Yehova Ndi Mulungu Woyamikira
Yehova Ndi Mulungu Woyamikira
“Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”—AHEBERI 6:10.
1. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anayamikira mkazi wachimoabu Rute?
YEHOVA amayamikira kwambiri khama la anthu amene moona mtima amafunafuna kuchita chifuniro chake, ndipo amawadalitsa kwambiri. (Aheberi 11:6) Mwamuna wokhulupirika Boazi ankadziwa bwino mbali yochititsa chidwi imeneyi ya umunthu wa Mulungu, chifukwa polankhula ndi mkazi wachimoabu Rute, amene anasamalira apongozi ake amasiye mwachikondi, iye anati: “Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova.” (Rute 2:12) Kodi Mulungu anadalitsa Rute? Inde! Ndipo nkhani yake inalembedwa m’Baibulo. Komanso, anakwatiwa ndi Boazi ndipo anakhala kholo la Mfumu Davide ndiponso Yesu Khristu. (Rute 4:13, 17; Mateyo 1:5, 6, 16) Chimenechi ndi chitsanzo chimodzi chokha mwa zitsanzo zambiri m’Baibulo zosonyeza kuti Yehova amayamikira atumiki ake.
2, 3. (a) N’chiyani chimachititsa kuti zochita za Yehova zosonyeza kuyamikira zikhale zapadera? (b) N’chifukwa chiyani Yehova amatha kuyamikira mochokera pansi pamtima? Perekani chitsanzo.
2 Yehova angaone kuti n’kusalungama kumbali yake ngati angasonyeze kusayamikira. Lemba la Aheberi 6:10 limati: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikira oyera ndipo mukupitirizabe kuwatumikira.” Chimene chikuchititsa kuti mawu amenewa akhale apadera n’choti, Mulungu amayamikira anthu okhulupirika ngakhale ali ochimwa ndi operewera pa ulemerero wake.—Aroma 3:23.
3 Popeza ndife opanda ungwiro, tingaone kuti zochita zathu zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu n’zosanunkha kanthu ndipo n’zosayenerera kulandira nazo madalitso ochokera kwa Mulungu. Komabe, Yehova amamvetsa bwino zolinga zathu komanso mmene zinthu zilili pa moyo wathu, ndipo amayamikira utumiki wathu womwe timachita ndi moyo wathu wonse. (Mateyo 22:37) Mwachitsanzo: Tiyerekezere kuti mayi wapeza mphatso ya mkanda wa m’khosi wotchipa uli patebulo lake. Akhoza kuona kuti mphatsoyo n’njosafunika kwenikweni n’kungoinyalanyaza. Komabe, powerenga khadi lomwe labwera pamodzi ndi mphatsoyo akuona kuti yachokera kwa mwana wake wamng’ono wamkazi, amene wawononga ndalama zake zonse zomwe ankasunga, kugula mphatsoyo. Mayiyo tsopano akuiona mphatsoyo mosiyana ndi poyamba paja. Mwina mpaka misozi ikulengeza m’maso mwake, ndipo akukupatira mwana wake uja n’kumuuza kuti akuyamikira kuchokera pansi pamtima.
4, 5. Kodi Yesu anatsanzira motani Yehova posonyeza kuyamikira?
4 Popeza Yehova amadziwa zolinga zathu ndiponso Luka 21:1-4.
zinthu zimene sitingathe kuchita, amatiyamikira tikam’patsa zonse zomwe tingathe, kaya n’zochepa kapena n’zambiri. Pankhani imeneyi, Yesu anasonyeza bwino zedi khalidwe la Atate wake. Takumbukirani nkhani ya m’Baibulo yonena za chopereka cha mkazi wamasiye. Nkhaniyo imati: “[Yesu] atakweza maso anaona anthu olemera akuponya zopereka zawo moponyamo zopereka. Kenako anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobili tiwiri tating’ono mmenemo. Ndipo iye anati: ‘Kunena zoona, Mkazi wamasiyeyu, ngakhale kuti ndi wosauka, waponya zochuluka kuposa onse amene aponya. Pakuti onsewa aponya zopereka zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene akanatha kuchirikiza nazo moyo wake.’”—5 Indedi, kuzindikira mmene mkaziyo analili, kuti anali wamasiye ndiponso wosauka, kunam’chititsa Yesu kudziwa mtengo weniweni wa mphatso yakeyo, ndipo anaiyamikira kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi Yehova. (Yohane 14:9) Kodi sizolimbikitsa kudziwa kuti mulimonse mmene zinthu zingakhalire pamoyo wanu, mukhoza kuyanjidwa ndi Mulungu wathu woyamikira ndi Mwana wake?
