Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

M’munda Mmene “Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”

M’munda Mmene “Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”

M’munda Mmene “Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”

Kumpoto kwenikweni kwa South America kuli chilumba chotchedwa Guajira. Kwenikweni chilumbachi chili kumpoto kwa dziko la Colombia ndi kumpoto chakumadzulo kwa dziko la Venezuela. Pachilumbapa pamatentha kwambiri ndipo pamagwa mvula yochepa. Pamatha kutentha mpaka madigiri seshasi 43, moti pamaoneka ngati chipululu. Ngakhale zili choncho, anthu a pachilumbachi ndi alimi akhama kwambiri. Komabe moyo wa pachilumbachi n’ngosangalatsa chifukwa choti pamawomba mphepo ya yaziyazi yochokera ku nyanja ndiponso mphepo ya mwera. Motero, pamabwera alendo odzaona malo okongola a pachilumbachi ndi kudzasangalala ku nyanja.

TAKULANDIRANI ku dziko la amwenye otchedwa Wayuu. Padziko lonse amwenye amenewa alipo 305,000, ndipo okwana 135,000 amakhala ku Colombia. Amwenyewa akhala kumeneku kuyambira kalekale, atsamunda a ku Spain asanayambe kulamulira chigawochi.

Amwenye amenewa amadalira ulimi wa ziweto ndi mbewu zina. Ena ndi asodzi ndipo ena amachita malonda ndi anthu a m’mayiko oyandikana nawo. Akazi ali ndi luso la zolukaluka zamitundu yowala kwambiri ndipo alendo odzaona malo amakonda kugula zolukazi.

Anthu amenewa ndi oona mtima komanso odziwa kuchereza alendo. Komabe nawonso amakumana ndi mavuto a “nthawi yovuta yoikika” ino. (2 Timoteyo 3:1) Umphawi ndi vuto limodzi lalikulu kwambiri m’derali, limene limachititsanso mavuto ena. Ena mwa mavutowa n’ngakuti anthu amakhala osaphunzira ndipo amasowa chithandizo chamankhwala. Komanso ana amakhala ndi vuto losowa chakudya m’thupi ndipo m’madera ena ana amakhala opulukira.

Kwa zaka zambiri, matchalitchi achikhristu akhala akutumiza amishonale kuti akalalikire kwa amwenyewa. Motero, sukulu zambiri za aphunzitsi ndiponso zogonera komweko n’zamishoni. Panopo, ambiri mwa amwenyewa anayamba kutsatira miyambo ina yomwe amati n’njachikhristu, monga kulambira zifanizo, ndi kubatiza ana akhanda. Komabe sanasiye kutsatira miyambo ndi zikhulupiriro za makolo awo.

Awayuu ambiri amaopa Mulungu ndipo amamvetsera zedi choonadi cha m’Baibulo chimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa. Chakumayambiriro kwa m’ma 1980, ku Guajira kunali Mboni seveni zokha za Chiwayuu, ndipo zitatu zinkakhala mu likulu la chilumbachi lotchedwa Ríohacha. Kuphatikiza pa Mboni zachimwenyezi, Mboni zinanso 20 zinkalalikira uthenga wabwino kumeneku m’Chisipanishi.

Kumva Uthenga M’chinenero Chawo

Kuphatikiza pa chinenero chawo cha Chiwayuunaiki, amwenye ambiri a ku Ríohacha amalankhulanso Chisipanishi pang’ono. Poyamba, ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu siinkaphula kanthu kwenikweni. Amwenyewa sankakhala omasuka kwa anthu amene si amtundu wawo. Mboni zikafika pakhomo pawo, ambiri mwa amwenyewa ankayankha m’chinenero chawo, osati m’Chisipanishi. Zikatere, Mbonizo zinkangochoka n’kupita khomo lina.

Koma cha kumapeto kwa 1994, ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ya ku Colombia inatumiza gulu la apainiya apadera, kapena kuti aphunzitsi a nthawi zonse a Baibulo, kukatumikira mu mpingo wa Ríohacha. Apainiyawo anapempha Mboni ina yachiwayuu kuti iwaphunzitse Chiwayuunaiki. Ataloweza mawu ochepa chabe omwe anganene polalikira, iwo analowa m’gawolo ndipo nthawi yomweyo anaona kuti amwenyewa anasintha kwambiri. Ngakhale kuti apainiyawo ankalankhula Chiwayuunaiki chothyokathyoka, amwenyewo anasangalala kwambiri ndipo ankamvetsera mwachidwi. Moti nthawi zina amwenyewo ankalolera kupitiriza machezawo m’Chisipanishi chothyokathyoka.

“Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”

Mtumwi Paulo anayerekezera ntchito yopanga ophunzira ndi kulima munda. Awayuu amamvetsa bwino fanizo limeneli poti ndi alimi. (1 Akorinto 3:5-9) Motero tinganene mophiphiritsira kuti m’munda mwa Awayuu “mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.”​—Yohane 4:35.

Neil, mmwenye wina wachiwayuu amene ankakhala ku Manaure, anali ndi matenda enaake obadwa nawo. Neil ankaona kuti Mulungu ndiye anafuna kuti iye akhale ndi matendawa moti anayesapo kudzipha. Wamboni wina amene ankalalikira nyumba ndi nyumba m’madera onse amene ankapitako chifukwa cha ntchito yake yolembedwa, anakambirana ndi Neil nkhani ya Ufumu wa Yehova. Apa n’kuti Neil ali ndi zaka 14 zokha. Poona kuti Neil ali ndi chidwi, Wamboniyo anayamba kuphunzira naye Baibulo. Neil anasangalala kwambiri kudziwa kuti Yehova n’ngwachikondi, moti anazindikira kuti si Mulungu amene anachititsa kuti iyeyo akhale ndi matenda. Anakhudzidwa mtima kwambiri atawerenga za lonjezo la Mulungu lakuti dziko lapansi lidzakhala paradaiso, yemwe simudzakhalanso matenda aliwonse.​—Yesaya 33:24; Mateyo 6:9, 10.

Panthawiyo, achibale a Neil anali paudani wosamwerana madzi ndi anthu a m’banja lina kumeneku. Pofuna kudziteteza, abale ake a Neil anachita miyambo inayake yamakolo. Neil akukumbukira kuti: “Poyamba ndinkaopa kuuza achibale anga kuti ndasintha chikhulupiriro changa. Makamaka ndinkaopa kuuza aakuluakulu a pambumba yathu, omwe amapatsidwa ulemu kwambiri.” Makolo a Neil anakwiya zedi kumva kuti iye akukana kutsatira miyambo yawo chifukwa choti inali yosemphana ndi Malemba ndiponso inali yokhudzana ndi zokhulupirira mizimu. Kenaka Neil anasamukira ku Ríohacha n’kuyamba kusonkhana ndi mpingo wa kumeneko. Pambuyo pake iye anabatizidwa. Mu 1993 anaikidwa kukhala mtumiki wothandiza, ndipo patatha zaka zitatu anakhala mpainiya wokhazikika. Kenaka mu 1997 anaikidwa kukhala mkulu mumpingo. Mu 2000, anakhala mpainiya wapadera.

Taganiziraninso chitsanzo cha Teresa, mmwenye wachiwayuu amene anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Mwamuna yemwe anangolowana naye, dzina lake Daniel, ankamunyoza ndi kum’menya komanso ankakonda kumenya ana awo atatu. Ngakhale kuti patsogolo pake Daniel anavomera kuti aziphunzira Baibulo pamodzi ndi Teresa, nthawi zambiri ankagona ku mowa ndi anzake, mwina kwa masiku anayi kapena asanu. Banja lake linasauka kwambiri. Teresa anapitirizabe kuphunzira Baibulo mokhulupirika n’kumapita ku misonkhano yachikhristu. Zimenezi zinam’thandiza Daniel kuona kufunika kophunzira Baibulo. Kenaka mwana wawo mmodzi anafa atagwera mwangozi m’chidebe cha madzi owira. Teresa anali ndi chisoni chachikulu chifukwa cha imfa ya mwana wake wamwamunayo. Komanso anzake ndi anansi ake anamuvutitsa kwambiri pomukakamiza kuti atsatire miyambo inayake ya maliro yosemphana ndi Malemba.

Panthawi yovutayi, banjali linalimbikitsidwa ndi Mboni za Yehova za m’mipingo ya pafupi. Pambuyo pa malirowo, abale ndi alongo a mumpingo wa Chiwayuunaiki anapitirizabe kulimbikitsa banjali poliyendera. Ataona chikondi chimene anthu a mumpingo anawasonyeza, Daniel anayamba kulimbikira ndiponso kupita patsogolo mwauzimu. Iye anasiya kumwa mowa ndiponso kuzunza Teresa. Kenako Daniel analembetsa ukwati wake kuboma, ndipo anayamba kulimbikira ntchito kuti athe kusamalira banja. Iye ndi mkazi wake anapita patsogolo mwauzimu ndipo anabatizidwa m’chaka cha 2003. Panopo iwowa akuphunzitsa Baibulo anthu angapo. Chifukwa choti Teresa amasonyeza chitsanzo chabwino, achibale ake tsopano ayamba kulandira ndi kumvetsera anthu a Mboni akabwera kudzawalalikira. Nawo ana a achemwali ake a Daniel akupita patsogolo. Panopo, wamwamuna ndi wofalitsa wosabatizidwa, ndipo aakazi awiri akuphunzira Baibulo ndiponso amafika ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Mlongo wake wa Daniel, amenenso mwana wake anamwalira pangozi, wayamba kuphunzira Baibulo pamodzi ndi banja lake lonse.

