Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochita za Angelo Zimakhudza Anthu

Zochita za Angelo Zimakhudza Anthu

Zochita za Angelo Zimakhudza Anthu

“Pambuyo pa izi, ndinaona mngelo wina akutsika kumwamba wokhala ndi ulamuliro waukulu . . . Iye anafuula ndi mawu amphamvu, amvekere: ‘Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa!’”​—CHIVUMBULUTSO 18:1, 2.

1, 2. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amagwiritsa ntchito angelo pochita chifuniro chake?

PAMENE mtumwi Yohane anali m’ndende pachilumba cha Patimo, anaona masomphenya olosera za m’tsogolo. Mtumwi wokalamba ameneyu anaona zinthu zochititsa chidwi pamene “mwa mzimu” anafika “m’tsiku la Ambuye.” Tsikulo linayamba Yesu Khristu atayamba kulamulira mu 1914 ndipo lidzafika mpaka kumapeto kwa Ulamuliro wake wa Zaka 1,000.​—Chivumbulutso 1:10.

2 Yehova Mulungu sanapereke yekha chivumbulutso chimenechi kwa Yohane, koma anachipereka kudzera mwa ena. Lemba la Chivumbulutso 1:1 limati: “Chivumbulutso choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anam’patsa, kuti aonetse akapolo ake zimene ziyenera kuchitika posachedwa. Yesuyo anatumiza mngelo wake kudzachipereka mwa zizindikiro kwa kapolo wake Yohane.” Yehova, kudzera mwa Yesu, anagwiritsa ntchito mngelo kuti auze Yohane zinthu zosangalatsa zimene zidzachitike “m’tsiku la Ambuye.” Nthawi ina, Yohane anaonanso “mngelo wina akutsika kumwamba wokhala ndi ulamuliro waukulu.” Kodi mngelo ameneyo anali ndi uthenga wotani? “Iye anafuula ndi mawu amphamvu, amvekere: ‘Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa!’” (Chivumbulutso 18:1, 2) Mngelo wamphamvu ameneyu anali ndi mwayi wapadera wolengeza za kugwa kwa Babulo Wamkulu, amene ndi ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga. Choncho, sitingakayikire kuti Yehova amagwiritsa ntchito kwambiri angelo pochita chifuniro chake. Tikambirana mwatsatanetsatane ntchito zimene angelo amachita pokwaniritsa cholinga cha Mulungu ndi mmene zochita zawo zimatikhudzira. Koma tisanatero, tiyeni tione kuti kodi angelo amenewa anakhalako bwanji.

Kodi Angelo Anakhalako Bwanji?

3. Kodi anthu ambiri ali ndi maganizo olakwika otani a angelo?

3 Anthu mamiliyoni ambiri masiku ano amakhulupirira kuti angelo aliko. Koma zina zimene amadziwa za angelowo n’zolakwika. Mwachitsanzo, anthu ena opembedza amakhulupirira kuti m’bale wawo kapena mnzawo akamwalira, amapita kumwamba kwa Mulungu ndipo amakakhala mngelo. Kodi izi n’zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa za kulengedwa kwa angelo, kukhalapo kwawo, ndi cholinga chimene analengedwera?

4. Kodi Malemba amatiuza kuti angelo anakhalako bwanji?

4 Mngelo amene ali ndi mphamvu ndi udindo waukulu pa onse ndi Mikayeli, mkulu wa angelo. (Yuda 9) Mngelo ameneyu si winanso ayi koma Yesu Khristu. (1 Atesalonika 4:16) Kalekale pamene Yehova anaganiza zoti akhale Mlengi, anayamba ndi kulenga mngelo mmodzi, Mwana wake. (Chivumbulutso 3:14) Kenako, Yehova analenga angelo ena onse kudzera mwa Mwana wake woyamba kubadwa ameneyo. (Akolose 1:15-17) Yehova anatcha angelowo ana ake pamene anafunsa Yobu kuti: “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira. . . . Kapena anaika ndani mwala wake wa pangondya, muja nyenyezi za m’mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?” (Yobu 38:4, 6, 7) Apa tikutha kuona kuti angelo anachita kulengedwa ndi Mulungu, ndipo anakhalako kalekale anthu asanakhaleko.

