Malangizo Othandizadi
Malangizo Othandizadi
MALANGIZO ambiri opezeka m’mabuku amakhala othandiza anthu amene zinthu zawathina kale. Koma malangizo a m’Baibulo si otero ayi. Inde, malangizo ake amathandiza anthu omwe ali m’mavuto, koma salekera pompa. Malangizo ake amathandiza munthu kupewa kuchita zinthu zomwe zingam’lowetse m’mavuto.
Baibulo limatha “kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira.” (Miyambo 1:4) Munthu ukamatsatira malangizo a m’Baibulo, “kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza; kukupulumutsa ku njira yoipa.” (Miyambo 2:11, 12) Taonani zitsanzo zingapo zosonyeza kuti kutsatira malangizo a m’Baibulo kumateteza thanzi lanu, kumathandiza kuti banja lanu lizisangalala, ndiponso kuti mukhale wodalirika pa ntchito.
Samalani ndi Mowa
Baibulo sililetsa kumwa mowa pang’ono. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti mowa ndi mankhwala ndithu polangiza Timoteyo kuti: “Uzimwanso vinyo pang’ono, chifukwa cha m’mimba mwako ndi kudwaladwala kwako kuja.” (1 Timoteyo 5:23, 24) Malemba ena m’Baibulo amasonyeza kuti cholinga cha Mulungu sichinali choti mowa ungokhala ngati mankhwala basi. Amati ‘vinyo amakondweretsa mtima wa munthu.’ (Salmo 104:15) Komabe Baibulo limachenjeza kuti tisakhale “akapolo a vinyo wambiri.” (Tito 2:3) Limati: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka.” (Miyambo 23:20, 21) Kodi chimachitika n’chiyani munthu akanyalanyaza malangizo abwinowa? Taonani zitsanzo zotsatirazi za m’mayiko angapo chabe.
Lipoti lokhudza nkhaniyi la m’chaka cha 2004, la Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse, linati: “Ku Ireland, chaka chilichonse mavuto obwera chifukwa cha mowa amawonongetsa ndalama zokwana [madola 3] biliyoni.” Lipotilo linatinso pa ndalama zankhaninkhanizi, “ndalama zokwana [madola 350] miliyoni zimalowa kuchipatala, [madola 380] miliyoni zimalowa pa ngozi zapamsewu, [madola 126] miliyoni zimalowa ku milandu, [madola 1,300] miliyoni zimawonongeka chifukwa chojomba ku ntchito.”
Chinthu choopsa kwambiri kuposa kuwonongetsa
ndalama n’chakuti uchidakwa umazunzitsa kwambiri anthu. Mwachitsanzo, ku Australia m’chaka chimodzi chokha anthu opitirira 500,000 anamenyedwapo ndi anthu oledzera. Ku France, akuti uchidakwa ndi umene umachititsa ndewu zambiri za pabanja. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti malangizo a m’Baibulo pankhaniyi n’ngothandiza?Pewani Chizolowezi Choipitsa Thupi
Kalekale mu 1942, kusuta fodya kudakali m’fasho, magazini ino inalangiza anthu kuti ayenera kupewa kusuta fodya chifukwa kumaphwanya mfundo za m’Baibulo. Chaka chimenecho, nkhani ina m’magazini ino inati anthu ofuna kusangalatsa Mulungu ayenera kumvera lamulo la m’Baibulo lakuti, ‘adziyeretse kuchotsa chilichonse choipitsa cha thupi ndi cha mzimu.’ (2 Akorinto 7:1) Tsopano patha zaka 65 ndipotu ambiri angavomereze kuti malangizo a m’Baibulowa n’ngothandizadi.
Mu 2006, Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linati kusuta fodya “ndi chinthu chachiwiri pa zinthu zomwe zikupha anthu ambiri padziko lonse.” Chaka chilichonse anthu amene akufa chifukwa cha fodya alipo pafupifupi 5 miliyoni. Pamene Edzi imapha anthu pafupifupi 3 miliyoni pachaka. M’zaka za m’ma 19 chakuti, anthu pafupifupi 100 miliyoni anafa chifukwa chosuta fodya. Awatu ndi anthu ochuluka mofanana ndi omwe anafa pankhondo zonse za m’zaka zimenezi. N’chifukwa chaketu masiku ano anthu ambiri akuvomereza kuti n’chinthu chanzeru kupewa fodya.
