Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ananu, Muzimvera Makolo Anu”

“Ananu, Muzimvera Makolo Anu”

“Ananu, Muzimvera Makolo Anu”

“Ananu, muzimvera makolo anu mwa Ambuye, pakuti kuchita zimenezi n’chilungamo.”​—AEFESO 6:1.

1. Kodi kumvera kungakutetezeni bwanji?

N’KUTHEKA kuti tili ndi moyo lero chifukwa chomvera, pamene ena anafa chifukwa chosamvera. Kumvera chiyani? Kumvera machenjezo, mwachitsanzo, machenjezo a matupi athu omwe anapangidwa ‘modabwitsa.’ (Salmo 139:14) Tiyerekezere kuti maso athu akuona mitambo yakuda, ndipo makutu athu akumva kugunda kwa mabingu. Kenaka, tsitsi lathu likuyendayenda chifukwa cha zing’aning’ani. Anthu amene akudziwa kuopsa kwa zizindikiro zimenezi amadziwa kuti limeneli ndi chenjezo. Choncho amakabisala kuti asavulazidwe ndi mvula ya zing’aning’ani ndi matalala yomwe yatsala pang’ono kugwa.

2. N’chifukwa chiyani ana amafunikira kuchenjezedwa, ndipo n’chifukwa chiyani ayenera kumvera makolo awo?

2 Ananu mumafunikira kuchenjezedwa za zinthu zimene zingakuvulazeni, ndipo makolo anu ali ndi udindo wokuchenjezani zimenezi. Mwina mukukumbukira kuti munauzidwapo kuti: “Usagwire moto. Ukuwotcha.” “Usayandikire madziwo. N’ngoopsa.” “Uziyang’ana mbali zonse za msewu usanawoloke.” Koma n’zomvetsa chisoni kuti ana ena avulazidwa kapenanso kuphedwa kumene chifukwa chosamvera. Kumvera makolo anu “n’chilungamo,” kapena kuti n’chinthu choyenera ndi chabwino. Komanso ndi nzeru. (Miyambo 8:33) Lemba lina la m’Baibulo limati “n’chokondweretsa” Ambuye wathu Yesu Khristu. Inde, Mulungu akukulamulani kuti muzimvera makolo anu.​—Akolose 3:20; 1 Akorinto 8:6.

Kumvera Kumapindulitsa Kosatha

3. Kodi kwa ambirife “moyo weniweniwo” ndi uti, ndipo ana angatani kuti adzakhale nawo?

3 Kumvera makolo anu kumateteza moyo wanu panopa, komanso kungakuchititseni kuti mudzasangalale ndi moyo “umene ukubwerawo,” umene umatchedwa “moyo weniweniwo.” (1 Timoteyo 4:8; 6:19) Moyo weniweniwo kwa ambirife udzakhala moyo wosatha padziko lapansi latsopano la Mulungu, limene walonjeza anthu amene amamvera malamulo ake mokhulupirika. Lamulo lina lofunika pa malamulo amenewa limati: “‘Lemekeza atate wako ndi amayi wako,’ ndilo lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo: ‘Kuti zinthu zikuyendere bwino, ndi kutinso ukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.’” Choncho mukamamvera makolo anu, mudzakhala osangalala. Mudzakhalanso ndi tsogolo labwino, ndipo mukhoza kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso.​—Aefeso 6:2, 3.

4. Kodi ana angalemekeze bwanji Mulungu kuti apindule?

4 Mukamalemekeza makolo anu mwakumvera, mumalemekezanso Mulungu, chifukwa ndiye akukuuzani kuti muziwamvera. Koma inuyonso mumapindula. Baibulo limati: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula.” (Yesaya 48:17; 1 Yohane 5:3) Kodi kumvera kumakupindulitsani bwanji? Kumakondweretsa amayi ndi abambo anu amene angasonyeze kukondwera kwawoko pochita zinthu zimene zidzakuchititsaninso inuyo kusangalala pa moyo wanu. (Miyambo 23:22-25) Koma chofunika koposa n’choti kumvera kwanu kumakondweretsa Atate wanu wakumwamba, ndipo adzakudalitsani kwambiri. Yesu ananena kuti: ‘Ndimachita zinthu zokondweretsa Mulungu nthawi zonse.’ Tiyeni tione mmene Yehova anadalitsira Yesu ndi kum’teteza.​—Yohane 8:29.

