Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Opani Yehova Kuti Mukhale ndi Moyo Wosangalala

Opani Yehova Kuti Mukhale ndi Moyo Wosangalala

Opani Yehova Kuti Mukhale ndi Moyo Wosangalala

“Opani Yehova, inu oyera mtima ake; chifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.”​—SALMO 34:9.

1, 2. (a) Kodi Matchalitchi Achikhristu amaphunzitsa zotani pankhani ya kuopa Mulungu? (b) Kodi tsopano tikambirana mafunso ati?

ABUSA a Matchalitchi Achikhristu amene amaphunzitsa kuti anthu ayenera kuopa Mulungu, nthawi zambiri amatero pogwiritsira ntchito chiphunzitso choti Mulungu amalanga ochimwa kumoto wamuyaya. Chiphunzitso chimenechi n’chosemphana ndi zimene Baibulo limanena zokhudza Yehova, zoti ndi Mulungu wachikondi ndi chilungamo. (Genesis 3:19; Deuteronomo 32:4; Aroma 6:23; 1 Yohane 4:8) Abusa ena a Matchalitchi Achikhristu satchula n’komwe za kuopa Mulungu. M’malo mwake, amaphunzitsa kuti Mulungu ndi wolekerera ndipo amasangalala ndi aliyense, kaya amachita zotani. Koma Baibulo siliphunzitsanso zimenezo.​—Agalatiya 5:19-21.

2 M’malo mwake, Baibulo limatilimbikitsa kuopa Mulungu. (Chivumbulutso 14:7) Mfundo imeneyo imabutsa mafunso. Mafunso ake ndi oti: N’chifukwa chiyani Mulungu wachikondi amafuna kuti tizimuopa? Kodi Mulungu amafuna tizimuopa motani? Kodi kuopa Mulungu kungatithandize bwanji? Tipeza mayankho a mafunso amenewa pamene tikupitiriza kukambirana Salmo 34.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Mulungu?

3. (a) Kodi lamulo loti muziopa Mulungu mumalimva bwanji? (b) N’chifukwa chiyani anthu oopa Yehova ali osangalala?

3 Yehova ayenera kuopedwa chifukwa ndi Mlengi ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. (1 Petulo 2:17) Komabe, kuopa kumeneko sikutanthauza kuti tizichita naye mantha kwambiri ngati kuti ndi mulungu wankhanza. Koma kumatanthauza kulemekeza kwambiri Yehova chifukwa cha udindo wake komanso mmene alili. Kumatanthauzanso kusafuna kumukhumudwitsa. Kuopa Mulungu n’kwabwino ndiponso kumatipindulitsa. Sikutipatsa nkhawa kapena kutiopseza. Yehova, “Mulungu wa chisangalalo,” amafuna kuti anthu amene anawalenga azisangalala ndi moyo. (1 Timoteyo 1:11) Koma kuti tikhale ndi moyo wosangalala, tiyenera kuchita zimene Mulungu amafuna. Ambiri amafunika kusintha moyo wawo kuti achite zimenezi. Onse amene amasintha moyo wawo amaona kuti mawu amene wamasalmo Davide ananena ndi oona. Mawuwa amati: “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino; wodala munthuyo wakukhulupirira Iye. Opani Yehova, inu oyera mtima ake; chifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.” (Salmo 34:8, 9) Anthu onse amene amaopa Yehova ali ndi unansi wabwino ndi iye, ndipo sasowa kanthu kalikonse kabwino.

4. Kodi Davide ndi Yesu ananena mawu olimbikitsa otani?

4 Taonani kuti Davide analemekeza anyamata ake powatcha “oyera mtima,” malinga ndi mmene mawuwa ankagwirira ntchito munthawi yake. Iwo anali mu mtundu woyera wa Mulungu. Ndiponso anali kuika moyo wawo pangozi kuti atsatire Davide. Ngakhale Davide anali kuthawa Mfumu Sauli, anali ndi chikhulupiriro kuti Yehova apitirizabe kuwapatsa zosowa za pamoyo wawo. Davide analemba kuti: “Misona ya mkango isowa nimva njala: koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.” (Salmo 34:10) Yesu anauzanso otsatira ake mawu olimbikitsa ngati amenewa.​—Mateyo 6:33.

