Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ziwanda Tingalimbane Nazo Bwanji?

Kodi Ziwanda Tingalimbane Nazo Bwanji?

Kodi Ziwanda Tingalimbane Nazo Bwanji?

“Angelo amene sanasunge malo awo oyambirira koma anasiya malo awo okhala, Mulungu anawasunga m’maunyolo kosatha mu mdima wandiweyani kuti akaweruzidwe tsiku lalikulu.”​—YUDA 6.

1, 2. Kodi anthu amafunsa mafunso otani okhudza Satana Mdyerekezi ndi ziwanda?

MTUMWI Petulo anachenjeza kuti: “Sungani maganizo anu, khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.” (1 Petulo 5:8) Ndiponso mtumwi Paulo ananena za ziwanda kuti: “Sindikufuna kuti mukhale ogawana ndi ziwanda. Sizingatheke kuti muzimwa chikho cha Yehova komanso chikho cha ziwanda; sizingatheke kuti muzidya pa ‘tebulo la Yehova’ komanso pa tebulo la ziwanda.”​—1 Akorinto 10:20, 21.

2 Koma kodi Satana Mdyerekezi ndi ziwanda ndi ndani? Kodi anakhalako bwanji ndipo anakhalako liti? Kodi Mulungu ndiye anawalenga? Kodi ali ndi mphamvu yotani pa anthu? Ngati n’zotheka, kodi tingadziteteze bwanji kwa iwo?

Kodi Satana ndi Ziwanda Anakhalako Bwanji?

3. Kodi mngelo wina wa Mulungu anakhala bwanji Satana Mdyerekezi?

3 Kalekale anthu atalengedwa ndipo ali m’munda wa Edene, mngelo wina wa Mulungu anapanduka. Anapanduka chifukwa chiyani? Chifukwa sanasangalale ndi udindo wake m’gulu la Yehova lakumwamba. Adamu ndi Hava atalengedwa, mngeloyo anapeza mpata woti awasiyitse kumvera ndi kulambira Mulungu woona n’kuyamba kulambira iyeyo. Mngelo ameneyo anadzipanga yekha kukhala Satana Mdyerekezi mwa kupandukira Mulungu ndi kulimbikitsa anthu awiri oyambirira kuti achimwe. Patapita nthawi, angelo ena anapandukanso. Kodi anapanduka bwanji?​—Genesis 3:1-6; Aroma 5:12; Chivumbulutso 12:9.

4. Chigumula cha Nowa chisanachitike, kodi angelo opanduka anachita chiyani?

4 Malemba amatiuza kuti nthawi inayake Chigumula cha Nowa chisanachitike, angelo ena anayamba kuchita chidwi kwambiri ndi akazi padziko lapansi. Baibulo limanena kuti: “Ana aamuna [akumwamba] a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.” Anachita zimenezi ndi cholinga choipa. Mabanja amenewa sanali oyenerera, ndipo anabereka zimphona zotchedwa Anefili. (Genesis 6:2-4) Angelo amene sanamvere Mulungu amenewa anagwirizana ndi Satana popandukira Yehova.

5. Yehova atawononga anthu ndi Chigumula, n’chiyani chinachitikira opandukawo?

5 Yehova atawononga anthu ndi Chigumula, Anefiliwo ndi amayi awo anawonongedwa limodzi. Angelo opandukawo sakanachitira mwina koma kuvula matupi awo aumunthu n’kubwerera kumwamba. Koma sanathe kubwerera kwa Mulungu ku “malo awo oyambirira.” M’malo mwake, anaponyedwa ku “mdima wandiweyani” wauzimu, wotchedwa Tatalasi.​—Yuda 6; 2 Petulo 2:4.

6. Kodi ziwanda zimanyenga bwanji anthu?

6 Kuchokera pamene angelo oipawo anataya “malo awo oyambirira,” anakhala ziwanda komanso anzake a Satana ndipo amamuthandiza pa ntchito zake zoipa. Kuchokera nthawi imeneyo, ziwanda sizinakhalenso ndi mphamvu yoti n’kuvala matupi aumunthu. Komabe zimatha kunyengerera amuna ndi akazi kuti achite zachiwerewere zamtundu uliwonse. Ziwandazo zimanyenganso anthu kwambiri kuti azichita zinthu zamizimu, monga matsenga, ufiti, ndi kuwombeza. (Deuteronomo 18:10-13; 2 Mbiri 33:6) Tsogolo la angelo oipa amenewa n’lofanana ndi la Mdyerekezi. Onse adzawonongedwa kosatha. (Mateyo 25:41; Chivumbulutso 20:10) Koma panopa tiyenera kuchirimika ndi kulimbana nawo. Tichita bwino kukambirana za mphamvu zimene Satana ali nazo ndi zimene ifeyo tingachite kuti tilimbane naye ndi ziwanda zake ndi kuwagonjetsa.

