Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi mawu a Paulo akuti mkazi wamasiye ayenera kukhala “mkazi wa mwamuna mmodzi,” kuti ayenerere thandizo la mpingo wachikhristu, amatanthauza chiyani?—1 Timoteyo 5:9, mawu amunsi.
Popeza kuti mtumwi Paulo ankanena za mkazi wamasiye, mawu akuti “mkazi wa mwamuna mmodzi” ayenera kuti ankanena za mkaziyo asanakhale wamasiye. Kodi zimenezi zingatanthauze kuti mkaziyo anakwatiwapo kamodzi kokha? Kapena kodi mawu a Paulo ali ndi tanthauzo lina? *
Ena ananenapo zoti Paulo ankanena za akazi amasiye amene anakwatiwapo kamodzi kokha. N’zoona kuti m’madera ambiri, mkazi wamasiye akapanda kukwatiwanso, ankaonedwa kuti ndi wakhalidwe labwino kwambiri. Koma maganizo amenewo amatsutsana ndi mawu ena amene Paulo ananena. Mwachitsanzo, polembera Akhristu a ku Korinto, ananena momveka bwino kuti ngakhale kuti iye ankaona kuti mkazi wamasiye ayenera kukhala wosakwatiwa kuti akhale wosangalala kwambiri, “mkaziyo ndi womasuka kukwatiwa ndi aliyense amene iye wafuna, kokha mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39, 40; Aroma 7:2, 3) Ndiponso, polembera kalata Timoteyo, Paulo anati: “Ndimafuna kuti akazi amasiye achitsikana azikwatiwa.” (1 Timoteyo 5:14) Choncho, panalibe kunyoza mkazi wamasiye ngati wasankha kukwatiwanso.
Ndiye tingati mawu amene Paulo analembera Timoteyo amatanthauza chiyani? Mawu akuti “mkazi wa mwamuna mmodzi” amapezeka pa vesi lokhali. N’zochititsa chidwi kuti mawu amenewa amafanana ndi mawu ena amene Paulo anagwiritsa ntchito kangapo, akuti “mwamuna wa mkazi mmodzi.” (1 Timoteyo 3:2, 12; Tito 1:6) Paulo ananena mawu amenewa pofotokoza ziyeneretso za oyang’anira achikhristu ndi za atumiki othandiza. Pankhani imeneyo, mawuwo akutanthauza kuti ngati mwamuna wokwatira akufuna kuyenerera udindo mumpingo wachikhristu, ayenera kukhala wokhulupirika kwa mkazi wake ndi wosanenezedwa za khalidwe loipa. * Choncho, zikuoneka kuti mawu a pa 1 Timoteyo 5:9 akunena mfundo yomweyi: Kuti mkazi wamasiye ayenerere thandizo la mpingo, anayenera kukhala wodzipereka ndi wokhulupirika kwa mwamuna wake ali moyo ndipo anafunikira kukhala ndi khalidwe labwino. Mfundo zinanso zimene Paulo anatchula za mkazi woyenerera thandizo, zimasonyezanso mfundo imeneyi.—1 Timoteyo 5:10.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Aroma ndi Agiriki m’nthawi ya atumwi, sankalola mkazi kukwatiwa ndi amuna angapo nthawi imodzi. Choncho, panalibe chifukwa choti Paulo alembere Timoteyo za nkhani imeneyi, kapena kudzudzula munthu amene anali kuchita zimenezi.
^ ndime 5 Mungawerenge zambiri pankhani imeneyi mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1996, tsamba 17, ndi “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 1981, tsamba 31.