Masiku Ano Anthu Ali ndi Nkhanza
Masiku Ano Anthu Ali ndi Nkhanza
MARÍA anali ndi zaka 64 ndipo ankakhala yekha. Tsiku lina anapezeka atafa m’nyumba mwake, atamenyedwa ndiponso atamangiriridwa pakhosi ndi waya.
Kudera lina, gulu la anthu litalusa linamenya apolisi atatu, powaganizira kuti anaba ana awiri. Anthuwo anathira petulo apolisi awiri ndi kuwayatsa moto mpaka kupserera. Wachitatuyo anathawa.
Kudera linanso, munthu wina yemwe sanatchule dzina lake, anaimbira foni apolisi. Iwo atamva uthenga wake, anapita ku malo amene anauzidwawo ndipo zimene anakapezako zinali zoopsa. Anapeza mitembo ya amuna anayi itakwiriridwa pafupi ndi nyumba. Inali itamangidwa nsalu m’maso, ndipo manja anali omangidwa. Mitemboyo atakaiunika kuchipatala, anapeza kuti anthuwo anawakwirira amoyo. Amuna amenewo anali alendo m’deralo.
Nkhanza zafotokozedwazi ndi zochitika zenizeni osati zongoonerera m’mafilimu. Zimenezi zinachitika posachedwapa kudziko lina la kum’mwera kwa United States ndipo zinalembedwa m’nyuzi. Koma sikuti zimenezi zikuchitika ku dziko lokhali ayi.
Nkhanza zafala kwambiri masiku ano. Timamva za mabomba, uchigawenga, umbanda, kumenyana, kuwomberana, ndi za kugwirira akazi ndi ana. Ndipo zimenezi ndi nkhanza zochepa chabe. Ofalitsa nkhani amasimba mobwerezabwereza za nkhanza zosaneneka, ndipo anthu ambiri sachitanso kakasi kuona ndi kumva zinthu zimenezi.
Poona zimenezi, mungadzifunse kuti: ‘Kodi dzikoli likulowera kuti? Kodi anthu asiya kuganizirana ndi kulemekeza moyo?’ Kodi umu ndi mmene anthu azikhalira?
Sikuti anthu nthawi zonse ndi ankhanza. Iwo amatha kukhala achifundo ndi okoma mtima. Mwachitsanzo, pali Harry wazaka 69 amene wakhala akudwala khansa. Mkazi wake ali ndi matenda opha ziwalo, koma anansi ndi mabwenzi awo amabwera kudzawathandiza. Harry anati: “Sindikudziwa kuti tikanatani pakanapanda anthu amenewa.” Kwawo ku Canada, akuti anthu osamalira okalamba opitirira theka ali ndi munthu yemwe akumusamalira woti si m’bale wawo. Inunso mukudziwa anthu ena amene ali okoma mtima ndi achifundo.
Nanga bwanji kuli nkhanza? N’chifukwa chiyani anthu amachita nkhanza? Kodi anthu amene amachitira nkhanza anzawo angasinthe? Kodi nkhanza zidzathadi? Ngati yankho lake ndi inde, zidzatha bwanji ndipo liti?
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Train: CORDON PRESS