Yesu Anali Wolimbikira Ntchito

5. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu anali wolimbikira ntchito?

5 Yesu anali mwana woyamba wa Mariya. Bambo wake womulera, Yosefe, anali kalipentala. Yesu nayenso anali kalipentala, ndipo zikuoneka kuti anaphunzira ntchitoyi kwa Yosefe. (Mateyo 13:55; Maliko 6:3; Luka 1:26-31) Kodi mukuganiza kuti Yesu anali kalipentala wotani? Ali kumwamba, mayi ake asanatenge pathupi pake mozizwitsa, iye analankhula ngati kuti ndi nzeru imene ikulankhula. Anati: “Ndinali pa mbali [pa Mulungu] ngati mmisiri; ndinam’sekeretsa tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse.” Mulungu anakondwera ndi Yesu, amene anali wolimbikira ntchito kumwamba. Kodi mukuganiza kuti ali mwana padziko lapansi ankalimbikiranso ntchito, n’kukhala kalipentala wabwino?​—Miyambo 8:30; Akolose 1:15, 16.

6. (a) N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti Yesu ali mwana ankagwira ntchito zapakhomo? (b) Kodi ana angatsanzire bwanji Yesu?

6 Baibulo limanena kuti kalelo ana ankasewera ndi anzawo. (Zekariya 8:5; Mateyo 11:16, 17) Mosakayikira, Yesu ali mwana, nthawi zina ankaseweranso ndi anzake. Komabe, popeza iye anali mwana woyamba m’banja lalikulu ndi losauka, mwachidziwikire ankagwira ntchito zapakhomo kuwonjezera pa kuphunzira ukalipentala kwa Yosefe. Kenako, Yesu anakhala mlaliki ndipo anadzipereka kwambiri pa utumiki wake mpaka analolera kudzimana zinthu zina. (Luka 9:58; Yohane 5:17) Kodi mukuona mmene mungatsanzirire Yesu? Kodi makolo anu amakuuzani kuti mukonze m’chipinda chanu kapena mugwire ntchito zina zapakhomo? Kodi amakulimbikitsani kulambira Mulungu mwa kupita ku misonkhano yachikhristu ndi kuuza anthu ena zimene mumakhulupirira? Kodi mukuganiza kuti Yesu ali mwana akanatani atapemphedwa kuchita zinthu ngati zimenezi?

Anali Wophunzira Baibulo Wakhama ndi Mphunzitsi Wabwino

7. (a) Kodi Yesu mwina anayendera limodzi ndi ndani pokachita Pasika? (b) Kodi Yesu anali kuti pamene anthu ena anayamba ulendo wobwerera, ndipo n’chifukwa chiyani anali kumeneko?

7 Amuna onse m’mabanja a Aisiraeli ankalamulidwa kupita kukalambira Yehova kukachisi panthawi ya madyerero atatu a Ayuda. (Deuteronomo 16:16) Yesu ali ndi zaka 12, mwina banja lake lonse linapita ku Yerusalemu kukachita Pasika. Mosakayikira ang’ono ake a Yesu ndi alongo ake anapita nawonso. N’kutheka kuti anayendanso limodzi ndi Salome, amene mwina anali mchemwali wake wa Mariya, limodzi ndi mwamuna wake Zebedayo ndi ana awo Yakobe ndi Yohane, amene anadzakhala atumwi. * (Mateyo 4:20, 21; 13:54-56; 27:56; Maliko 15:40; Yohane 19:25) Pobwerera, Mariya ndi Yosefe mwina anaganiza kuti Yesu ali ndi achibale awo, choncho sanazindikire msanga kuti iye palibe. Patatha masiku atatu, Mariya ndi Yosefe anam’peza Yesu m’kachisi, “atakhala pakati pa aphunzitsi. Anali kuwamvetsera ndi kuwafunsa mafunso.”​—Luka 2:44-46.

