Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi

Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi

Tikweze Dzina la Yehova Pamodzi

“Bukitsani pamodzi ndi ine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.”​—SALMO 34:3.

1. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chabwino chotani panthawi ya utumiki wake padziko lapansi?

USIKU, pa Nisani 14 m’chaka cha 33 C.E., Yesu ndi atumwi ake anaimba limodzi nyimbo zotamanda Yehova m’chipinda chapamwamba, m’nyumba inayake ku Yerusalemu. (Mateyo 26:30) Imeneyi inali nthawi yomaliza kuti Yesu achite zimenezi ndi atumwi ake. Ndipo zinali zoyenerera kuti Yesu amalize msonkhano umenewu ndi atumwiwo mwa njira imeneyi. Kuchokera pachiyambi cha utumiki wake mpaka pamapeto, Yesu analemekeza Atate ake ndipo anauza anthu mwakhama za dzina la Mulungu. (Mateyo 4:10; 6:9; 22:37, 38; Yohane 12:28; 17:6) Kwenikweni, anachita zinthu mogwirizana ndi mawu olimbikitsa amene wamasalmo ananena, oti: “Bukitsani pamodzi ndi ine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.” (Salmo 34:3) Iye ndi chitsanzo chabwinodi kwa ife!

2, 3. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Salmo 34 lili ndi nkhani zokhudza ulosi? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhani ino ndi yotsatira?

2 Patatha maola ochepa kuchokera pamene anaimbira limodzi ndi Yesu nyimbo zotamanda Mulungu, mtumwi Yohane anaona Mbuye wake ndi achifwamba awiri akuphedwa pa mitengo yozunzikirapo. Asilikali a Aroma anathyola miyendo ya achifwambawo kuti afe mwamsanga. Komabe, Yohane analemba kuti asilikaliwo sanathyole miyendo ya Yesu. Pofika kwa Yesu, anapeza kuti wafa kale. Yohane anafotokoza mu Uthenga Wabwino umene analemba, kuti kumeneku kunali kukwaniritsidwa kwa vesi lina la Salmo 34, lomwe limati: “Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.”​—Yohane 19:32-36; Salmo 34:20.

3 Salmo 34 lilinso ndi mfundo zina zambiri zomwe zingathandize Akhristu. Choncho, munkhani ino ndi yotsatira, tikambirana zomwe zinkachitika pa nthawi imene Davide ankalemba salmo limeneli. Tikambirananso mfundo zolimbikitsa zimene zili m’salmoli.

Davide Anathawa Sauli

4. (a) N’chifukwa chiyani Davide anadzozedwa kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli? (b) N’chifukwa chiyani Sauli ‘ankam’konda kwambiri’ Davide?

4 Davide ali mnyamata, Sauli anali mfumu ya Isiraeli. Koma Sauli anasiya kumvera Yehova, ndipo Yehova anasiyanso kum’konda. Choncho Samueli anauza Sauli kuti: “Yehova anang’amba ufumu wa Israyeli lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.” (1 Samueli 15:28) Kenaka Yehova anauza Samueli kuti adzoze Davide, mwana womaliza wa Jese, kuti adzakhale mfumu yotsatira ya Isiraeli. Panthawi imeneyi, Mfumu Sauli ankangokhala ndwii chifukwa mzimu wa Mulungu unali utam’chokera. Davide anali wodziwa kuimba ndipo anatumizidwa ku Gibeya kuti azikatumikira mfumuyi. Nyimbo za Davide zinkam’tsitsimula Sauli, ndipo mfumuyi ‘inkam’konda kwambiri’ Davide.​—1 Samueli 16:11, 13, 21, 23.

