Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Osangalala Kudikira Yehova

Osangalala Kudikira Yehova

Osangalala Kudikira Yehova

KODI munayamba mwadyapo chipatso chosapsa? N’kutheka kuti simunachimve kukoma. Zipatso zimatenga nthawi kuti zipse, ndipotu ndi bwino kudikira kuti mudzadye zitapsa bwinobwino. Pali zinthu zinanso zimene zimakhala bwino kuzidikira. Baibulo limati: “N’kokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.” (Maliro 3:26; Tito 2:13) Kodi Akhristu azidikira Yehova m’njira zotani? Kodi tingapindule bwanji pamene tikudikira Yehova?

Kodi Kudikira Mulungu N’kutani Makamaka?

Akhristufe ‘tikudikira ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ Tikudikira kudzapumula ku mavuto athu iye akadzabweretsa “chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:7, 12) Yehovanso payekha akudikira kudzachotsa zoipa zonse, koma akudziletsa kuti adzapulumutse Akhristu m’njira yoti dzina lake lidzalemekezedwe. Baibulo limati: “Mulungu, ngakhale kuti akufuna kusonyeza mkwiyo wake ndi kuonetsa mphamvu zake, koma analekerera moleza mtima kwambiri ziwiya za mkwiyo zoyenera kuwonongedwa, kuti asonyeze ukulu wa ulemerero wake kwa ziwiya zachifundo.” (Aroma 9:22, 23) Monga mmene anachitira m’nthawi ya Nowa, Yehova akudziwa nthawi yabwino yopulumutsa anthu ake masiku ano. (1 Petulo 3:20) Motero, kudikira Mulungu kumatanthauzanso kudikira nthawi yake yochitira zinthu.

Podikira tsiku la Yehova, nthawi zina tingathe kukhumudwa kwambiri poona mmene makhalidwe a m’dzikoli akuipiraipira. Tikamamva choncho, ndi bwino kuganizira mawu a Mika, mneneri wa Mulungu, akuti: “Watha wachifundo m’dziko, palibe woongoka mwa anthu.” Mneneriyu anapitiriza kuti: “Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa.” (Mika 7:2, 7) Kodi pa lembali akunena kudikira kotani? Popeza kuti nthawi zambiri kudikira kumawawa, kodi tingakhale bwanji osangalala podikira Mulungu?

Kukhala Osangalala Pamene Tikudikira

Tingaphunzire kwa Yehova maganizo abwino pankhani ya kudikira. Iye sanasiyepo kukhala “Mulungu wa chisangalalo.” (1 Timoteyo 1:11) Amasangalala akamadikira chifukwa choti panthawiyi amapitirizabe kuchita zinthu zothandiza kukwaniritsa cholinga chake choti anthu omwe amam’konda adzafike pokhala angwiro. Ichi ndicho chinali cholinga chake polenga anthuwo. (Aroma 5:12; 6:23) Amasangalala kuona zotsatirapo za zimene akuchitazo, chifukwa amaona anthu ambirimbiri amene akopeka mtima n’kuyamba kulambira m’njira yoona. Yesu anati: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.” (Yohane 5:17) Kuchita zinthu zothandiza anthu ena n’kofunika kwambiri kuti tikhale osangalala. (Machitidwe 20:35) Akhristu oona nawonso sakungodikira manja ali lendee. Koma amapitirizabe kuchita zinthu zothandiza ena kuphunzira za cholinga cha Mulungu polenga anthu.

Anthu okhulupirika, nthawi zonse amasangalala kutamanda Mulungu kwinaku akudikira nthawi ya Mulungu yochitira zinthu. Taonani chitsanzo cha wamasalmo Davide. Davide anazunzidwa ndi mfumu yake, anaperekedwa ndi mnzake wapamtima, ndipo ngakhale mwana wake amene anamuukira. Kodi zikanatheka kuti Davide akhale wosangalala pa mavuto onsewa, kwinaku akudikira Yehova kudzam’chotsa m’mavutowa panthawi yake? Salmo 71, lomwe mwina linalembedwa ndi Davide, limati: “Koma ine ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzawonjeza kukulemekezani. Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu.” (Salmo 71:14, 15) Davide sanamve kuwawa podikira koma anasangalala chifukwa choti podikirapo analinso kutamanda Yehova ndi kulimbikitsa ena kulambira m’njira yoona.​—Salmo 71:23.

