Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wolemala Koma Wodzipereka

Wolemala Koma Wodzipereka

Wolemala Koma Wodzipereka

MUKANGOMUONA Leonardo, simungakhulupirire kuti amagwira ntchito ya zomangamanga. Alibe manja. Manja ake anaduka pa ngozi kuntchito. Ngakhale zili choncho, mungaone pa chithunzipa kuti Leonardo anali kugwira ntchito yomanga ku Acajutla, ku El Salvador.

Kuti azigwira nawo ntchito yomangamanga, Leonardo anapangitsa zida zakezake. Anapangitsa kachitsulo kenakake kamene anakamangirira kumbali ina ya fosholo. Ndiye ankalowetsa mkono wake wamanja m’kachitsuloka ndipo amalaisha dothi kuliponyera mu wilibala. Kogwirira anamangirirako tizitsulo timene amalowetsamo mikono pokankha wilibala. N’chifukwa chiyani anadzipereka kugwira nawo ntchito imeneyi?

Kumene Leonardo amakhala, kunali ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu, kapena kuti malo amene Mboni za Yehova zimalambiriramo, ndipo iye anafuna kugwira nawo ntchitoyo. Iye anali ndi zifukwa zambiri zomveka zoti asagwire nawo ntchitoyo. Anali pa ntchito yolembedwa, anali wolemala, ndipo anali mtumiki wothandiza mumpingo. Ngakhale zinali choncho, anafunabe kutumikira Mulungu pantchitoyo.

Kodi nanunso muli ndi mtima womwewu potumikira Mulungu? Leonardo akanafuna, akanatenga chilema chake ngati chifukwa choti asagwirire ntchitoyo, koma anagwiritsa ntchito nzeru zake kupangitsa zida zakezake kuti agwire nawo ntchito imene sakanatha. Anali kutumikira Mulungu ‘ndi maganizo ake onse.’ (Mateyo 22:37) Kaya akhale olemala kapena ayi, padziko lonse anthu amene amagwira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova amakhala ndi mtima wodzipereka. Misonkhano imene imachitika ku Nyumba za Ufumu ndi ya onse, ndi inu nomwe.