Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Inuyo Mumayembekezeradi Kuti Akufa Adzauka?

Kodi Inuyo Mumayembekezeradi Kuti Akufa Adzauka?

Kodi Inuyo Mumayembekezeradi Kuti Akufa Adzauka?

“Kudzakhala kuuka” kwa akufa.​—MACHITIDWE 24:15.

1. N’chifukwa chiyani imfa imaoneka kuti n’njosapeweka?

“CHILICHONSE m’dzikoli n’chopeweka kupatulapo imfa ndi misonkho.” Mawu amenewa analembedwa mu 1789 ndi mtsogoleri wakale wa dziko la United States a Benjamin Franklin. Anthu ambiri amaona kuti awa ndi mawu anzeru kwambiri. Ngakhale zili choncho, pali anthu ambiri akatangale amene amazemba misonkho. Komatu palibe munthu amene amazemba imfa. Patokha, palibe aliyense amene angazembe imfa mpaka kalekale. Imfa imatsata munthu aliyense. Manda amameza anzathu ndi achibale athu ndipo sakhuta ayi. (Miyambo 27:20) Komano pali mfundo ina yolimbikitsa yoti muiganizire.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani imfa ili yopeweka ndithu ngakhale kuti anthu ambiri saganiza choncho? (b) Kodi m’nkhani ino tikambirana chiyani?

2 Mawu a Yehova amatipatsa chiyembekezo chosakayikitsa chakuti akufa adzauka, n’kukhalanso ndi moyo. Izi si zongolakalaka chabe, ndipotu palibe chilichonse m’chilengedwe chonse chimene chingaletse Yehova kukwaniritsa zimenezi. Motero ngakhale kuti anthu ambiri masiku ano amaona kuti imfa ndi chinthu chosapeweka, pali anthu ena amene amaona kuti n’njopeweka ndithu. N’chifukwa chiyani amaona choncho? N’chifukwa choti “khamu lalikulu” ndiponso losawerengeka lidzapulumuka “chisautso chachikulu” chimene chichitike posachedwapa. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14) Iwowa adzapitiriza kukhala pa dziko pano ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha. Motero, kwa iwo imfa si chinthu chosapeweka ayi. Ndipotu “Imfa . . . idzawonongedwa.”​—1 Akorinto 15:26.

3 Tizitsanzira Paulo posakayika ngakhale pang’ono kuti akufa adzauka. Iye anati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Tiyeni tikambirane mafunso atatu okhudza kuuka kwa akufa. Funso loyamba n’lakuti, kodi n’chifukwa chiyani chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chili chosakayikitsa ngakhale pang’ono? Lachiwiri n’lakuti, kodi inuyo panokha mungalimbikitsidwe bwanji ndi chiyembekezochi? Ndipo lachitatu n’lakuti, kodi chiyembekezo chimenechi chingakukhudzeni bwanji panopa?

Chiyembekezochi N’chosakayikitsa Ngakhale Pang’ono

4. Kodi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa n’chofunika motani pa cholinga cha Yehova?

4 Pali zifukwa zingapo zimene zimatsimikizira kuti chiyembekezo cha kuuka kwa akufa n’chosakayikitsa ngakhale pang’ono. Chifukwa chachikulu kwambiri n’chakuti, chiyembekezochi n’chofunikira kwambiri kuti cholinga cha Yehova chikwaniritsidwe. Kumbukirani kuti Satana anachimwitsa anthu, ndipo kuchimwako kunawabweretsera imfa. Motero Yesu ananena za Satana kuti: “Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake.” (Yohane 8:44) Koma Yehova analonjeza kuti “mkazi” Wake kapena gulu lake la kumwamba, lomwe amalifanizira ndi mkazi lidzabereka “mbewu” imene idzalalire mutu wa “njoka yakale ija,” kapena kuti kuwonongeratu Satana moti asadzakhalekonso. (Genesis 3:1-6, 15; Chivumbulutso 12:9, 10; 20:10) Yehova anayamba kuvumbula pang’onopang’ono cholinga chake chokhudza Mbewu yaumesiya ndipo zinaoneka kuti Mbewuyi idzachita zambiri osati kungowononga Satana basi. Mawu a Mulungu amati: “Choncho, Mwana wa Mulungu anaonekera, kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yohane 3:8) Imfa yobwera chifukwa cha uchimo umene tinayamwira kwa Adamu ndiyo ntchito yaikulu kwambiri mwa ntchito zonse za Satana zimene Yehova wakonza kudzachotsa, pogwiritsa ntchito Yesu Khristu. Nsembe ya dipo ya Yesu ndiponso kuuka kwa akufa n’kofunika kwambiri kuti zimenezi zidzatheke.​—Machitidwe 2:22-24; Aroma 6:23.

