Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Okhulupirika kwa Khristu ndi kwa Kapolo Wake

Khalani Okhulupirika kwa Khristu ndi kwa Kapolo Wake

Khalani Okhulupirika kwa Khristu ndi kwa Kapolo Wake

“Mbuye wake . . . adzamuika kuyang’anira zinthu zake zonse.”​—MATEYO 24:45-47.

1, 2. (a) Kodi Malemba amati Mtsogoleri wathu ndani? (b) N’chiyani chimasonyeza kuti Khristu akutsogolera mpingo wachikhristu?

“MUSATCHEDWE ‘atsogoleri,’ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.” (Mateyo 23:10) Ponena mawu amenewa, Yesu anatsindika kwa otsatira ake kuti palibe aliyense padziko lapansi amene adzakhale mtsogoleri wawo. Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi yekha kumwamba, Yesu Khristu. Yesu anachita kuikidwa ndi Mulungu kuti akhale mtsogoleri. Yehova “anamuukitsa kwa akufa . . . namuika mutu wa zinthu zonse kaamba ka mpingo, umene ndi thupi lake.”​—Aefeso 1:20-23.

2 Popeza Khristu ndi “mutu wa zinthu zonse” mumpingo wachikhristu, ali ndi mphamvu pazonse zimene zimachitika mmenemo. Amaona chilichonse chimene chimachitika mu mpingo. Amayang’anitsitsa kuti adziwe kuti moyo wauzimu wa gulu lililonse la Akhristu, kapena mpingo uliwonse, uli bwanji. Tikuona zimenezi m’chivumbulutso chimene mtumwi Yohane anapatsidwa cha kumapeto kwa nthawi ya atumwi. Polankhula ndi mipingo 7, Yesu ananena kasanu konse kuti anadziwa ntchito zawo, zinthu zimene ankachita bwino, ndi zofooka zawo, ndipo anawalangiza ndi kuwalimbikitsa. (Chivumbulutso 2:2, 9, 13, 19; 3:1, 8, 15) Tikukhulupirira kuti Khristu ankadziwanso bwino moyo wauzimu wa mipingo ina ya ku Asiya Mina, Palesitina, Suriya, Babulo, Girisi, Italiya ndi kwinanso. (Machitidwe 1:8) Nanga bwanji lerolino?

Kapolo Wokhulupirika

3. N’chifukwa chiyani Khristu akuyerekezedwa ndi mutu pamene mpingo wake ukuyerekezedwa ndi thupi?

3 Yesu atauka kwa akufa koma atatsala pang’ono kupita kumwamba kwa Atate wake, anauza ophunzira ake kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Ananenanso kuti: “Dziwani ichi! Ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mateyo 28:18-20) Apa anati apitiriza kukhala nawo monga Mutu wawo. M’kalata zake zopita kwa Akhristu ku Efeso ndi ku Kolose, mtumwi Paulo anayerekezera mpingo wachikhristu ndi “thupi,” limene Mutu wake ndi Khristu. (Aefeso 1:22, 23; Akolose 1:18) Buku lina lofotokoza za Baibulo limati mawu ofanizira mpingo ndi thupi amenewa “samangosonyeza mgwirizano ndi Mutu, koma kuti Mutuwu umagwiritsa ntchito ziwalozo pochita chifuniro chake.” (The Cambridge Bible for Schools and Colleges) Kodi Khristu wakhala akugwiritsa ntchito gulu liti chiyambireni kulamulira mu Ufumu wake mu 1914?​—Danieli 7:13, 14.

4. Malinga ndi ulosi wa Malaki, kodi Yehova ndi Khristu Yesu anapeza chiyani atayendera kachisi wauzimu?

4 Malaki analosera kuti Yehova, “Ambuye,” limodzi ndi “mthenga [wake] wa chipangano,” amene ndi Mwana wake Khristu Yesu atangoyamba kulamulira, adzabwera kudzaweruza ndi kudzayendera “kachisi” Wake, kapena kuti nyumba yake yophiphiritsa yopembedzeramo. Zikuoneka kuti “nthawi yoikika” yakuti ‘chiweruzo chiyambe pa nyumba ya Mulungu’ inafika m’chaka cha 1918. * (Malaki 3:1; 1 Petulo 4:17) Panthawi imeneyi, anthu amene ankati ndi atumiki a Mulungu ndipo ankamulambira moona padziko lapansi, anayesedwa. Matchalitchi Achikhristu, amene kwa zaka mazana ambiri anaphunzitsa anthu ziphunzitso zosalemekeza Mulungu ndipo anapha nawo anthu ambirimbiri pankhondo yoyamba ya padziko lonse, anakanidwa. Koma Akhristu okhulupirika odzozedwa ndi mzimu amene analipo, anayesedwa ndi kuyengedwa monga ndi moto, ndipo anavomerezedwa. Choncho anakhala kwa Yehova anthu opereka “zopereka m’chilungamo.”​—Malaki 3:3.