5. N’chifukwa chiyani Sauli anasintha mmene ankamuonera Davide, ndipo Davide anachita chiyani?

5 M’kupita kwa nthawi, zinaoneka kuti Yehova anali ndi Davide. Yehova anathandiza Davide kuti agonjetse Goliati, chimphona cha Afilisiti. Ndiponso anali naye pamene anthu anayamba kumulemekeza mu Isiraeli chifukwa cha luso lake pankhondo. Koma Sauli ataona kuti Yehova akudalitsa Davide, anayamba kum’chitira nsanje, ndi kudana naye kwambiri. Kawiri konse, mfumu Sauli anafuna kulasa Davide ndi mkondo pamene anali kumuimbira zeze. Nthawi ziwiri zonsezi, Davide anatha kulewa mkondowo. Sauli atayeseranso kumupha kachitatu, Davide, mfumu yam’tsogolo ya Isiraeli, anaona kuti ayenera kuthawa kuti apulumutse moyo wake. Kenaka, chifukwa choti Sauli ankayesetsabe kuti am’gwire ndi kumupha, Davide anaganiza zothawira kunja kwa Isiraeli.​—1 Samueli 18:11; 19:9, 10.

6. N’chifukwa chiyani Sauli analamula kuti anthu a ku Nobi aphedwe?

6 Akuthawira ku malire a dziko la Isiraeli, Davide anaima mu mzinda wa Nobi, komwe kunali chihema cha Yehova. Zikuoneka kuti Davide pothawa anaperekezedwa ndi anyamata angapo, ndipo Davide atafika mu mzindawu anapempha chakudya choti iyeyo ndi anyamatawo adye. Sauli anauzidwa kuti mkulu wa ansembe wapatsa Davide ndi anyamata ake chakudya ndiponso lupanga limene linali la Goliati. Pokwiya, Sauli analamula kuti anthu onse a mumzindawo, kuphatikizapo ansembe 85, aphedwe.​—1 Samueli 21:1, 2; 22:12, 13, 18, 19; Mateyo 12:3, 4.

Anapulumukanso Atatsala Pang’ono Kuphedwa

7. N’chifukwa chiyani ku Gati sikunali kwabwino kuti Davide abisaleko?

7 Atachoka ku Nobi, Davide anapitiriza kuthawa ndipo anayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 40 kulowera kumadzulo m’dziko la Afilisiti, ndipo anakabisala kwa Mfumu Akisi ya ku Gati, kwawo kwa Goliati. Mwina Davide ankaganiza kuti Sauli sangakam’funefune ku Gati. Koma pasanapite nthawi, antchito a mfumu ya ku Gati anam’zindikira Davide. Iye atamva anthu akunena kuti am’zindikira, ‘anaopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati.’​—1 Samueli 21:10-12.

8. (a) Kodi Salmo 56 likutiuza chiyani za zomwe zinachitikira Davide ku Gati? (b) Kodi Davide anapulumuka bwanji atatsala pang’ono kuphedwa?

8 Kenaka Afilisitiwo anam’gwira Davide. Mwina panthawi imeneyi m’pamene Davide analemba salmo lokhudza mtima lopempha Yehova kuti: “Sungani misozi yanga m’nsupa yanu.” (Salmo 56:8 ndi timawu tapamwamba) Ponena mawu amenewa, anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro kuti Yehova sangaiwale chisoni chake koma adzam’samalira mwachikondi ndi kum’teteza. Davide anaganiziranso momwe anganamizire mfumu ya Afilisiti. Anachita zinthu ngati kuti anali wamisala. Mfumu Akisi ataona zimenezi, anawakalipira antchito ake pom’bweretsera munthu “wamisala.” N’zoonekeratu kuti Yehova anadalitsa zimene Davide anachita. Kenaka Davide anathamangitsidwa mu mzindawo, ndipo apanso anapulumuka atangotsala pang’ono kuphedwa.​—1 Samueli 21:13-15.

9, 10. N’chifukwa chiyani Davide analemba Salmo 34, ndipo mwina ankaganizira ndani polemba salmoli?

9 Baibulo silitiuza ngati anthu amene anali ku mbali ya Davide anathawira naye limodzi ku Gati, kapena ngati anakhala m’midzi yoyandikana ndi mzindawo kuti aziona ngati kukubwera adani. Mulimonse mmene zinalili, anthuwo ayenera kuti anasangalala Davide atakumana nawonso n’kuwauza kuti Yehova anam’pulumutsanso. Zimenezi zinachititsa Davide kulemba Salmo 34, monga momwe timawu tapamwamba pa salmoli tikusonyezera. M’mavesi 7 oyambirira a salmoli, Davide anatamanda Mulungu chifukwa chom’pulumutsa. Anapemphanso anthu omwe anali ku mbali yake kuti akweze Yehova limodzi naye popeza ndi Mpulumutsi Wamkulu wa anthu Ake.​—Salmo 34:3, 4, 7.