8. Kodi Yesu anachita chiyani kukachisi, ndipo n’chifukwa chiyani anthu anadabwa naye?

8 Kodi Yesu anali “kuwafunsa mafunso” aphunzitsiwo motani? Mwina sanali kufunsa n’cholinga chongofuna kudziwa zinthu. Liwu lachigiriki limene analigwiritsa ntchito pano likhoza kutanthauza kufunsa kwa kukhoti, choncho kungaphatikizepo kufunsa mafunso ofufuza. Zoonadi, ngakhale ali mwana, Yesu anali wophunzira Baibulo amene anadabwitsa aphunzitsi achipembedzo ophunzira. Baibulo limati: “Onse amene anali kumumvetsera anadabwa kwambiri chifukwa cha kumvetsa zinthu kwake ndi mayankho ake.”​—Luka 2:47.

9. Kodi mungatsatire bwanji chitsanzo cha Yesu pankhani yophunzira Baibulo?

9 Kodi Yesu ali mwana anatha bwanji kudabwitsa aphunzitsi odziwa bwino ntchito yawo ndi zinthu za m’Baibulo zimene ankadziwa? Iye anali ndi mwayi wokhala ndi makolo oopa Mulungu amene anam’phunzitsa malangizo a Mulungu kuyambira ali khanda. (Eksodo 12:24-27; Deuteronomo 6:6-9; Mateyo 1:18-20) Mosakayikira Yosefe ankapita ndi Yesu ali mwana kusunagoge kukamvera anthu akuwerenga ndi kukambirana Malemba. Kodi nanunso muli ndi mwayi wokhala ndi makolo amene amaphunzira nanu Baibulo ndi kupita nanu kumisonkhano yachikhristu? Mofanana ndi Yesu, kodi mumaona kufunika kwa zimene makolo anu amachita? Kodi mumauza ena zimene mukuphunzira, ngati mmene Yesu anachitira?

Yesu Anali Wogonjera

10. (a) N’chifukwa chiyani makolo a Yesu anayenera kudziwa komwe iye anali? (b) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chabwino chotani kwa ana?

10 Kodi mukuganiza kuti Mariya ndi Yosefe anamva bwanji atam’peza Yesu m’kachisi patatha masiku atatu? Mosakayikira, mtima wawo unakhala m’malo. Koma Yesu anadabwa kuona kuti makolo ake sankadziwa komwe iye anali. Makolo akewo ankadziwa za kubadwa kwake kozizwitsa. Komanso, ngakhale kuti sankadziwa zonse, anayenera kudziwa zinthu zina zokhudza udindo wake wam’tsogolo monga Mpulumutsi ndi Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyo 1:21; Luka 1:32-35; 2:11) Choncho Yesu anawafunsa kuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Simunadziwe kodi kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?” Koma pomvera, Yesu ananyamuka limodzi ndi makolo ake n’kubwerera kwawo ku Nazarete. Baibulo limati: “Anapitiriza kuwamvera.” Komanso, “mayi wake anasunga mosamalitsa mawu onsewa mu mtima mwake.”​—Luka 2:48-51.

11. Pankhani ya kumvera, kodi mungaphunzire chiyani kwa Yesu?

11 Kodi mumaona kuti n’zophweka kutsanzira Yesu, n’kumamvera makolo anu nthawi zonse? Kapena kodi mumaona kuti sadziwa zinthu zamakono, ndiponso kuti inuyo mumadziwa zambiri kuposa iwowo? N’zoona kuti inuyo mukhoza kudziwa zambiri zokhudza zinthu zina, monga mafoni a m’manja, makompyuta, kapena zipangizo zina zamakono. Koma taganizirani za Yesu, amene anadabwitsa aphunzitsi odziwa bwino ntchito yawo ndi “kumvetsa zinthu kwake ndi mayankho ake.” Mwina mungavomereze kuti inuyo simudziwa zambiri poyerekezera ndi iyeyo. Komabe, Yesu ankagonjera makolo ake. Zimenezi sizikutanthauza kuti nthawi zonse ankagwirizana ndi maganizo awo. Koma “anapitiriza kuwamvera” mpaka kukula. Kodi mungaphunzire chiyani ku chitsanzo chake?​—Deuteronomo 5:16, 29.