Yehova Anadalitsa Mkusi Woopa Mulungu
6, 7. N’chifukwa chiyani Yehova anayamikira Ebedi-Meleki, ndipo anachita motani zimenezi?
6 Malemba amasonyeza mobwerezabwereza kuti Yehova amayamikira anthu amene amachita chifuniro chake. Taganizirani zimene anachita ndi Mkusi wina woopa Mulungu, Ebedi-Meleki. Mkusiyu anakhala ndi moyo mu nthawi ya Yeremiya ndipo ankagwira ntchito m’nyumba ya Mfumu yosakhulupirika ya Yuda, Zedekiya. Ebedi-Meleki anamva zoti akulu a Yuda anamunamizira mneneri Yeremiya mlandu woukira boma ndipo anam’ponya m’chitsime kuti afe ndi njala. (Yeremiya 38:1-7) Podziwa kuti Yeremiya anali kudedwa kwambiri chifukwa cha uthenga umene anali kulalikira, Ebedi-Meleki analolera kuika moyo wake pangozi n’kupita kukalankhula ndi mfumu. Mkusiyu analankhula molimba mtima, kuti: “Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m’zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anam’ponya m’dzenje; ndipo afuna kufa m’menemo chifukwa cha njala.” Molamulidwa ndi mfumu, Ebedi-Meleki anatenga amuna 30 n’kukapulumutsa mneneri wa Mulunguyo.—Yeremiya 38:8-13.
7 Yehova anaona kuti Ebedi-Meleki anali ndi chikhulupiriro, chimene chinam’thandiza kuthetsa mantha alionse amene akanakhala nawo. Choncho, kudzera mwa Yeremiya, Yehova anayamikira Ebedi-Meleki, ndipo anati: “Taona, ndidzafikitsira mudzi uwu mawu anga kuusautsa, osauchitira zabwino . . . Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo . . . ndipo sudzaperekedwa m’manja a anthu amene uwaopa. Pakuti ndidzakupulumutsatu . . . koma udzakhala nawo moyo wako ngati chofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine.” (Yeremiya 39:16-18) Indedi, Yehova anapulumutsa Ebedi-Meleki, komanso Yeremiya, m’manja mwa akulu a Yuda oipa aja ndipo kenako anawapulumutsanso kwa Ababulo, amene anawononga Yerusalemu. Lemba la Salmo 97:10 limati: “[Yehova] asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m’manja mwa oipa.”
“Atate Wako Amene Amaona Kosaonekako, Adzakubwezera”
8, 9. Monga mmene Yesu anasonyezera, kodi Yehova amayamikira mapemphero otani?
8 Umboni wina wosonyeza kuti Yehova amayamikira mawu athu osonyeza kudzipereka kwa Mulungu ndipo amaona kuti mawuwa ndi amtengo wapatali tingauone m’zimene Baibulo limanena pa nkhani ya pemphero. Munthu wina wanzeru anati: “Pemphero la oongoka mtima lim’kondweretsa [Mulungu].” (Miyambo 15:8) M’masiku a Yesu, atsogoleri ambiri achipembedzo ankapemphera pamaso pa anthu, osati chifukwa chokondadi Mulungu, koma pongofuna kudzionetsera kwa anthuwo. Yesu anati: “Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse.” Ndipo analangiza otsatira ake kuti: “Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka; ukatero Atate wako amene amaona kuchokera kosaonekako adzakubwezera.”—Mateyo 6:5, 6.