10 Davide ndi anyamata ake anakabisala m’phanga la ku Adulamu. Phanga limeneli linali kudera la mapiri ku Isiraeli, pamtunda wa makilomita pafupifupi 15 kum’mawa kwa Gati. Aisiraeli omwe sankasangalala ndi ulamuliro wa Mfumu Sauli anayamba kubwera kuphangako kudzakhala ndi Davide ndi anyamata ake. (1 Samueli 22:1, 2) Pamene Davide ankalemba mawu omwe ali pa Salmo 34:8-22, mwina ankaganizira anthu amenewa. Mfundo zomwe zili m’mavesi amenewa n’zothandizanso kwa ife masiku ano, ndipo tipindula pokambirana mwatsatanetsatane salmo losangalatsali.

Kodi Cholinga Chachikulu Pamoyo Wanu N’chofanana ndi cha Davide?

11, 12. Kodi tili ndi zifukwa zotani zolemekezera Yehova nthawi zonse?

11 “Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kum’lemekeza kwake kudzakhala m’kamwa mwanga kosalekeza.” (Salmo 34:1) Popeza Davide ankakhala mothawathawa, ayenera kuti ankada nkhawa kuti azipeza bwanji zosowa za moyo wake. Koma mawu amenewa akusonyeza kuti Davide anapitirizabe kukhala ndi mtima wofuna kulemekeza Yehova, ngakhale kuti anali ndi nkhawa zimenezi. Iye alidi chitsanzo chabwino kwa ife tikamakumana ndi mavuto. Kaya tili ku sukulu, ku ntchito, tili limodzi ndi Akhristu anzathu, kapena tikulalikira, cholinga chathu chachikulu chizikhala chofuna kulemekeza Yehova. Tangoganizirani zifukwa zambirimbiri zomwe tili nazo zochitira zimenezi. Mwachitsanzo, pali zinthu zambiri zomwe tingaziphunzire ndi kusangalala nazo m’chilengedwe cha Yehova chochititsa chidwichi. Ndipo taganizirani zimene Yehova wachita pogwiritsira ntchito mbali yapadziko lapansi ya gulu lake. Yehova wagwiritsira ntchito anthu okhulupirika kuchita zinthu zazikulu, ngakhale kuti ndi opanda ungwiro. Kodi ntchito za Mulungu tingaziyerekezere ndi za anthu amene dzikoli limawalambira? Kodi simukugwirizana ndi Davide, amene analemba kuti: “Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye; ndipo palibe ntchito zonga zanu.”​—Salmo 86:8.

12 Mofanana ndi Davide, timafuna kulemekeza Yehova nthawi zonse chifukwa cha ntchito zake zosayerekezeka. Komanso, timasangalala kwambiri podziwa kuti Ufumu wa Mulungu tsopano uli m’manja mwa wolowa ufumu wa Davide, Yesu Khristu, amene adzalamulire kosatha. (Chivumbulutso 11:15) Zimenezi zikusonyeza kuti mapeto a dongosolo lino la zinthu ayandikira. Moyo wosatha wam’tsogolo wa anthu oposa 6 biliyoni uli pa ngozi. Panopa, kuposa kale lonse, tikufunika kuuza anthu za Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzawachitire posachedwapa, komanso tikufunika kuwathandiza kuti alemekeze Yehova limodzi nafe. Inde, cholinga chathu chachikulu pamoyo chiyenera kukhala chogwiritsira ntchito mpata uliwonse kulimbikitsa anthu kuti avomereze “uthenga wabwino” nthawi isanathe.​—Mateyo 24:14.

13. (a) Kodi Davide anatamanda ndani, ndipo zimenezi zinakhudza mtima anthu otani? (b) Kodi n’chiyani chikuchititsa anthu ofatsa kulowa mu mpingo wachikhristu masiku ano?

