Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nkhanza Zidzathadi?

Kodi Nkhanza Zidzathadi?

Kodi Nkhanza Zidzathadi?

ANTHU ambiri akafunsidwa, sachedwa kuvomereza kuti masiku ano anthu amachita nkhanza chifukwa cha kudzikonda. Mtima wa dziwa zako umene unafesedwa zaka zambiri zapitazo wabala anthu ambiri odzikonda. Ambiri amachita chilichonse, ngakhale nkhanza, kuti apeze zimene akufuna. Amene amachita zimenezi si anthu okha komanso mayiko.

Moyo wa anthu sukuwerengeredwanso. Anthu ena mpaka amasangalala kuchitira anzawo nkhanza. Ali ngati zigawenga zimene zimati zimazunza anthu chifukwa chongofuna kusangalala basi. Palinso anthu ena mamiliyoni ambiri amene amakonda mafilimu achiwawa ndi ankhanza. Chifukwa cha zimenezi, makampani opanga mafilimu otere amapeza ndalama zambiri. Ambiri akamaonerera ndi kuwerenga kawirikawiri zinthu zankhanza m’mafilimu ndi panyuzi, amaiwaliratu mtima wachifundo.

Nthawi zambiri munthu akachitidwa nkhanza, amakhala ndi mtima wokakala. Pofotokoza za chiwawa chimene anthu amachita chifukwa cha nkhanza, Noemí Díaz Marroquín, amene amaphunzitsa pa yunivesite ina ku Mexico, anati: “Munthu amachita kuphunzira chiwawa, ndipo ndi chikhalidwe . . . Timaphunzira kuchita chiwawa ngati anthu kumene tikukhala amachilola ndi kuchilimbikitsa.” Choncho nthawi zina, anthu oti anachitidwapo nkhanza nawonso amachitira anzawo nkhanza, mwina zofanana ndi zimene anachitiridwa.

Penanso, anthu amene amamwetsa mowa ndi mankhwala osokoneza bongo amakhala ankhanza. Anthu enanso amachita nkhanza chifukwa chosasangalala ndi boma ngati silikuthandiza anthu mokwanira. Pofuna kuti maganizo awo amvedwe, amayamba nkhanza ndi uchigawenga ndipo nthawi zambiri amene amavutika ndi anthu osalakwa.

Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi anthu anangophunzira okha nkhanza? N’chifukwa chiyani anthu ali ndi nkhanza masiku ano?’

Kodi Anayambitsa Nkhanza Ndani Kwenikweni?

Baibulo limatiuza kuti Satana Mdyerekezi ali ndi mphamvu padzikoli, ndipo limati ndi “mulungu wa dongosolo lino la zinthu.” (2 Akorinto 4:4) Iye ndi wodzikonda ndi wankhanza kwambiri m’chilengedwe chonse. Ndipo Yesu anamufotokoza bwino kuti iye ndi “wopha anthu” ndi “tate wake wa bodza.”​—Yohane 8:44.

Kuyambira pamene Adamu ndi Hava anapanduka, Satana wakhala akugwiritsa ntchito mphamvu zake pa anthu. (Genesis 3:1-7, 16-19) Patadutsa zaka pafupifupi 1,500 kuchokera pamene anthu oyambawo anapandukira Yehova, angelo opanduka anavala matupi a anthu, anakwatira akazi, ndipo anabereka zimphona zotchedwa Anefili. Kodi Anefiliwo anali ndi khalidwe lotani? Dzina lawo limatipatsa yankho. Limatanthauza “Ogwetsa,” kapena kuti “anthu okonda kugwetsa anzawo.” Ayenera kuti anali anthu achiwawa, ndipo nkhanza ndi makhalidwe oipa zimene anayambitsa, sizikanathera kwina koma kuchigumula chochokera kwa Mulungu basi. (Genesis 6:4, 5, 17) Ngakhale kuti Anefili anawonongedwa ndi Chigumula, atate awo anabwerera kumwamba ndi kukhala ziwanda.​—1 Petulo 3:19, 20.

Zimene zinachitikira mnyamata wachiwanda nthawi ya Yesu, zimatsimikizira kuti angelo opandukawo ali ndi mtima wankhanza. Chiwandacho chinkagwetsa ndi kutsalimitsa mwanayo, kumugwetsera kumoto ndi m’madzi kuti afe. (Maliko 9:17-22) N’zoonekeratu kuti “makamu a mizimu yoipa” amenewa anatengera mtima wanjiru wa mkulu wawo wankhanza, Satana Mdyerekezi.​—Aefeso 6:12.

