Mmene Hana Anapezera Mtendere
Mmene Hana Anapezera Mtendere
MAYI wina wokhulupirika akupemphera mokweza mawu potamanda Yehova. Iye akuona kuti Mulungu wamuutsa kuchoka mu fumbi, kutanthauza kuti wam’chotsera chisoni n’kumupatsa chimwemwe.
Mayiyu dzina lake ndi Hana. Kodi n’chiyani chinam’thandiza kuti afike pokhala wachimwemwe? Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene iyeyu anakumana nazo? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tikambirane nkhani ya mayiyu.
Banja Lamavuto
Hana anali mmodzi wa akazi awiri a Elikana, Mlevi yemwe ankakhala ku dera la Efraimu. (1 Samueli 1:1, 2a; 1 Mbiri 6:33, 34) Ngakhale kuti mitala siinali mbali ya cholinga cha Mulungu polenga anthu, m’Chilamulo cha Mose inali yololeka ndipo munali malamulo okhudza mitala. Banja la Elikana linkalambira Yehova, komabe nthawi zambiri pa mitala sipankalephera kukhala mikangano. Ndipotu izi n’zimene zinkachitika m’banja la Elikana.
Hana anali wosabereka, koma mkazi wina wa Elikana, dzina lake Penina, anali ndi ana angapo. Motero, Penina ankam’chitira Hana zamtopola.—1 Samueli 1:2b.
Akazi a ku Isiraeli ankaona kuti kusabereka ndi chinthu chochititsa manyazi kwambiri. Ndipo ankaonanso kuti kukhala mkazi wosabereka kumasonyeza kuti Mulungu samakuwerengera. Koma Baibulo silinena chilichonse chosonyeza kuti Hana sankabereka chifukwa choti Mulungu sankamukonda. M’malo molimbikitsa mnzake wosaberekayu, Penina anapezerapo mwayi wom’chitira zamtopola kuti aziwawidwa mtima.
Maulendo Opita ku Kachisi wa Yehova
Ngakhale kuti m’banja la Elikana munali kusamvana kotere, chaka n’chaka banjalo linkapita ku kachisi wa Yehova ku Silo. * Ulendowu unali wa makilomita 60, kupita n’kubwera ndipo zikuoneka kuti ankayenda wapansi. Hana ayenera kuti ankavutika kwambiri panthawi imeneyi chifukwa choti Penina ndi ana ake ankapatsidwa magawo angapo a nsembe yoyamika, pamene Hanayo ankapatsidwa gawo limodzi lokha. Pamenepa, Penina ankapezerapo mwayi wom’pweteketsa mtima Hana, kuti azidandaula poganiza kuti Yehova ndiye “anatseka mimba yake.” Zimenezi zinali kuchitika chaka n’chaka, moti Hana anafika pomangolira n’kumakana kudya. Motero maulendo osangalatsawa, kwa Hana anali opweteketsa mtima kwambiri. Komabe, Hana sanasiye kuyenda maulendo amenewa, opita ku kachisi wa Yehova.—1 Samueli 1:3-7.
Kodi mukuona chitsanzo chabwino chimene Hana anatipatsa? Kodi mukakhumudwa mumatani? Kodi mumadzipatula pakati pa Akhristu anzanu? Hana sanatero ayi. Iye anali ndi chizolowezi chopezeka pakati pa olambira a Yehova. Ifenso tizitero ngakhale tikakhala m’mavuto.—Salmo 26:12; 122:1; Miyambo 18:1; Aheberi 10:24, 25.
