Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musasiye Kukhala Oyamikira

Musasiye Kukhala Oyamikira

Musasiye Kukhala Oyamikira

“Ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri!”​—SALMO 139:17.

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira Mawu a Mulungu, ndipo wamasalmo anasonyeza bwanji kuyamikira kwake?

PAMENE kachisi wa Yehova anali kukonzedwa ku Yerusalemu, anapeza chinthu chochititsa chidwi kwambiri. Mkulu wa Ansembe, Hilikiya anapeza “buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.” Mosakayikira linali buku lenileni loyambirira lomwe linamalizidwa kulembedwa zaka pafupifupi 800 m’mbuyomo. Kodi mukuganiza kuti Mfumu Yosiya yemwe anali woopa Mulungu, anamva bwanji bukulo litaperekedwa kwa Iye? Zoonadi, analiona kuti linali lamtengo wapatali ndipo nthawi yomweyo anauza Safani mlembi kuti aliwerenge mokweza.​—2 Mbiri 34:14-18.

2 Masiku ano, Mawu a Mulungu, athunthu kapena mbali yake chabe, angawerengedwe ndi anthu mabiliyoni ambiri. Koma kodi zimenezi zachititsa kuti Malembawa akhale osafunika kwambiri? Ayi ndithu! Ndipotu, Malembawa ali ndi malingaliro enieni a Wamphamvuyonse, amene analembedwa kuti atipindulitse. (2 Timoteyo 3:16) Posonyeza mmene ankawaonera Mawu a Mulungu, wamasalmo Davide analemba kuti: “Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri.”​—Salmo 139:17.

3. N’chiyani chikusonyeza kuti Davide anali munthu womvetsetsa mwakuya zinthu zauzimu?

3 Davide sanasiye kuyamikira Yehova, Mawu ake, ndiponso makonzedwe ake a kulambira koona. Masalmo ochuluka abwino kwambiri amene Davide analemba amasonyeza mmene iye ankamvera. Mwachitsanzo, pa Salmo 27:4, analemba kuti: “Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi: Kuti ndikhalitse m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m’Kachisi wake.” M’Chiheberi choyambirira, mawu akuti “kufunsitsa” amatanthauza kuganiza mwakuya, kuonetsetsa, kuyang’ana mwachisangalalo ndi mokopeka. N’zachionekere kuti Davide ankamvetsetsa mwakuya zinthu zauzimu ndipo anali kuyamikiradi zinthu zauzimu zimene Yehova anali kupereka komanso ankasangalala ndi mbali iliyonse ya choonadi imene Yehova ankaulula. Tifunika kutsanzira chitsanzo chake choyamikira chimenechi.​—Salmo 19:7-11.

Yamikirani Mwayi Wodziwa Choonadi cha M’Baibulo

4. N’chiyani chinachititsa Yesu ‘kukondwera kwambiri mwa mzimu woyera’?

4 Kuzindikira Mawu a Mulungu sikudalira kuti munthu akhale wanzeru kapena akhale ndi maphunziro apamwamba akudziko, amene amalimbikitsa kudzikuza. M’malo mwake, zimadalira pa chisomo cha Yehova, chimene amapereka kwa anthu odzichepetsa ndi oona mtima, amene amazindikira zosowa zawo zauzimu. (Mateyo 5:3; 1 Yohane 5:20) Yesu ataganizira mwakuya mfundo yakuti mayina a anthu ena opanda ungwiro anali kulembedwa m’mwamba, “anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera ndi kunena kuti: ‘Atate ndikutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa zinthu izi mwazibisa kwa anzeru ndi ozama m’maphunziro, koma mwaziulula kwa tiana.’”​—Luka 10:17-21.

5. N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu sanayenere kuona mopepuka choonadi cha Ufumu chimene chinaululidwa kwa iwo?

5 Atamaliza kupereka pemphero lochokera pansi pamtima limenelo, Yesu anatembenukira kwa ophunzira ake n’kunena kuti: “Osangalala ali anthu amene maso awo amaona zimene inu mukuonazi. Pakuti ndikukuuzani, Aneneri ndi mafumu ambiri analakalaka kuona zimene mukuzionazi, koma sanazione, ndi kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.” Inde, Yesu analimbikitsa otsatira ake okhulupirika kuti asaone mopepuka choonadi cha Ufumu chamtengo wapatali chimene chinali kuululidwa kwa iwo. Choonadi chimenechi sichinaululidwe kwa mibadwo ya atumiki a Mulungu m’mbuyomo, ndipo mosakayikira sichinaululidwe kwa “Aneneri ndi mafumu” a m’nthawi ya Yesu.​—Luka 10:23, 24.