5. (a) Kodi otsatira a Yesu ambiri anali otani? (b) Kodi Yesu anapereka malangizo otani pankhani ya kuopa?

5 Ambiri mwa anthu amene anamva Yesu akulankhula anali Ayuda osauka. Choncho Yesu “anawamvera chisoni, chifukwa anali okalikakalika ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mateyo 9:36) Kodi anthu osauka oterowo akanalimba mtima kutsatira Yesu? Kuti athe kuchita zimenezi, akanafunika kuopa Yehova, osati anthu. Yesu anati: “Musamaope amene amapha thupi lokha, amene sakhozanso kuchita zoposa pamenepa. Koma ndikuuzani woti muzimuopa: Muziopa iye amene amati akapha, amakhalanso ndi mphamvu zoponya munthu m’Gehena. Ndithu ndikukuuzani, muziopa Ameneyu. Mpheta zisanu amazigulitsa makobili awiri ochepa mphamvu, si choncho nanga? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa izo imaiwalika kwa Mulungu. Ndipo ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu analiwerenga. Musachite mantha; ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.”​—Luka 12:4-7.

6. (a) Kodi ndi mawu a Yesu ati amene alimbikitsa Akhristu? (b) N’chifukwa chiyani Yesu ali chitsanzo chabwino kwambiri cha kuopa Mulungu?

6 Adani akamafuna kukakamiza anthu oopa Yehova kuti asiye kutumikira Mulungu, atumiki akewo angachite bwino kukumbukira malangizo a Yesu, oti: “Aliyense wovomereza pamaso pa anthu kuti ali wogwirizana ndi ine, Mwana wa munthunso adzavomereza pamaso pa angelo a Mulungu kuti ali wogwirizana ndi iye. Koma aliyense wondikana ine pamaso pa anthu, adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.” (Luka 12:8, 9) Mawu amenewa alimbikitsa Akhristu, makamaka m’mayiko amene kulambira koona kuli koletsedwa. Akhristu amenewa amapitirizabe kulemekeza Yehova pamisonkhano ndi muulaliki koma mwakabisira. (Machitidwe 5:29) Yesu anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri cha “kuopa . . . Mulungu.” (Aheberi 5:7) Ponena za Yesu, Mawu aulosi ananeneratu kuti: “Mzimu wa Yehova udzam’balira iye mzimu . . . wakuopa Yehova; ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova.” (Yesaya 11:2, 3) Choncho Yesu ndi amene angatiphunzitse bwino kwambiri ubwino woopa Mulungu.

7. (a) Kodi tingati Akhristu amamvera bwanji zimene Davide ananena? (b) Kodi makolo angatsatire bwanji chitsanzo chabwino cha Davide?

7 Onse amene amatsatira chitsanzo cha Yesu ndi kumvera zimene anaphunzitsa, tingati akumvera zimene Davide ananena, zoti: “Idzani ananu ndimvereni ine: ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.” (Salmo 34:11) M’pomveka kuti Davide anawatcha anyamata ake kuti “ananu” chifukwa ankamuona ngati mtsogoleri wawo. Davideyo anathandiza otsatira ake mwauzimu kuti akhale ogwirizana ndiponso kuti Mulungu aziwayanja. Chimenechi n’chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo achikhristu. Yehova wawapatsa udindo woti ‘alere ana awo m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.’ (Aefeso 6:4) Makolo akamakambirana ndi ana awo zinthu zauzimu tsiku lililonse ndi kuphunzira nawo Baibulo nthawi zonse, amawathandiza kuopa Yehova ndi kukhala ndi moyo wosangalala.​—Deuteronomo 6:6, 7.

