Kuwala N’kodabwitsa
Kuwala N’kodabwitsa
NGATI munayesapo kufunafuna njira mu mdima, mukudziwa mmene zimavutira kuti muipeze. Komatu, mungasangalale kwambiri mutaona kuwala. N’kutheka kuti nthawi ina munakumanapo ndi vuto limene mungaliyerekezere ndi kufunafuna njira mumdima. Ndiyeno m’kupita kwanthawi munaona kuwala, kutanthauza kuti munapeza njira yothetsera vutolo. Kuona kuwala mumdima n’kosangalatsa kwambiri mofanana ndi kupeza njira yothetsera vuto linalake.
M’nthawi ya atumwi, anthu ambiri anali mu mdima wauzimu. Polembera anthu omwe anasiya zikhulupiriro zawo zakale ndi kulowa Chikhristu, mtumwi Petulo anati: “[Mulungu] anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.” (1 Petulo 2:9) Iwo anaona kuti kusintha kumeneku kunali ngati kuchoka mu mdima wandiweyani n’kulowa m’kuwala. Tingakuyerekezerenso ndi munthu yemwe akukhala payekha ndipo alibe chiyembekezo chilichonse. Kenako iye akutengedwa ndi banja lina la mwanaalirenji.—Aefeso 2:1, 12.
“Unasiya Chikondi Chimene Unali Nacho Poyamba”
Akhristu oyambirira anapeza “choonadi,” chomwe ndi chikhulupiriro chenicheni chachikhristu. (Yohane 18:37) Iwo anaona kuwala kodabwitsa kwa choonadi ndipo anasintha kuchoka mu mdima wauzimu n’kulowa m’kuwala. Koma m’kupita kwanthawi, changu chomwe Akhristu ena anali nacho poyamba chinazilala. Mwachitsanzo, chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, mumpingo wa ku Efeso munali vuto lalikulu kwambiri. Ndipo Yesu Khristu woukitsidwayo anadziwa vutolo, ndipo anati: “Ndakupeza ndi mlandu uwu, unasiya chikondi chimene unali nacho poyamba. Choncho, kumbukira apo unali usanagwe, lapa ndi kuchita ntchito za poyamba.” (Chivumbulutso 2:4, 5) Akhristu a ku Efeso anafunikira kuyambanso kukonda Mulungu ndiponso choonadi.
Nanga bwanji ifeyo? Nafenso tikusangalala chifukwa taona kuwala kwa choonadi chosangalatsa cha Mawu a Mulungu. Ngakhale kuti timakonda choonadi, mavuto omwe anthu onse amakumana nawo angachepetse chikondi chimenechi. Ndipo kuwonjezera pa mavuto amenewa tingakhalenso ndi mavuto ena osautsa kwambiri a “m’masiku otsiriza.” Tikukhala m’dziko lomwe lili mu “nthawi yovuta.” Ndipo m’dzikoli muli anthu “odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika,” (2 Timoteyo 3:1, 2) Iwo angatifooketse ndipo chikondi chathu pa Yehova chingazilale.
Ngati tasiya chikondi chomwe tinali nacho poyamba, tifunikira ‘kukumbukira pamene tinali tisanagwe, ndipo tilape.’ Tifunikira kukhala anthu okonda zinthu zauzimu monga momwe tinalili poyamba. Kuwonjezera pamenepa, tiyenera kusamala kwambiri kuti chikondi chathu pa choonadi chisazilale. Chotero, ife tonse tifunikira kukhalabe osangalala ndi a maganizo abwino, ndipo tipitirize kukonda Mulungu ndi choonadi chake.
‘Choonadi Chomwe Chimatimasula’
Kuwala kwa choonadi cha m’Malemba n’kodabwitsa chifukwa choti Baibulo limayankha mafunso ofunika omwe aimitsa mitu anthu kwa zaka zambirimbiri. Ena a mafunso amenewa ndi awa: N’chifukwa chiyani tili ndi moyo? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? N’chifukwa chiyani zoipa zimachitika? Kodi munthu akamwalira amakhala ndi moyo kwinakwake? Yehova watidziwitsa choonadi chosangalatsa chonena za
ziphunzitso za m’Baibulo. Kodi sitingayamikire ndi mtima wonse? Tisayerekeze dala kunyalanyaza zinthu zimene taphunzira.Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Nsembe ya dipo ya Yesu yatimasula ku uchimo ndi imfa. Choonadi cha mtengo wapatalichi chatimasulanso kuti tikhale odziwa zinthu, ndiponso tikhale ndi chiyembekezo, mosiyana ndi dzikoli limene lili mu mdima. Kusinkhasinkha ndi kuyamikira zimene taphunzira kungatithandize kuti tizikonda kwambiri Yehova ndiponso Mawu ake.
M’kalata yopita kwa Akhristu a ku Tesalonika, mtumwi Paulo anati: “Pamene munalandira mawu a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu ayi, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu. Mawu amenewa akugwiranso ntchito mwa inu okhulupirira.” (1 Atesalonika 2:13) Anthu a ku Tesalonika anamva ndi ‘kulandira mawu a Mulungu mwachimwemwe.’ Iwo sanalinso “mu mdima.” Koma anakhala “ana a kuwala.” (1 Atesalonika 1:4-7; 5:4, 5) Akhristu amenewa anadziwa kuti Yehova ndiye Mlengi ndipo ndi wamphamvuyonse, wanzeru, wachikondi, ndiponso wachifundo. Mofanana ndi otsatira Khristu ena, Akhristu a ku Tesalonika anaphunzira kuti Yehova anakonza zoti machimo awo afafanizidwe ndi nsembe ya dipo ya Mwana wake, Yesu Khristu.—Machitidwe 3:19-21.