Masiku ano, mphamvu ya ziwanda ndi imene imalimbikitsa anthu kuchita nkhanza. Izi ndi zimene Baibulo linalosera kuti: “M’masiku otsiriza, idzafika nthawi yovuta yoikika. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, . . . odzimva, odzikweza, . . . osayamika, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa, osagwirizanitsika, odyerekeza, osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino, achiwembu, aliuma, otukumuka chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma mphamvu ya kulambira Mulungu siitha kuwasintha.”​—2 Timoteyo 3:1-5.

Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti nthawi yathu ino ndi yovuta kwambiri chifukwa chakuti pamene Khristu Yesu anayamba kulamulira mu Ufumu wa Mulungu mu 1914, Satana ndi ziwanda zake anaponyedwa pansi kuchokera kumwamba. Baibulo limati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ali ndi mkwiyo waukulu, podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”​—Chivumbulutso 12:5-9, 12.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti zinthu sizingasinthe? Díaz Marroquín, amene tamutchula kale uja, anati “anthu atha kusiya” khalidwe loipa. Komabe, chifukwa chakuti Satana ali ndi mphamvu padziko lonse, munthu masiku ano sangathe kusiya chiwawa pokhapokha atalola mphamvu ina yoposa ya Satana kulamulira maganizo ndi zochita zake. Kodi mphamvu imeneyi ndi iti?

Kodi Zingatheke Munthu Kusintha?

Mwayi wake, mzimu woyera wa Mulungu ndi wamphamvu kwambiri kuposa china chilichonse, ndipo umatha kugonjetsa mphamvu iliyonse ya ziwanda. Umalimbikitsa chikondi ndi moyo wabwino. Kuti aliyense amene akufuna kukondweretsa Yehova akhale ndi mzimu wake, sayenera kuchita nkhanza ngakhale pang’ono. Zimenezi zimafuna kuti munthu asinthe khalidwe lake kuti ligwirizane ndi chifuniro cha Mulungu. Koma kodi chifuniro chimenechi ndi chiyani? Ndi chakuti tiziyesetsa kutengera khalidwe la Mulungu. Kuti tichite zimenezi, tiziona ena monga mmene Mulungu amawaonera.​—Aefeso 5:1, 2; Akolose 3:7-10.

Mukaphunzira za mmene Mulungu amachitira zinthu, mudzaona kuti Yehova ali ndi chidwi ndi munthu wina aliyense. Sanayambe wachitirapo munthu wina aliyense, ngakhale nyama imene, nkhanza. * (Deuteronomo 22:10; Salmo 36:7; Miyambo 12:10) Nkhanza imamunyansa ndipo amadana ndi onse amene amachitira anzawo nkhanza. (Miyambo 3:31, 32) Umunthu watsopano umene Yehova amafuna kuti Akhristu akhale nawo, umawathandiza kuona anzawo ngati owaposa ndi kuwalemekeza. (Afilipi 2:2-4) Umunthu watsopano umenewu ndi “kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” Khalidwe linanso lofunika ndi chikondi, chifukwa “ndicho chomangira umodzi changwiro.” (Akolose 3:12-14) Kodi simukuona kuti dziko lingakhale bwino ngati anthu atakhala ndi makhalidwe amenewa?

Komabe, mwina simukukhulupirira kuti anthu angasinthedi. Tiyeni tione chitsanzo chimodzi. Martín * ankakonda kuzazira ndi kumenya modetsa nkhawa mkazi wake pamaso pa ana awo. Tsiku lina, zinthu zinavuta kwambiri mpaka ana awo anathawira ku nyumba yapafupi kukapempha thandizo. Patapita zaka, banjalo linayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Martín anaphunzira mmene munthu ayenera kukhalira ndi mmene ayenera kuchitira ndi anzake. Kodi anasintha? Mkazi wake anafotokoza kuti: “Kale, mwamuna wanga akapsa mtima, sitimamwa madzi. Chifukwa cha zimenezi, pabanja pathu panali chipwirikiti chokhachokha kwa nthawi yaitali. Ndikusowa mawu abwino othokozera Yehova chifukwa chothandiza Martín kusintha. Pano iye ndi tate ndi mwamuna wabwino kwambiri.”

