Chitsanzo cha Kuona Mtima
Chitsanzo cha Kuona Mtima
NELMA ndi Mkhristu amene amagwira ntchito yokonza tsitsi ku Cruzeiro do Sul, m’dziko la Brazil. Posachedwapa kukhulupirika kwake kunayesedwa. Kudera lawo kutasefukira madzi, Nelma anapatsidwa zovala ndi mayi wina yemwe nthawi zambiri ankamukonza tsitsi. Akuonaona zovalazo, anapeza ndalama zokwana madola 1,000 m’matumba a thalauza.
Ndalama zimene Nelma anapezazi zinali zokwana malipiro ake a miyezi 7 ndipo zikanamuthandiza kwambiri. Nyumba yake ndi katundu wambiri wa bambo ake komanso wa abale ake zinali zitawonongeka ndi madzi. Ndalama zimenezi zikanamuthandiza kukonzera nyumba yake komanso kuthandizira abale ake. Komabe, chifukwa cha kuphunzira Baibulo, chikumbumtima chake sichinamulole kutenga ndalamazi.—Aheberi 13:18.
Tsiku lotsatira anapita mwamsanga kuntchito, n’kukaimbira foni mkazi amene anamupatsa zovala uja. Nelma anamuthokoza mkaziyo chifukwa cha zovala zimene anamupatsa komanso anamuuza kuti sangasunge ndalama zimene anapeza mu zovalazo. Mkaziyo anasangalala kwambiri kulandira ndalamazo, chifukwa zinali zoti alipirire antchito ake. Mkaziyo anati: “Kuona mtima n’kosowa kwambiri masiku ano.”
Anthu ambiri amaona kuti kukhala woona mtima kulibe phindu lililonse. Komabe, anthu amene amayesetsa kukondweretsa Mulungu woona, Yehova, amaona kuti kuona mtima n’kofunika kwambiri. (Aefeso 4:25, 28) Nelma anati: “Ndikanatenga ndalamazi sindikanatha kugona tulo usiku.”