Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Inde, N’losavuta Kuwerenga, Koma Kodi N’lolondola?

Inde, N’losavuta Kuwerenga, Koma Kodi N’lolondola?

Inde, N’losavuta Kuwerenga, Koma Kodi N’lolondola?

MU September chaka cha 2005, tchalitchi cha Angilikani chinavomereza ndi mtima wonse kutulutsidwa kwa Baibulo lotchedwa The 100-Minute Bible (Baibulo la mphindi 100). Baibuloli linakonzedwa kuti liziwerengedwa mu mphindi 100 zokha. Limafotokoza mwachidule Malemba Achiheberi m’zigawo 17, ndipo chigawo chilichonse n’chokwana tsamba limodzi. Malemba Achigiriki afotokozedwa mwachidule m’zigawo 33. Choncho anachotsa mbali zina za Baibulo zomwe wowerenga wina anati “n’zosasangalatsa.” Inde, n’losavuta kuwerenga, koma kodi n’lolondola?

Kupatulapo pa kuchotsa dzina la Mulungu, Yehova, anthu ophunzira Baibulo mwakhama adzaonanso zolakwika zina m’Baibulo limeneli. (Salmo 83:18) Mwachitsanzo, chigawo choyamba chimanena kuti Mulungu “analenga kumwamba ndi dziko lapansi m’masiku 6.” Komabe, lemba la Genesis 1:1 limanena mosavuta kuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Kenaka, nkhani yoyambirirayo imafotokoza kulengedwa kwa zinthu zokhudzana ndi dziko lapansi, komwe kunatenga “masiku” kapena kuti nyengo 6. Ndiyeno, lemba la Genesis 2:4 limalongosola mwachidule nyengo yonse yolenga, n’kuitcha kuti ‘tsiku limene Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.’

Baibulo la The 100-Minute Bible, limanena kuti Yobu, munthu wokhulupirika, anaukiridwa ndi “mmodzi mwa atumiki a [Mulungu], Satana, . . . yemwe udindo wake unali woti akhale woneneza wa anthu.” Kodi mukuona kulakwika kwa mawu amenewa? Mawu akuti “Satana” amatanthauza “Wotsutsa.” M’malo mokhala mtumiki wa Mulungu, Satana kwenikweni ndi mdani wamkulu wa Mulungu ndipo anadziika yekha kukhala woneneza anthu.​—Chivumbulutso 12:7-10.

Nanga bwanji mbali ya Malemba Achigiriki Achikristu ya Baibulo la The 100-Minute Bible? Mu fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Baibulo latsopanoli limati Yesu amayanja anthu amene anathandiza “munthu aliyense, kaya akhale wonyozeka bwanji,” koma Yesu kwenikweni ananena kuti amadalitsa anthu amene amachitira zabwino otsatira mapazi ake, kapena kuti “abale” ake. (Mateyo 25:40) Chidule cha Chivumbulutso chimauza owerenga kuti “Roma, yemwe ndi Babulo wamkulu, adzawonongedwa kotheratu.” Komabe, ophunzira Baibulo akudziwa kuti mu zolembedwa zoyambirira, palibe paliponse pamene pangachititse munthu kufika pofotokoza “Babulo Wamkulu” mwanjira imeneyi.​—Chivumbulutso 17:15–18:24.

Kwa anthu amene akufunafuna kudziwa Mlengi wathu ndi kumvetsa zolinga zake, palibe chomwe chingalowe m’malo mwa Baibulo lonse lathunthu. N’zoonadi, kuwerenga Baibulo kumatenga nthawi yaitali kuposa mphindi 100, koma kuchita zimenezo kumabweretsa madalitso osaneneka. (Yohane 17:3) Lolerani kugwira ntchito imeneyi kuti mupeze madalitso amenewo.​—2 Timoteyo 3:16, 17.