Chimenechi ndi chitsanzo chimodzi chabe. Padziko lonse, anthu mamiliyoni ambiri amene aphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, zankhanza anaiwalako. Ndithudi, anthu amatha kusintha!

Nkhanza Zitha Posachedwa

M’tsogolo muno Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma lokhazikitsidwa kumwamba limene Khristu Yesu ndiye Wolamulira wake wachifundo, udzayamba kulamulira anthu onse padziko lapansi. Ufumuwo wayeretsa kale kumwamba kuchotsako Satana, make wa nkhanza, ndi ziwanda zake. Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa zonse zimene anthu ake okonda mtendere padziko lapansi akufuna. (Salmo 37:10, 11; Yesaya 11:2-5) Imeneyi ndiyo njira yokha yothetsera mavuto padziko lapansi. Koma bwanji ngati podikirira Ufumu umenewu, ena akuchitirani nkhanza?

Kubwezera nkhanza sikuthandiza. Koma kumangowonjezera nkhanzazo. Baibulo limatiuza kuti tizidalira Yehova, amene nthawi yake ikakwana ‘adzapatsa munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.’ (Yeremiya 17:10) (Onani bokosi lakuti “Kodi Mungatani Mutachitidwa Nkhanza?”) N’zoona kuti mungavutike chifukwa chochitidwa nkhanza. (Mlaliki 9:11) Koma Mulungu akhoza kuthetsa mavuto onse obwera chifukwa cha nkhanza, ngakhale imfa imene. Iye walonjeza kuti onse amene anafa chifukwa cha nkhanza, amenenso akuwakumbukira, adzakhalanso ndi moyo.​—Yohane 5:28, 29.

Ngakhale kuti masiku ano tikhoza kuchitidwa nkhanza, timalimba mtima chifukwa chakuti ndife mabwenzi apamtima a Mulungu ndiponso timakhulupirira kwambiri malonjezo ake. Mwachitsanzo, Sara analera ana aamuna awiri popanda mwamuna ndipo anaonetsetsa kuti aphunzira bwino. Koma atakalamba, ana akewo anamutaya osam’patsa thandizo lililonse. Panopa, Sara, amene tsopano ndi Mkhristu, akuti: “Ngakhale kuti ndimamva chisoni ndi zimene zinachitikazo, Yehova sananditaye. Akundithandiza kudzera mwa abale ndi alongo anga auzimu, amene amandisamalira nthawi zonse. Ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu adzathetsa mavuto anga ndi a anthu onse amene amadalira mphamvu yake ndi kumvera malamulo ake.”

Kodi abale ndi alongo auzimu amene Sara anawatchulawo ndani? Ndi Akhristu anzake a Mboni za Yehova. Iwo ndi gulu la padziko lonse la abale achifundo, amene amakhulupirira kuti posachedwapa nkhanza zidzatha. (1 Petulo 2:17) Zimenezi zikadzachitika, sipadzatsala aliyense, kaya akhale Satana Mdyerekezi, amene anayambitsa nkhanza, kapena wina aliyense amene amatengera zochita zake. Mlembi wina anatcha nthawi yathu ino “nthawi ya nkhanza,” ndipo nthawi imeneyi idzatha. Bwanji nanunso osaphunzira za chiyembekezo chimenechi kwa Mboni za Yehova?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri za makhalidwe ndi umunthu wa Mulungu, onani buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 17 Mayina ena asinthidwa.

[Bokosi patsamba 6]

Kodi Mungatani Mutachitidwa Nkhanza?

Mawu a Mulungu ali ndi malangizo othandiza a zimene mungachite mutachitidwa nkhanza. Nawa mawu anzeru amene mungagwiritse ntchito:

“Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.”​—Miyambo 20:22.

“Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa . . . , usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira.”​—Mlaliki 5:8.

“Osangalala ali iwo amene ali ofatsa, popeza adzalandira dziko lapansi.”​—Mateyo 5:5.

“Chotero zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”​—Mateyo 7:12.

“Musabwezere choipa pa choipa. Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino. Ngati n’kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Okondedwa, musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu; pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’”​—Aroma 12:17-19.

“Ngakhale Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti musatire mapazi ake mosamalitsa. . . . Pamene anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.”​—1 Petulo 2:21-23.

[Zithunzi patsamba 7]

Yehova waphunzitsa anthu ambiri kusiyiratu nkhanza