6, 7. (a) Kodi tili ndi zifukwa zotani zoyamikirira choonadi cha Mulungu? (b) Kodi masiku ano pali kusiyana kotani kumene kukuoneka pakati pa chipembedzo choona ndi chonyenga?

6 Masiku ano, tili ndi zifukwa zambiri zoyamikirira choonadi cha Mulungu popeza Yehova, kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” wachititsa kuti anthu ake amvetsetse mozama Mawu ake. (Mateyo 24:45; Danieli 12:10) Ponena za nthawi yamapeto, mneneri Danieli analemba kuti: “Ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.” (Danieli 12:4) Kodi si mukuvomereza kuti masiku ano chidziwitso chonena za Mulungu ‘chachuluka’ ndiponso kuti atumiki a Yehova akudyetsedwa bwino mwauzimu?

7 Tikuonadi kusiyana kwakukulu pakati pa kulemera kwauzimu kwa anthu a Mulungu ndi chisokonezo chimene chili m’zipembedzo za Babulo Wamkulu. Zotsatirapo zake n’zakuti, anthu ambiri amene akhumudwa kapena kunyansidwa ndi chipembedzo chonyenga ayamba kutsatira kulambira koona. Iwo ndi anthu onga nkhosa amene ‘sakufuna kugawana ndi [Babulo Wamkulu] machimo ake’ kapena “kulandira gawo la miliri yake.” Yehova ndi atumiki ake akuitanira anthu onse oterewa mu mpingo woona wachikhristu.​—Chivumbulutso 18:2-4; 22:17.

Anthu Oyamikira Akukhamukira kwa Mulungu

8, 9. Kodi mawu amene ali pa Hagai 2:7 akukwaniritsidwa motani masiku ano?

8 Ponena za nyumba yake yauzimu yolambiriramo, Yehova ananeneratu kuti: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero.” (Hagai 2:7) Ulosi wochititsa chidwi umenewu unakwaniritsidwa m’nthawi ya Hagai pamene otsalira a anthu a Mulungu obwezeretsedwa anamanganso kachisi ku Yerusalemu. Masiku ano, mawu a Hagai akukwaniritsidwanso m’njira ina mogwirizana ndi kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova.

9 Anthu mamiliyoni ambiri akhamukira kale kukachisi wophiphiritsira kuti akalambire Mulungu “ndi mzimu ndi choonadi,” ndipo chaka chilichonse masauzande ambiri a “zofunika za amitundu onse” akupitirizabe kukhamukira ku kachisiyo. (Yohane 4:23, 24) Mwachitsanzo, lipoti lapachaka lapadziko lonse la chaka chautumiki cha 2006, likusonyeza kuti anthu okwanira 248,327 anabatizidwa posonyeza kudzipereka kwawo kwa Yehova. Zimenezi zikutanthauza kuti pa avereji, anthu atsopano okwanira 680 anali kubatizidwa tsiku lililonse. Chifukwa choti anthuwa amakonda choonadi ndiponso amafuna kutumikira Yehova monga olengeza Ufumu, ndi umboni woti anakokedwadi ndi Mulungu.​—Yohane 6:44, 65.

10, 11. Fotokozani nkhani imene ikusonyeza mmene anthu afikira poyamikira choonadi cha m’Baibulo.

10 Ambiri mwa anthu oona mtima amenewa anakopeka ndi choonadi chifukwa anatha kusiyanitsa “pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.” (Malaki 3:18) Taganizirani zimene zinachitikira Wayne ndi mkazi wake Virginia, omwe anali a tchalitchi chachipulotesitanti koma anali ndi mafunso ambiri omwe sankapeza mayankho ake. Banjali linkadana ndi nkhondo ndipo onse awiri anali osokonezeka maganizo ndi okhumudwa kuona atsogoleri achipembedzo akudalitsa asilikali ndiponso zida za nkhondo. Banjali litayamba kukalamba, linali kuona kuti anthu ena a m’tchalitchimo ankalinyalanyaza, ngakhale kuti Virginia anaphunzitsapo Sande sukulu kwa zaka zingapo. Iwo anati: “Palibe aliyense amene ankatiyendera kapena kudera nkhawa moyo wathu wauzimu. Tchalitchichi chinkangofunako ndalama zathu basi. Tinali okhumudwa kwambiri.” Banjali linakhumudwa kuposa pamenepa litamva kuti tchalitchi chawocho chayamba kuloleza kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.