5. Kodi angelo ali magulu angati, ndipo magulu akewo ndi ati?

5 Lemba la 1 Akorinto 14:33 limati: “Mulungu, si Mulungu wa chisokonezo, koma wa mtendere.” Choncho, Yehova anaika ana ake auzimu m’magulu atatu: (1) aserafi, amene amatumikira ku mpando wachifumu wa Mulungu, amalengeza chiyero chake, ndipo amaonetsetsa kuti anthu ake akhale oyera mwauzimu; (2) akerubi, amene amakweza ulamuliro wa Yehova; ndiponso (3) angelo ena, amenenso amachita chifuniro chake. (Salmo 103:20; Yesaya 6:1-3; Ezekieli 10:3-5; Danieli 7:10) Kodi zochita za angelo zimakhudza anthufe motani?​—Chivumbulutso 5:11.

Kodi Angelo Amagwira Ntchito Yotani?

6. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito akerubi kuchita chiyani m’munda wa Edene?

6 M’Baibulo angelo amatchulidwa koyamba pa Genesis 3:24. Pamenepo pamati: “[Yehova] anamuingitsa munthuyo; nakhazika Makerubi cha kum’mawa kwake kwa munda wa Edene, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.” Akerubiwo analetsa Adamu ndi Hava kuti asalowenso m’mundawo. Zimenezi zinachitika pasanapite nthawi yaitali anthu atalengedwa. Kodi angelo akhala akugwira ntchito yotani kuchokera nthawi imeneyo?

7. Kodi tanthauzo la liwu lakuti “mngelo” m’Chiheberi ndi m’Chigiriki likutiuza chiyani za ntchito ina ya angelo?

7 M’Baibulo angelo amatchulidwa pafupifupi maulendo 400. Liwu lachiheberi ndi lachigiriki loti “mngelo” lingamasuliridwe kuti “mthenga.” Choncho angelo akhala akupereka kwa anthu mauthenga ochokera kwa Mulungu. Monga taonera m’ndime ziwiri zoyambirira, Yehova anagwiritsa ntchito mngelo kuti apereke uthenga wake kwa mtumwi Yohane.

8, 9. (a) Kodi Manowa ndi mkazi wake anamva bwanji mngelo atawafikira? (b) Kodi makolo angaphunzire chiyani pa zimene Manowa anachita mngelo wa Mulungu atam’fikira?

8 Angelo amathandizanso ndi kulimbikitsa atumiki a Mulungu padziko lapansi. Mwachitsanzo, panthawi ya Oweruza mu Isiraeli, Manowa ndi mkazi wake wosabereka ankafuna mwana kwambiri. Yehova anatuma mngelo wake kuti akauze mkazi wa Manowa zoti akhala ndi mwana. Nkhaniyo imati: “Taona udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israyeli m’dzanja la Afilisti.”​—Oweruza 13:1-5.

9 Patapita nthawi, mkazi wa Manowa anabala mwana wamwamuna, dzina lake Samsoni, amene anakhala wotchuka m’nkhani za m’Baibulo. (Oweruza 13:24) Mwanayo asanabadwe, Manowa anapempha kuti mngeloyo abwerenso kudzawalangiza za mmene angamulerere. Manowa anafunsa kuti: “Makhalidwe ake a mwanayo ndi machitidwe ake adzatani?” Mngelo wa Yehova anabwereza malangizo amene anauza mkazi wa Manowa. (Oweruza 13:6-14) Manowa ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri. Koma masiku ano, angelo safikira anthu ngati mmene ankachitira kale. Ngakhale zili choncho, makolo mofanana ndi Manowa, atha kupempha Yehova malangizo olerera ana awo.​—Aefeso 6:4.

10, 11. (a) Kodi Elisa komanso mnyamata wake anatani ataona gulu lankhondo la ku Suriya? (b) Kodi kuganizira zimene zinachitikazi kungatithandize bwanji?

10 Chitsanzo china chakuti angelo amathandiza anthu ndi zimene zinachitika pa nthawi ya mneneri Elisa. Iye ankakhala ku mzinda wa ku Isiraeli wotchedwa Dotana. Tsiku lina, mnyamata wa Elisa atadzuka m’mawa kwambiri n’kuyang’ana panja, anaona kuti mzindawo unali utazingidwa ndi akavalo ndi magaleta ankhondo. Mfumu ya ku Suriya inali itatumiza gulu lankhondo lalikulu kuti ligwire Elisa. Kodi mnyamata wa Elisa ataona zimenezi anatani? Anagwidwa ndi mantha aakulu n’kufuula kuti: “Kalanga ine, mbuye wanga! tichitenji?” Anali atatheratu nzeru. Koma Elisa anayankha kuti: “Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” Kodi pamenepa anatanthauzanji?​—2 Mafumu 6:11-16.

