wa anthu pafupifupi 50. Tawuniyo inandikumbutsa za chigawo chakumadzulo kwa dziko la United States monga mmene amachisonyezera m’mafilimu a Hollywood. Ndikamaganizira za m’mbuyomo, ndimaona kuti ndine mmishonale wamba. Sindinagwidwepo ndi ng’ona, kuukiridwa ndi anthu achiwawa, kusokera m’chipululu, kapena sitima kundiphwanyikirapo pa nyanja. Koma kwa ine, ntchito yopanga ophunzira ndi yomwe ndasangalala nayo kwambiri.

Mmodzi mwa amayi oyambirira amene ndinaphunzira nawo Baibulo ku Santa Cruz anali Antonia. Kuphunzitsa m’Chisipanishi kunkandivuta moti nthawi ina, kamwana kakamuna ka Antonia kanati: “Amama, kodi amalakwitsira dala kuti tiziseka?” Antonia anakhala wophunzira, ndipo Yolanda, mwana wake wamkazi, nayenso anakhala wophunzira. Yolanda anali ndi mnzake, wophunzira za malamulo, yemwe anzake ankam’tchula kuti Dito, amenenso anayamba kuphunzira Baibulo ndi kupezeka pa misonkhano. Pomuphunzitsa Dito, ndinaphunzira kanthu kena ponena za kuphunzitsa choonadi cha Baibulo. Ndinaphunzira kuti: Nthawi zina anthu amafunika kuwalimbikitsa.

Dito atayamba kusapezekapezeka pa nthawi ya phunziro lake, ndinamuuza kuti: “Dito, Yehova sakukukakamiza kuti ukhale ku mbali ya Ufumu wake. Uyenera kusankha wekha kuchita zimenezo.” Atayankha kuti amafuna kutumikira Mulungu, ndinati: “Panopa uli ndi zithunzi za mtsogoleri woukira boma. Kodi mlendo ataziona zinthu zimenezi anganene kuti unasankha kukhala ku mbali ya Ufumu wa Mulungu?” Chimenecho n’chilimbikitso chimene ankafunikira.

Patangopita masabata awiri, anthu anaukira boma, ndipo ophunzira a kuyunivesiteko ndi apolisi anayamba kuwomberana. Dito anakuwa, kuuza mnzake kuti: “Tiye tithawe!” “Ayi! Lero ndi tsiku lalikulu lomwe takhala tikuliyembekezera,” anatero mnzakeyo, uku akunyamula mfuti kuthamangira pa denga la yunivesiteyo. Ameneyu anali mmodzi mwa anzake 8 a Dito amene anaphedwa tsiku limenelo. Taganizani mmene ndimasangalalira n’kamaona Dito, amene akanafa ngati sakanakhala Mkhristu woona.

Kuona Mzimu wa Yehova Ukugwira Ntchito

Tsiku lina ndinkadutsa pafupi ndi khomo lina, ndikumaganiza kuti pakhomo limenelo ndafikapo kale, ndipo mayi wa panyumbapo anandiitana. Dzina la mayiyu linali Ignacia. Ignacia ankadziwa za Mboni za Yehova, koma chifukwa cha kutsutsa kwa mwamuna wake Adalberto, yemwe anali wapolisi wadzitho, sanathe kukula mwauzimu. Sankamvetsetsa ziphunzitso zambiri zoyambirira za m’Baibulo, choncho ndinayamba kuphunzira naye Baibulo. Ngakhale kuti Adalberto anayesetsa kuti atisiyitse kuphunzira Baibulo, kwa nthawi yaitali ndinkatha kucheza naye nkhani zina. Chimenechi chinali chiyambi choti tikhale mabwenzi.

Taganizani chimwemwe chomwe ndinali nacho poona Ignacia akukhala wodalirika mu mpingo, akumasamalira zosowa zauzimu ndiponso zakuthupi za amene amafunikira chitonthozo. M’kupita kwa nthawi, mwamuna wake ndi ana awo atatu anakhala Mboni. Pamene Adalberto anamvetsa uthenga wabwino, anapitanso ku polisi kuja n’kukalalikira mwakhama kwambiri moti apolisi 200 analembetsa kuti azilandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Yehova Amakulitsa

Nditatumikira ku Santa Cruz kwa zaka 6, ananditumiza ku La Paz, mzinda waukulu wa ku Bolivia, kumene ndinatumikira kwa zaka 25 zotsatira. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1970, kunyumba yomwe inali nthambi ya Mboni za Yehova ku La Paz kunkakhala anthu 12 okha. Pamene ntchito yolalikira inkawonjezeka n’kumafuna malo aakulu, nyumba ina inamangidwa kuti ikhale nthambi mu mzinda womwe unkakula mofulumira wa Santa Cruz. Nthambi anaisamutsira kumeneko mu 1998, ndipo ndinaitanidwa kukakhala mmodzi wa otumikira pathambiyo, yomwe inali ndi anthu oposa 50.

Mpingo umodzi umene unali ku Santa Cruz mu 1966 tsopano unasanduka mipingo yoposa 50. Mboni zomwe zinalipo 640 ku Bolivia pa nthawi imeneyo, panopa zafika pafupifupi 18,000!

N’zosangalatsa kuti utumiki wanga ku Bolivia wakhala waphindu. Komabe, ndimalimbikitsidwa ndi kukhulupirika kwa Akhristu anzanga kulikonse kumene ali. Tonse timakondwera kuona madalitso a Yehova pa ntchito yolalikira Ufumu. N’zosangalatsadi kwambiri kugwira nawo ntchito yopanga ophunzira.​—Mateyo 28:19, 20.

[Chithunzi patsamba 13]

Kuchita upainiya ku Scotland

[Chithunzi patsamba 15]

Kutumikira pa ofesi ya nthambi ku Bolivia; (chithunzi chaching’ono) pa mwambo womaliza maphunziro a kalasi ya nambala 42 ya Gileadi