Momwe Tingasonyezere Kuopa Mulungu

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani tingafune kukhala ndi moyo woopa Mulungu? (b) Kodi kuletsa lilime lathu kuti lisatchule zoipa kumatanthauza kuchita chiyani?

8 Monga taonera kale, kuopa Yehova sikutilanda chimwemwe. Davide anafunsa kuti: “Munthu wokhumba moyo ndani, wokonda masiku, kuti aone zabwino?” (Salmo 34:12) N’zachionekere kuti kuopa Yehova n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi moyo wautali ndi wosangalala. Komabe, n’zosavuta kunena kuti, “Ndimaopa Mulungu.” Koma n’zovuta kuti khalidwe lathu lisonyeze zimenezi. N’chifukwa chake Davide anafotokozanso momwe tingasonyezere kuopa Mulungu.

9 “Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo.” (Salmo 34:13) Mtumwi Petulo anauziridwa kugwira mawu mbali imeneyi ya Salmo 34 atamaliza kulangiza Akhristu kuti azikondana. (1 Petulo 3:8-12) Tikaletsa lilime lathu kuti lisatchule zoipa, tidzapewa kufalitsa miseche imene ingavulaze anthu ena. M’malo mwake, tikamalankhula ndi anthu ena, nthawi zonse tidzayesetsa kulankhula zinthu zolimbikitsa. Komanso, tidzayesetsa kukhala olimba mtima ndi kunena zoona.​—Aefeso 4:25, 29, 31; Yakobe 5:16.

10. (a) Kodi kufutuka pa zoipa kumatanthauza chiyani? (b) Kodi kuchita zabwino kumaphatikizapo chiyani?

10 “Futuka pazoipa, nuchite zabwino, funa mtendere ndi kuulondola.” (Salmo 34:14) Timapewa zinthu zimene Mulungu amaletsa, monga chiwerewere, kuona zinthu zolaula, kuba, kukhulupirira mizimu, chiwawa, kuledzera, ndi kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo. Timapewanso zosangalatsa zimene zimakhala ndi zonyansa zimenezi. (Aefeso 5:10-12) M’malo mwake, timagwiritsira ntchito nthawi yathu kuchita zinthu zabwino. Chinthu chabwino kwambiri chomwe tingachite ndicho kulalikira nthawi zonse za Ufumu ndi kupanga ophunzira, kuthandiza anthu kuti adzapulumuke. (Mateyo 24:14; 28:19, 20) Kuchita zabwino kumaphatikizaponso kukonzekera misonkhano yachikhristu ndi kupezekapo, kupereka ndalama zothandizira pa ntchito ya padziko lonse, kusamalira Nyumba yathu ya Ufumu, ndi kuthandiza Akhristu ovutika.

11. (a) Kodi Davide anatsatira bwanji mtendere umene ankaulimbikitsa? (b) Kodi mungatani kuti ‘mulondole mtendere’ mumpingo?

11 Davide anapereka chitsanzo pankhani yolondola mtendere. Kawiri konse, anapeza mpata wophera Sauli. Koma panthawi zonsezi, anapewa chiwawa ndipo kenaka analankhula mwaulemu ndi mfumuyo n’cholinga chokhazikitsa mtendere. (1 Samueli 24:8-11; 26:17-20) Kodi masiku ano tingatani ngati mumpingo mwachitika zinthu zimene zingasokoneze mtendere? Tiyenera ‘kufunafuna mtendere ndi kuulondola.’ Choncho, tikaona kuti zinthu sizili bwino pakati pa ifeyo ndi Mkhristu mnzathu, timamvera malangizo a Yesu akuti: “Ukayanjane ndi m’bale wako choyamba.” Tikatero, tingathe kupitiriza kuchita mbali zina za kulambira koona.​—Mateyo 5:23, 24; Aefeso 4:26.

