Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinthu Chofunika Kuchidziwa Kuposa Zanyengo

Chinthu Chofunika Kuchidziwa Kuposa Zanyengo

Chinthu Chofunika Kuchidziwa Kuposa Zanyengo

PAFUPIFUPI mtundu uliwonse wa anthu uli ndi miyambi yokhudza zanyengo. Mwambi wina umati: ‘Ili kutali mvula, mpesa umera m’ng’amba.’ Koma odziwa zanyengo masiku ano amafotokoza zanyengo mogwirizana ndi za m’mabuku.

M’nthawi ya Yesu, anthunso ankakonda kuyang’ana mmene kunja kulili kuti adziwe mmene nyengo ikhalire. Yesu anauza Ayuda ena kuti: “Kunja kukamada munazolowera kunena kuti, ‘nyengo yake ikhala yabwino, chifukwa kuthambo kwachita cheza’; koma mmawa mumanena kuti, ‘lero kukuoneka kuti kugwa mvula, chifukwa kuthambo kwachita cheza, koma kuli mdima wamvula.’ Mumadziwa kumasulira kaonekedwe ka thambo, koma . . . “ Koma chiyani? Yesu anapitiriza kunena mawu ochititsa chidwi awa: “Simungathe kumasulira zizindikiro za nthawi ino.”​—Mateyo 16:2, 3.

Kodi “zizindikiro za nthawi ino” n’chiyani? Ndi umboni woonekeratu wosonyeza kuti Yesu anali Mesiya weniweni wotumizidwa ndi Mulungu. Zochita zake zinali zoonekeratu monga dzuwa kumwamba. Komabe, Ayuda ambiri ananyalanyaza zizindikiro zosonyeza kuti Mesiya anali atabwera ndipotu izi zinali zofunika kuposa zanyengo.

Masiku anonso, pali chizindikiro chofunika kuchimvetsa kuposa kuyenda kwa dzuwa kumwamba. Yesu analosera kuti dziko loipali lidzawonongedwa kuti pabwere dziko labwino. Iye anatchulapo zinthu zingapo zimene zidzasonyeze kuti kuwonongedwa kumeneku kwatsala pang’ono. Zinthuzi anati zizidzachitika panthawi imodzi. Zina mwa izo ndizo nkhondo za padziko lonse ndi njala. Iye anati zizindikiro zimenezi zikadzayamba kuoneka, ndiye kuti nthawi ya Mulungu yowononga dzikoli yayandikira.​—Mateyo 24:3-21.

Kodi inuyo mukutha kuona “zizindikiro za nthawi ino“?