Kodi Satana Mphamvu Zake N’zotani?

7. Kodi Satana ali ndi mphamvu zotani padzikoli?

7 Satana wakhala akutonza Yehova kwa zaka zambiri. (Miyambo 27:11) Ndipo wasokeretsa anthu ambiri. Lemba la 1 Yohane 5:19 limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Ndiye chifukwa chake Mdyerekezi anayesa Yesu pofuna kum’patsa ulamuliro ndi ulemerero wa “maufumu onse a padziko lapansi.” (Luka 4:5-7) Mtumwi Paulo ananena za Satana kuti: “Tsopano, ngati uthenga wabwino umene tilengeza ndi wophimbika, uli wophimbika pakati pa anthu amene akuwonongeka. Mwa anthu amenewa, mulungu wa dongosolo lino la zinthu wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira, kuti asaone kuwala kwa uthenga wabwino waulemerero wonena za Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu.” (2 Akorinto 4:3, 4) Satana ndi “wabodza komanso tate wake wa bodza,” koma amadzionetsera ngati “mngelo wa kuwala.” (Yohane 8:44; 2 Akorinto 11:14) Ali ndi mphamvu komanso nzeru zimene amagwiritsa ntchito kuchititsa khungu maganizo a olamulira a dzikoli ndi anthu awo. Iye wanyenga anthu pofalitsa nkhani zabodza ndiponso pogwiritsa ntchito zikhulupiriro za zipembedzo.

8. Kodi Baibulo limanena chiyani za mphamvu za Satana?

8 Mphamvu za Satana zinaonekera nthawi ya mneneri Danieli, cha m’ma 500 B.C.E. Yehova atatuma mngelo kuti akapereke uthenga wolimbikitsa kwa Danieli, chiwanda chimene chinali “kalonga wa ufumu wa Perisiya” chinalimbana ndi mngeloyo. Mngelo wokhulupirika ameneyo anatsekerezedwa masiku 21 mpaka “Mikaeli, wina wa akalonga omveka,” anabwera kudzam’thandiza. Nkhani yomweyo imanenanso za chiwanda chimene chinali “kalonga wa Helene.” (Danieli 10:12, 13, 20) Ndipo pa Chivumbulutso 13:1, 2, Satana akufotokozedwa ngati “chinjoka” chimene chikupatsa chilombo choimira andale “mphamvu yake, mpando wake wachifumu, komanso ulamuliro wake waukulu.”

9. Kodi Akhristu akulimbana ndi ndani?

9 Choncho m’pomveka kuti mtumwi Paulo analemba kuti: “Sitikulimbana ndi anthu a thupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi maboma, ndi maulamuliro, ndi olamulira dziko a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo a kumwamba.” (Aefeso 6:12) Ngakhale masiku ano, makamu osaoneka a ziwanda otsogozedwa ndi Satana Mdyerekezi, ali ndi mphamvu pa olamulira aumunthu ndi anthu awo. N’chifukwa chake anthu akuchita zinthu zoipa kwambiri, monga kupululutsa mafuko a anthu, uchigawenga, ndi umbanda. Tsopano tiyeni tione zimene tingachite kuti tilimbane ndi makamu amphamvu a mizimu yoipa ndi kuigonjetsa.

Kodi Tingadziteteze Bwanji?

10, 11. Kodi Satana ndi angelo ake oipa tingalimbane nawo bwanji?

10 Sitingalimbane ndi Satana ndi angelo ake oipa mwa mphamvu kapena nzeru zathu zokha. Paulo akutilangiza kuti: “Pitirizani kupeza mphamvu mwa Ambuye ndi mwa nyonga zake zazikulu.” Tiyenera kuyang’ana kwa Mulungu kuti atiteteze. Paulo akuwonjezera kuti: “Valani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu kuti muthe kuchirimika polimbana ndi machenjera a Mdyerekezi . . . Nyamulani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu, kuti mukathe kulimbika m’tsiku loipa, ndipo mutachita zonse bwino lomwe, mukachirimike.”​—Aefeso 6:10, 11, 13.