“Thawani Dama”
Koma anthu ambiri savomereza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana. Anthu ena ananamizidwa kuti Baibulo limaletseratu chilakolako chilichonse cha kugonana. Komano zoona zake n’zakuti Baibulo limapereka malangizo othandiza a mmene anthu ayenera kuonera nkhani ya kugonana. Baibulo limaphunzitsa kuti kugonana kuyenera kuchitika pakati pa mwamuna ndi mkazi okwatirana basi. (Genesis 2:24; Mateyo 19:4-6; Aheberi 13:4) Kugonana ndi njira yoti mwamuna ndi mkazi okwatirana azisonyezana chikondi. (1 Akorinto 7:1-5) Ana amene amabadwa m’banjamo amakhala mosangalala chifukwa choti makolo awowo akukondana.—Akolose 3:18-21.
Pankhani ya chiwerewere, Baibulo limati: “Thawani dama.” (1 Akorinto 6:18) Kodi chifukwa chimodzi chothawira dama n’chiyani? Vesili limapitiriza kunena kuti: “Tchimo lina lililonse limene munthu angachite ndi la kunja kwa thupi lake, koma amene amachita dama amachimwira thupi lake la iye mwini.” Kodi chimachitika n’chiyani munthu akapanda kutsatira malangizo a m’Baibulo pankhani imeneyi?
Taganizirani zimene zikuchitika ku United States. Kuposa m’mayiko ena onse olemera, chaka chilichonse m’dzikoli atsikana ambiri
zedi, okwana 850,000, amatenga mimba ndipo ena amachotsa mimbazo. Komano ambiri amene amaberekawo, ana ake amakhala apathengo. N’zosachita kufunsa kuti ambiri mwa atsikanawa amayesetsa kupatsa ana awowo malangizo abwino ndi kuwalera mwachikondi. Ndipotu ena amakwanitsa kulera anawo bwinobwino. Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri ana aamuna a atsikana amenewa akakula amakathera kundende ndipo aakazi amaberekanso ana apathengo adakali ana. Wofufuza wina, Robert Lerman, anati: “Masiku ano pali mavuto ambiri amene abwera chifukwa choti ana ambiri akuleredwa ndi mayi kapena bambo awo okha. Ena mwa mavutowa ndiwo kuchuluka kwa ana osiya sukulu, kuchuluka kwa uchidakwa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ana otenga mimba zapathengo, ndi ana olowerera n’kumachita zaumbanda.”Amene ali ndi khalidwe la chiwerewere amadziputiranso mavuto ena osiyanasiyana monga matenda ndiponso nkhawa. Mwachitsanzo, magazini ya Pediatrics inati: “Pali umboni wosonyeza kuti nthawi zambiri achinyamata okonda zachiwerewere amadwala kwambiri matenda ovutika maganizo ndiponso amadzipha.” Ponenapo za matenda ena okhudza nkhaniyi, bungwe lina la zaumoyo ku America linati: “Anthu oposa theka pa anthu onse a ku [United States] adzakhalapo ndi matenda opatsirana pogonana pa nthawi inayake m’moyo wawo.” Taganizirani mavuto ndiponso zowawa zimene anthu akanatha kupewa akanati azimvera malangizo a m’Baibulo pankhaniyi.
Muzigwirizana Kwambiri M’banja
Sikuti Baibulo limangochenjeza kuti tipewe makhalidwe otilowetsa m’mavuto basi. Taonani malangizo ake othandiza a zimene tiyenera kuchita kuti banja lathu likhale losangalala.
Mawu a Mulunguwa amati: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awoawo.” (Aefeso 5:28) Baibulo limalimbikitsa amuna kuti asamachite zinthu mosawerengera akazi awo koma limati azikhala nawo “mowadziwa bwino, kupatsa ulemu mkazi monga chiwiya chosalimba.” (1 Petulo 3:7) Pankhani ya mikangano imene ingabuke, Baibulo limalimbikitsa amuna kuti: “Musaleke kukonda akazi anu ndipo musawapsere mtima.” (Akolose 3:19) Kodi simukuvomereza kuti mwamuna amene amatsatira malangizo amenewa amakondedwa ndi kulemekezedwa ndi mkazi wake?
Baibulo limalangiza akazi kuti: “Akazi agonjere amuna awo monga kugonjera Ambuye, chifukwa mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso Khristu alili mutu wa mpingo . . . Mkazi akhale ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.” (Aefeso 5:22, 23, 33) Kodi simukuvomereza kuti mkazi amene amatsatira malangizo amenewa akamalankhula kwa mwamuna wake kapena akamanena za iye amakondedwa kwambiri ndi mwamunayo?