Kumvera N’kovuta

12. Kodi kumvera kungapulumutse bwanji moyo wanu?

12 Kumvera nthawi zonse, n’kovuta. Zimene zinachitika zaka zingapo zapitazo zikusonyeza zimenezi. Atsikana awiri anali atatsala pang’ono kuwoloka msewu woyenda magalimoto 6 panthawi imodzi, m’malo modutsa pa mlatho wapamwamba wa anthu oyenda pansi. “Tiyeko John,” anatero atsikanawo polimbikitsa mnzawo amene anali kupita ku mlatho wapamwambawo. “Kodi sukupita nafe limodzi?” Pamene John ankakayikakayika, mtsikana mmodzi anamunyoza kuti, “Awanso mantha inu!” Ngakhale kuti John sankachita mantha, anati, “Ndikungofuna kumvera mayi anga basi.” Ali pa mlathopo patapita kanthawi, anamva matayala akukhula pansi ndipo atasuzumira anaona galimoto ikugunda atsikana aja. Mtsikana mmodzi anafa, ndipo winayo anavulala kwambiri moti anamudula mwendo. Amayi a atsikanawo, amene anauza ana awowo kuti azidutsa pa mlatho wapamwamba uja, anadzauza amayi a John kuti, “Zikanakhala bwino ana anga akanakhala omvera ngati mwana wanu.”​—Aefeso 6:1.

13. (a) N’chifukwa chiyani muyenera kumvera makolo anu? (b) Kodi ndi pa zochitika ziti pamene zingakhale zoyenera kuti mwana asamvere makolo ake?

13 N’chifukwa chiyani Mulungu amati: “Ananu, muzimvera makolo anu”? Mukamamvera makolo anu, mumamveranso Mulungu. Komanso, makolo anu akudziwa zambiri kuposa inuyo. Mwachitsanzo, zaka zisanu ngozi imene taifotokoza pamwambapa isanachitike, mwana wa anzawo a amayi a John anaphedwa akuwoloka msewu womwe uja. N’zoona kuti nthawi zina zimavuta kumvera makolo anu, koma Mulungu akuti muyenera kutero. Komabe makolo anu kapena anthu ena akakuuzani kuti muname, mube, kapena muchite chinthu chilichonse chimene Mulungu amaletsa, muyenera “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” N’chifukwa chake pambuyo ponena kuti “muzimvera makolo anu,” Baibulo limapitiriza kuti, “mwa Ambuye.” Zimenezi zikutanthauza kumvera makolo anu m’zinthu zonse zogwirizana ndi malamulo a Mulungu.​—Machitidwe 5:29.

14. N’chifukwa chiyani munthu wangwiro savutika kwambiri kumvera, koma n’chifukwa chiyani angafunikebe kuphunzira kumvera?

14 Mukanakhala wangwiro, kapena kuti “wosaipitsidwa, wolekanitsidwa kwa ochimwa,” ngati mmene Yesu analili, kodi mukuganiza kuti simukanavutika kumvera makolo anu nthawi zonse? (Aheberi 7:26) Mukanakhala wangwiro, simukanakhala ndi mtima wofuna kuchita zoipa, ngati mmene mulili panopa. (Genesis 8:21; Salmo 51:5) Koma ngakhale Yesu anafunika kuphunzira kumvera. Baibulo limati: “Ngakhale [Yesu] anali Mwana [wa Mulungu], anaphunzira kumvera mwa mavuto amene anakumana nawo.” (Aheberi 5:8) Kodi mavuto anathandiza bwanji Yesu kuphunzira kumvera, chinthu chomwe sanafunikire kuphunzira kumwamba?

15, 16. Kodi Yesu anaphunzira bwanji kumvera?

15 Yehova anatsogolera Yosefe ndi Mariya kuti ateteze Yesu ali mwana. (Mateyo 2:7-23) Koma patapita nthawi Mulungu anasiya kuteteza Yesu mozizwitsa. Yesu anazunzika kwambiri moti Baibulo limati “anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha . . . ndi kulira kwakukulu ndi misozi.” (Aheberi 5:7) Kodi zimenezi zinachitika liti?