13 “Moyo wanga udzatamanda Yehova; ofatsa adzakumva nadzakondwera.” (Salmo 34:2) Apa, Davide sanali kudzitama chifukwa cha zinthu zimene anachita bwino. Mwachitsanzo, sanadzitame chifukwa cha mmene ananamizira mfumu ya ku Gati. Anazindikira kuti Yehova anam’teteza ali ku Gati, ndi kuti anathawa chifukwa cha thandizo lake. (Miyambo 21:1) Choncho Davide sanadzitame, koma anatamanda Yehova. Zimenezi zinachititsa anthu ofatsa kuyamba kukonda Yehova. Yesu nayenso anakweza dzina la Yehova, ndipo zimenezi zinachititsanso anthu odzichepetsa ndi ophunzitsika kuyamba kukonda Yehova. Masiku ano, anthu ofatsa a m’mayiko onse akulowa mu mpingo wapadziko lonse wa Akhristu odzozedwa, womwe Yesu ndiye Mutu wake. (Akolose 1:18) Anthu ofatsawa amakhudzidwa mtima akamva dzina la Mulungu likulemekezedwa ndi atumiki ake odzichepetsa ndiponso akamvetsetsa uthenga wa m’Baibulo mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu.​—Yohane 6:44; Machitidwe 16:14.

Misonkhano Imalimbitsa Chikhulupiriro Chathu

14. (a) Kodi Davide anaona kuti kulemekeza Yehova payekha n’kokwanira? (b) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pankhani ya kusonkhana n’cholinga cholemekeza Mulungu?

14 “Bukitsani pamodzi ndi ine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.” (Salmo 34:3) Davide anaona kuti kungolemekeza Yehova payekha si kokwanira. Iye anapempha mokoma mtima anthu amene anali nawo kuti akweze dzina la Mulungu limodzi naye. Mofanana ndi zimenezi, Yesu Khristu, yemwe ndi Davide Wamkulu, ankasangalala kulemekeza Yehova ndi anthu ena. Ankachita zimenezi kusunagoge wakwawo, pamadyerero kukachisi wa Mulungu ku Yerusalemu, ndiponso limodzi ndi otsatira ake. (Luka 2:49; 4:16-19; 10:21; Yohane 18:20) Ndi mwayi wapadera kwambiri kutsatira chitsanzo cha Yesu, n’kumalemekeza Yehova nthawi iliyonse yomwe tingathe kuchita zimenezi limodzi ndi okhulupirira anzathu, makamaka panopa pamene ‘tikuona kuti tsikulo likuyandikira.’​—Aheberi 10:24, 25.

15. (a) Kodi zimene zinachitikira Davide zinakhudza bwanji anthu omwe anali naye? (b) Kodi timapindula bwanji chifukwa chopita ku misonkhano?

15 “Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m’mantha anga onse.” (Salmo 34:4) Zinthu ngati zimenezi zinali zofunika kwambiri kwa Davide. Choncho anawonjezera kuti: “Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nam’pulumutsa m’masautso ake onse.” (Salmo 34:6) Tikakhala ndi okhulupirira anzathu, timakhala ndi mipata yambiri yofotokoza zinthu zolimbikitsa zosonyeza momwe Yehova watithandizira kupirira mavuto. Zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro cha okhulupirira anzathu, monga momwe zimene Davide ananena zinalimbitsira chikhulupiriro cha anthu omwe anali ku mbali yake. Anthu omwe anali ndi Davide ‘anayang’ana [Yehova] nasanguluka: ndipo pankhope pawo sipanachite manyazi.’ (Salmo 34:5) Iwo sanachite manyazi ngakhale kuti ankathawa Mfumu Sauli. Anali ndi chikhulupiriro choti Mulungu anali ndi Davide, ndipo nkhope zawo zinali zosangalala. Mofanana ndi zimenezi, anthu amene akungophunzira kumene choonadi komanso amene akhala Akhristu kwa nthawi yaitali amadalira Yehova kuti awathandize. Popeza adzionera okha Yehova akuwathandiza, nkhope zawo n’zosangalala ndipo zimasonyeza kuti ndi otsimikiza mtima kukhalabe okhulupirika.