5. Malinga ndi ulosi wa Yesu wonena za “kukhalapo” kwake, kodi “kapolo” wokhulupirika anadzapezeka kuti ndi ndani?

5 Mogwirizana ndi ulosi wa Malaki, chizindikiro chokhala ndi mbali zambiri chimene Yesu anapatsa ophunzira ake kuti azindikire nthawi ya ‘kukhalapo kwake ndi ya mapeto a dongosolo lino la zinthu,’ chinalinso ndi mbali ina yofotokoza za gulu la “kapolo.” Yesu anati: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuyang’anira antchito ake a pakhomo, kuwapatsa chakudya chawo panthawi yoyenera? Kapolo ameneyu adzakhala wosangalala ngati mbuye wake pobwera adzam’peza akuchita zimenezo! Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kuyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyo 24:3, 45-47) Khristu, “pobwera” kudzayendera “kapolo” ameneyu mu 1918, anapeza ophunzira ake odzozedwa komanso okhulupirika amene kuyambira 1879 ankagwiritsa ntchito magazini ino ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo kuti apereke ‘chakudya chauzimu panthawi yoyenera.’ Anawavomera kukhala gulu lake, kapena kuti “kapolo” wake, ndipo mu 1919 anawapatsa udindo woyang’anira zinthu zake zonse padziko.

Kuyang’anira Zinthu za Khristu Padziko Lapansi

6, 7. (a) Kodi Yesu anatchula “kapolo” wake wokhulupirika ndi mawu ena ati? (b) Kodi mawu akuti “mdindo” amene Yesu ananena akusonyeza chiyani?

6 Miyezi ingapo Yesu asananene ulosi wake wa chizindikiro cha kukhalapo kwake, umene unanenanso za “kapolo” womuimira padziko, anatchulapo za “kapolo” ameneyu m’njira yosiyana. Njira imeneyi imathandiza kumvetsa udindo wosiyanasiyana wa kapoloyu. Yesu ananena kuti: “Ndani kwenikweni ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kuyang’anira gulu la atumiki ake, kumawapatsa chakudya chawo panthawi yake? Ndikukuuzani ndithu, Adzamuika kukhala woyang’anira zinthu zake zonse.”​—Luka 12:42, 44.

7 Pano kapoloyu akutchedwa ndi mawu akuti mdindo, amene anawamasulira kuchokera ku mawu achigiriki otanthauza “woyang’anira nyumba kapena malo.” Sikuti gulu la mdindoli ndi gulu la anthu ophunzira amene amangofotokoza mfundo zochititsa chidwi za m’Baibulo. Kuwonjezera pa kupereka chakudya chauzimu “panthawi yake,” “mdindo wokhulupirika” ameneyu anali woti aikidwe kuyang’anira gulu lonse la atumiki a Khristu ndi “zinthu zake zonse” padziko lapansi. Kodi zinthu zakezi ndi chiyani?

8, 9. Kodi “zinthu” zimene kapolo wapatsidwa kuyang’anira ndi chiyani?

8 Kapoloyu alinso ndi udindo woyang’anira zinthu zimene otsatira a Khristu amagwiritsa ntchito poyendetsa utumiki wawo padziko lonse, monga likulu ndi maofesi a nthambi a Mboni za Yehova. Amayang’aniranso malo opembedzerako monga Nyumba za Ufumu ndi Nyumba za Msonkhano. Chofunika kwambiri ndi chakuti kapoloyu amayang’aniranso dongosolo lolimbikitsa anthu mwauzimu lophunzira Baibulo pamisonkhano ya mlungu ndi mlungu ndiponso pamisonkhano yaikulu. Pamisonkhano imeneyi, pamakhala nkhani zofotokoza kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo. Ndiponso pamaperekedwa malangizo a panthawi yake a mmene anthu angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pamoyo wawo.

9 Udindo winanso wa mdindo ameneyu ndi woyang’anira ntchito yofunika kwambiri yolalikira “uthenga wabwino uwu wa ufumu” ndi kupanga “ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.” Ntchito imeneyi imafuna kuphunzitsa anthu kuti asunge zinthu zonse zimene Khristu, Mutu wa mpingo, amalamula kuti achite nthawi ya mapeto ino. (Mateyo 24:14; 28:19, 20; Chivumbulutso 12:17) Ntchito yolalikira ndi yophunzitsa yabala “khamu lalikulu” lokhulupirika la anzawo a otsalira odzozedwa. Ndithudi khamuli, limene ndi “zofunika za amitundu,” lili zina mwa “zinthu” za Khristu zimene kapolo wokhulupirika amayang’anira.​—Chivumbulutso 7:9; Hagai 2:7.

Bungwe Lolamulira Loimira Kapolo

10. Kodi ndi bungwe lanji logamula nkhani zosiyanasiyana limene linaliko panthawi ya atumwi, ndipo zogamula zawo zinali ndi ubwino wanji kumipingo?

10 Udindo waukulu wa kapolo wokhulupirika umafunanso kuti azigamula nkhani zambiri. Mumpingo woyambirira wachikhristu, atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anali kuimira kapolo panthawiyo, ndipo ankagamula nkhani zokhudza mpingo wonse wachikhristu. (Machitidwe 15:1, 2) Zimene bungwe lolamulira limeneli lagamula, zinkatumizidwa ku mipingo kudzera m’kalata ndi abale oyendayenda amene ankaimira bungwelo. Akhristu oyambirira akalandira malangizo omveka bwino amenewa, ankasangalala ndipo chifukwa cha mtima wawo wogonjera bungwe lolamulira, pankakhala mtendere ndi umodzi.​—Machitidwe 15:22-31; 16:4, 5; Afilipi 2:2.

11. Kodi Khristu akugwiritsa ntchito ndani masiku ano kutsogolera mpingo wake, ndipo tiyenera kuliona bwanji gulu limeneli la Akhristu odzozedwa?

11 Masiku ano, mofanana ndi masiku a Akhristu oyambirira, Bungwe Lolamulira la otsatira Khristu padziko lapansi lapangidwa ndi kagulu ka oyang’anira odzozedwa ndi mzimu. Khristu, Mutu wa mpingo, amagwiritsa ntchito “dzanja lake lamanja,” limene limaimira mphamvu zake, potsogolera amuna okhulupirika amenewa kuyang’anira ntchito ya Ufumu. (Chivumbulutso 1:16, 20) M’nkhani ya moyo wake, Albert Schroeder, amene anali m’Bungwe Lolamulira kwa zaka zambiri ndipo anamaliza moyo wake padziko posachedwapa, analemba kuti: “Bungwe Lolamulira limakumana pa Lachitatu lililonse, kutsegula msonkhanowo ndi pemphero kufunsa kaamba ka chitsogozo cha mzimu wa Yehova. Kuyesayesa kwenikweni kumapangidwa kuwona kuti nkhani iliyonse yomwe ikusamaliridwa ndi chosankha chilichonse chomwe chapangidwa chili m’chigwirizano ndi Mawu a Mulungu Baibulo.” * Choncho timakhulupirira Akhristu odzozedwa ndi okhulupirika amenewa ndi mtima wonse. Tiyenera kumvera makamaka iwowo potsatira malangizo a Paulo akuti: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankha mlandu.”​—Aheberi 13:17.

Perekani Ulemu Woyenera kwa Kapolo Wokhulupirika

12, 13. Kodi zifukwa za m’Malemba zoperekera ulemu ku gulu la kapolo n’zotani?

12 Chifukwa chachikulu choperekera ulemu woyenera ku gulu la kapolo wokhulupirika n’chakuti tikamatero, timakhala tikupereka ulemu kwa Mbuye, Yesu Khristu. Polankhula za odzozedwa, Paulo analemba kuti: “Amene anaitanidwa ali mfulu ndi kapolo wa Khristu. Munagulidwa ndi mtengo wake.” (1 Akorinto 7:22, 23; Aefeso 6:6) Choncho, tikamagonjera mokhulupirika potsogoleredwa ndi kapolo wokhulupirika ndi Bungwe lake Lolamulira, timakhala tikugonjera Khristu, Mbuye wa kapoloyo. Kupereka ulemu woyenera ku gulu limene Khristu akugwiritsa ntchito kuyang’anira zinthu zake padziko lapansi ndiyo njira ina imene ‘timavomerezera poyera kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.’​—Afilipi 2:11.

13 Chifukwa china cha m’Malemba choperekera ulemu kwa kapolo wokhulupirika ndi chakuti Akhristu odzozedwa amene ali pa dziko, mophiphiritsira amatchedwa kuti “kachisi” amene Yehova amakhalamo “mwa mzimu.” Choncho iwowo ndi ‘oyera.’ (1 Akorinto 3:16, 17; Aefeso 2:19-22) Yesu waika zinthu zake m’manja mwa gululi, limene akulitcha kachisi woyera. Zimenezi zikutanthauza kuti gulu la kapololi lili ndi ulamuliro ndi udindo wogamula nkhani zina mumpingo wachikhristu. N’chifukwa chake, onse mumpingo amaona kuti ali ndi udindo waukulu ndi wopatulika wotsatira ndi kumvera malangizo a kapolo wokhulupirika ndi Bungwe lake Lolamulira. Ndithudi, “nkhosa zina” zimaona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza gulu la kapololi posamalira zinthu za Mbuye.​—Yohane 10:16.

Kuthandiza Kapolo Mokhulupirika

14. Malinga ndi ulosi wa Yesaya, kodi nkhosa zina zimatsata bwanji gulu la kapolo wodzozedwa pambuyo ndipo n’chifukwa chiyani zikutchedwa “antchito yosalipidwa”?

14 Mneneri Yesaya analosera kuti nkhosa zina zidzagonjera Isiraeli wauzimu modzichepetsa. Iye anati: “Atero Yehova, [Antchito yosalipidwa a, NW] Aigupto, ndi malonda a Kusi, ndi a Sabea, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m’maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.” (Yesaya 45:14) Masiku ano, nkhosa zina zimatsata mophiphiritsira gulu la kapolo wodzozedwa ndi Bungwe lake Lolamulira pambuyo, mwa kugonjera utsogoleri wawo. Monga “antchito yosalipidwa,” nkhosa zina zimadzipereka kugwiritsa ntchito mphamvu ndi chuma chawo kuthandiza pa ntchito yolalikira padziko lonse, imene Khristu anapatsa otsatira ake odzozedwa.​—Machitidwe 1:8; Chivumbulutso 12:17.

15. Kodi ulosi wa pa Yesaya 61:5, 6 umati chiyani za ubale umene ulipo pakati pa nkhosa zina ndi Isiraeli wauzimu?

15 Nkhosa zina ndi zokondwa ndi zothokoza potumikira Yehova moyang’aniridwa ndi gulu la kapolo ndi Bungwe lake Lolamulira. Zimadziwa kuti odzozedwa ndiwo “Isiraeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) “Alendo” ndi “anthu akunja” ophiphiritsa amenewa ndi anzawo a Isiraeli wauzimu. Iwo amasangalala kugwira ntchito monga “olima” ndi ‘okonza minda yamphesa’ motsogoleredwa ndi odzozedwawo, amene ndi “ansembe a Yehova” ndi “atumiki a Mulungu.” (Yesaya 61:5, 6) Iwowo amalalikira mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse. Amathandizanso gulu la kapolo ndi mtima wonse poweta ndi kusamalira bwinobwino anthu onga nkhosa amene amawapeza.

16. N’chifukwa chiyani nkhosa zina zimathandiza kapolo mokhulupirika?

16 Nkhosa zina zikudziwa bwino kuti zapindula kwambiri ndi khama la kapolo wokhulupirika pozipatsa chakudya chauzimu panthawi yake. Modzichepetsa zimazindikira kuti popanda kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, sizikanadziwa zambiri kapena sizikanadziwa n’komwe choonadi cha m’Baibulo. Sizikanadziwa za ulamuliro wa Yehova, kuyeretsedwa kwa dzina lake, Ufumu wake, miyamba yatsopano ndi dziko latsopano, mizimu ya akufa, mmene akufa alili, ndipo sizikanadziwanso kuti Yehova ndi Mwana wake ndani kapena kuti mzimu woyera n’chiyani. Chifukwa cha kukhulupirika kwawo ndiponso mtima wawo woyamikira, nkhosa zina zimakonda ndipo zimathandiza “abale” odzozedwa a Khristu amene ali padziko lapansi nthawi ya mapeto ino.​—Mateyo 25:40.

17. Kodi Bungwe Lolamulira laona kuti ndi bwino kuchita chiyani, ndipo tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

17 Odzozedwa akucheperachepera pa dziko lapansi, choncho n’zosatheka kuti akhale m’mipingo yonse kuyang’anira zinthu za Khristu. N’chifukwa chake, Bungwe Lolamulira limasankha abale ena a nkhosa zina kuti aziyang’anira maofesi a nthambi, zigawo, madera, ndi mipingo ya Mboni za Yehova. Kodi abusa aang’ono amenewa timawaona bwanji, ndipo zimenezi zimasonyeza bwanji kuti ndife okhulupirika kwa Khristu ndi kapolo wake? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mungawerenge zambiri pankhaniyi mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 2004, masamba 13-18, ndi ya December 1, 1992, tsamba 13.

^ ndime 11 Ili mu Nsanja ya Olonda ya March 1, masamba 10-17.

Kubwereza

• Kodi Mtsogoleri wathu ndani, ndipo n’chiyani chimasonyeza kuti amadziwa mmene zinthu zilili m’mipingo?

• Poyendera “kachisi,” kodi ndani anapezeka kuti ndi kapolo wokhulupirika, ndipo zinthu zimene anapatsidwa kuyang’anira n’chiyani?

• Kodi zifukwa za m’Malemba zothandizira gulu la kapolo mokhulupirika n’zotani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 23]

“Zinthu” zimene “mdindo” akuyang’anira ndi monga maofesi, misonkhano, ndi ntchito yolalikira

[Chithunzi patsamba 25]

Nkhosa zina zimathandiza gulu la kapolo wokhulupirika zikamalalikira mwachangu