Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwambo Wofunika Kukumbukira

Mwambo Wofunika Kukumbukira

Mwambo Wofunika Kukumbukira

Lolemba, pa April 2

Pa Nisani 14, m’chaka cha 33 C.E., Yesu anagawira atumwi ake chikho cha vinyo ndi mtanda wa mkate wosafufumitsa. Atatero anawalangiza kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira ine.”​—Luka 22:19.

Choncho, Mboni za Yehova padziko lonse zimasonkhana kamodzi pachaka kuti zikumbukire imfa ya Yesu. Amachita zimenezi potsatira malangizo amene Yesu anapereka tsiku limenelo. Chaka chino, tsiku la Nisani 14 lidzayamba Lolemba, pa April 2, dzuwa litalowa. Tikukuitanani kuti mudzakhale nafe pamsonkhanowu pokumbukira imfa ya Yesu. Tikukupemphani kuti mufunse nthawi ndi malo kwa Mboni za Yehova kwanuko.