Tsanzirani Kukoma Mtima kwa Yehova
Tsanzirani Kukoma Mtima kwa Yehova
YEHOVA MULUNGU amapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kusonyeza kukoma mtima m’njira zosiyanasiyana, ngakhale kwa anthu osayamika ndi oipa. Ndipo amawalimbikitsa oipawo kuti alape. (Luka 6:35) Akhristu nawonso, poti ali m’goli lofewa la Khristu, amalimbikitsidwa kuti avale khalidwe la kukoma mtima ndiponso kuti ayesetse kukhala ndi zipatso za mzimu wa Mulungu, zomwe palinso kukoma mtima. (Agalatiya 5:22; Akolose 3:12) Akamatero amadzichitira umboni kuti ndi atumiki a Mulungu.—2 Akorinto 6:4-6.
Khalidwe la Yehova la Kukoma Mtima Kwachikondi
Kukoma mtima kwachikondi ndi khalidwe lamtengo wapatali la Yehova Mulungu, lomwe iye amasangalala nalo kwambiri. Yehova amasonyeza khalidweli nthawi zonse akamachita zinthu ndi anthu. (Salmo 36:7) Akanati asamatero, bwenzi anthu onse atatha kalekale. (Maliro 3:22) N’chifukwa chake pamene Mose ankadandaulira Yehova kuti achitire chifundo Aisiraeli osamvera anati, Mulunguyo akhululuke chifukwa cha dzina lake lalikulu ndiponso chifukwa choti ndi Mulungu wachifundo, kapena kuti wokoma mtima mwachikondi.—Numeri 14:13-19.
Malemba amasonyeza kuti khalidwe lake la kukoma mtima kwachikondi, kapena kuti chikondi chokhulupirika, Yehova amalisonyeza m’njira zosiyanasiyana ndiponso m’zochitika zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, amalisonyeza populumutsa ndi kusunga anthu ake, ndiponso powateteza ndi kuwalanditsa pa mavuto awo. (Salmo 6:4; 31:16, 21; 40:11) Anthu amene Mulungu wasankha amawathandiza powasonyeza khalidweli.—Salmo 44:26.
Mtundu wa Isiraeli utakhazikitsidwa, Yehova anapitirizabe kusonyeza khalidwe lake la kukoma mtima kwachikondi mogwirizana ndi pangano limene anachita ndi mtunduwu. (Eksodo 15:13) Yehova anaonetsa khalidweli kwa Davide ndiponso Ezara pamodzi ndi anthu omwe anali naye. (2 Samueli 7:15; Ezara 7:28; 9:9) Pochirikiza pangano la ufumu limene anapanga ndi Davide, Yehova anapitiriza kusonyeza kukoma mtima kwachikondi ngakhale panthawi imene Yesu anafa. Yehova anatero mwa kuukitsa munthu wake ‘wokhulupirikayu’ pokwaniritsa ulosi wakuti: “Ine ndidzapatsa anthu inu zinthu za kukoma mtima kwachikondi zokhulupirika zimene ndinalonjeza Davide.”—Machitidwe 13:34; Yesaya 55:3.
Khalidwe la kukoma mtima kwachikondili ndi limene limachititsa kuti anthu azikopeka ndi Yehova. (Yeremiya 31:3) Iwo amathokoza Yehova chifukwa cha khalidwe lakeli ndipo amam’lemekeza ndi kum’tamanda nalo. Amauzanso ena za khalidweli. Ndithudi, khalidweli lili ngati njira yosangalatsa kwambiri kuyendamo.—Salmo 25:10.
Nthawi zambiri khalidwe la Yehova losangalatsa kwambirili, limatchulidwa mogwirizana ndi makhalidwe enanso okoma a Mulungu, monga chifundo, chisomo, choonadi, kukhululuka, chilungamo, mtendere, ndi chiweruzo.—Eksodo 34:6; Nehemiya 9:17; Salmo 85:10.
Khalidwe la Mulungu la Kukoma Mtima kwa M’chisomo
Mulungu anaonetsa khalidwe la kukoma mtima kwa m’chisomo kwa anthu onse m’njira yapadera. Iye anawamasula ku imfa pogwiritsira ntchito dipo ndipo anatero kudzera mwa magazi a Mwana wake wokondedwa, Khristu Yesu. (Aefeso 1:7) Pogwiritsa ntchito khalidwe lake la kukoma mtima kwa m’chisomo, Mulungu akupereka chipulumutso kwa anthu osiyanasiyana. (Tito 2:11) Motero mpake kuti Paulo ananena mfundo yotsatirayi: “Ndiyetu ngati anasankhidwa mwa kukoma mtima kwa m’chisomo, si mwa ntchitonso ayi; zitati zitero, kukoma mtima kumeneko sikungakhalenso kukoma mtima.”—Aroma 11:6.
