Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mpingo Uyenera Kutamanda Yehova

Mpingo Uyenera Kutamanda Yehova

Mpingo Uyenera Kutamanda Yehova

“Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga, pakati pa mpingo ndidzakutamandani ndi nyimbo.”​—AHEBERI 2:12.

1, 2. N’chifukwa chiyani mpingo ndi wofunika kwambiri, ndipo cholinga chake chachikulu n’chiyani?

KUYAMBIRA kale kwambiri, anthu akhala otetezeka ndiponso paubale wabwino m’banja. Koma Baibulo limatchula banja lina limene anthu ake ambirimbiri padziko lonse, n’ngotetezeka ndiponso akusangalala ndi ubale wapadera kwambiri. Banja limeneli ndi mpingo wachikhristu. Kaya muli m’banja lachikondi ndi logwirizana kapena ayi, muyenera kuyamikira zimene Mulungu wapereka mu mpingo. N’zodziwikiratu kuti ngati muli mu mpingo wa Mboni za Yehova, mukuvomereza kuti mukusangalaladi ndi ubale wabwino ndiponso ndinu otetezeka.

2 Mpingo si gulu wamba, komanso si bungwe kapena gulu la anthu okonda masewera ndiponso zosangalatsa zinazake. Koma mpingo wapangidwa n’cholinga chotamanda Yehova Mulungu. Zimenezi zakhala choncho kuyambira kalekale, malinga ndi kufotokoza kwa buku la Masalmo. Ndipotu lemba la Salmo 35:18 limati: “Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu, m’chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.” Mofananamo, Salmo 107:31, 32 limatilimbikitsa kuti: “Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwiza zake za kwa ana a anthu! Am’kwezenso mu msonkhano wa anthu.”

3. Malinga ndi kunena kwa Paulo, kodi mpingo umachita chiyani?

3 Mtumwi Paulo anafotokoza cholinga china cha mpingo pamene anautcha “nyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo. Mpingowo ndiwo mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Timoteyo 3:15) Kodi Paulo ankanena za mpingo uti? Kodi mawu oti “mpingo” agwiritsidwa ntchito m’njira zotani m’Baibulo? Kodi mpingo umakhudza motani moyo ndiponso chiyembekezo chathu? Kuti tipeze mayankho, tiyeni tione mmene Baibulo limagwiritsira ntchito mawu oti “mpingo.”

4. Kodi mawu oti “mpingo” nthawi zambiri amagwiritsidwa ntchito motani m’Malemba Achiheberi?

4 Mawu achiheberi amene nthawi zambiri amamasuliridwa kuti “mpingo,” “msonkhano,” ndi “khamu” m’Baibulo la Buku Lopatulika, anachokera ku mawu omwe amatanthauza ‘kusonkhanitsa.’ (Deuteronomo 4:10; 9:10) Wamasalmo anagwiritsa ntchito mawu oti “msonkhano” ponena za angelo kumwamba, ndipo angagwiritsidwenso ntchito pofotokoza gulu la anthu oipa. (Salmo 26:5; 89:5-7) Komabe nthawi zambiri Malemba Achiheberi amagwiritsa ntchito mawuwa ponena za Aisiraeli. Yehova analonjeza kuti Yakobo adzakhala“khamu la anthu,” ndipo zinachitikadi. (Genesis 28:3; 35:11; 48:4) Aisiraeli anaitanidwa, kapena anasankhidwa kuti akhale “msonkhano wa Yehova,” “msonkhano wa Mulungu” woona.​—Numeri 20:4; Nehemiya 13:1; Yoswa 8:35; 1 Samueli 17:47; Mika 2:5.

