Ndakhala Ndikudikirira Ufumu Womwe “Suli Mbali ya Dziko Lino”
Mbiri ya Moyo Wanga
Ndakhala Ndikudikirira Ufumu Womwe “Suli Mbali ya Dziko Lino”
Yosimbidwa ndi Nikolai Gutsulyak
Kwa masiku 41, ndinali m’ndende pakati pa chipwirikiti cha akaidi ogalukira boma. Ndili m’tulo, mwadzidzidzi ndinangomva mizinga ikulira ndipo ndinagalamuka. Nthawi yomweyo ndinaona asilikali ndi akasinja akuthamangira m’ndendemo ndipo anali kulimbana ndi akaidi. Moyo wanga unali pa ngozi.
KODI ndinapezeka bwanji pachipwirikiti chimenechi? Dikirani ndifotokoze. Mu 1954, ndili ndi zaka 30, Mboni za Yehova zambiri m’boma la Soviet Union zinatsekeredwa m’ndende chifukwa chosalowerera m’nkhani zandale ndiponso chifukwa chouza ena za Ufumu wa Mulungu. Inenso ndinatsekeredwa pachifukwa chomwechi. M’ndendemo, tinalimo Mboni 80, amuna 46 ndi akazi 34. Tinali m’ndende yapafupi ndi mudzi wa Kengir kuchigawo chapakati cha Kazakhstan. Kumeneko tinkakhala ndi akaidi zikwizikwi ndipo tinkagwira ntchito yakalavula gaga.
Apa n’kuti Joseph Stalin, mtsogoleri wa dziko la Soviet Union, anali atamwalira mu 1953. Akaidi ambiri anayembekezera kuti chifukwa cha kusintha kwa boma ku Moscow, madandaulo awo a mmene ankakhalira m’ndendemo amveka. Koma madandaulo awo sanamveke ndipo anakhumudwa kwambiri moti mpaka anagalukira boma. Panthawi ya chipwirikiti imeneyi, Mbonife sitikanachitira mwina koma kufotokozera zigawengazo ndi asilikali olondera akaidi kuti sitilowerera nawo pa zinthu ngati zimenezi. Kuti tichite
zimenezi tinafunikira kukhulupirira Mulungu.Tsiku Limene Anagalukira
Akaidi anagalukira boma pa May 16. Patadutsa masiku awiri, akaidi opitirira 3,200 ananyanyala ntchito. Ananyanyala ntchitoyo chifukwa anafuna kuti boma likonze zinthu m’ndendemo ndiponso kuti akaidi amene anawamanga pa zifukwa zandale apatsidwe ufulu wina ndi wina. Zinthu zinachitika mwachanguchangu. Choyamba, zigawengazo zinathamangitsira kunja asilikali owalondera. Kenako zinaboolaboola mpanda. Zitatero, zinagwetsa mpanda umene unalekanitsa chigawo cha amuna ndi cha akazi kuti amuna ndi akaziwo azikhala pamodzi. Masiku otsatira, panachitika zoseketsa moti akaidi ena anakwatirana. Amene anawakwatitsa anali ansembe ndipo ansembewo analinso akaidi. M’zigawo zitatu za ndendeyo kumene kunayambira chipolowe, ambiri mwa akaidi 14,000 anagalukira nawo.
Zigawengazo zinakhazikitsa kabungwe kokambirana ndi asilikali a boma. Koma sipanapite nthawi, akaidi a m’kabungwe kameneka anakangana, ndipo akaidi ovuta kwambiri anatenga ulamuliro wa ndendeyo. Apa zinthu zinaipiraipira. Atsogoleri a zigawengazi anakhazikitsa madipatimenti osiyanasiyana. Anakhazikitsa dipatimenti ya zachitetezo, ya zankhondo ndiponso yofalitsa nkhani, ati kuti pakhale bata ndi mtendere. Atsogoleriwo anali kuulutsa mauthenga awo amtopola kudzera m’zokuzira mawu zimene anazimangirira ku mitengo yomwe anazika kuzungulira ndendeyo. Anachita zimenezi kuti alimbikitse mzimu wachipanduko. Zigawengazo sizinalole aliyense kuthawa, zinakhaulitsa aliyense wotsutsana nazo, ndipo zinaneneratu kuti zipha aliyense amene sizigwirizana naye. Panalinso mphekesera zoti akaidi ena anaphedwa kumene.
