Kodi Timangoyembekezera Kuti Ena Ndiwo Azinena Zoona?
Kodi Timangoyembekezera Kuti Ena Ndiwo Azinena Zoona?
“NDIMADANA ndi bodza, ndiponso ndimadana ndi zoti munthu azindinamiza,” anatero mtsikana wina wazaka 16. Ambirife timaganiza chimodzimodzi. Timafuna kuti zomwe tamva, kaya mochita kuuzidwa m’pakamwa kapena kuwerenga, zikhale zoona. Komabe, kodi timanena zoona pamene tikuuza anthu ena zinthu?
Pa kafukufuku yemwe anachitika ku Germany, anthu ambiri omwe anafunsidwa mafunso anayankha kuti “kunama pa nkhani zazing’ono n’cholinga chodziteteza kapena kuteteza anzako ndi kololeka, ndiponso n’kofunika kuti anthu azigwirizana ndi anzawo.” Ndipo mtolankhani wina analemba kuti: “Kunena zoona zokhazokha nthawi zonse n’kwabwino koma si kosangalatsa.”
Kodi n’kutheka kuti timafuna anthu ena azinena zoona koma ifeyo nthawi zina timaona kuti sitifunikira kunena zoona? Kodi zili n’kanthu ngati titanena zoona kapena ayi? Kodi kuipa kwa bodza n’kotani?
Bodza Limabweretsa Mavuto
Taganizirani za mavuto amene amakhalapo chifukwa cha bodza. Kunama kumachititsa kuti mwamuna ndi mkazi wake ndiponso anthu apachibale asamakhulupirirane. Miseche yopanda umboni imawononga mbiri ya munthu. Chinyengo cha anthu olembedwa ntchito chimapangitsa kuti eni mabizinesi azigwiritsa ntchito ndalama zambiri, ndipo zimenezi zimachititsa kuti katundu wawo akwere mtengo kwambiri. Kulemba zabodza pa zikalata za misonkho kumachititsa kuti maboma asapeze ndalama zokwanira zogwirira ntchito zothandiza anthu. Bodza la anthu ochita kafukufuku limawononga tsogolo labwino la ntchito yawo komanso limawononga mbiri ya mabungwe otchuka. Mabizinesi achinyengo amene amati ndi olemeretsa mwachangu amabera anthu ndalama zomwe akhala akusunga moyo wawo wonse kapenanso amawabweretsera mavuto oposa pamenepa. Choncho n’zosadabwitsa kuti Baibulo limatiuza kuti pazinthu zomwe zimamunyansa Yehova pali “lilime lonama” ndiponso “mboni yonama yonong’ona mabodza.”—Miyambo 6:16-19.
Anthu ambiri akamanama zingabweretse mavuto kwa munthu payekha ndiponso kwa anthu ochuluka. Ndi ochepa amene angatsutse mfundo imeneyi. Nangano, n’chifukwa chiyani anthu amanama dala? Ndipo kodi nthawi iliyonse yomwe munthu wanena zinthu zomwe si zoona ndiye kuti akunama? Tikambirana mayankho a mafunso amenewa ndi ena mu nkhani yotsatira.
[Chithunzi patsamba 3]
Mabodza amachititsa kuti mwamuna ndi mkazi wake asamakhulupirirane