Paulo anatchula khalidweli kuposa wolemba Baibulo wina aliyense. M’makalata ake 14, iye analitchula koposa ka 90. Paulo anali ndi zifukwa zokwanira zogogomezera khalidweli, chifukwatu poyamba iye anali “wonyoza ndi wozunza ndiponso wachipongwe.” Komano iye anati: “Komabe anandichitira chifundo chifukwa ndinali wosadziwa ndi wopanda chikhulupiriro. Koma kukoma mtima kwa m’chisomo cha Ambuye wathu kunakula kwambiri, limodzi ndi chikhulupiriro, ndi chikondi mwa Khristu Yesu.” (1 Timoteyo 1:13, 14) Paulo sananyoze kukoma mtima kwa m’chisomo kumeneku, monga anthu ena opusa achitira. M’malo mwake, anasangalala ndiponso anathokoza kwambiri Mulungu pom’sonyeza khalidweli ndipo analimbikitsa enanso amene anasonyezedwa khalidweli kuti ‘asaphonye cholinga chake.’—Machitidwe 20:24.
Khalidwe la Anthu la Kukoma Mtima Kwachikondi
M’Baibulo muli nkhani zambirimbiri za anthu amene anasonyeza anzawo khalidwe la kukoma mtima kwachikondi. Mwachitsanzo, Sara anasonyeza mwamuna wake chikondi chokhulupirika choterechi panthawi imene anali m’dziko la adani. Sara anatero mwa kuteteza mwamuna wakeyo ponena kuti ndi mchimwene wake. (Genesis 20:13) Yakobo anapempha Yosefe kuti amukomere mtima mwachikondi pomulonjeza kuti asadzamuike ku Iguputo akadzafa. (Genesis 47:29; 50:12, 13) Rahabi anapempha kuti Aisiraeli amukomere mtima mwachikondi posapha azibale ake, chifukwa nayenso anakomera mtima amuna a ku Isiraeli amene anadzazonda mzindawo. (Yoswa 2:12, 13) Boazi anayamikira Rute chifukwa cha kukoma mtima kwake. (Rute 3:10) Yonatani anapempha Davide kuti am’komere mtima Yonataniyo komanso mbumba yake.—1 Samueli 20:14, 15.
Anthu amasonyeza khalidwe la kukoma mtima pa zolinga ndiponso zifukwa zosiyanasiyana. Nthawi zina anthu amangokoma mtima pa nthawi inayake chifukwa cha chikhalidwe chawo chochereza ena kapena chifukwa cha mtima wawo wachifundo, koma zimenezi pazokha sizisonyeza kuti anthuwo n’ngoopa Mulungu. (Yerekezani ndi Machitidwe 27:1, 3; 28:1, 2.) Nkhani ya munthu wina wa mumzinda wotchedwa Beteli, imasonyeza kuti anthu amene anam’komera mtima munthuyu, kwenikweni anatero chifukwa choti ankafuna kum’pempha zinazake. (Oweruza 1:22-25) Pali anthu ena amene anapempha anzawo kuti awakomere mtima chifukwa choti opemphawo anathandizapo opemphedwawo panthawi ina, ndipo mwina opemphawo n’kuti panthawiyo ali pamavuto enaake. (Genesis 40:12-15) Koma ena sankabwezera kukoma mtima kumeneku.—Genesis 40:23.
Monga mmene buku la Miyambo limasonyezera, pali ambiri onena kuti n’ngokoma mtima, koma ndi ochepa chabe amene amakomadi mtima. (Miyambo 20:6) Sauli ndiponso Davide anabwezera kukoma mtima kwachikondi kumene anthu ena anawasonyezapo. Zikuonekanso kuti mafumu a Isiraeli anali odziwika ndithu kuti anali anthu okoma mtima kwambiri, mwina powayerekezera ndi mafumu achikunja. (1 Samueli 15:6, 7; 2 Samueli 2:5, 6; 1 Mafumu 20:31) Komabe, panthawi ina Davide atachita zinthu mokoma mtima, ena anam’bwezera zachipongwe poganiza kuti Davideyo akungonamizira.—2 Samueli 10:2-4.
Anthu amene akufuna kuti Mulungu azisangalala nawo ayenera “kukonda chifundo” ndiponso ‘kuchitirana chifundo ndi kukomerana mtima.’ (Mika 6:8; Zekariya 7:9) Buku la Miyambo limati: “[Chochititsa kuti tikonde] munthu ndicho kukoma mtima kwake,” ndipo munthu wotere amadalitsidwa kwambiri. (Miyambo 19:22; 11:17) Mulungu anakumbukira ndiponso anasangalala ndi kukoma mtima kumene mtundu wa Isiraeli unamusonyeza udakali waung’ono. (Yeremiya 2:2) Komano utafika pokhala ngati “mtambo wam’mawa ndi ngati mame akuphwa mamawa,” Yehova sanasangalale nawo, chifukwa anati “ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ayi.”—Hoseya 6:4, 6.
Mulungu anadzudzula mtundu wa Isiraeli chifukwa choti unali wosakoma mtima ndipotu kwenikweni Mulunguyo anakoma mtima powadzudzula choncho. (Hoseya 4:1) Mulungu analangizanso mtunduwo kuti uyambenso kusonyeza kukoma mtima ndi chilungamo kuti ubwerere kwa iye. (Hoseya 12:6) Tiyenera kuonetsa makhalidwe amenewa nthawi zonse ngati tikufuna kuti Mulungu ndiponso anthu azitikonda.—Yobu 6:14.