Elikana anayesetsa kum’thandiza Hana ndi kum’limbikitsa kuti amasuke kunena zakukhosi kwake. Elikana anafunsa kuti: “Hana, umaliriranji? Ndipo umakaniranji kudya? Ndipo mtima wako 1 Samueli 1:8) N’kutheka kuti Elikana sankadziwa zamtopola zimene Penina ankachitira Hana, ndipo Hanayo mwina ankangopirira osanena kanthu. Mulimonsemo, Hana anasonyeza kuti anali wokhwima mwauzimu chifukwa anafuna mtendere posiya nkhaniyi m’manja mwa Yehova popemphera.
uwawa ninji? Ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?” (Hana Analumbira
Anthu ankadya nawo nsembe zoyamika ku kachisi wa Yehova. Hana, atachoka ku malo odyera anapemphera kwa Mulungu. (1 Samueli 1:9, 10) Iye anati: “Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.”—1 Samueli 1:11.
Hana ananena pemphero lachindunji. Iye anapempha kuti akufuna mwana wamwamuna yemwe adzam’pereke kwa Yehova kuti akhale Mnazara kwa moyo wake wonse. (Numeri 6:1-5) Lumbiro lotereli linayenera kuvomerezedwa ndi mwamuna wake, ndipo zimene Elikana anachita pambuyo pake zikusonyeza kuti anavomereza lonjezo la mkazi wake wokondedwayu.—Numeri 30:6-8.
Eli, mkulu wa ansembe, anaganiza kuti Hana waledzera chifukwa cha mmene anali kupempherera. Milomo ya Hana inali kunjenjemera, koma Eli sankamva mawu aliwonse, chifukwa choti iye anali kupemphera chamumtima. Anali kupemphera mokhudzidwa mtima kwambiri. (1 Samueli 1:12-14) Ndiye tangoganizirani mmene Hana anamvera Eli atamudzudzula kuti waledzera! Komatu iye anamuyankha mwaulemu mkulu wa ansembeyo. Eli atazindikira kuti Hana anali kupemphera ‘mwa kuchuluka kwa kudandaula kwake ndi kuvutika kwake,’ iye anati: “Mulungu wa Israyeli akupatse chopempha chako.” (1 Samueli 1:15-17) Zitatero, Hana anayambanso kudya, ndipo “nkhope yake siinakhalanso yachisoni.”—1 Samueli 1:18.
Kodi tingaphunzire chiyani pankhani imeneyi? Tikamapemphera kwa Yehova chifukwa choti tili ndi nkhawa, tizimuuza mmene tikumvera ndipo tizim’pempha mokhudzidwa mtima. Tikayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe poyesa kuthetsa vutolo, tizisiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Palibe njira ina yabwino kuposa imeneyi.—Miyambo 3:5, 6.
Atumiki a Yehova akapemphera mokhudzidwa mtima nthawi zambiri amapeza mtendere wa m’maganizo monga anachitira Hana. Pankhani ya kupemphera Paulo anati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Tikasenza Yehova nkhawa zathu, tiyenera kum’lola kuti atithandize pa nkhawazo. Kenaka, monga anachitira Hana, tisamadenso nkhawa.—Salmo 55:22.
Mwana Yemwe Anaperekedwa kwa Yehova
Kenaka Mulungu anam’kumbukira Hana ndipo anakhala ndi pakati n’kubereka mwana wamwamuna. (1 Samueli 1:19, 20) Iyi ndi nkhani imodzi mwa nkhani zochepa m’Baibulo zosonyeza Mulungu akuthandiza kuti mtumiki wake wam’tsogolo abadwe. Mwanayo, dzina lake Samueli, anadzakhala mneneri wa Yehova ndipo anadzakhala ndi mbali yofunika kwambiri pokhazikitsa mafumu a Isiraeli.
N’zosakayikitsa kuti Hana anayamba kuphunzitsa Samueli za Yehova adakali khanda. Koma kodi anaiwala lumbiro lake lija? Ayi ndithu, sanaiwale ngakhale pang’ono. Iye anati: “Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire.” Samueli ataleka kuyamwa, mwina ali ndi zaka zitatu kapena kuposerapo, Hana anapita naye ku kachisi wa Yehova kuti azikakhala komweko, monga analumbirira.—1 Samueli 1:21-24; 2 Mbiri 31:16.