Yamikirani Thandizo la Angelo

16. Kodi Yehova wapulumutsa bwanji anthu ake pogwiritsira ntchito angelo?

16 “Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.” (Salmo 34:7) Davide sanaganize kuti iye yekha ndi amene angapulumutsidwe ndi Yehova. N’zoona kuti Davide anali wodzozedwa wa Yehova, mfumu yam’tsogolo ya Isiraeli, koma ankadziwa kuti Yehova amagwiritsira ntchito angelo ake kuteteza olambira ake onse okhulupirika, kaya ndi apamwamba kapena otsika. Masiku ano, olambira oona akutetezedwanso ndi Yehova. Akuluakulu a boma anayesetsa kupulula Mboni za Yehova ku Germany panthawi yomwe chipani cha Nazi chinkalamulira. Anayesetsanso kupulula Mboni za Yehova ku Angola, ku Malawi, ku Mozambique, ndi ku mayiko ena ambiri, koma analephera. M’malo mwake, anthu a Yehova m’mayiko amenewa zinthu zikuwayenderabe bwino pamene akukweza dzina la Mulungu pamodzi. Chifukwa chiyani? Chifukwa Yehova amagwiritsira ntchito angelo ake kuteteza ndi kutsogolera anthu ake.​—Aheberi 1:14.

17. Kodi angelo a Mulungu amatithandiza m’njira zotani?

17 Komanso, Yehova akhoza kuchititsa kuti aliyense wokhumudwitsa anthu ena achotsedwe pakati pa anthu ake. (Mateyo 13:41; 18:6, 10) Ndipo angelo amachotsa zopinga zimene zingatisokoneze potumikira Mulungu, ndiponso amatiteteza ku zinthu zimene zingawononge unansi wathu ndi Yehova, ngakhale kuti nthawi zina sitidziwa akamachita zimenezi. Koposa zonse, amatitsogolera pa ntchito yolengeza “uthenga wabwino wosatha” kwa anthu onse, kuphatikizapo m’madera amene ntchito yolalikira imaika pa ngozi moyo wa olalikirawo. (Chivumbulutso 14:6) Nkhani zambiri zosonyeza kuti angelo akuthandiza anthu zalembedwa m’mabuku ofotokoza za m’Baibulo ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. * Zinthu ngati zimenezi zimachitika kwambiri moti n’zoonekeratu kuti sizichitika zokha.

18. (a) Kodi tiyenera kutani kuti angelo azitithandiza? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tikambirana chiyani?

18 Kuti angelo apitirize kutitsogolera ndi kutiteteza, tiyenera kupitiriza kukweza dzina la Yehova ngakhale pamene tikutsutsidwa. Kumbukirani kuti mngelo wa Mulungu ‘amazinga ndi kutchinjiriza iwo akuopa [Yehova]’ okha. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kodi kuopa Mulungu n’kutani, ndipo tingakhale bwanji anthu oopa Mulungu? N’chifukwa chiyani Mulungu wachikondi angafune kuti tizimuopa? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Onani buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 550; 2005 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, tsamba 53-54; Nsanja ya Olonda ya March 1, 2000, tsamba 5-6; ya January 1, 1991, tsamba 27; ndi ya February 15, 1991, tsamba 26.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Davide anapirira mayesero otani ali mnyamata?

• Mofanana ndi Davide, kodi cholinga chachikulu pamoyo wathu n’chiyani?

• Kodi misonkhano yachikhristu timaiona bwanji?

• Kodi Yehova amatithandiza bwanji pogwiritsira ntchito angelo ake?

[Mafunso]

[Mapu patsamba 21]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Rama

Gati

Zikilaga

Gibea

Nobi

Yerusalemu

Betelehemu

Adulamu

Kehila

Hebroni

Zifi

Horesi

Karimeli

Maoni

En-gedi

Nyanja Yamchere

[Mawu a Chithunzi]

Map: Based on maps copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel

[Chithunzi patsamba 21]

Davide anakwezabe dzina la Yehova ngakhale pamene anali kuthawathawa

[Chithunzi patsamba 23]

Chikhulupiriro chathu chimalimba tikamva ena akufotokoza pa misonkhano yachikhristu zinthu zolimbikitsa zomwe zawachitikira