11 Panthawi imeneyo, mdzukulu wawo wamkazi ndipo kenako mwana wawo wamkazi anakhala Mboni za Yehova. Ngakhale kuti Wayne ndi Virginia poyamba anakwiya chifukwa cha zimenezi, patapita nthawi anasintha maganizo ndipo anavomera kuyamba phunziro la Baibulo. Wayne anati: “Pamiyezi itatu yokha, tinaphunzira zinthu zambiri za m’Baibulo kuposa zimene tinaphunzira pa zaka 70! Tinali tisanamvepo kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, ndipo sitinkadziwa chilichonse chonena za Ufumu ndiponso dziko lapansi la Paradaiso.” Posapita nthawi, banja loona mtima limeneli linayamba kupezeka pa misonkhano yachikhristu ndiponso kupita nawo mu utumiki. Virginia anati: “Tikufuna tiuze aliyense choonadi.” Onse awiri anabatizidwa m’chaka cha 2005, ali ndi zaka za m’ma 80. Iwo anati: “Tsopano tapeza banja lachikhristu lenileni.”

Yamikirani Kuti Ndinu ‘Okonzeka . . . Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino’

12. Kodi Yehova nthawi zonse amapereka chiyani kwa atumiki ake, ndipo tiyenera kuchita chiyani kuti tipindule?

12 Yehova nthawi zonse amathandiza atumiki ake kuchita chifuniro chake. Mwachitsanzo, Nowa analandira malangizo omveka bwino ndiponso achindunji a mmene angamangire chingalawa. Ntchito imeneyi inafunika kugwiridwa bwino nthawi yoyamba yomweyo. Ndipo anaigwiradi bwino. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Nowa anachita “monga mwa zonse anam’lamulira iye Mulungu, momwemo anachita.” (Genesis 6:14-22) Masiku anonso, Yehova akukonzekeretsa bwino atumiki ake kuti achite chifuniro chake. Ndipotu, ntchito yathu yaikulu ndi yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene unakhazikitsidwa, ndi kuthandiza anthu oyenerera kuti akhale ophunzira a Yesu Khristu. Ndipo monga mmene zinalili ndi Nowa, kuti tipambane tiyenera kukhala omvera. Tiyenera kumvera ndi kutsatira malangizo amene Yehova amapereka kudzera m’Mawu ake ndiponso m’gulu lake.​—Mateyo 24:14; 28:19, 20.

13. Kodi Yehova amatiphunzitsa pogwiritsa ntchito chiyani?

13 Kuti tikwanitse ntchito imeneyi, tiyenera kuphunzira ‘kulondoloza bwino’ chida chathu chachikulu, Mawu a Mulungu, omwe ndi “opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteyo 2:15; 3:16, 17) Monga mmene zinalili Chikhristu chitangoyamba kumene, Yehova amatipatsa maphunziro ofunikira kudzera mu mpingo wachikhristu. Masiku ano, m’mipingo 99,770 padziko lonse lapansi, mumachitika Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndiponso Msonkhano wa Utumiki mlungu uliwonse. Misonkhano imeneyi cholinga chake n’choti itithandize pa utumiki wathu. Kodi mumasonyeza kuyamikira misonkhano yofunika imeneyi mwa kupezekapo nthawi zonse ndiponso kugwiritsa ntchito zinthu zimene mumaphunzira?​—Aheberi 10:24, 25.

14. Kodi atumiki a Yehova amasonyeza bwanji kuyamikira mwayi wawo wotumikira Mulungu? (Muneneponso za tchati chomwe chili pa masamba 27 mpaka 30.)