9 N’zoona kuti Yesu sanali kudana ndi kupemphera pa gulu, chifukwa iyenso ankapemphera pa gulu pazochitika zina. (Luka 9:16) Yehova amayamikira kwambiri tikamapemphera kwa iye kuchokera pansi pa mtima, opanda cholinga chilichonse chofuna kudzionetsera kwa ena. Ndipotu, mapemphero a patokha ndi amene amasonyeza bwino ngati timakonda kwambiri Mulungu ndiponso ngati timam’khulupirira. N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti kawirikawiri Yesu ankafunafuna malo ayekha kuti apemphere. Anachitapo zimenezi “m’mamawa kukali mdima.” Ndipo panthawi ina, “anakwera m’phiri yekhayekha kukapemphera.” Ndipo asanasankhe atumwi ake 12, Yesu anachezera yekhayekha kupemphera kwa Mulungu usiku wonse.—Maliko 1:35; Mateyo 14:23; Luka 6:12, 13.
10. Ngati mapemphero athu amasonyeza kuti akuchokera pansi pamtima ndipo ngati amasonyeza zimene zili mumtima mwathu, kodi tingakhale otsimikiza za chiyani?
10 Tangoganizani mmene Yehova ankatcherera khutu ku zimene Mwana wake ankalankhula kuchokera pansi pamtima! Indedi, Yesu nthawi zina anali kupemphera “ndi kulira kwakukulu ndi misozi, ndipo anamvedwa chifukwa cha kuopa kwake Mulungu.” (Aheberi 5:7; Luka 22:41-44) Ngati mapemphero athu amasonyeza kuona mtima koteroko ndiponso ngati amasonyeza zimene zili mumtima mwathu, tingakhale otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba amatchera khutu ndiponso amawayamikira. Zoonadi, “Yehova ali pafupi ndi onse . . . akuitanira kwa Iye m’choonadi.”—Salmo 145:18.
11. Kodi Yehova amamva bwanji ndi zinthu zimene timachita pamene anthu ena sakutiona?
11 Ngati Yehova amayamikira tikamapemphera kwa iye tili tokha, Iye angayamikirenso kwambiri tikamamumvera panthawi imene tili tokha. Zoonadi, Yehova amadziwa zimene timachita pamene anthu ena sakutiona. (1 Petulo 3:12) Indedi, kukhala omvera pamene tili tokha n’chizindikiro chabwino choti tili ndi “mtima wangwiro” kwa Yehova, mtima umene uli ndi zolinga zabwino ndiponso wosasunthika pa zinthu zabwino. (1 Mbiri 28:9) Khalidwe loterolo limakondweretsa kwambiri mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11; 1 Yohane 3:22.
12, 13. Kodi tingateteze bwanji maganizo ndi mtima wathu ndi kukhala ngati wophunzira wokhulupirika Natanayeli?
Aheberi 4:13; Luka 8:17) Tikamayesetsa kupewa zinthu zimene sizikondweretsa Yehova, timakhala ndi chikumbumtima chabwino ndipo timasangalala kudziwa kuti Mulungu akutiyanja. Inde, sitikayikira kuti Yehova amayamikiradi munthu amene ‘akuyenda mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake.’—Salmo 15:1, 2.
12 Motero, Akhristu okhulupirika amapewa machimo a mseri amene amawononga maganizo ndi mtima, monga kuonerera zinthu zolaula ndiponso zachiwawa. Ngakhale kuti machimo ena angakhale obisika kwa anthu, timazindikira kuti “zinthu zonse zili pambalambanda ndi zoonekera poyera pamaso pake. Inde, pamaso pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.” (13 Komabe, kodi tingateteze bwanji maganizo ndi mtima wathu m’dziko limene ladzala ndi zoipali? (Miyambo 4:23; Aefeso 2:2) Kuphatikiza pa kugwiritsa ntchito zinthu zauzimu zonse zimene Yehova amapereka, tiyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tipewe zoipa ndi kuchita zabwino, ndipo tiyenera kuchita zimenezo mwamsanga kuti zilakolako zoipa zisakule ndi kubala uchimo. (Yakobe 1:14, 15) Taganizirani mmene mungasangalire ngati Yesu atanena za inu monga mmene ananenera za Natanayeli kuti: ‘Onani [munthu], amene mwa iye mulibe chinyengo.’ (Yohane 1:47) Natanayeli, yemwe ankatchedwanso Batolomeyo, kenaka anapatsidwa mwayi wokhala mmodzi wa atumwi 12 a Yesu.—Maliko 3:16-19.