Kudikira Yehova si kowawa ngati kudikira basi imene yachedwa. Kuli ngati kudikira kuti mwana akule m’njira yoti makolo ake azidzam’nyadira. Panthawi yodikirayo, makolo amachita zinthu zambiri monga kuphunzitsa mwanayo, kumuwongolera, ndi kumudzudzula m’njira yoyenerera. Zonsezi amazichita n’cholinga choti mwanayo akadzakula adzakhale mwana wonyaditsa. Ifenso tikamadikira Yehova timasangalala kuthandiza anthu kuyandikira kwa Mulungu. Nafenso timafuna kuti Mulungu azisangalala nafe, ndipo pamapeto pake adzatipulumutse.

Kusataya Mtima

Kudikira Yehova kumatanthauzanso kupitiriza kum’konda ndi kum’tumikira popanda kutaya mtima. Zimenezi zimakhala zovuta nthawi zina. Atumiki ambiri a Mulungu masiku ano amakhala m’madera amene anthu amanyoza aliyense amene amakhulupirira malonjezo a Mulungu pamoyo wake. Komano taganizirani chitsanzo cha Aisiraeli okhulupirika amene sanataye mtima pa zaka 70 zimene anali akapolo ku Babulo. Kodi n’chiyani chinawathandiza kuti asataye mtima? N’zosakayikitsa kuti kuwerenga masalmo kunawathandiza. Mbali imodzi ya masalmo yomwe iyenera kuti inawalimbikitsa pa nthawiyi, imati: “Ndiyembekeza mawu ake. Moyo wanga uyang’anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha. Isiraeli, uyembekezere Yehova.”​—Salmo 130:5-7.

Ayuda amene sanataye mtima powerenga ndiponso kuuza ena za chiyembekezo chawo anadalitsidwa pamene Babulo anagonjetsedwa ndi adani. Mwamsanga, Ayuda ambirimbiri okhulupirika anayambapo ulendo wopita ku Yerusalemu. Baibulo limanena za nthawiyi kuti: “Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, . . . pakamwa pathu panadzala ndi kuseka.” (Salmo 126:1, 2) Ayudawo sanataye mtima, koma anapitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Ndipo sanasiye kuimba nyimbo zotamanda Yehova.

Izi n’zimenenso amachita Akhristu oona amene akudikira Mulungu pa nthawi ya “mapeto a dongosolo lino la zinthu.” Nawonso amachita khama nthawi zonse kuti alimbitse chikhulupiriro chawo. Amaphunzira Mawu a Mulungu, amalimbikitsana, ndipo amatamanda Yehova polalikira uthenga wabwino wa Ufumu.​—Mateyo 24:3, 14.

Kudikira Mulungu Kuti Tiphunzirepo Kanthu pa Chilango Chake

Yeremiya, mneneri wa Mulungu analemba kuti: “N’kokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.” (Maliro 3:26) Pamenepa, Yeremiya anali kutanthauza kuti zikanakhala bwino anthu a Mulungu akanati asamadandaule kuti Yehova anawalanga polola kuti Yerusalemu awonongedwe. M’malo mwake, iwo anayenera kusangalala kuti anaphunzirapo kanthu pa chilangocho. Anayenera kutero poganizira za kusamvera kwawo ndi kuona kuti ankafunikadi kusintha maganizo awo.​—Maliro 3:40, 42.

Njira imene chilango cha Yehova chimatipindulitsira tingaiyerekezere ndi mmene zipatso zimakhwimira. Baibulo limanena mawu otsatirawa pankhani ya kulanga kwa Mulungu: “Kwa aja amene aphunzitsidwa nako, kumabala chipatso cha mtendere, ndicho chilungamo.” (Aheberi 12:11) Zipatso zimatenga nthawi kuti zipse, motero kusintha maganizo athu kuti agwirizane ndi zimene mawu a Mulungu amatiphunzitsa, kumatenganso nthawi. Mwachitsanzo, ngati khalidwe lathu linalake losayenera litachititsa kuti titaye mwayi winawake wotumikira mumpingo, mtima wodikira Mulungu ungatithandize kuti tisafooke kwambiri n’kufika potayiratu mtima. Pamenepa, mawu ouziridwa a Davide otsatirawa angatilimbikitse: “Mkwiyo [wa Mulungu] ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.” (Salmo 30:5) Tikakhala ndi mtima wodikira ndi kutsatira malangizo a Mawu a Mulungu ndi gulu lake, nthawi yathu ya “kufuula kokondwera” idzafika.