5. Kodi kuuka kwa akufa kudzalemekeza motani dzina la Yehova?

5 Yehova akufunitsitsa kulemekeza dzina lake. Satana ananena bodza loipitsa dzina la Mulungu ndiponso wakhala akulimbikitsa mabodza osiyanasiyana. Iye ananama kuti ngati Adamu ndi Hava atadya chipatso chimene Mulungu anawaletsa, ‘sadzafa ayi.’ (Genesis 2:16, 17; 3:4) Kuyambira panthawiyi, Satana wakhala akufalitsa mabodza ambiri otere, monga bodza lakuti pali chinachake mwa munthu chimene sichifa munthuyo akamwalira. Koma Yehova adzavumbula mabodza onsewa mwa kuukitsa akufa. Adzapereka umboni wakuti iyeyo ndiye Wosunga ndiponso Wobwezeretsa moyo ndipo umboniwu udzakhalapo mpaka kalekale.

6, 7. Kodi Yehova amamva bwanji pankhani ya kuukitsa akufa, ndipo timadziwa bwanji mmene iye amamvera?

6 Yehova akufunitsitsa kudzaukitsa akufa. Baibulo limanena momveka bwino mmene Yehova amamvera pa nkhaniyi. Mwachitsanzo, taganizirani mawu otsatirawa, amene munthu wokhulupirika Yobu, analemba mouziridwa: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga. Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; Mukadakhumba ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:14, 15) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani?

7 Yobu ankadziwa kuti akadzamwalira, adzadikira kaye kwa nthawi ndithu kuti adzaukitsidwe. Nthawi imeneyi ankaiona ngati nthawi yosapeweka koma yokhala ndi mapeto ake. Sankakayika ngakhale pang’ono kuti pamapeto pake adzatuluka m’manda. Yobu ankadziwa kuti adzapeza mpumulo. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti ankadziwa mmene Yehova amamvera. Ankadziwa kuti Yehova ‘adzakhumba’ kuonanso mtumiki wake wokhulupirika. Inde, Mulungu amafuna kwambiri kuukitsa anthu onse olungama. Yehova adzaperekanso mwayi kwa ena kuti akhale m’Paradaiso padziko lapansi kwamuyaya. (Luka 23:43; Yohane 5:28, 29) Ichitu ndi cholinga cha Mulungu, ndiye kodi ndani angamuletse kuchikwaniritsa?

8. Kodi Yehova “wapereka chitsimikizo” m’njira yotani pankhani ya chiyembekezo chathu?

8 Kuukitsidwa kwa Yesu kumachititsa kuti chiyembekezo chathu chikhale chosakayikitsa ngakhale pang’ono. Polankhula kwa anthu aku Atene, Paulo anati: “[Mulungu] wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa munthu amene iye wamuika. Ndipo wapereka chitsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa kwa akufa.” (Machitidwe 17:31) Ena mwa anthu omvetserawo ananyodola Paulo chifukwa chonena za kuuka kwa akufa. Koma anthu ambiri ndithu anakhulupirira. N’kutheka kuti anachita chidwi kumva kuti chiyembekezo chimenechi n’chosakayikitsa ngakhale pang’ono. Mwa kuukitsa Yesu, Yehova anachita chozizwitsa choposa zonse. Anam’chotsa Mwana wakeyo muimfa n’kumusandutsa munthu wauzimu wamphamvu kwambiri. (1 Petulo 3:18) Yesu anaukitsidwa ndi ulemerero waukulu kwambiri kuposa umene anali nawo asanabwere padziko pano. Panopo Yesu ali ndi moyo wosafa ndipo ndi wachiwiri kwa Yehova yekha basi, motero ndi woyenerera kulandira maudindo apamwamba zedi kwa Atate ake. Yesu ndiyo njira imene Yehova amagwiritsa ntchito poukitsa anthu onse, kaya okakhala kumwamba kapena odzakhala padziko pano. Yesu mwini ananena kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” (Yohane 5:25; 11:25) Poukitsa Mwana wake, Yehova anali kupereka chitsimikizo choti aliyense wokhulupirika ayembekezere zimenezi.