11 Elisa anadziwa kuti panali gulu la angelo loti liwathandize. Koma mnyamata wake sanadziwe chifukwa sanaone chilichonse. Choncho “Elisa anapemphera, nati, Yehova, mum’tsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anam’tsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akum’zinga Elisa.” (2 Mafumu 6:17) Mnyamatayo tsopano anaona gulu la angelolo. Ifenso titha kuona ndi maso auzimu kuti angelo, motsogozedwa ndi Yehova ndi Khristu, amathandiza ndi kuteteza anthu a Yehova.

Angelo Anathandiza Anthu Nthawi ya Khristu

12. Kodi Mariya analimbikitsidwa bwanji ndi mngelo Gabiriele?

12 Tiyeni tione mmene mngelo Gabiriele analimbikitsira namwali wachiyuda Mariya asanamuuze uthenga wakuti: “Udzakhala ndi pathupi nudzabereka mwana wamwamuna, ndipo udzam’patse dzina lakuti Yesu.” Uthengawo unali wodabwitsa. N’chifukwa chake, mngelo wotumidwa ndi Mulunguyo, anamuuza kuti: “Usaope Mariya, pakuti Mulungu wakukomera mtima.” (Luka 1:26, 27, 30, 31) Mawu amenewa ayenera kuti analimbikitsadi Mariya n’kumutsimikizira kuti anali wokondedwa ndi Mulungu.

13. Kodi angelo anam’thandiza bwanji Yesu?

13 Chitsanzo chinanso chosonyeza kuti angelo amathandiza anthu ndi zimene zinachitika kwa Yesu m’chipululu. Iye atakana katatu ziyeso za Satana, angelo anam’thandiza. Nkhaniyo imatiuza kuti pamapeto pa ziyeso zimenezo, “Mdyerekezi uja anamusiya, ndiyeno kunabwera angelo ndi kuyamba kum’tumikira.” (Mateyo 4:1-11) Zofanana ndi zimenezi zinachitika usiku woti Yesu mawa lake amwalira. Iye ali ndi mtima wachisoni, anagwada n’kupemphera kuti: “‘Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni chikho ichi. Komatu chifuniro chanu chichitike, osati changa.’ Pamenepo mngelo wochokera kumwamba anaonekera kwa iye ndi kumulimbikitsa.” (Luka 22:42, 43) Nanga angelo amatithandiza bwanji masiku ano?

Angelo Amathandiza Anthu Masiku Ano

14. Kodi Mboni za Yehova zapirira chizunzo m’mayiko ati masiku ano, ndipo zotsatira zake n’zotani?

14 Tikayang’ana mbiri yamakono ya ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova, kodi sitiona umboni wakuti angelo akuthandizapo? Mwachitsanzo, anthu a Yehova anapirira chizunzo cha boma la chipani cha Nazi ku Germany ndi kumadzulo kwa Ulaya, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse isanayambe ndiponso ili m’kati. (1939-45). M’maboma ankhanza achifasizimu a m’mayiko achikatolika a Italy, Spain, ndi Portugal, anapirira chizunzo chimene chinatenga nthawi yotalikirapo. Ndiponso anapirira chizunzo kwa zaka zambiri ku Soviet Union ndi kumayiko amene ankalamulidwa ndi dzikolo. Tisaiwalenso chizunzo chimene Mboni zapirira m’mayiko ena a mu Africa. * Posachedwapa, atumiki a Yehova azunzidwa mwankhanza m’dziko la Georgia. Satana wachita zonse zomwe angathe kuti aletse ntchito ya Mboni za Yehova. Koma kutengera gulu lonse, iwo apirira zonsezi ndipo gululo lakula. Mwa zina, zimenezi zatheka chifuwa chakuti angelo akuwateteza.​—Salmo 34:7; Danieli 3:28; 6:22.

15, 16. Kodi Mboni za Yehova zimathandizidwa bwanji ndi angelo pantchito yawo yolalikira padziko lonse?

15 Mboni za Yehova zimaona kuti ntchito yawo yopatsidwa ndi Mulungu ndi yofunika kwambiri. Ntchito imeneyi ndi yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse ndi kupanga ophunzira mwa kuphunzitsa anthu achidwi choonadi cha m’Baibulo. (Mateyo 28:19, 20) Koma Mbonizo zimadziwa kuti sizingachite ntchito imeneyi popanda kuthandizidwa ndi angelo. Choncho, zimalimbikitsidwa nthawi zonse ndi zimene lemba la Chivumbulutso 14:6, 7 limanena. Lembali limati: “[Ine Yohane] ndinaona mngelo winanso akuuluka mu mlengalenga chapafupi. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa okhala padziko lapansi, ndi ku dziko lililonse, fuko, lilime, ndi mtundu uliwonse. Mofuula anali kunena kuti: ‘Opani Mulungu ndi kum’patsa ulemerero, chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika. Chotero lambirani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.’”