11 Paulo kawiri konse akulimbikitsa Akhristu anzake kuvala “zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.” Mawu akuti “zonse” akusonyeza kuti, popanda kuikirapo mtima, sitingakwanitse kulimbana ndi ziwanda. Kodi zida zauzimu zimene Akhristu masiku ano akufunikira kuti alimbane ndi ziwanda n’ziti?

Kodi N’chiyani Chingatithandize ‘Kuchirimika’?

12. Kodi Akhristu angamangirire bwanji choonadi m’chiuno mwawo?

12 Paulo akufotokoza kuti: “Chirimikani, mutamangirira zolimba choonadi m’chiuno mwanu, mutavalanso choteteza pachifuwa cha chilungamo.” (Aefeso 6:14) Zida ziwiri zimene azitchula pano ndi lamba ndi choteteza pachifuwa. Msilikali ankafunikira kumanga kwambiri lamba wake kuti ateteze chiuno chake ndi kuti athe kunyamula lupanga lake lolemera. Chimodzimodzinso ifeyo. Tiyenera kudzimangirira kwambiri ndi choonadi cha m’Baibulo kuti tizichitsatira pa moyo wathu. Kodi ifeyo tili ndi ndandanda yowerengera Baibulo tsiku ndi tsiku? Kodi timaliwerenga banja lonse? Kodi tili ndi chizolowezi pabanja pathu chokambirana lemba la tsiku? Ndipo, kodi timawerenga ndi kudziwa mfundo zatsopano zofotokozedwa m’mabuku a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”? (Mateyo 24:45) Ngati timatero, ndiye kuti tikuyesetsa kutsatira malangizo a Paulo. Tilinso ndi mavidiyo ndi ma DVD amene tingapezemo malangizo a m’Malemba. Tikagwiritsitsa choonadi, chingatithandize kusankha zinthu mwanzeru ndi kupewa njira yolakwika.

13. Kodi mtima wathu wophiphiritsa tingauteteze bwanji?

13 Choteteza pachifuwa chimene msilikali ankavala chinkateteza mtima ndi ziwalo zina zofunika kwambiri. Mkhristu angatetezenso mtima wake wophiphiritsa, kapena kuti umunthu wake. Angachite zimenezi mwa kukonda chilungamo cha Mulungu ndi mwa kutsatira mfundo zolungama za Yehova. Choteteza pachifuwa chophiphiritsa chimatithandiza kuti tisamanyalanyaze Mawu a Mulungu. Tikayamba ‘kudana nacho choipa, ndi kukonda chokoma,’ timaletsa mapazi athu kuti asayende pa “njira iliyonse yoipa.”​—Amosi 5:15; Salmo 119:101.

14. Kodi ‘kuveka mapazi athu nsapato zokonzekera uthenga wabwino wa mtendere’ kumatanthauza chiyani?

14 Asilikali achiroma ankavala nsapato zolimba kwambiri kuti azitha kuyenda mtunda wautali pamisewu imene inkapita kulikonse mu ufumu wa Roma. Kodi mawu akuti “mapazi anu mutawaveka nsapato zokonzekera uthenga wabwino wa mtendere” amatanthauza chiyani kwa Akhristu? (Aefeso 6:15) Amatanthauza kuti ndife okonzeka kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu nthawi ina iliyonse. (Aroma 10:13-15) Tikamalimbikira kuchita utumiki wachikhristu, timatetezedwa ku “machenjera” a Satana.​—Aefeso 6:11.

15. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti chishango chachikulu cha chikhulupiriro n’chofunika kwambiri? (b) Kodi ‘mivi yoyaka moto’ imene ingafooketse chikhulupiriro chathu n’chiyani?

15 Paulo akupitiriza kuti: “Koposa zonse, nyamulani chishango chachikulu cha chikhulupiriro, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipitsitsayo.” (Aefeso 6:16) Popereka malangizo amenewa, iye akuyamba ndi mawu akuti “koposa zonse.” Mawu amenewa akusonyeza kuti chida chimenechi n’chofunika kwambiri. Chikhulupiriro chathu sichiyenera kufooka ngakhale pang’ono. Mofanana ndi chishango chachikulu, chikhulupiriro chathu chimatiteteza ku ‘mivi yoyaka moto’ ya Satana. Kodi mivi imeneyi ingaimire chiyani masiku ano? Imeneyi ingakhale mawu achipongwe, mabodza, ndi mawu ena osokeretsa amene adani athu ndi ampatuko amafalitsa poyesa kufooketsa chikhulupiriro chathu. “Mivi” imeneyi ingakhalenso ziyeso zofuna zinthu zakuthupi, zimene zingatitangwanitse ndi kugula katundu wambiri kapena kutilimbikitsa kupikisana ndi anthu ena amene atengeka ndi moyo wapamwamba. Mwina iwo akugula nyumba ndi galimoto zambambande kapena amadzionetsera ndi zovala zamakono ndi zodzikongoletsera zapamwamba. Kaya ena achite zotani, ife tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri moti n’kuzimitsa ‘mivi yoyaka moto’ imeneyi. Kodi tingachite chiyani kuti tikhalebe ndi chikhulupiriro cholimba?​—1 Petulo 3:3-5; 1 Yohane 2:15-17.