Popeza kuti zigawengazo zinkayembekezera kuti asilikali a boma aziukira, zinachita zonse zotheka pokonzekera kudziteteza. Atsogoleriwo analamula kuti aliyense akhale ndi chida pofuna kuti pakhale akaidi ambiri amene angadzateteze ndendeyo. Ndiye, akaidiwo anazula zitsulo za m’mawindo n’kupangira mipeni ndi zida zina. Anapezanso mfuti ndi mabomba.
Anatikakamiza Kuti Tigalukire Nawo
Panthawi imeneyo, zigawenga ziwiri zinandipeza, mmodzi ali ndi mpeni wakuthwa m’manja mwake. Ndipo anandikakamiza kuti nditenge mpeniwo. Anati: “Eko mpeniwu, udzizitetezera.” Ndinapempha Yehova chamumtima kuti ndidekhe. Kenako ndinamuyankha kuti: “Ndine Mkhristu wa Mboni za Yehova. Ine ndi Mboni zinzanga tili m’ndende muno chifukwa chakuti sitilimbana ndi anthu koma makamu a mizimu. Ndipo zida zathu polimbana ndi mizimuyo ndi chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo chathu cha Ufumu wa Mulungu.”—Aefeso 6:12.
Munthuyo anandidabwitsa chifukwa anagwedeza mutu wake kusonyeza kuti wamvetsa. Koma mnzakeyo anandimenya. Kenako onse awiriwo anapita. Zigawengazo zinafufuza Mboni za Yehova m’ndende monsemo ndi cholinga choti azikakamize kugalukira nawo. Ngakhale anatero, abale ndi alongo athu onse anakaniratu.
Pamsonkhano wina, zigawengazo zinakambirana za nkhani imeneyi kuti Mboni za Yehova zikukana kugalukira nawo. Pokambiranapo anati: “Anthu a zipembedzo zonse monga Apentekositi, Adiventisiti, Abaputisiti, ndi ena onse, akugalukira nawo. Koma Mboni za Yehova zokha zikukana. Titani nawo anthu amenewa?” Wina anati angachite bwino atatenga wa Mboni mmodzi n’kumuwotcha pa moto kuti atiopseze. Koma mkaidi wina, amene anzake ankamulemekeza kwambiri chifukwa anagwirapo ntchito ya usilikali, anaimirira ndi kunena kuti: “Imeneyo si nzeru yabwino. Tiyeni tiwatenge onse ndi kukawaika m’chipinda chimodzi chakumphepete kufupi ndi khomo la ndende ino. Mwanjira imeneyo, asilikali akatiukira ndi akasinja, ndiye kuti Mbonizi zidzakhala zoyambirira kuphedwa. Ndipo sitidzakhala ndi mlandu wozipha.” Ena onse anagwirizana naye.
Anatiika pa Malo Oti Tikanaphedwa
Sipanapite nthawi, akaidi anayenda uku ndi uku m’ndendemo akumakuwa kuti, “Amboni za Yehova tulukani!” Kenako anatikusira tonse 80 kuchipinda chimene anatikonzera kufupi ndi khomo. Anachotsa mabedi a m’chipindacho kuti malo apezeke ndipo anatilamula kulowa mmenemo. Imeneyi inakhala ndende yathu tsopano.
Kuti pakhaleko ulemu, alongo athu anasokerera nsalu pamodzi, ndipo tinatenga nsaluzo n’kugawa chipindacho pawiri kuti kwina kuzikhala amuna kwina akazi. (Panthawi ina, Mboni ina ya ku Russia inajambula chipinda chimenechi, chomwe chili m’munsimu.) Mmenemo tinali kukhala mothithikana, ndipo nthawi zambiri tinkapemphera, kumupempha Yehova ndi mtima wonse kuti atipatse nzeru ndi “mphamvu yoposa yachibadwa.”—2 Akorinto 4:7.
Panthawi yonseyi, tinali pa malo oopsa kwambiri. Mbali inayi kunali zigawenga ndipo inayo kunali asilikali a boma, ife tinali pakati. Sitinadziwe kuti magulu amenewa atani tsopano. M’bale wina wokalamba komanso wokhulupirika anati: “Musakayike, Yehova satitaya.”