Kuopa Mulungu Kuli ndi Madalitso Ochuluka

12, 13. (a) Kodi anthu oopa Mulungu akupindula bwanji masiku ano? (b) Kodi olambira okhulupirika adzakhala ndi mwayi waukulu wotani posachedwapa?

12 “Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwawo.” (Salmo 34:15) Zimene Mulungu anachitira Davide zikusonyeza kuti mawu amenewa n’ngoona. Masiku ano, tili ndi chimwemwe chachikulu ndi mtendere wamumtima chifukwa tikudziwa kuti Yehova akutiteteza. Tili ndi chikhulupiriro kuti nthawi zonse adzatipatsa zosowa zathu, ngakhale pamene tikuvutika kwambiri. Tikudziwa kuti monga zinanenedweratu, posachedwapa olambira oona onse adzaukiridwa ndi Gogi wa Magogi ndiponso adzaona “tsiku la Yehova lalikulu loopsa.” (Yoweli 2:11, 31; Ezekieli 38:14-18, 21-23) Kaya tidzakumana ndi zotani panthawiyo, mawu a Davide adzakwaniritsidwa, akuti: “Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva, nawalanditsa ku masautso awo onse.”​Salmo 34:17.

13 Zidzakhala zosangalatsa kwambiri panthawi imeneyo kuona Yehova akukweza dzina lake lalikulu. Mitima yathu idzalemekeza kwambiri Yehova kuposa kale lonse, ndipo otsutsa onse adzawonongedwa mwamanyazi. “Nkhope ya Yehova itsutsana nawo akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chawo padziko lapansi.” (Salmo 34:16) Udzakhaladi mwayi waukulu kwambiri kupulumutsidwa n’kulowa m’dziko latsopano ndiponso lolungama la Mulungu.

Malonjezo Amene Amatithandiza Kupirira

14. N’chiyani chingatithandize kupirira ngakhale tikukumana ndi masautso?

14 Kuti tipitirize kumvera Yehova m’dziko la anthu oipali timafunika kupirira. Kuopa Mulungu kumatithandiza kwambiri kuti tikhale omvera. Chifukwa choti tikukhala mu nthawi yovuta, atumiki ena a Yehova amakumana ndi mavuto aakulu ndipo mtima wawo umasweka ndiponso amakhwethemuka. Komabe, akhoza kukhala ndi chikhulupiriro chonse kuti kudalira Yehova kungawathandize kupirira. Mawu a Davide ndi olimbikitsadi, akuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi,” kapena kuti okhwethemuka. (Salmo 34:18) Davide anapitiriza kunena mawu olimbikitsa, oti: “Masautso a wolungama mtima achuluka: koma Yehova am’landitsa mwa onsewa.” (Salmo 34:19) Kaya tikumane ndi masautso ochuluka bwanji, Yehova ali ndi mphamvu zokwanira kutipulumutsa.

15, 16. (a) Kodi Davide anamva za chiyani atangomaliza kulemba Salmo 34? (b) N’chiyani chingatithandize kupirira mayesero?

15 Davide atangomaliza kulemba Salmo 34, anamva za zomwe zinagwera anthu a ku Nobi, amene Sauli anawapha limodzi ndi ansembe ambiri. Davide ayenera kuti anamva chisoni kwambiri podziwa kuti Sauli anachita izi chifukwa chopsa mtima ndi zimene zinachitika Davide atapita ku Nobiko. (1 Samueli 22:13, 18-21) Mosakayikira, Davide anapempha Yehova kuti am’thandize, ndipo ayenera kuti anatonthozedwa podziwa kuti kudzakhala kuuka “kwa olungama.”​—Machitidwe 24:15.