16. Kodi n’chiyani chingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu?

16 Tiyenera nthawi zonse kuchita phunziro la Baibulo laumwini ndi kupemphera ndi mtima wonse kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Tingapemphe Yehova kuti atipatse chikhulupiriro cholimba ndipo tiyenera kuchita zinthu zogwirizana ndi mapemphero athuwo. Mwachitsanzo, kodi mlungu ndi mlungu timakonzekera bwinobwino Phunziro la Nsanja ya Olonda kuti tikayankhepo? Pajatu chikhulupiriro chathu chimalimba tikamaphunzira Baibulo ndi mabuku amene amalifotokoza.​—Aheberi 10:38, 39; 11:6.

17. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ‘tilandire chisoti cholimba cha chipulumutso’?

17 Paulo akumaliza kufotokoza zida zauzimu ndi malangizo akuti: “Landirani chisoti cholimba cha chipulumutso, ndi lupanga la mzimu, ndilo mawu a Mulungu.” (Aefeso 6:17) Chisoti chinkateteza mutu ndi ubongo wa msilikali, zimene ankagwiritsa ntchito poganiza. Ifenso Akhristu, chiyembekezo chathu chimateteza maganizo athu. (1 Atesalonika 5:8) M’malo moganizira kwambiri za zinthu za m’dzikoli ndi chuma chake, tiziganizira kwambiri za chiyembekezo chimene Mulungu watipatsa, ngati mmene Yesu anachitira.​—Aheberi 12:2.

18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza kuwerenga Baibulo nthawi zonse?

18 Chida chomaliza chimene chingatiteteze ku mphamvu za Satana ndi ziwanda zake ndi mawu a Mulungu, kapena kuti uthenga wa m’Baibulo. Ichi n’chifukwa chinanso chimene sitiyenera kunyalanyaza kuwerenga Baibulo nthawi zonse. Tikadziwa bwino Mawu a Mulungu, timatetezeka ku mabodza a Satana ndi ziphunzitso zosokeretsa za ziwanda ndiponso ku mawu oipa otineneza amene ampatuko amafalitsa.

“Muzipemphera pa Chochitika Chilichonse”

19, 20. (a) Kodi n’chiyani chimene chidzachitikire Satana ndi ziwanda zake? (b) Kodi n’chiyani chingatilimbitse mwauzimu?

19 Satana ndi ziwanda zake atsala pang’ono kuchotsedwa limodzi ndi dziko loipali. Satana akudziwa kuti “wangotsala ndi kanthawi kochepa.” Iye ndi wokwiya ndipo akuchita nkhondo ndi anthu “osunga malamulo a Mulungu, ndi amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.” (Chivumbulutso 12:12, 17) M’pofunika kuti tilimbane ndi Satana ndi ziwanda zake.

20 Tikuthokoza kwambiri malangizo amenewa akuti tivale zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu. Pomaliza nkhani imeneyi, Paulo akutilangiza kuti: “Muzipemphera pa chochitika chilichonse mu mzimu, mwa mtundu uliwonse wa pemphero ndi pembedzero. Kuti muchite zimenezi, khalani maso mosalekeza ndi kuchita pembedzero m’malo mwa oyera onse.” (Aefeso 6:18) Pemphero lingatilimbitse mwauzimu ndi kutithandiza kukhala maso. Tiyeni timvere mawu a Paulo ndi kupitirizabe kupemphera, chifukwa tikatero tidzatha kulimbana ndi Satana ndi ziwanda zake.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi Satana ndi ziwanda zake anakhalako bwanji?

• Kodi Mdyerekezi mphamvu zake n’zotani?

• Kodi tingadziteteze bwanji kwa Satana ndi ziwanda zake?

• Kodi tingavale bwanji zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 26]

“Ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu”

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi mukuzidziwa zida 6 zankhondo yathu yauzimu?

[Zithunzi patsamba 29]

Kodi n’chifukwa chiyani kuchita zinthu izi kumatiteteza kwa Satana ndi ziwanda zake?