Alongo athu okondedwa, aakulu ndi aang’ono omwe, anapirira kwambiri. Mlongo wina anali ndi zaka pafupifupi 80 ndipo anafunikira thandizo lapadera. Ena anali odwala ndipo anafunikira chithandizo cha mankhwala. Panthawi yonse imene tinali m’chipindachi, zigawengazo sizinalole kuti tizitseka chitseko n’cholinga choti zizitiona. Usiku kunkabwera akaidi atanyamula mfuti. Nthawi zina tinkawamva akunena kuti “Ufumu wa Mulungu uli m’tulo.” Masana, akatilola kupita ku chipinda chodyera, tinkakhala pamodzi ndi kupemphera kwa Yehova kuti atiteteze kwa anthu achiwawa.
Tikakhalanso m’chipinda chathu chogona, tinkayesetsa kulimbikitsana mwauzimu. Mwachitsanzo, nthawi zambiri m’bale anali kusimba nkhani ya m’Baibulo mongokweza mawu pang’ono kuti timve. Kenako ankagwirizanitsa nkhaniyo ndi zimene tinali kukumana nazo. M’bale wina wokalamba ankakonda kulankhula za asilikali a Gideoni. Iye anatikumbutsa kuti: “Amuna 300 onyamula zida zoimbira anamenyana m’dzina la Yehova ndi asilikali okwanira 135,000. Onse 300 anabwerako ali bwinobwino.” (Oweruza 7:16, 22; 8:10) Nkhani imeneyi ndi nkhani zinanso za m’Baibulo, zinkatilimbikitsa kwambiri. Nthawi imeneyo n’kuti nditakhala Mboni nthawi yochepa, koma nditaona chikhulupiriro cholimba cha abale ndi alongo amene anakhala Mboni nthawi yaitali, ndinalimbikitsidwa kwambiri. Ndinaonadi kuti Yehova ali nafe.
Nkhondo Iyambika
Patadutsa milungu ingapo, nkhawa inakula m’ndendemo posadziwa kuti chichitike n’chiyani. Zokambirana pakati pa zigawenga ndi boma zinafika povuta kwambiri. Atsogoleri a zigawengazo anaumirira kuti boma ku Moscow litumize nthumwi idzakambirane nawo. Boma nalonso linaumirira kuti zigawengazo zitule pansi zida zawo ndi kubwerera ku ntchito. Palibe anafuna kugonja. Apa n’kuti asilikali a boma atazungulira ndendeyo, kudikirira kuti akangolamulidwa, alowe m’kati kuti akalimbane ndi zigawengazo. Nazonso zigawenga zinali zokonzeka kumenyana nawo, ndipo zinali zitatchingatchinga malowo n’kusonkhanitsa zida zambirimbiri. Aliyense anali kuyembekezera kuti nthawi ina iliyonse nkhondo iyamba.
Pa June 26 tili m’tulo, tinadzidzimuka titangomva mizinga ikulira. Akasinja anagwetsa mpanda ndi kulowa m’ndendemo. Pambuyo pawo panali asilikali amene anali kuwombera mfuti. Ndipo akaidi aamuna ndi aakazi omwe anathamangira komwe kunali kuchokera akasinjawo, uku akukuwa kuti “Tiyeni nawo!” Anali kuponya miyala, mabomba ochita kupanga okha, ndi chilichonse chomwe anali nacho. Panali nkhondo yadzaoneni ndipo Mbonife tinali pakatikati pa chipwirikiti chimenechi. Tinadzifunsa kuti, kodi Yehova ayankha bwanji mapemphero athu ndi kutithandiza?
Mwadzidzidzi, tinangoona asilikali alowa ku chipinda chathu n’kukuwa kuti: “Tulukani, anthu oyera inu! Fulumirani! Pitani panja pa mpanda!” Mkulu wa asilikaliwo anawalamula kuti asatiwombere koma akhale nafe n’kutiteteza. Nkhondo ili m’kati, ife tinakhala pa udzu kunja kwa mpanda. Maola anayi amene tinakhala pamenepo, tinamva mabomba akuphulika m’katimo, mfuti zikulira, anthu akukuwa ndi kubuula. Kenako, panangoti zii. Kutacha m’mawa, tinaona asilikali akunyamula mitembo kuchokera m’ndendemo. Tinamva kuti anthu mazanamazana avulala ndipo ena aphedwa.
Tsiku lomwelo, msilikali wina amene ndinkamudziwa anatipeza ndipo mwamatama anandifunsa kuti: “Nikolai, wakupulumutsani ndani? Ifeyo kapena Yehova?” Tinamuthokoza ndi mtima wonse potipulumutsa, ndiponso tinamuuza kuti, “Tikukhulupirira kuti Yehova, Mulungu wathu wamphamvuyonse, wakutsogolerani kuti mutipulumutse ngati mmene anachitira kale m’nthawi za m’Baibulo.”—Ezara 1:1, 2.
Msilikali ameneyo anafotokozanso mmene asilikaliwo anatidziwira ndi kumene tinali. Anati pokambirana ndi zigawenga, asilikaliwo anaimba mlandu zigawengazo poziganizira kuti zapha akaidi amene sanali kumbali yawo. Pokana mlanduwo, zigawengazo zinati Mboni za Yehova sizinagalukire nawo ndipo sanaziphe. Chilango chimene anangozipatsa Mbonizo chinali chakuti anaziika ku chipinda chimodzi. Umu ndi mmene asilikaliwo anadziwira kumene tinali.
Tinakhulupirika ku Ufumu wa Mulungu
Mlembi wodziwika kwambiri wa ku Russia, dzina lake Aleksandr Solzhenitsyn, analemba zimene zinachitikazi akaidiwo atagalukira boma. Analemba zimenezi m’buku lake lakuti The Gulag Archipelago. Pofotokoza chifukwa chimene akaidiwo anagalukira, anagwira mawu awo akuti: “Chimene ife tikufuna ndi ufulu, . . . ndani atipatse ufuluwo?” Ifenso Mboni za Yehova m’ndendemo tinkafuna ufulu. Ndipo ufulu umene tinkafuna sikumasulidwa m’ndende kokha, koma ufulu woperekedwa ndi Ufumu wa Mulungu. Tili m’ndende, tinkadziwa kuti tinafunikira mphamvu yochokera kwa Mulungu kuti tipirire n’kukhala okhulupirika ku Ufumu wake. Ndipo Yehova anatipatsa zonse zofunikira. Anatithandiza kupambana popanda kugwiritsa ntchito mipeni kapena mabomba.—2 Akorinto 10:3.
Yesu Khristu anauza Pilato kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino. Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo.” (Yohane 18:36) Ndiye ife pokhala otsatira Khristu, sitinatenge nawo mbali pamikangano yandale. Tinasangalala kuti panthawi ya chipwirikiti komanso chitatha, anthu ena anaona kukhulupirika kwathu ku Ufumu wa Mulungu. Pothirirapo ndemanga za khalidwe lathu panthawi imeneyo, Solzhenitsyn analemba kuti: “Mboni za Yehova zinaona kuti ndi ufulu wawo kutsatira malamulo awo ndendende ndipo sizinathandize nawo kutchinga kapena kulondera malowo.”
Padutsa zaka zoposa 50 tsopano kuchokera pamene chipwirikiticho chinachitika. Koma ndimati ndikakumbukira, ndimathokoza kwambiri chifukwa ndinaphunzirapo zinthu zambiri zosaiwalika, monga kudalira Yehova ndi kukhulupirira ndi mtima wonse kuti iye ali ndi mphamvu yotithandiza. Kunena zoona, mofanana ndi Mboni zinzanga zapamtima za kumayiko omwe kale anali Soviet Union, ndaonadi kuti Yehova amapereka ufulu, chitetezo, ndi chipulumutso kwa anthu onse amene amadikirira Ufumu womwe “suli mbali ya dziko lino.”
[Zithunzi pamasamba 8, 9]
Ndende ya ku Kazakhstan komwe tinali
[Chithunzi patsamba 10]
Chithunzi cha chipinda cha Mboni, chigawo cha akazi
[Chithunzi patsamba 11]
Ndili ndi abale anga, titamasulidwa