16 Kwenikweni, zinachitika m’maola omaliza a moyo wa Yesu padziko lapansi, pamene Satana anachita zonse zotheka kuti amugonjetse. Zikuoneka kuti Yesu ankada nkhawa kwambiri kuti akafa ngati munthu wochita zoipa, adzaipitsa mbiri ya Atate ake. Chotero, pamene “anapitiriza kupemphera zolimba [m’munda wa Getsemane] thukuta lake linaoneka ngati madontho amagazi likugwera pansi.” Patapita maola angapo, Yesu anamva kupweteka kwambiri akufa pa mtengo wozunzikirapo mpaka analira ndi “kulira kwakukulu ndi misozi.” (Luka 22:42-44; Maliko 15:34) Choncho “anaphunzira kumvera mwa mavuto amene anakumana nawo” ndipo anakondweretsa mtima wa Atate ake. Panopa Yesu ali kumwamba ndipo akationa tikuvutika chifukwa chofuna kukhala omvera, nayenso zimam’pweteka.​—Miyambo 27:11; Aheberi 2:18; 4:15.

Kuphunzira Kumvera

17. Kodi muyenera kumva bwanji mukapatsidwa chilango?

17 Bambo ndi mayi anu akamakulangani, amasonyeza kuti akukufunirani zabwino, ndiponso kuti amakukondani. Baibulo limati: “Ndi mwana wanji amene atate wake sam’langa?” Kodi sizikanakhala zomvetsa chisoni makolo anu akanakhala kuti sakukondani mokwanira moti sayesetsa kukulangani? Mofanana ndi zimenezi, Yehova amakulangani chifukwa chokukondani. “Zoonadi, palibe kulanga kumene kumamveka kosangalatsa panthawiyo, komatu kumakhala kowawa. Koma pambuyo pake, kwa aja amene aphunzitsidwa nako, kumabala chipatso cha mtendere, ndicho chilungamo.”​—Aheberi 12:7-11.

18. (a) Kodi kulanga mwana ndi umboni wa chiyani? (b) Kodi mwaona kuti chilango choterocho chathandiza bwanji anthu?

18 Mfumu Solomo ya ku Isiraeli, yomwe Yesu anati ndi yanzeru kwambiri, inanenapo zoti makolo afunika kulanga ana awo mwachikondi. Mfumuyi inalemba kuti: “Wolekerera mwanake osam’menya amuda; koma wom’konda am’yambize kum’langa.” Solomo ananenanso kuti munthu akalangidwa mwachikondi, moyo wake ukhoza kupulumutsidwa ku imfa. (Miyambo 13:24; 23:13, 14; Mateyo 12:42) Mlongo wina akukumbukira kuti ali mwana, akavuta pa misonkhano bambo ake ankamuuza kuti akafika kunyumba, akam’langa. Panopa amasangalala akakumbukira zimene bambo ake anachita, chifukwa ankam’langa mwachikondi ndipo zimenezi zam’thandiza kukhala ndi moyo wabwino.

19. Kodi muyenera kumvera makolo anu makamaka chifukwa chiyani?

19 Ngati muli ndi makolo amene amakukondani mokwanira moti amayesetsa kukulangani mwachikondi, muyenera kuyamikira. Muziwamvera, ngati mmene Ambuye wathu Yesu Khristu ankamvera makolo ake, Yosefe ndi Mariya. Koma muziwamvera makamaka chifukwa choti Atate wanu wakumwamba, Yehova Mulungu, akukuuzani kuti muzitero. Mukatero mudzapindula, ndipo ‘zinthu zidzakuyenderani bwino, ndiponso mudzakhala moyo wautali padziko lapansi.’​—Aefeso 6:2, 3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 841, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ana angapindule bwanji akamamvera makolo awo?

• Kodi Yesu ali mwana anapereka bwanji chitsanzo chomvera makolo ake?

• Kodi Yesu anaphunzira bwanji kumvera?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 24]

Yesu ali ndi zaka 12 ankadziwa bwino Malemba

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi Yesu anaphunzira bwanji kumvera chifukwa cha mavuto?