16 Mawu amenewa akusonyeza kuti angelo akuthandiza ndi kutsogolera ntchito yaikulu imeneyi yolalikira padziko lonse imene Mboni za Yehova zikuchita. Yehova akugwiritsa ntchito angelo ake kuti atsogolere anthu amtima wabwino kwa Mboni zake. Ndiponso angelo atsogolera Mboni kuti zipeze anthu oyenerera. Ichi ndi chifukwa chake nthawi zambiri wa Mboni za Yehova amakumana ndi munthu panthawi imene munthuyo ali pa mavuto ndipo akufunikira thandizo lauzimu. Zimenezi zimachitika kawirikawiri moti sizingangokhala zochitika mwamwayi.

Angelo Adzagwira Ntchito Yofuna Chamuna Patsogolopa

17. Kodi Aasuri zinawayendera bwanji mngelo mmodzi atawaukira?

17 Kuwonjezera pa kukhala amithenga ndi othandiza anthu a Yehova, angelo alinso ndi ntchito ina. Kale, Mulungu anawagwiritsa ntchito kupereka chilango. Mwachitsanzo, zaka za m’ma 700 B.C.E., mzinda wa Yerusalemu unazingidwa ndi gulu lalikulu la asilikali a ku Asuri. Kodi Yehova anatani? Anati: “Ndidzatchinjiriza mudzi uno kuupulumutsa, chifukwa cha ine mwini, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.” Baibulo limatiuza zimene zinachitika kuti: “Kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m’misasa ya Aasuri zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo.” (2 Mafumu 19:34, 35) Magulu a asilikali angachuluke bwanji, sangaime kwa mngelo mmodzi yekha.

18, 19. Kodi angelo adzagwira ntchito yotani patsogolopa, ndipo ntchitoyo idzakhudza bwanji anthu?

18 Patsogolopa, Mulungu adzagwiritsa ntchito angelo kupereka chilango kwa anthu. Nthawi imeneyo, Yesu adzabwera “ndi angelo ake amphamvu m’moto wa lawilawi.” Cholinga chawo chidzakhala ‘chobwezera chilango kwa osadziwa Mulungu ndi kwa osamvera uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.’ (2 Atesalonika 1:7, 8) Kodi zimenezi zidzawakhudza bwanji anthu? Anthu amene amakana uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene ukulalikidwa pa dziko lonse adzawonongedwa. Amene ‘adzabisike tsiku la mkwiyo wa Yehova’ n’kupulumuka ndi okhawo amene amafuna Yehova, chilungamo, ndi chifatso.​—Zefaniya 2:3.

19 Tikuthokoza kuti Yehova akugwiritsa ntchito angelo ake amphamvu pothandiza ndi kulimbikitsa anthu amene amam’lambira pa dziko. Kumvetsa ntchito imene angelo amachita pokwaniritsa cholinga cha Mulungu kumatilimbikitsa kwambiri. Zili choncho chifukwa chakuti tiyenera kudziteteza kwa angelo ena amene anapandukira Yehova ndipo akutsogoleredwa ndi Satana. M’nkhani yotsatira tidzakambirana zimene Akhristu oona angachite kuti adziteteze ku mphamvu za Satana Mdyerekezi ndi ziwanda zake.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri za zizunzo zimenezi, onani mabuku akuti Mboni za Yehova m’Malawi​—Nkhani ya Kukhulupirika Kwawo, Mboni za Yehova m’Mozambique​—Mbiri ya Kusunga Umphumphu, Mboni za Yehova M’Zambia​—Nkhani Yonena za Mphamvu ya Chikhulupiriro, Yearbook of Jehovah’s Witnesses ya 1983 (Angola), 1972 (Czechoslovakia), 2000 (Czech Republic), 1992 (Ethiopia), 1974 ndi 1999 (Germany), 1982 (Italy), 2004 (Moldova), 1994 (Poland), 1983 (Portugal), 1978 (Spain), ndi 2002 (Ukraine).

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi angelo anakhalako bwanji?

• Kodi angelo ankagwira ntchito yotani m’nthawi za m’Baibulo?

• Kodi lemba la Chivumbulutso 14:6, 7 limatiuza chiyani za ntchito ya angelo lerolino?

• Kodi angelo adzagwira ntchito yotani patsogolopa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 22]

Manowa ndi mkazi wake analimbikitsidwa ndi mngelo

[Chithunzi patsamba 23]

“Okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo”