Kufunafuna Malangizo Othandiza
Kufunafuna Malangizo Othandiza
Kodi ndingateteze bwanji thanzi langa?
Nanga tingatani kuti banja lathu lizisangalala?
Ndingatani kuti ndikhalitse pa ntchito?
KODI munayamba mwadzifunsapo mafunso amenewa? Nanga munapeza mayankho othandizadi? Mabuku pafupifupi 2,000 osiyanasiyana opereka malangizo pankhani zofunika zimenezi, akufalitsidwa chaka chilichonse. Mwachitsanzo, m’dziko la Britain lokha, anthu amawononga ndalama zokwana mapaundi 80 miliyoni (pafupifupi madola 150 miliyoni) chaka chilichonse, pogula mabuku opereka malangizo pamavuto a anthu. Ndipo ku United States, anthu amawononga ndalama zokwana madola 600 miliyoni chaka chilichonse, pogula mabuku amenewa. Choncho, zikuoneka kuti mwina si inu nokha amene mukufunafuna malangizo othandiza pa mavuto a tsiku ndi tsiku.
Ponena za malangizo opezeka m’mabuku ambirimbiriwa, wolemba mabuku wina anati: “Mabuku ambiri atsopano amangobwereza zimene zinalembedwa kale.” N’zoonadi, malangizo ambiri a m’mabukuwa amangobwereza nzeru zimene zinalembedwa kale. Ndipotu nzeru zimenezi zili m’buku lakale kwambiri kuposa lililonse. Bukuli lafalitsidwa kwambiri padziko lonse kuposa buku lililonse. Buku lonseli kapena zigawo zake zina, azimasulira m’zinenero zokwana 2,400. Ndipotu padziko lonse pasindikizidwa mabuku amenewa okwana pafupifupi 5 biliyoni. Bukuli si lina ayi, koma Baibulo!
Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo.” (2 Timoteyo 3:16) Komano sikuti Baibulo linalembedwa kuti likhale longolangiza chabe. Chifukwa chachikulu chimene analilembera n’chakuti lisonyeze cholinga cha Mulungu polenga anthu. Ngakhale zili choncho, Baibulo lili ndi mfundo zambiri za mmene tingapiririre mavuto athu. Limanenanso kuti anthu amene amatsatira malangizo ake, zinthu zimawayendera bwino. (Yesaya 48:17, 18) Kaya anthu akhale osiyana mitundu, chikhalidwe, kapena maphunziro, aliyense akamatsatira malangizo a m’Baibulo zinthu zimamuyendera bwino. Bwanji osawerenga nkhani yotsatirayi kuti muone nokha malangizo othandiza a m’Baibulo pankhani zokhudza thanzi, banja, ndiponso ntchito?