16 Masiku ano, chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chimatilimbikitsanso. Tikudziwa kuti palibe chilichonse chomwe adani athu angachite chomwe chingativulaze mpaka kalekale. (Mateyo 10:28) Davide ananena mawu osonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chofanana ndi chimenechi, akuti: “Iye asunga mafupa ake onse [a wolungama]: silinathyoka limodzi lonse.” (Salmo 34:20) Vesi limeneli linakwaniritsidwa kwa Yesu. Ngakhale kuti Yesu anaphedwa mwankhanza, palibe fupa lake lililonse lomwe ‘linathyoledwa.’ (Yohane 19:36) Tikaganizira tanthauzo lina la Salmo 34:20, lembali limatitsimikizira kuti Akhristu odzozedwa ndi anzawo a “nkhosa zina” sangavulazidwe mpaka kalekale, kaya akumane ndi mayesero otani. Tinganene mophiphiritsira kuti mafupa awo sadzathyoledwa.​—Yohane 10:16.

17. Kodi adani osalapa a anthu a Yehova adzakumana ndi zotani?

17 Koma oipa zinthu sizidzawayendera bwino. Posachedwapa, adzakolola zomwe afesa. “Mphulupulu idzamupha woipa: ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.” (Salmo 34:21) Onse amene akupitiriza kutsutsa anthu a Mulungu adzawonongedwa. Pavumbulutso la Yesu Khristu, “adzawaweruza kuti alandire chilango cha chiwonongeko chamuyaya.”​—2 Atesalonika 1:9.

18. Kodi a “khamu lalikulu” anawomboledwa kale m’lingaliro lotani, ndipo m’tsogolo muno chidzawachitikire n’chiyani?

18 Salmo la Davide limeneli linatha ndi mawu olimbikitsa awa: “Yehova awombola moyo wa anyamata ake, ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.” (Salmo 34:22) Chakumapeto kwa ufumu wake wa zaka 40, Mfumu Davide anati: “[Mulungu]. . . anapulumutsa moyo wanga m’nsautso monse.” (1 Mafumu 1:29) Mofanana ndi Davide, posachedwapa anthu oopa Yehova azidzati akakumbukira zakale, azisangalala chifukwa chowomboledwa ku mlandu uliwonse wobwera ndi uchimo komanso chifukwa chopulumutsidwa ku mayesero awo. Panopa, Akhristu odzozedwa ambiri alandira kale mphoto yawo yakumwamba. A “khamu lalikulu” ochokera m’mitundu yonse akugwirizana ndi otsalira a abale a Yesu potumikira Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, Yehova amawaona kuti ndi oyera. Izi zili choncho chifukwa amakhulupirira mphamvu yowombola ya magazi omwe Yesu anakhetsa. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, adzapindula kwambiri ndi nsembe ya dipo. Akadzatero adzatha kufika pokhala angwiro.​—Chivumbulutso 7:9, 14, 17; 21:3-5.

19. Kodi a “khamu lalikulu” ndi ofunitsitsa kuchita chiyani?

19 Kodi anthu olambira Mulungu a “khamu lalikulu” adzalandira madalitso onsewa chifukwa chiyani? N’chifukwa choti akufunitsitsa kupitirizabe kuopa Yehova, kumulemekeza ndi kumumvera pom’tumikira. Zoonadi, kuopa Yehova kumatithandiza kukhala ndi moyo wosangalala panopa, ndiponso kumatithandiza ‘kugwira zolimba moyo weniweniwo,’ womwe ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.​—1 Timoteyo 6:12, 18, 19; Chivumbulutso 15:3, 4.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuopa Mulungu, ndipo kodi kuopa Mulungu kumatanthauza chiyani?

• Kodi munthu woopa Mulungu amakhala ndi khalidwe lotani?

• Kodi kuopa Mulungu kuli ndi madalitso otani?

• Kodi ndi malonjezo ati amene amatithandiza kupirira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Kulambira koona kukaletsedwa, anthu oopa Yehova amachita zinthu mwanzeru

[Chithunzi patsamba 28]

Chinthu chabwino kwambiri chomwe tingachitire anzathu ndicho kuwauza uthenga wabwino wa Ufumu