Kukhwima Maganizo Mwauzimu Kumatenga Nthawi

Ngati panopo mudakali wamng’ono kapena ngati mwangobatizidwa kumene, n’kutheka kuti mukufunitsitsa kukhala ndi maudindo enaake mu mpingo. Koma zimatenga nthawi kuti munthu afike pokhwima maganizo mwauzimu n’kumayendetsa maudindo amenewa bwinobwino. Motero, zaka zoyambirirazi zikhale mwayi wanu woti mukule mwauzimu. Mwachitsanzo, unyamata ndi nthawi yabwino kwambiri yowerenga Baibulo lonse, yoyesetsa kukhala ndi makhalidwe achikhristu, ndiponso yophunzira luso lopanga ophunzira. (Mlaliki 12:1) Mukadzichepetsa n’kusonyeza mtima wodikira, nthawi ya Yehova yokupatsani maudindo otere idzafika.

Ntchito yopanga ophunzira imafunanso kuleza mtima. Ntchitoyi ili ngati ulimi, chifukwatu mlimi ayenera kupitiriza kuthirira mbewu zake mpaka Mulungu atazichititsa kuti zimere. (1 Akorinto 3:7; Yakobe 5:7) Kuthandiza anthu ena kuti ayambe kukhulupirira ndiponso kumumvetsa bwino Yehova, kumatenga miyezi kapena mwinanso zaka zambiri mukuwaphunzitsa Baibulo moleza mtima. Kudikira Yehova kumatanthauzanso kupirira, ngakhale ngati poyamba, ophunzirawo sakuchitapo kanthu pa zimene akuphunzirazo. Kusonyeza pang’ono pokha kuti akuyamikira zimene akuphunzirazo, n’chizindikiro chakuti mwina akukhudzidwa mtima ndi mzimu wa Yehova. Mukaleza mtima, mungadzasangalale kuona Yehova akuthandiza munthu mukuphunzira nayeyo kukhala wophunzira wa Khristu.​—Mateyo 28:20.

Kusonyeza Chikondi Podikira

Taganizirani chitsanzo ichi cha mmene kudikira kumasonyezera chikondi ndi kusakayika. Pali gogo wina wamkazi yemwe amakhala m’chigawo chachipululu chotchedwa Andes, ku South America. M’mudzi wawo wonsewo, muli Mboni ziwiri zokha basi; iyeyu ndi mlongo wina. Ndiye tangoganizirani chisangalalo chimene amakhala nacho akamva kuti Akhristu anzawo akubwera kudzawaona. Komano nthawi ina, woyang’anira woyendayenda anasochera, ali paulendo wokayendera alongowa kwa nthawi yoyamba. Anabwereranso n’kuyamba kufunafuna njira yolondola, choncho anachedwa kwa maola ambiri ndithu. Ndiye cha m’bandakucha, woyang’anirayu anaona mudziwo uli patali. M’deralo munalibe magetsi motero anadabwa kuona kuwala. Ndiye atafika polowera m’mudziwo anasangalala kwambiri kuona kuti kuwalako kunali kwa nyali imene gogo uja anainyamula m’mwamba. Gogoyo sankakayika ngakhale pang’ono zoti mlendoyu abwera, motero anali kudikira.

Ifenso timaleza mtima monga anachitira gogoyu, n’kumadikira Yehova mosangalala. Sitikayika kuti adzakwaniritsa malonjezo ake. Ndipo monga woyang’anira woyendayenda uja, nafenso timasangalala ndi anthu omwe amatidikira mwachikondi. Moti sizodabwitsa kuti Mulungu amasangalala ndi anthu amene amam’dikira. Baibulo limati: “Yehova akondwera nawo . . . iwo akuyembekeza chifundo chake.”​—Salmo 147:11.

[Chithunzi patsamba 18]

Anthu amene amachita zinthu zosiyanasiyana zotamanda Yehova amasangalala kumudikira