5. Kodi ndi mawu ati achigiriki omwe amasuliridwa kuti “mpingo,” ndipo mawuwa angagwiritsidwe ntchito motani?

5 Mawu ena ofanana ndi amenewa ndi mawu achigiriki oti ek·kle·siʹa, ndipo anachokera ku mawu achigiriki otanthauza “kuitana.” Mawuwa angagwiritsidwe ntchito ponena za gulu lomwe si lachipembedzo, monga “msonkhano” umene Demetiriyo anaitanitsa ku Efeso n’cholinga chotsutsa Paulo. (Machitidwe 19:32, 39, 41) Koma Baibulo nthawi zambiri limagwiritsa ntchito mawuwa pofotokoza mpingo wachikhristu. Mabaibulo ena amamasulira mawuwa kuti “tchalitchi,” koma buku lotanthauzira mawu a m’Baibulo la The Imperial Bible-Dictionary limati, mawuwa “satanthauza nyumba yeniyeni imene Akhristu amasonkhanamo polambira.” Koma n’zochititsa chidwi kuti m’Malemba Achigiriki Achikhristu, mawu oti “mpingo” agwiritsidwa ntchito m’njira zinayi zosiyanasiyana.

Mpingo Wodzozedwa wa Mulungu

6. Kodi n’chiyani chimene Davide ndi Yesu anachita mu mpingo?

6 Pogwira mawu a Davide opezeka pa Salmo 22:22 onena za Yesu, mtumwi Paulo analemba kuti: “‘Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga, pakati pa mpingo ndidzakutamandani ndi nyimbo.’ Chotero, [Yesu] anayenera ndithu kukhala ngati “abale” ake m’zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika pa zinthu za Mulungu.” (Aheberi 2:12, 17) Davide anatamanda Mulungu pakati pa mpingo wa Isiraeli wakale. (Salmo 40:9) Koma kodi Paulo ankatanthauzanji pamene ananena kuti Yesu anatamanda Mulungu “pakati pa mpingo”? Kodi ndi mpingo uti umenewu?

7. M’Malemba Achigiriki Achikhristu, kodi mawu oti “mpingo” kwenikweni amagwiritsidwa ntchito motani?

7 Zimene timawerenga pa lemba la Aheberi 2:12, 17 n’zofunika kwambiri. Zikusonyeza kuti Khristu nayenso anali mu mpingo ndipo analengeza dzina la Mulungu kwa abale ake mu mpingowo. Kodi abale amenewo ndani? Iwo ndi abale a Khristu odzozedwa ndi mzimu, “otenga mbali m’chiitano cha kumwamba,” ndipo ali mbali ya “mbewu ya Abulahamu.” (Aheberi 2:16–3:1; Mateyo 25:40) Chotero m’Malemba Achigiriki Achikhristu, mawu oti “mpingo” kwenikweni amanena za gulu lonse la Akhristu odzozedwa ndi mzimu. Akhristu odzozedwa a 144,000 amenewa amapanga “mpingo wa woyamba kubadwayo, wa iwo amene analembedwa kumwamba.”​—Aheberi 12:23.

8. Kodi Yesu anasonyezeratu motani kuti mpingo wachikhristu udzapangidwa?

8 Yesu anasonyeza kuti “mpingo” wachikhristu umenewu udzapangidwa. Kutatsala chaka chimodzi kuti aphedwe, Yesu anauza Petulo kuti: “Iwe ndiwe Petulo, ndipo pathanthwe ili ndidzamangapo mpingo wanga, ndipo zipata za Manda sizidzaugonjetsa.” (Mateyo 16:18) Petulo ndi Paulo ankadziwa bwino ndithu kuti Yesu ndiye anali thanthwe lonenedweratu. Petulo analemba kuti anthu omwe akumangidwa kukhala “miyala yamoyo” ya nyumba yauzimu pathanthweli, lomwe ndi Khristu, anali “anthu odzakhala chuma chapadera, kuti [akalengeze] zabwino zopambana” za amene anawaitana.​—1 Petulo 2:4-9; Salmo 118:22; Yesaya 8:14; 1 Akorinto 10:1-4.