“Mkulu wa Ansembe Wachifundo ndi Wokhulupirika”
14. Kodi Yesu anaona bwanji zimene Mariya anachita poyerekezera ndi mmene anthu ena anazionera?
14 Popeza Yesu ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo,” Yehova, nthawi zonse amatsanzira bwino Atate wake posonyeza kuyamikira anthu amene akutumikira Mulungu ndi mtima woyera. (Akolose 1:15) Mwachitsanzo, patatsala masiku asanu kuti apereke moyo wake, Yesu ndi ophunzira ake anaitanidwa ku nyumba ya Simoni wa ku Betaniya. Usiku umenewo, Mariya, yemwe anali mlongo wake wa Lazaro ndiponso Malita, “anatenga mafuta onunkhira, nado weniweni, wokwera mtengo” (mtengo wake unali wofanana ndi malipiro a munthu a chaka chonse). Ndipo anathira mafutawo pamutu ndi pamapazi a Yesu. (Yohane 12:3) Anthu ena anati: “N’kuwonongeranji chonchi?” Komabe, Yesu anaona zimene Mariya anachita mosiyana kwambiri ndi enawo. Iye anaona kuti kumeneko ndi kuwolowa manja kosaneneka ndiponso kwa tanthauzo lalikulu poganizira za imfa ndi kuikidwa m’manda kwake kumene kunatsala pang’ono kuchitika. Choncho, m’malo modzudzula Mariya, Yesu anam’yamikira. Iye anati: “Kulikonse kumene uthenga wabwinowu udzalalikidwa m’dziko lonse, zimene mayiyu wachita zidzasimbidwanso.”—Mateyo 26:6-13.
15, 16. Kodi timapindula bwanji chifukwa choti Yesu anakhalapo munthu n’kumatumikira Mulungu?
15 Ndi mwayi waukulu zedi kuti Yesu, woyamikira chotereyu, ndiye Mtsogoleri wathu. Ndipotu, chifukwa choti Yesu anakhalapo munthu zinam’pangitsa kukonzekera ntchito imene Yehova anali kum’sungira. Ntchito yake inali yotumikira monga Mkulu wa Ansembe ndiponso Mfumu, choyamba kwa mpingo wa anthu odzozedwa, kenako kwa dziko lonse lapansi.—Akolose 1:13; Aheberi 7:26; Chivumbulutso 11:15.
16 Yesu asanabwere pa dziko lapansi, anali kale ndi chidwi chachikulu ndi anthu ndiponso ankawakonda kwambiri. (Miyambo 8:31) Mwakukhala munthu, anadziwa bwino mayesero amene timakumana nawo potumikira Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “[Yesu] anayenera ndithu kukhala ngati ‘abale’ ake m’zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika . . . Popeza kuti iye mwini anavutika poyesedwa, amatha kuthandiza iwo amene akuyesedwa.” Yesu akhoza ‘kutimvera chisoni pa zofooka zathu’ chifukwa “wayesedwa m’zonse ngati ifeyo, napezekabe wopanda uchimo.”—Aheberi 2:17, 18; 4:15, 16.
17, 18. (a) Kodi makalata opita ku mipingo 7 ya ku Asiyamina amasonyeza bwanji kuyamikira kwa Yesu kochokera pansi pa mtima? (b) Kodi Akhristu odzozedwawo anali kukonzekeretsedwera chiyani?
17 Yesu ataukitsidwa, m’pamene zinaonekera bwino kwambiri kuti Iye akumvetsa bwino ziyeso zimene otsatira ake anali kukumana nazo. Taganizirani za makalata ake opita ku mipingo 7 ya ku Chivumbulutso 2:8-10.
Asiyamina, omwe mtumwi Yohane analemba. Yesu anauza mpingo wa ku Simuna kuti: “Ndikudziwa chisautso chako ndi umphawi wako.” Pamenepa, Yesu kwenikweni anali kunena kuti, ‘Ndikumvetsa bwino mavuto anu. Ndikudziwadi zimene mukukumana nazo.’ Kenaka, popeza iyemwini anazunzika mpaka kuphedwa, Yesu analankhula ndi chifundo ndi ulamuliro, kuti: “Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa, ndipo ndidzakupatsa kolona wa moyo.”—18 Makalata opita ku mipingo 7 amenewa ndi odzadza ndi mawu amene akusonyeza kuti Yesu ankadziwa bwinobwino mavuto amene ophunzira ake anali kukumana nawo ndipo anawayamikira ophunzirawo mochokera pansi pamtima chifukwa cha moyo wawo wokhulupirika. (Chivumbulutso 2:1–3:22) Kumbukirani kuti anthu amene Yesu ankalankhula nawowa anali Akhristu odzozedwa omwe anali ndi chiyembekezo chokalamulira naye limodzi kumwamba. Mofanana ndi Mbuye wawo, anali kukonzekeretsedwera ntchito yawo yapamwamba yokathandiza kupereka mwachifundo phindu la nsembe ya dipo ya Khristu kwa anthu ofunikira thandizo.—Chivumbulutso 5:9, 10; 22:1-5.
