Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusamala Posankha Chipembedzo?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusamala Posankha Chipembedzo?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusamala Posankha Chipembedzo?

AMBIRIFE tikafuna kugula zinthu, timapita kumene tingakapeze zinthu zambiri zoti tisankhepo. Pamsika pakakhala zipatso ndi ndiwo zamasamba zosiyanasiyana, timasankha zimene timakonda komanso zopatsa thanzi banja lathu. Ngati m’sitolo muli zovala zambiri za masokedwe ndi mitundu yosiyanasiyana zoti tingakwanitse kugula, timasankha zimene zingatikhale bwino. Nthawi zina timasankha zinthu osati chifukwa chakuti ndi zofunika kwenikweni, koma chifukwa chakuti ifeyo timazikonda. Koma tiyenera kudziwa kuti zosankha zina n’zofunika kwambiri chifukwa zimakhudza moyo wathu. Mwachitsanzo, kusankha zakudya zopatsa thanzi kapena anzathu amene angatithandize. Nangano, bwanji za kusankha chipembedzo? Kodi chipembedzo chathu chiyenera kukhala nkhani ya makonda basi? Kapena kodi ndi nkhani yaikulu imene ingakhudze kwambiri moyo wathu?

Pali zipembedzo zambiri zomwe tingasankhepo. Masiku ano, m’mayiko ambiri muli ufulu wachipembedzo, ndipo anthu ambiri akuona kuti akhoza kusiya chipembedzo cha makolo awo. Pakafukufuku wina amene anachitika ku United States, anapeza kuti anthu 80 pa anthu 100 alionse m’dzikoli “amakhulupirira kuti zipembedzo zambiri zimatsogolera ku chipulumutso.” Pakafukufuku yemweyo, “munthu mmodzi pa anthu asanu alionse amene anafunsidwa anati anasintha chipembedzo atakula.” Kafukufuku wina ku Brazil anasonyeza kuti pafupifupi munthu mmodzi pa anthu anayi alionse anasintha chipembedzo chawo.

Kale, anthu osiyana zipembedzo ankakangana kwambiri za ziphunzitso zawo. Koma masiku ano, anthu ambiri amangoti, ‘Mukhoza kusankha chipembedzo chilichonse chimene mukufuna.’ Koma kodi zimenezo n’zoona? Kodi chipembedzo chimene mungasankhe chingakuthandizeni pa moyo wanu?

Munthu wanzeru akamagula malonda amafunsa komwe malondawo achokera. Inunso mungachite bwino kufunsa kuti, ‘Kodi zipembedzo zosiyanasiyanazi zinayamba bwanji, ndipo zinayamba chifukwa chiyani?’ Baibulo limayankha mafunso amenewa.

Kodi Zipembedzo Zimayamba Bwanji?

Kale ku Isiraeli, Mfumu Yerobiamu anayambitsa chipembedzo chatsopano. Anachita zimenezi zaka pafupifupi 1,000 Yesu asanabwere pa dziko lapansi. Yerobiamu anali mfumu yoyamba ya ufumu wakumpoto wa Isiraeli. Anali ndi ntchito yovuta yolimbikitsa anthu kutsatira zolinga zake. “Mfumu inakhala upo, napanga ana a ng’ombe awiri agolidi, nati kwa iwo, kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisrayeli inu milungu yanu.” (1 Mafumu 12:28) N’zoonekeratu kuti mfumuyo inagwiritsira ntchito chipembedzo pofuna kuti anthuwo asamapitenso ku Yerusalemu kukalambira. Chipembedzo chimene Yerobiamu anayambitsa chinakhalapo kwa zaka zambiri ndipo chinapweteketsa anthu ochuluka pamene Mulungu analanga mtundu wa Isiraeli wopandukawo. Yerobiamu anayambitsa chipembedzochi kuti alimbitse boma lake. Zipembedzo zina zaboma zimene zilipobe mpaka lero nazonso zinayamba n’cholinga chopezerapo mwayi wolamulira.

Mtumwi Paulo anatchula cholinga china chimene anthu amakhala nacho poyambitsa chipembedzo chatsopano. Anati: “Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu yopondereza idzalowa pakati panu ndipo siidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. Ndipo pakati pa inu nomwe padzauka anthu amene adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti akanganule ophunzira aziwatsatira.” (Machitidwe 20:29, 30) Atsogoleri odzikuza nthawi zambiri amayambitsa zipembedzo kuti atchuke. Matchalitchi amene amanamizira kuti ndi achikhristu agawikanagawikana.

Kodi Zipembedzo Zimafuna Kusangalatsa Ndani?

Anthu ena angayambitse chipembedzo chatsopano pofuna kusangalatsa anthu anzawo. Mwachitsanzo, magazini ya Economist inafotokoza za matchalitchi akuluakulu a ku United States. Nkhaniyo inati matchalitchi amenewa akukula chifukwa “amatsatira mfundo imene mabizinesi onse amene amayenda bwino amatsatira: mfundo yosangalatsa makasitomala.” Ena “amagwiritsa ntchito mavidiyo, masewero, ndi nyimbo zamakono pokometsa mapemphero awo.” Atsogoleri ena achipembedzo m’matchalitchi amenewa akuti amaphunzitsa anthu awo kuti akhale “olemera, athanzi labwino ndi opanda nkhawa.” Magazini ya Economist inatinso, ngakhale kuti matchalitchi amenewa anthu amawanena kuti akuchita bizinesi yosangalatsa anthu kapena “yophunzitsa anthu kudzithandiza okha,” matchalitchiwa “akungochita zinthu zimene anthu akufuna.” Pomaliza, nkhaniyo inati: “Mgwirizano wa bizinesi ndi chipembedzo ukuyenda bwino kwambiri.”

Matchalitchi ena sachita kuonetsera poyera kuti ali ngati bizinesi. Ngakhale ndi choncho, zochita za matchalitchiwa amene “akungochita zinthu zimene anthu akufuna,” zimatikumbutsa za chenjezo la Paulo. Iye analemba kuti: “Idzafika nthawi imene anthu sadzafunanso chiphunzitso chopindulitsa, koma mogwirizana ndi zilakolako za iwo eni, adzadzipezera okha aphunzitsi kuti amve zowakomera m’khutu. Adzachotsa makutu awo ku choonadi, nadzatembenukira ku nkhani zonama.”​—2 Timoteyo 4:3, 4.

Zipembedzo zambiri zinayamba chifukwa chofuna mwayi wolamulira, kutchuka, ndi kukondedwa ndi anthu m’malo mofuna kusangalatsa Mulungu. Choncho n’zosadabwitsa kuti zipembedzo zimachitanso zinthu zoipa ngati nkhanza kwa ana, katangale, nkhondo, kapena uchigawenga. Nthawi zambiri, zipembedzo zimakhala zachinyengo. Kodi mungatani kuti musanyengedwe?

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Zipembedzo zambiri zinayamba chifukwa chofuna mwayi wolamulira, kutchuka, ndi kukondedwa ndi anthu m’malo mofuna kusangalatsa Mulungu