“Ambuye, N’chifukwa Chiyani Simunachitepo Kanthu?”
“Ambuye, N’chifukwa Chiyani Simunachitepo Kanthu?”
AWATU ndi mawu omwe Papa Benedikito wa chi 16 ananena pa May 28, 2006, atafika ku malo amene kale anali ndende yozunzirako anthu ku Auschwitz, m’dziko la Poland. Ali ku malo amenewa, omwe Anazi anapherako Ayuda miyandamiyanda pamodzi ndi anthu ena, iye anati: “Anthu akafika pa malowa amadzifunsa mafunso ambirimbiri. Nthawi zambiri amadzifunsa kuti: “Kodi Mulungu anali kuti panthawiyi? N’chifukwa chiyani sanachitepo kanthu? N’chifukwa chiyani analola kuti zinthu ziipe chonchi, mpaka anthu miyandamiyanda kuphedwa? . . . Tiyenera kupitirizabe kum’dandaulira Mulungu modzichepetsa koma mofuula kuti: Chonde chitanipo kanthu! Musaiwale anthu omwe munalenga.”
Mawu a Papawa anachititsa anthu ambiri kunenapo maganizo awo osiyanasiyana. Ena anaona kuti iye anazemba kutchula zinthu zina, monga kuzunzidwa kwa Ayuda ku Auschwitz. Pamene ena anaona kuti mawuwo anali onyalanyaza pempho la Papa Yohane Paulo Wachiwiri, loti anthu akhululuke machimo omwe tchalitchi chinachita. Mtolankhani wachikatolika, Filippo Gentiloni, anati: “Funso limene papayu anafunsa lakuti, kodi Mulungu anali kuti panthawiyi, n’lovuta kwambiri. M’pake kuti anthu amene anafunsidwa kuti anenepo maganizo awo pafunsoli, ankayankha kuti funso limene iwowo akufuna liyankhidwe ndi funso losavuta lakuti, nanga Papa Payasi wa chi 12 anali kuti?” Pamenepa anthuwo ankatanthauza kuti n’chifukwa chiyani Papa Payasi wa chi 12 sanachitepo kanthu panthawi yomwe Anazi ankapha anthu ambirimbiriyi.
Anthu ambirimbiri amene anaphedwa ndi Anazi ndiponso kuphedwa kwa anthu miyandamiyanda komwe kwachitika m’mbiri yonse ya anthu, kumatsimikizira mfundo yakuti “wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Ndipotu, Mlengi wathu sanakhale chete pamene nkhanza zimenezi zinkachitika. Kudzera m’Baibulo, iye wafotokoza zifukwa zimene walolera zoipa komanso watitsimikizira kuti sanatiiwale ayi. Ndipotu nthawi imene Mulungu walola anthu kudzilamulira itha posachedwapa. (Yeremiya 10:23) Kodi mukufuna kudziwa zambiri zokhudza zimene Mulungu adzatichitire? Mboni za Yehova zingakonde kukuthandizani kupeza yankho lochokera m’Baibulo la mafunso amene anaimitsa mutu Papa Benedikito wa chi 16.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Oświęcim Museum