9. Kodi mpingo wa Mulungu unayamba kupangidwa liti?

9 Kodi ndi liti pamene “anthu odzakhala chuma chapadera” anayamba kupanga mpingo wachikhristu? Panali pa Pentekoste mu 33 C.E. pamene Mulungu anatsanulira mzimu woyera pa ophunzira omwe anasonkhana mu Yerusalemu. Zimenezi zitangochitika, Petulo anakamba nkhani yogwira mtima kwambiri kwa Ayuda ndiponso anthu otembenukira ku Chiyuda. Anthu ambiri anakhudzidwa mtima kwabasi atamva za kuphedwa kwa Yesu m’nkhaniyi, ndipo analapa ndi kubatizidwa. Mbiri ya m’Baibulo imasonyeza kuti anthu okwana 3,000 analapa ndi kubatizidwa. Ndipo atangochita zimenezi anakhala mu mpingo watsopano wa Mulungu womwe unali kukula. (Machitidwe 2:1-4, 14, 37-47) Mpingowu unali kukula kwambiri chifukwa Ayuda ndi anthu otembenukira ku Chiyuda anavomereza mfundo yoti mtundu wa Isiraeli sunalinso mpingo wa Mulungu. M’malo mwake, Akhristu odzozedwa omwe amapanga “Isiraeli [wauzimu] wa Mulungu” ndi amene anakhala mpingo woona wa Mulungu.​—Agalatiya 6:16; Machitidwe 20:28.

10. Kodi pali ubale wotani pakati pa Yesu ndi mpingo wa Mulungu?

10 Nthawi zambiri Baibulo limasiyanitsa Yesu ndi odzozedwa, monga m’mawu oti “ndikulankhula za Khristu ndi mpingo.” Yesu ndi mutu wa mpingo umenewu wa Akhristu odzozedwa ndi mzimu. Paulo analemba kuti Mulungu anamuika Yesu kukhala “mutu wa zinthu zonse kaamba ka mpingo, umene ndi thupi lake.”(Aefeso 1:22, 23; 5:23, 32; Akolose 1:18, 24) Masiku ano, padziko lapansi pangotsala anthu odzozedwa ochepa kwambiri mu mpingo umenewu. Koma ndife otsimikiza kuti Yesu Khristu, yemwe ali mutu wawo, amawakonda. Ndipotu, lemba la Aefeso 5:25 limafotokoza mmene Yesu amamvera ponena za iwo kuti: “Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” Iye amawakonda chifukwa choti iwo ndi akhama popereka kwa Mulungu “nsembe ya chitamando, ndiyo chipatso cha milomo . . . inde, milomo imene imalengeza dzina lake poyera,” monga mmene Yesu anachitira pamene anali padziko lapansi.​—Aheberi 13:15.

Matanthauzo Ena a Mawu oti “Mpingo”

11. Kodi Malemba Achigiriki Achikhristu amagwiritsa ntchito mawu oti “mpingo” m’njira yachiwiri iti?

11 M’Baibulo, nthawi zina mawu oti “mpingo” amagwiritsidwa ntchito ponena za kagulu kocheperapo, osati gulu lonse la Akhristu odzozedwa a 144,000 omwe apanga “mpingo wa Mulungu.” Mwachitsanzo, Paulo analembera kagulu kena ka Akhristu kuti: “Pewani kukhala okhumudwitsa kwa Ayuda, ngakhalenso kwa Agiriki, ndi mpingo wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:32) N’zodziwikiratu kuti ngati Mkhristu wa ku Korinto akanachita zinthu zosayenera akanakhumudwitsa ena. Koma kodi zikanathekadi kukhumudwitsa Agiriki, Ayuda kapena odzozedwa kuchokera nthawi imeneyo mpaka masiku ano? N’zosatheka. Motero zikuoneka kuti pa vesili, “mpingo wa Mulungu” ukutanthauza Akhristu omwe anakhalako panthawi inayake. Choncho tinganene kuti Mulungu akutsogolera, akuthandiza kapena akudalitsa mpingo, kutanthauza Akhristu onse omwe anakhalako panthawi inayake. Kapenanso tinganene za chimwemwe ndiponso mtendere zomwe zili mu mpingo wa Mulungu masiku ano, kutanthauza abale onse achikhristu.