Atapereka nsembe kwa Yehova, Hana ndi mwamuna wake anakam’siya Samueli m’manja mwa Eli. N’zoonekeratu kuti Hana anali atakagwira padzanja kamwana kakeka pamene ankamuuza 1 Samueli 1:25-28; 2:11.
Eli kuti: “Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova. Ndinam’pempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye; chifukwa chake inenso ndinam’pereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova.” Motero, umu ndi mmene Samueli anayambira moyo wotumikira Mulungu.—Koma Hana ankamukumbukirabe Samueli. Malemba amati: “Amake ankam’sokera mwinjiro waung’ono, nabwera nawo kwa iye chaka ndi chaka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wake kudzapereka nsembe ya pachaka.” (1 Samueli 2:19) N’zoonekeratu kuti Hana ankam’pempherera Samueli. Ndipo n’zosakayikitsa kuti chaka chilichonse akapita ku kachisiko, ankamulimbikitsa kuti akhalebe wokhulupirika pochita utumiki wake kwa Mulungu.
Panthawi ina yotere, Eli anadalitsa makolo a Samueli ndipo anauza Elikana kuti: “Yehova akupatse mbewu ndi mkazi uyu m’malo mwa iye amene munam’pempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwawo. Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana aamuna atatu, ndi ana aakazi awiri.” Mogwirizana ndi mawu amenewo, Hana ndi Elikana anadalitsidwa pobereka ana ena atatu aamuna ndi awiri aakazi.—1 Samueli 2:20, 21.
Elikana ndi Hana anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo achikhristu. Tingati makolo ambiri apereka kwa Yehova ana awo aamuna ndi aakazi, powalimbikitsa kupita kwina kuti akachite utumiki wa nthawi zonse. Tikuyamikira makolo achikondiwa chifukwa chopereka ana awowa kwa Yehova ndipo iye adzawadalitsa.
Pemphero la Hana Lachisangalalo
Hana yemwe anali wosabereka uja, tsopano anasangalala kwambiri. Kawirikawiri Malemba satchulapo za mapemphero onenedwa ndi akazi. Koma tikudziwa mapemphero awiri a Hana, opezeka m’Malemba. Koyambako ankapemphera atasokonezeka maganizo chifukwa cha vuto lake, ndipo kachiwiriko ankapemphera posangalala ndi kuthokoza Yehova. Hana anayamba pempherolo ponena kuti: “Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova.” Iye anasangalala n’kunena kuti “inde chumba chabala” ana, ndipo anatamanda Yehova ponena kuti Iye ‘amakuzanso, n’kuutsa waumphawi m’fumbi.’ N’zoonadi, Iye ‘amanyamula wosowa kuchoka padzala.’—1 Samueli 2:1-10.
Nkhani youziridwa ya Hana imasonyeza kuti kupanda ungwiro kapena khalidwe la mtopola la anthu ena lingatipweteke mtima kwambiri. Komabe, tisalole ziyeso zotere kutilepheretsa kutumikira Yehova mwachimwemwe. Iye ndi Wakumva pemphero, amene amathandiza anthu ake okhulupirika akam’dandaulira. Amawalanditsa m’mavuto ndi kuwapatsa mtendere wochuluka ndiponso madalitso osiyanasiyana.—Salmo 22:23-26; 34:6-8; 65:2.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Baibulo limatcha likulu la kulambira koonali kuti ndi “kachisi” wa Yehova. Komabe, panthawiyi likasa la chipangano linkakhala mu chihema. Kachisi weniweni woyamba anamangidwa mu ulamuliro wa Mfumu Solomo.—1 Samueli 1:9; 2 Samueli 7:2, 6; 1 Mafumu 7:51; 8:3, 4.
[Chithunzi patsamba 17]
Hana anapereka Samueli kwa Yehova