19, 20. Kodi anthu amene akupanga “khamu lalikulu” akusonyeza bwanji kuyamikira Yehova ndi Mwana wake?
19 Komabe, chikondi cha Yesu pa otsatira ake odzozedwa chikufikanso kwa “nkhosa zina” zokhulupirika, ndipo ambiri mwa anthu amenewa tsopano akupanga gulu limene lidzakhale “khamu lalikulu . . . lochokera m’dziko lililonse,” lomwe lidzapulumuke pa ‘chisautso chachikulu’ chimene chikubwera patsogolopa. (Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9, 14) Anthu amenewa akukhamukira ku mbali ya Yesu chifukwa amayamikira nsembe yake ya dipo ndiponso chiyembekezo chawo cha moyo wosatha. Kodi amasonyeza motani kuyamikira kwawo? Amatero mwa ‘kum’chitira [Mulungu] utumiki wopatulika usana ndi usiku.’—Chivumbulutso 7:15-17.
20 Lipoti lapachaka lapadziko lonse la chaka chautumiki cha 2006, limene lalembedwa pa masamba 27 mpaka 30, likupereka umboni waukulu woti atumiki okhulupirika amenewa akuchitiradi Yehova “utumiki wopatulika usana ndi usiku.” Ndipotu, pachaka chimodzi chimenechi, iwo pamodzi ndi otsalira ochepa a gulu la Akhristu odzozedwa anathera maola okwana 1,333,966,199 mu ntchito yolalikira, omwe akufanana ndi zaka zoposa 150,000!
Pitirizani Kuyamikira!
21, 22. (a) Posonyeza kuyamikira, n’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kusamala makamaka masiku ano? (b) Kodi tidzakambirana chiyani mu nkhani yotsatira?
21 Pochita zinthu ndi anthu opanda ungwiro, Yehova ndi Mwana wake asonyeza kuyamikira kwakukulu ndiponso kodabwitsadi. Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri saganizira za Mulungu. M’malo mwake amaika maganizo awo onse pa zofuna zawo. Pofotokoza anthu a “m’masiku otsiriza,” Paulo analemba kuti: “Anthu adzakhala odzikonda kotheratu, okonda ndalama . . . Adzakhala osayamika m’pang’ono pomwe.” (2 Timoteyo 3:1-5, Phillips) Anthu oterewa ndi osiyana kwambiri ndi Akhristu oona. Akhristu oonawa amapemphera mochokera pansi pamtima, amamvera mosanyinyirika, ndiponso amatumikira ndi mtima wonse posonyeza kuti akuyamikira Mulungu chifukwa cha zonse zomwe wawachitira.—Salmo 62:8; Maliko 12:30; 1 Yohane 5:3.
22 Mu nkhani yotsatira, tidzaona zina mwa zinthu zauzimu zambiri zimene Yehova watipatsa mwachikondi. Tikamakambirana za ‘mphatso zabwino’ zimenezi, tiyeni tikulitse kwambiri mtima wathu woyamikira.—Yakobe 1:17.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti ndi Mulungu woyamikira?
• Kodi tingakondweretse bwanji mtima wa Yehova pamene anthu ena sakutiona?
• Kodi Yesu anasonyeza kuyamikira m’njira ziti?
• Kodi kukhala munthu kunam’thandiza bwanji Yesu kuti akhale wolamulira wachifundo ndiponso woyamikira?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 17]
Monga mmene kholo limasangalalira ndi zochepa zimene mwana wake wachita, Yehova amayamikira tikamam’patsa zonse zomwe tingathe