“Anatiumiriza Kupita Basi!”
“Anatiumiriza Kupita Basi!”
ANTHU a kumayiko a kum’mawa ali ndi khalidwe lochereza alendo. Mwachitsanzo, ku India zimatheka banja kugona ndi njala kuti adyetse mlendo. Ku Iran, mayi panyumba amasunga chakudya chambiri kuti kukabwera alendo nthawi ina iliyonse, adzadye.
Anthu ambiri otchulidwa m’Baibulo analinso ndi khalidwe lochereza alendo. Wina amene anali chitsanzo chabwino kwambiri pakhalidwe limeneli ndi Lidiya. Ameneyu ayenera kuti anachita kutembenuka kulowa Chiyuda ndipo ankakhala ku Filipi, mzinda waukulu wa ku Makedoniya. Tsiku lina la sabata, mtumwi Paulo ndi anzake anapeza Lidiya ndi akazi ena kumtsinje wa ku Filipi. Yehova anatsegula mtima wa Lidiya kuti atchere khutu pamene Paulo anali kulankhula. Mapeto ake, anabatizidwa pamodzi ndi a m’banja lake. Kenako anachonderera alendowo kuti: “Abale ngati inu mwaona kuti ndine wokhulupirika kwa Yehova, mukalowe m’nyumba yanga ndi kukhala mmenemo.” Luka, mnzake wa Paulo, anati: “Moti anatiumiriza kupita basi!”—Machitidwe 16:11-15.
Mofanana ndi Lidiya, Akhristu masiku ano amachereza okhulupirira anzawo monga oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo. Akhristuwo ‘amawaumiriza’ kukhala basi. Ndiponso amene amalandira alendo amasangalala ndi macheza olimbikitsa ndi ubale wachikhristu. Ngakhale kuti Mboni za Yehova zambiri zilibe chuma, ‘zimakhala zochereza’ alendo. (Aroma 12:13; Aheberi 13:2) Zimakhala ndi chisangalalo chifukwa cha mtima wawo wopatsa. Yesu ananenadi zoona pamene anati: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.