Chakudya Chauzimu M’Chiwayuunaiki

Mu 1998, kabuku kakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! * kanatuluka m’Chiwayuunaiki. Kabuku kameneka kanakhala kothandiza kwambiri polalikira ndi pophunzitsira Baibulo. Ndipo m’chaka cha 2003, abale angapo anaphunzitsidwa kuti azimasulira mabuku athu m’Chiwayuunaiki ku Ríohacha. Tsopano pali timabuku tambiri chifukwa cha khama la abalewa. Zimenezi zathandiza kwambiri kuti anthu ophunzira Baibulo olankhula Chiwayuunaiki awonjezeke.

Kungoyambira mu 2001, nkhani zina zikamakambidwa pa misonkhano ya chigawo amazimasulira m’Chiwayuunaiki. Ndipotu anthu amene akuphunzira Baibulo amalimbikitsidwa kwambiri mwauzimu akamamvetsera nkhani m’chinenero chawochi. Anthu amenewa ali ndi chiyembekezo choti m’tsogolomu sewero la Baibulo lizidzakhalanso m’Chiwayuunaiki.

Ntchito Yolalikira Ikuyenda Bwino

Pamtunda wa makilomita 100, kumpoto cha kum’mawa kwa Ríohacha, kuli tauni yotchedwa Uribia. Mpingo wa Chiwayuunaiki wa kumeneku uli ndi ofalitsa 16, ndipo ambiri akuyesetsa kulalikira amwenye ambiri amene amakhala kumadera akumidzi. Ponena za ulendo wina woterewu, mkulu wina wa mumpingo umenewu anati: “Tinapita ku mudzi wa pafamu ina ya ziweto womwe uli ndi nyumba zowerengeka. Nyumbazi n’zifupizifupi ndipo zili ndi mawindo ang’onoang’ono. Kutsogolo kwa nyumba iliyonse kuli malo ochezera a denga la zomera zinazake za m’chipululu. Dengali limaperekanso mthunzi wabwino pocheza ndi alendo. Tinasangalala kwabasi chifukwa anthu ambiri anasonyeza chidwi, ndipo tinakonza zodzabwererakonso kuti tikayambe kuphunzira nawo Baibulo. Titabwererako, tinazindikira kuti anthu ambiri anali osadziwa kuwerenga ndi kulemba. Anthuwo anatiuza kuti kuderali kuli sukulu imene inatsekedwa chifukwa chosowa ndalama. Mkulu woyang’anira sukuluyo anatipatsa chilolezo choti tizigwiritsa ntchito kalasi imodzi pasukulupo pophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba komanso pochititsa maphunziro a Baibulo. Ndipotu zimenezi zachititsa kuti amwenye sikisi aphunzire kuwerenga ndi kulemba komanso kuti azichita bwino kwambiri pakuphunzira kwawo Baibulo. Tachita chidwi kwambiri ndi mmene anthuwa akukondera uthenga wa m’Baibulo, ndipo tikukonza zoti tizichita misonkhano kumudzi umenewu.”

Mboni zina zomwe si zachiwayuu zikuchita ntchito yotamandika kwambiri chifukwa zaphunzira Chiwayuunaiki ndipo zikuthandiza anthu a kuderali. Pachilumba cha Guajira, pali mipingo eyiti ya chinenero chimenechi komanso magulu awiri akutali.

N’zoonekeratu kuti Yehova akudalitsa khama la atumiki amenewa polalikira uthenga wabwino. Ndithudi, Awayuu ambiri angathe kuphunzira choonadi chifukwa cha ntchitoyi. Tikunena pano, Awayuu amene akuzindikira zosowa zawo zauzimu ayamba kale kukhala ophunzira a Khristu. Tikupempha Yehova kuti atumize antchito ambiri oti akakolole m’mundawu, chifukwa “mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.”​—Mateyo 9:37, 38.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mapu patsamba 16]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

VENEZUELA

COLOMBIA

LA GUAJIRA

Manaure

Ríohacha

Uribia

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

Wayuu camp below: Victor Englebert