Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Akhristu ayenera kupewa zakumwa ndi zakudya monga khofi, tiyi, ndi chokoleti, zokhala ndi mankhwala a caffeine?

Baibulo sililetsa Akhristu kudya kapena kumwa zinthu zokhala ndi mankhwala amenewa. Ngakhale zili choncho, Malemba ali ndi mfundo zimene zingatithandize kusankha mwanzeru. Choyamba, tiyeni tione chifukwa chake anthu ena amapewa zakumwa ndi zakudya zoterezi.

Chifukwa chachikulu ndi chakuti anthu ena amati mankhwala amenewa ali m’gulu la mankhwala osokoneza bongo, popeza ali ndi mphamvu yochangamutsa munthu. Ndiponso amatha kumulowerera munthu. Buku lina la zamankhwala limati: “Munthu akamamwa caffeine wambiri kwa nthawi yaitali, amamulowerera moti zingamuvute kwambiri kusiya. Munthu akangoti wasiya mwadzidzidzi, amayamba kumva mutu, kunyong’onyeka, kusakhazikika mtima, nkhawa, ndi chizungulire.” Mavuto obwera chifukwa chosiya kudya kapena kumwa zinthu za mankhwalawa, akufuna kuwaika m’buku lofotokoza za matenda a maganizo pamodzi ndi mavuto obwera chifukwa chosiya mankhwala osokoneza bongo. (Diagnostic and Statistical Manual of Mental Disorders) M’pake kuti Akhristu ena amaona kuti mwina si bwino kudya kapena kumwa zinthu zokhala ndi mankhwalawa chifukwa safuna kuti awalowerere ngakhale pang’ono ndipo amafuna kukhala odziletsa.​—Agalatiya 5:23.

Anthu ena amakhulupirira kuti mankhwala amenewa angawononge thanzi la munthu ndiponso la mwana wosabadwa. Akhristu amakonda Mulungu ‘ndi moyo wawo wonse,’ choncho sachita chilichonse chimene chingafupikitse moyo wawo. Ndipo popeza amalamulidwa kukonda mnansi wawo, amapewa zinthu zimene zingavulaze mwana wosabadwa.​—Luka 10:25-27.

Kodi n’zomveka kukhala ndi nkhawa zotere? Pali kusiyana maganizo pankhani yakuti mankhwalawa amayambitsa matenda osiyanasiyana. Akatswiri ena amati khofi ndi wothandiza. Mu 2006, magazini ya Time inati: “Poyamba, kafukufuku anasonyeza kuti [caffeine] angayambitse khansa ya m’chikhodzodzo, kuthamanga kwa magazi ndi matenda ena. Koma kafukufuku waposachedwa watsutsa zimenezi komanso wasonyeza kuti mankhwalawa ndi othandiza kwambiri. Akuti amateteza munthu ku matenda a chiwindi, a manjenje, a shuga, a muubongo, a miyala m’ndulu, a maganizo, ngakhalenso mwina mitundu ina ya khansa.” Pankhani ya zinthu zokhala ndi mankhwalawa, magazini ina inati: “Nkhani yagona pa kusadya kwambiri zinthu zimenezi.”

Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha zimene angachite poganizira zimene zafalitsidwa pa nkhani ya mankhwala amenewa ndiponso mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo, mayi woyembekezera angasankhe kupewa zakumwa kapena zakudya zokhala ndi mankhwalawa ngati ataona kuti zingavulaze mwana wake wosabadwa. Ngati Mkhristu sapeza bwino akapanda kudya kapena kumwa zinthu zimenezi, ndiye kuti mankhwalawa amulowerera, ndipo ndi bwino atasiya kaye. (2 Petulo 1:5, 6) Akhristu ena alemekeze zimene wasankhazo, ndipo asamuumirize kuchita zimene iwo akufuna.

Kaya mwasankha kusiya zakudya ndi zakumwa zoterezi kapena ayi, musaiwale malangizo a Paulo akuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”​—1 Akorinto 10:31.