14 Mwa kuchita khama mu utumiki, mamiliyoni ambiri a anthu a Mulungu padziko lonse lapansi akusonyeza kuyamikira maphunziro amene amalandira. Mwachitsanzo, m’chaka cha utumiki cha 2006, ofalitsa Ufumu okwanira 6,741,444 anathera maola okwanira 1,333,966,199 m’bali zonse za ntchitoyi, zimene zinaphatikizapo kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba okwanira 6,286,618. Zimenezi ndi mfundo zina chabe zolimbikitsa zimene zandandalikidwa mu lipoti lapachaka lapadziko lonse. Tikukupemphani kuti muone bwinobwino lipotili ndipo likulimbikitseni, monga mmene abale athu oyambirira mosakayikira analimbikitsidwira kwambiri ndi lipoti lonena za kukula kwa ntchito yolalikira m’nthawi yawo.​—Machitidwe 1:15; 2:5-11, 41, 47; 4:4; 6:7.

15. N’chifukwa chiyani aliyense wa ife sayenera kugwa mphwayi pamene akutumikira Yehova ndi mtima wonse?

15 Mawu amphamvu achitamando amene amapita kwa Mulungu chaka chilichonse, amasonyeza kuti atumiki a Yehova akuyamikira kwambiri kukhala ndi mwayi womudziwa Yehova ndiponso womuchitira umboni. (Yesaya 43:10) Zoonadi, nsembe zachitamando zimene abale ndi alongo athu ena okalamba, odwala kapena ofooka amapereka, zingafanizidwe ndi chopereka cha mkazi wamasiye. Koma tisaiwale kuti Yehova ndi Mwana wake amayamikiradi onse amene amatumikira Mulungu ndi mtima wonse, pamene akuchita zonse zomwe angathe.​—Luka 21:1-4; Agalatiya 6:4.

16. Pazaka zaposachedwapa, kodi Mulungu watipatsa mabuku ati ophunzitsira?

16 Kuwonjezera pa kutiphunzitsa utumiki, Yehova, kudzera m’gulu lake, amatipatsa mabuku abwino kwambiri ophunzitsira. Pa zaka zaposachedwapa, mabuku ophunzitsira amene tapatsidwa ndi monga, Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, ndipo posachedwapa, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Anthu amene amayamikiradi mabuku amene tapatsidwawa, amawagwiritsa ntchito bwino muutumiki.

Gwiritsani Bwino Ntchito Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani

17, 18. (a) Kodi ndi mbali ziti za m’buku la Baibulo limaphunzitsa chiyani zimene mumakonda kusonyeza anthu muutumiki wanu? (b) Kodi woyang’anira dera wina anati chiyani ponena za buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?

17 Buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lili ndi machaputala 19 ndiponso lili ndi zakumapeto zofotokoza nkhani mwatsatanetsatane, ndipo n’lolembedwa m’njira yosavuta kumva. Chifukwa cha zimenezi, bukuli likuthandiza kwambiri mu utumiki. Mwachitsanzo, chaputala 12 chili ndi mutu wakuti “Kukhala ndi Moyo Wokondweretsa Mulungu.” Mutu umenewu umafotokoza kwa wophunzira mmene angakhalire bwenzi la Mulungu, ndipo zimenezi ndi zinthu zimene anthu ambiri sanayambe aganizapo kuti n’zotheka. (Yakobe 2:23) Kodi anthu akuliona motani buku lophunzitsira Baibulo limeneli?

18 Woyang’anira dera wina ku Australia anati buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani “limakopa mwamsanga eni nyumba ndipo amachita nalo chidwi n’kuyamba kukambirana nafe.” Anawonjezera kuti, bukuli n’losavuta kugwiritsa ntchito moti “lachititsa ofalitsa a Ufumu ambiri kuyambiranso kukhala odzidalira ndi achimwemwe mu utumiki. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ena akuti bukuli ndi lamtengo wapatali ngati golide!”

19-21. Fotokozani nkhani zina zimene zikusonyeza kufunika kwa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.