12. Kodi m’Baibulo, mawu oti “mpingo” agwiritsidwa ntchito m’njira yachitatu iti?

12 Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti “mpingo” m’njira yachitatu ponena za Akhristu onse okhala ku dera linalake. Izi zili choncho chifukwa Baibulo limati: “Mpingo mu Yudeya yense, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo ya mtendere.” (Machitidwe 9:31) M’dera lalikulu limeneli munali magulu angapo a Akhristu. Ndipo magulu onsewa omwe anali mu Yudeya, Galileya ndi Samariya ankatchulidwa kuti “mpingo.” Tikaganizira za chiwerengero cha anthu omwe anabatizidwa pa Pentekoste mu 33 C.E. ndiponso omwe anabatizidwa pambuyo pake, zikuoneka kuti panali magulu angapo omwe ankasonkhana nthawi zonse mu Yerusalemu. (Machitidwe 2:41, 46, 47; 4:4; 6:1, 7) Herode Agiripa Woyamba analamulira Yudeya mpaka imfa yake mu 44 C.E. Ndipo lemba la 1 Atesalonika 2:14 likusonyeza bwino kuti cha m’ma 40 C.E., m’Yudeya munali mipingo ingapo. Motero tikamawerenga zoti Herode anali “kuzunza ena a mu mpingo,” zingatanthauze mipingo ingapo yomwe inali kusonkhana mu Yerusalemu.​—Machitidwe 12:1.

13. Kodi njira yachinayi ndiponso yodziwika kwambiri yomwe Baibulo limagwiritsira ntchito mawu akuti “mpingo” ndi iti?

13 Njira yachinayi ndiponso yodziwika kwambiri imene Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti “mpingo” ndi pamene limanena za kagulu kochepa kwambiri, kamene kangakhale ka Akhristu a mpingo umodzi wokha, monga amene amasonkhana m’nyumba. Paulo anatchulapo za “mipingo ya ku Galatiya.” Ndipotu m’dera lalikulu limeneli la Aroma munali mipingo ingapo. Ponena za mipingo ya kuderali, Paulo anagwiritsa ntchito kawiri mawu akuti “mipingo,” zomwe zingaphatikizepo ina yomwe inali ku Antiokeya, Debe, Lusitara, ndi Ikoniyo. Akulu oyenerera kapena kuti oyang’anira anaikidwa mu mipingo imeneyi. (1 Akorinto 16:1; Agalatiya 1:2; Machitidwe 14:19-23) Malinga ndi kunena kwa Malemba, mipingo yonseyo inali “mipingo ya Mulungu.”​—1 Akorinto 11:16; 2 Atesalonika 1:4.

14. Kodi tinganene chiyani tikaona mmene mawu akuti “mpingo” agwiritsidwira ntchito m’Malemba?

14 Nthawi zina, anthu opezeka pamisonkhano yachikhristu ankakhala ochepa, ongokwana m’nyumba ya munthu. Ngakhale zinali choncho, mawu akuti “mpingo” amatanthauzabe magulu otero. Mipingo yodziwika yotero inali m’nyumba ya Purisika ndi Akula, Numfa, ndi Filemoni. (Aroma 16:3-5; Akolose 4:15; Filemoni 2) Masiku ano, zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri ku mipingo imene ili yaing’ono ndiponso yomwe imasonkhana m’nyumba ya munthu. M’nthawi ya atumwi, Yehova ankawerengera mipingo yaing’ono yoteroyo. Masiku anonso Yehova amawerengera mipingo ing’onoing’ono ndipo amaidalitsa ndi mzimu wake.

Mipingo Imatamanda Yehova

15. Kodi mzimu woyera unaonekera motani kuti unkagwira ntchito m’mipingo ina yoyambirira?

15 Taona kale kuti Yesu anatamanda Mulungu pakati pa mpingo kuti akwaniritse lemba la Salmo 22:22. (Aheberi 2:12) Otsatira ake okhulupirika anafunikira kuchita chimodzimodzi. M’nthawi ya atumwi pamene Akhristu anadzozedwa ndi mzimu woyera kuti akhale ana a Mulungu ndiponso abale a Khristu, mzimu woyera unayamba kugwira ntchito mwapadera kwa ena a iwo. Akhristuwo analandira mphatso zapadera za mzimu woyera. Mphatso zapaderazi zinali mawu a nzeru kapena kuzindikira, mphamvu yochiritsa ndi kunenera, ngakhale mphamvu yotha kulankhula malilime osadziwika kwa iwo.​—1 Akorinto 12:4-11.