Pankhani yolera ana, malangizo a m’Baibulo kwa makolonu n’ngakuti muzilankhula ndi ana anu “pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:7) Abambo ndiwo makamaka akuuzidwa kuti azilangiza ana awo mwachikondi ndi kuwaphunzitsa makhalidwe abwino. Mawu a Mulungu amati: “Atate, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malango a Yehova.” (Aefeso 6:4) Ana nawonso akuuzidwa kuti: “Muzimvera makolo anu” ndiponso kuti “lemekeza atate wako ndi amayi wako.” *—Aefeso 6:1, 2.
Kodi inuyo mukuona kuti mabanja angapindule potsatira malangizo amenewa? Mwina mungadzifunse kuti, ‘zikumveka bwino ndithu, komano kodi zingathekedi?’ Tapitani ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova m’dera lanulo. Kumeneko mukapeza mabanja amene akuyesetsa kutsatira malangizo anzeru a m’Baibulo. Kalankhulaneni nawo. Kaoneni khalidwe limene akusonyezana. Mukaona nokha kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kumathandizadi kuti mabanja akhale osangalala.
Wantchito Wakhama ndi Bwana Wabwino
Kodi Baibulo limapereka malangizo otani otithandiza kuti tikhale odalirika pa ntchito tsiku ndi tsiku? Limati munthu wogwira ntchito mwaluso amakondedwa. Mfumu yanzeru Solomo inafunsa kuti: “Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.” (Miyambo 22:29) Komano ‘waulesi’ ali ngati “utsi [wowawa] m’maso” mwa om’lemba ntchito. (Miyambo 10:26) Baibulo limalimbikitsa antchito kuti azigwira moona mtima ndiponso mwakhama. “Wakubayo asabenso, koma agwire ntchito molimbika, kugwira ndi manja ake ntchito yabwino.” (Aefeso 4:28) Azitsatira malangizo amenewa ngakhale ngati bwana palibe. “Khalani omvera azimbuye anu a kuthupi pa zinthu zonse, osati mwa chiphamaso, ngati ofuna kukondweretsa anthu, koma moona mtima, moopa Yehova.” (Akolose 3:22) Ngati inuyo muli ndi antchito, kodi simungakonde wantchito amene amamvera malangizo amenewa?
Anthu amene ali ndi antchito Baibulo limawakumbutsa kuti: “Wantchito ndi woyenera kulandira malipiro ake.” (1 Timoteyo 5:18) Lamulo limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli linati anthu anayenera kulipira antchito awo panthawi yake ndiponso mokwanira. Mose analemba kuti: “Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m’mawa.” (Levitiko 19:13) Kodi simungasangalale kugwira ntchito kwa munthu amene amatsatira malangizo a m’Baibulowa pokulipirani m’nthawi yake ndiponso mokwanira?
Chitsime Chachikulu cha Nzeru
Kodi mukudabwa kuona kuti Baibulo, lomwe ndi buku lakale kwambiri, lili ndi malangizo othandiza chonchi masiku ano? Chifukwa chimene malangizo a m’Baibulo akhalabe othandiza kwa nthawi yaitali chonchi, pamene malangizo a m’mabuku ena ambirimbiri atha ntchito, n’chakuti Baibulo si mawu a anthu, koma ndi “mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13.
Tikukulimbikitsani kuti mupeze nthawi yoti mudziwe bwino Mawu a Mulunguwa. Ngati mutatero, mudzayamba kukonda kwambiri Mlembi wa Baibulo, Yehova Mulungu. Tsatirani malangizo ake kuti mutetezedwe ndi kuthandizidwa pamoyo wanu. Mukamatero ‘mumayandikira Mulungu, ndipo iyenso amakuyandikirani.’ (Yakobe 4:8) Palibenso buku lina limene lingakuthandizeni choncho.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 20 Kuti mudziwe mfundo zambiri za m’Baibulo zimene zingathandize banja lanu, onani buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 4]
Kodi mumaona kuti zimene Baibulo limanena pankhani ya mowa n’zothandiza?
[Chithunzi patsamba 5]
Kodi mumavomereza malangizo a m’Baibulo akuti tizipewa fodya?
[Zithunzi patsamba 7]
Kutsatira malangizo a m’Baibulo kumalimbikitsa moyo wabanja
[Mawu a Chithunzi patsamba 5]
Globe: Based on NASA photo