Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungadziwe Bwanji Kupembedza Koona?

Kodi Mungadziwe Bwanji Kupembedza Koona?

Kodi Mungadziwe Bwanji Kupembedza Koona?

ZIPEMBEDZO zambiri zimati chiphunzitso chawo chimachokera kwa Mulungu. Choncho tingachite bwino kutsatira mawu a mtumwi wa Yesu, Yohane, amene analemba kuti: “Okondedwa, musamakhulupirire mawu alionse ouziridwa, koma yesani mawu ouziridwawo kuti muone ngati ali ochokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onyenga ambiri alowa m’dziko.” (1 Yohane 4:1) Kodi tingayese bwanji chinthu kuti tione ngati chimachokera kwa Mulungu kapena ayi?

Chinthu chilichonse chochokera kwa Mulungu chimaonetsa makhalidwe ake, makamaka chikondi. Mwachitsanzo, timatha kununkhiza, zimene zimaonetsa chikondi cha Mulungu chifukwa timasangalala ndi fungo labwino la zinthu ngati maluwa kapena buledi wongophulidwa kumene pamoto. Ndiponso timatha kuona zinthu ngati dzuwa likamalowa, gulugufe wokongola, kapena mwana akamamwetulira. Umenewu ndi umboni woti Mulungu amatikonda. Timathanso kumva nyimbo zokoma zikamaimbidwa, mbalame zikamalira, kapena mawu a munthu amene timam’konda. Izinso ndi umboni woti Mulungu amatikonda. Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, umunthu wathu umaonetsanso chikondi cha Mulungu. Timasangalala kusonyeza chikondi chifukwa tinapangidwa “m’chifanizo [cha Mulungu].” (Genesis 1:27) Choncho zimene Yesu ananena n’zoona. Iye anati: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Ngakhale kuti Yehova ali ndi makhalidwe ambiri, chikondi ndi khalidwe lake lalikulu.

Buku lochokera kwa Mulungu liyenera kuonetsanso chikondi chake. Zipembedzo za dzikoli zili ndi mabuku ambiri akale. Kodi mabukuwa amaonetsadi chikondi cha Mulungu?

Zoona zake n’zakuti, mabuku ambiri akale azipembedzo amangofotokoza pang’ono za mmene Mulungu amatikondera kapena mmene tingamukondere. Choncho, anthu mamiliyoni ambiri satha kupeza yankho akamafunsa funso loti, “N’chifukwa chiyani chilengedwe chimaonetsa chikondi cha Mulungu pamene kuvutika ndi kuipa kukupitirizabe? Pamabuku onse akale achipembedzo, ndi Baibulo lokha limene limafotokoza bwino chikondi cha Mulungu. Limatiphunzitsanso mmene tingasonyezere chikondicho.

Buku Lofotokoza Chikondi

Mawu a Mulungu, Baibulo, amati Yehova ndi “Mulungu wachikondi.” (2 Akorinto 13:11) Baibulo limafotokozanso kuti chifukwa cha chikondi chake, Yehova anapatsa anthu oyambirira moyo wopanda matenda kapena imfa. Koma anthu atapandukira ulamuliro wa Mulungu, anayamba kuvutika. (Deuteronomo 32:4, 5; Aroma 5:12) Choncho Yehova anachitapo kanthu pofuna kuthetsa zimenezi. Mawu a Mulungu amati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Malemba Opatulika amapitiriza kunena za chikondi cha Mulungu pofotokoza kuti Mulungu wakhazikitsa ufumu wangwiro, womwe wolamulira wake ndi Yesu, kuti ubweretsenso mtendere kwa anthu.​—Danieli 7:13, 14; 2 Petulo 3:13.

Baibulo limafotokoza mwachidule zimene anthu ayenera kuchita, kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu koposa komanso loyamba. Lachiwiri, lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha.’ Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa.” (Mateyo 22:37-40) Baibulo limanena kuti linauziridwa ndi Mulungu. Ndipo, popeza limaonetsa bwino lomwe makhalidwe ake, tingakhale ndi chikhulupiriro chonse kuti linachokera kwa “Mulungu wachikondi.”​—2 Timoteyo 3:16.

Choncho tikhoza kudziwa buku limene linachokeradi kwa Mulungu ngati bukulo limaonetsa chikondi. Olambira oona amadziwikanso ndi chikondi chifukwa amachisonyeza potsanzira Mulungu.

Kodi Anthu Okonda Mulungu Tingawadziwe Bwanji?

Anthu amene amakondadi Mulungu amaoneka kwambiri, makamaka panopa pamene tikukhala m’nthawi imene Baibulo limati ndi ‘masiku otsiriza.’ Anthu ambiri akukhala “odzikonda, okonda ndalama, . . . okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”​—2 Timoteyo 3:1-4.