19 Mkazi wina wa ku Guyana ananena kwa mpainiya yemwe anafika pa golosale yake kuti: “Ayenera kuti ndi Mulungu amene wakutumizani.” Mwamuna amene mkaziyo ankakhala naye limodzi, anali atangomusiya kumene limodzi ndi ana awo awiri ang’onoang’ono. Mpainiyayo anatsegula buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pa chaputala choyamba ndipo anawerenga mokweza ndime 11, pansi pa kamutu kakang’ono kakuti “Kodi Mulungu Amamva Bwanji Akamaona Zinthu Zopanda Chilungamo Zimene Zimatichitikira?” Mpainiyayo anati: “Mfundozo zinamukhudza mtima kwambiri, moti mpaka anaimirira n’kupita kuseri kwa golosale yake, komwe anakalira kwambiri.” Mkazi ameneyu anavomera kuchita phunziro la Baibulo nthawi zonse ndi mlongo wina wakomweko ndipo akupitabe patsogolo.

20 José, yemwe amakhala ku Spain, mkazi wake anamwalira pa ngozi ya galimoto. Pofuna kutonthozedwa, anayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ndipo analandiranso thandizo kuchokera kwa akatswiri a maganizo. Komabe, akatswiri a maganizowo sanathe kuyankha funso limene linkavutitsa kwambiri maganizo a José lakuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti mkazi wanga amwalire?” Tsiku lina José anakumana ndi Francesc, yemwe ankagwira naye ntchito pakampani imodzi. Francesc anamuuza kuti akambirane mutu 11 wa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, wakuti “N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?” José anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene Malemba amafotokoza ndiponso fanizo la mphunzitsi ndi mwana wasukulu. Anayamba kuphunzira mwakhama, anapezeka pa msonkhano wadera, ndipo tsopano amapezeka pa misonkhano ku Nyumba ya Ufumu.

21 Roman, mwamuna wabizinesi wa zaka 40 wa ku Poland, wakhala akulemekeza Mawu a Mulungu kuyambira kalekale. Koma chifukwa chakuti anali wotanganidwa ndi ntchito yake, anangopita patsogolo pang’ono ndi phunziro lake la Baibulo kenako n’kusiya. Komabe, anakapezeka pa msonkhano wachigawo ndipo analandira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kenaka, anapita patsogolo msanga. Iye anati: “Ndi buku limeneli, ziphunzitso zonse zoyambirira za m’Baibulo zimamveka bwino moti munthu amatha kuona bwinobwino chithunzi chonse.” Tsopano Roman akuphunzira Baibulo nthawi zonse ndipo akupita patsogolo kwambiri.

Pitirizani Kuyamikira

22, 23. Kodi tingapitirize bwanji kusonyeza kuyamikira kwathu chifukwa cha chiyembekezo chimene tili nacho?

22 Monga mmene anafotokozera pa msonkhano wachigawo wosangalatsa kwambiri wa “Chipulumutso Chayandikira,” Akhristu oona amalakalaka “chipulumutso chosatha” chimene Mulungu analonjeza. Chipulumutsochi chidzatheka chifukwa cha magazi okhetsedwa a Yesu Khristu. Palibenso njira ina yabwino yosonyezera kuyamikira kochokera pansi pamtima chifukwa cha chiyembekezo chimenechi, kuposa kupitiriza kuyeretsedwa “ku ntchito zakufa, kuti tichite utumiki wopatulika kwa Mulungu wamoyo.”​—Aheberi 9:12, 14.

23 Inde, n’zozizwitsadi kuona olengeza Ufumu oposa 6 miliyoni akupirira mokhulupirika potumikira Mulungu, panthawi ino imene anthu akulimbikitsidwa kuposa kale lonse kuchita zinthu zodzisangalatsa okha. Komanso ndi umboni woti atumiki a Yehova amayamikira kwambiri mwayi wotumikira Mulungu, podziwa kuti ‘kugwiritsa ntchito kwawo sikupita pachabe mwa Ambuye.’ Choncho musasiye kukhala ndi mtima woyamikira woterowo!​—1 Akorinto 15:58; Salmo 110:3.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi wamasalmo akutiphunzitsa chiyani ponena za kuyamikira Mulungu ndi zinthu zauzimu zimene amapereka?

• Kodi mawu a pa Hagai 2:7 akukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

• Kodi Yehova wathandiza bwanji atumiki ake kuti athe kum’tumikira bwino?

• Kodi mungachite chiyani kuti musonyeze kuti mumayamikira ubwino wa Yehova?

[Mafunso]

[Tchati pamasamba 27-30]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 2006 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Zithunzi patsamba 25]

Yehova amatipatsa zofunikira zonse kuti tichite chifuniro chake