16. Kodi cholinga chimodzi cha mphatso zapadera za mzimu woyera n’chiyani?

16 Ponena za kulankhula malilime, Paulo anati: “Ndiimbe chitamando ndi mphatso ya mzimu, koma ndiimbenso ndi maganizo anga.” (1 Akorinto 14:15) Iye anazindikira kuti anthu ena anafunika kumva mawu ake kuti anthuwo alangizidwe. Cholinga cha Paulo chinali kutamanda Yehova mu mpingo. Iye analimbikitsa anthu ena omwe anali ndi mphatso za mzimu woyera kuti: “Yesetsani kukhala nazo zochuluka kuti mumange mpingo,” kutanthauza mpingo umene ankasonyezako mphatsozo. (1 Akorinto 14:4, 5, 12, 23) N’zoonekeratu kuti Paulo ankachita chidwi ndi mipingo chifukwa ankadziwa kuti mu mpingo uliwonse, Akhristu anali ndi mwayi wotamanda Mulungu.

17. Kodi ndi madalitso ati omwe timawalandira masiku ano m’mipingo yathu?

17 Yehova akupitirizabe kuthandiza ndiponso kugwiritsira ntchito mpingo wake. Iye akudalitsa gulu lonse la Akhristu odzozedwa omwe ali padziko lapansi masiku ano. Zimenezi zikuoneka chifukwa cha chakudya chauzimu chochuluka chimene anthu a Mulungu akulandira. (Luka 12:42) Ndipotu iye akudalitsa gulu lonse la abale padziko lapansi. Ndiponso akudalitsa mipingo, imene timasonkhanako kuti titamande Mlengi wathu mwa zochita ndi zolankhula zathu zolimbikitsa. Zimene timaphunzitsidwa ku mipingoyi, zimatithandiza kuti tizitha kutamandabe Mulungu ngakhale panthawi ina pamene sitili ndi mpingo wathu ndipo tikuchita zinthu zina.

18, 19. Kodi mu mpingo uliwonse Akhristu odzipereka afunikira kuchita chiyani?

18 Takumbukirani kuti mtumwi Paulo anauza Akhristu mu mpingo wa ku Filipi, ku Makedoniya kuti: “Ine ndikupitiriza kupemphera kuti . . . mudzazidwe ndi zipatso zolungama zodzera mwa Yesu Khristu, kuti Mulungu akalemekezedwe ndi kutamandidwa.” Zimenezi zinatanthauza kulankhula ndi anthu ena za chikhulupiriro chawo mwa Yesu ndiponso chiyembekezo chawo chosangalatsa. (Afilipi 1:9-11; 3:8-11) Motero Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Kudzera mwa [Yesu], tiyeni nthawi zonse tipereke kwa Mulungu nsembe ya chitamando, ndiyo chipatso cha milomo yathu, inde, milomo imene imalengeza dzina lake poyera.”​—Aheberi 13:15.

19 Kodi mumasangalala potamanda Mulungu “pakati pa mpingo,” monga mmene Yesu anachitira? Ndipo kodi mumasangalalanso potamanda Yehova mwa kulalikira kwa anthu omwe panopo sanam’dziwebe ndipo sakum’tamanda. (Aheberi 2:12; Aroma 15:9-11) Mayankho athu angadalire mmene ifeyo timaonera kufunika kwa mpingo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. M’nkhani yotsatira, tiona mmene Yehova akutsogolerera ndi kugwiritsira ntchito mpingo wathu, ndiponso mmene tingaonere kufunika kwa mpingo m’moyo wathu masiku ano.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi “mpingo wa Mulungu” wa Akhristu odzozedwa unapangidwa motani?

• Kodi m’Baibulo, mawu akuti “mpingo” agwiritsidwa ntchito m’njira zina zitatu ziti?

• Ponena za mpingo, kodi Davide, Yesu, ndi Akhristu a m’nthawi ya atumwi anafunikira kuchita chiyani, ndipo zimenezi zikutikhudza motani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Kodi Yesu anali maziko a mpingo uti?

[Chithunzi patsamba 23]

Magulu a Akhristu ankakumana monga “mipingo ya Mulungu”

[Chithunzi patsamba 24]

Mofanana ndi Akhristu a ku Benin, tingatamande Yehova pamisonkhano