Kodi anthu okonda Mulungu mungawadziwe bwanji? Baibulo limati: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.” (1 Yohane 5:3) Kukonda Mulungu kumalimbikitsa anthu kutsatira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu ali ndi malamulo onena za kugonana ndi kukwatirana. Kugonana kumaloledwa pakati pa anthu okwatirana okha, ndiponso ukwati suyenera kutha. (Mateyo 19:9; Aheberi 13:4) Mkazi wina wa ku Spain, amene ankaphunzira za umulungu, anapita ku msonkhano kumene Mboni za Yehova zinali kuphunzira malamulo a makhalidwe a m’Baibulo moikirapo mtima. Ndipo anati: “Ndinachokako nditalimbikitsidwa kwambiri osati chifukwa cha nkhani zokha za m’Malemba zimene zinali zothandiza, koma chifukwa cha mgwirizano womwe uli pakati pa anthuwo, makhalidwe awo abwino, ndi ulemu wawo.”

Kuwonjezera pa kukonda kwawo Mulungu, Akhristu amadziwikanso ndi mmene amasonyezera chikondi kwa anzawo. Ntchito yofunika kwambiri kwa iwo ndi youza ena za Ufumu wa Mulungu, umene ndi wokhawo womwe umapatsa anthu chiyembekezo chenicheni. (Mateyo 24:14) Palibe njira ina imene angathandizire nayo anansi awo koposa kuwaphunzitsa za Mulungu. (Yohane 17:3) Akhristu amasonyezanso chikondi m’njira zina. Amathandiza anthu ovutika. Mwachitsanzo, pamene chivomezi chinawononga zinthu kwambiri ku Italy, nyuzipepala ina ya m’dzikolo inasimba kuti Mboni za Yehova “zimathandiza kwambiri anthu amene akuvutika. Ndipo zimachita zimenezi popanda kuganizira chipembedzo chawo.”

Akhristu oona samangokonda Mulungu ndi anansi, amakondananso okhaokha. Yesu anati: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana wina ndi mnzake. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana wina ndi mnzake. Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.”​—Yohane 13:34, 35.

Kodi chikondi chimene Akhristu oona ali nacho kwa wina ndi mnzake chimaonekadi kuti n’chapadera? Ema, amene amagwira ntchito ya m’nyumba kwa munthu wina, anaona zimenezi. Ku La Paz, Bolivia, kumene amakhala, anthu amasankhana mtundu chifukwa mitundu ina ndi yosauka ndiponso ina ndi yolemera. Iye anati: “Ulendo woyamba umene ndinapita ku msonkhano wa Mboni za Yehova, ndinaona mwamuna wina amene anavala bwino atakhala pansi ndipo akulankhula ndi mayi wina wochokera ku mtundu wosauka. Sindinaonepo zimenezo. Pomwepo, ndinadziwa kuti anthuwa ndi anthu a Mulungu.” Mtsikana winanso wa ku Brazil, dzina lake Miriam, anati: “Sindinakhalepo wachimwemwe, ngakhale m’banja lathu. Nthawi yoyamba imene ndinaonapo anthu akukondana inali imene ndinapezeka pakati pa Mboni za Yehova.” Ku United States, mkonzi wa nkhani zofalitsidwa pa TV, polembera Mboni za Yehova, anati: “Anthu ambiri akanakhala kuti amachita zimene inu mumachita pa chipembedzo chanu, dziko lino silikanakhala mmene lililimu. Ineyo ndine mmodzi wa ofalitsa nkhani amene ndimadziwa kuti gulu lanu ndi lachikondi komanso limakhulupirira kwambiri Mlengi.”

Funafunani Kupembedza Koona

Olambira oona amadziwika chifukwa cha chikondi. Yesu anati munthu akapeza chipembedzo choona, amakhala ngati wapeza njira yolondola yoti aitsatire. Chipembedzo choona ndi njira yokhayo yotsogolera ku moyo wosatha. Yesu anati: “Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita ku chiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo; koma chipata cholowera kumoyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.” (Mateyo 7:13, 14) Ndi gulu limodzi lokha la Akhristu oona limene mogwirizana limayenda ndi Mulungu panjira ya chipembedzo choona. Choncho muyenera kusamala posankha chipembedzo. Ngati mutapeza njirayo ndi kuitsatira, mudzakhala ndi moyo wabwino kwambiri, chifukwa njira imeneyi ndiyo njira yachikondi.​—Aefeso 4:1-4.

Mungakhaledi osangalala mukamayenda m’njira ya kupembedza koona. Kuyenda m’njirayi kuli ngati mukuyenda ndi Mulungu. Mulungu angakuphunzitseni kukhala wanzeru ndi wachikondi kuti muzigwirizana bwino ndi anthu ena. Angakuphunzitseninso za cholinga cha moyo, ndiponso mungamvetsetse malonjezo a Mulungu n’kukhala ndi tsogolo labwino. Ngati mutafunafuna chipembedzo choona n’kuchipeza, simudzadandaula n’komwe kuti khama lanu lapita pachabe.

[Chithunzi patsamba 5]

Pamabuku onse akale kwambiri a chipembedzo, ndi Baibulo lokha limene limafotokoza za chikondi cha Mulungu

[Zithunzi patsamba 7]

Akhristu oona amadziwika chifukwa amakonda anzawo