Ngakhale kuti Atesalonika sanadziwe mfundo zonse za choonadi cha m’Baibulo, iwo ankadziwa kumene akanazipeza. Malemba ouziridwa angathandize munthu wa Mulungu kukhala “woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteyo 3:16, 17) Akhristu ku Tesalonika anapitiriza kuphunzira ndipo nthawi ndi nthawi ankaona kuti kuwala kochokera kwa Mulungu n’kodabwitsadi. M’pake kuti iwo ankasangalala nthawi zonse. (1 Atesalonika 5:16) Ifenso timachita chimodzimodzi.
Kuunika kwa Panjira Pathu
Potchula chifukwa chake kuwala kuli kodabwitsa, wamasalmo anaimba kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105) Mawu a Mulungu akamatitsogolera timasankha bwino zinthu zoti tichite ndipo timakhala ndi moyo wosangalatsa. Tisakhale ngati chombo chomwe changotengedwa ndi mphepo. Kudziwa choonadi ndi kuchigwiritsa ntchito kumatiteteza kuti tisakhale “otengekatengeka ngati kuti tikukankhidwa ndi mafunde, ndiponso otengeka uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso.”—Aefeso 4:14.
Baibulo limati: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” Ndipo limapitiriza kuti: “Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti am’thandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.” (Salmo 146:3, 5) Ndipo kudalira Yehova kumatithandiza kuthetsa mantha ndiponso nkhawa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Timapindula kwambiri tikamatsogoleredwa ndi kuwala kwa Mawu a Mulungu.
Walani Monga Zounikira M’dziko
Chifukwa china chimene kuwala kwa Mawu a Mulungu kulili kodabwitsa n’chakuti, kumathandiza anthu kuti akhale ndi mwayi wochita Mateyo 28:18-20.
nawo ntchito yofunika kwambiri. Yesu analangiza otsatira ake kuti: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu. Ndipo dziwani ichi! Ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.” Iye asananene lamuloli anati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.”—Tangoganizirani kuti Yesu ndiye akuthandiza Akhristu oona pantchito yawo yolalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo kwa anthu amitundu yonse. Chifukwatu iye analonjeza otsatira ake kuti adzakhala nawo. Yesuyo akuwathandizadi kutumikira pamene “akuonetsa kuwala kwawo” mwa njira imeneyi ndiponso mwa “ntchito zabwino.” (Mateyo 5:14-16) Angelo nawonso akuchita nawo ntchito yolengezayi. (Chivumbulutso 14:6) Nanga bwanji Yehova Mulungu? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathirira, koma Mulungu ndiye anakulitsa.” Ulidi mwayi wapadera kukhala pakati pa anthu omwe ndi “antchito anzake a Mulungu.”—1 Akorinto 3:6, 9.
Taganiziranso madalitso omwe timakhala nawo tikamachita ntchito yomwe Mulungu watipatsayi. Palibe chomwe tingayerekezere ndi mwayi womwe Mulungu watipatsa woti ‘tiziwala monga zounikira m’dzikoli.’ Tikamasonyeza kuwala kwa Mawu a Mulungu polankhula, ndiponso pochita zinthu, timathandizadi anthu oona mtima. (Afilipi 2:15) Ndipo tingasangalale pamene tikulalikira ndiponso kuphunzitsa anthu mwachangu. Zingakhale choncho chifukwa chakuti ‘Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito zathu ndi chikondi chimene tinachisonyeza pa dzina lake.’—Aheberi 6:10.
‘Gulani Mankhwala Opaka M’maso’
Mu uthenga umene analembera mpingo wa m’nthawi ya atumwi wa ku Laodikaya, Yesu anati: ‘Gulani kwa ine . . . mankhwala opaka m’maso anu kuti muone. Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga.’ (Chivumbulutso 3:18, 19) Mankhwala “opaka m’maso,” kutanthauza ziphunzitso ndi malangizo a Yesu, angathetsedi khungu lauzimu. Ngati tikufuna kuti tiziona zinthu zomwe zikutichitikira ndiponso tsogolo lathu m’njira yauzimu, tiyenera kulandira malangizo a Yesu ndi kuwatsatira. Tiyeneranso kutsatira malangizo omwe ali m’Baibulo lonse. Tiyenera kukhala ndi maganizo ofanana ndi a Khristu ndiponso kutsatira chitsanzo chake. (Afilipi 2:5; 1 Petulo 2:21) Koma mankhwala a Yesuwa si aulere ayi. Iye anati: ‘Muwagule kwa ine.’ Mtengo wake umaphatikizapo nthawi ndi khama lathu.
Tikachoka mu mdima n’kulowa m’chipinda chowala, zingatenge kanthawi kuti maso athu ayambe kuona bwinobwino. Mofananamo, zimatenga nthawi kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kuyamba kuona kuwala kwa choonadi. Pamafunika nthawi kuti tisinkhesinkhe pa zinthu zomwe tikuphunzira ndiponso kuti tione mmene choonadi chilili chamtengo wapatali. Koma mtengo wake si wokwera monyanyira. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti kuwalaku n’kodabwitsa kapena kuti n’kwa mtengo wapatali.
[Chithunzi patsamba 14]
‘Gulani kwa ine . . . mankhwala opaka m’maso anu kuti muone’