9. Kodi umboni wolembedwa m’Baibulo umatitsimikizira bwanji kuti akufa adzaukadi?

9 Anthu aonapo kuuka kwa akufa ndipo nkhani zotere zalembedwa m’Mawu a Mulungu. M’Baibulo muli nkhani zatsatanetsatane za anthu eyiti amene anaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo padziko lapansi. Zozizwitsa zimenezi sizinachitike mwakabisira, koma nthawi zambiri zinkachitika anthu ena akuona. Yesu anaukitsa Lazaro, amene anali atamwalira kwa masiku anayi, ndipo anamuukitsira pa gulu la anthu olira maliro, pomwe mosalephera panali achibale ake, anzake, ndi anthu omwe ankakhala nawo pafupi. Uwu unali umboni woonekeratu wakuti Yesu anatumizidwa ndi Mulungu moti ngakhale adani a Yesu achipembedzo sanatsutse kuti Yesu anaukitsa munthu. M’malo mwake anakonza chiwembu chopha Yesu komanso Lazaroyo. (Yohane 11:17-44, 53; 12:9-11) Inde, tisakayike ngakhale pang’ono kuti akufa adzaukadi. Mulungu watipatsa umboni wolembedwa wa anthu amene anaukitsidwapo kalelo ndipo watero kuti atitonthoze ndi kulimbitsa chikhulupiriro chathu.

Kulimbikitsidwa ndi Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa

10. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tilimbikitsidwe ndi nkhani za m’Baibulo za kuuka kwa akufa?

10 Kodi mumafuna kulimbikitsidwa moyo wanu ukakhala pangozi? Chinthu chimodzi chosakayikitsa chimene chingatilimbikitse ndicho nkhani za kuuka kwa akufa zomwe zili m’Baibulo. Kuwerenga nkhani zimenezi ndi kuzisinkhasinkha, kungatithandize kuona kuti chiyembekezo cha kuuka kwa akufa n’chenichenidi. (Aroma 15:4) Zimenezi si nkhani zongopeka ayi. Zinachitikadi kwa anthu ngati ifeyo, omwe ankakhala padziko lapansi pompano. Tiyeni tione mwachidule nkhani imodzi yotere. Iyi ndi nkhani yosimba za kuuka koyamba kolembedwa m’Baibulo.

11, 12. (a) Kodi mayi wamasiye wa ku Zarefati anakumana ndi tsoka lotani, ndipo mayiyu anatani zimenezi zitangochitika? (b) Fotokozani mphamvu zimene Yehova anapatsa mneneri wake Eliya pofuna kuti athandize mayi wamasiyeyo.

11 Taganizirani zimene zinachitika. Mneneri Eliya anali atakhala ku nyumba kwa mayi wina wamasiye wa ku Zarefati, ndipo ankakhala m’chipinda chosanja cha nyumbayo. Iyi inali nthawi yovuta zedi. M’dera lonselo munali chilala ndi njala moti anthu ambiri anali kufa. Panthawiyo Yehova anagwiritsira ntchito Eliya kuchita chozizwitsa china kwa nthawi yaitali pofuna kuyamikira chikhulupiriro cha mayi wamasiye wodzichepetsayo. Mayiyo ndi kamwana kake anangotsala pang’ono kufa ndi njala, chifukwa anatsala ndi chakudya chodya nthawi imodzi basi. Zitatero, Mulungu anapatsa mphamvu Eliya yochita chozizwitsa kuti ufa ndi mafuta a mayiyu asathe. Komano anakumana ndi vuto lina lalikulu. Mwana uja anadwala mwadzidzidzi mpaka anasiya kupuma. Mayiyo ayenera kuti anasokonezeka kwabasi. Umasiye wakewo pawokha unali vuto lalikulu kwabasi, ndiye taganizirani mmene anamvera mwana wake yekhayo atamwaliranso. Chisoni chinam’kulira kwambiri moti mpaka anayamba kuimba mlandu Eliya ndi Mulungu wake, Yehova. Kodi pamenepa mneneriyo anatani?

12 Eliya sanadzudzule mayi wamasiyeyo chifukwa choloza chala anthu olakwika. M’malo mwake iye anati: “Ndipatse mwana wako.” Ndiye atatenga mwana wakufayo n’kupita naye m’chipinda chosanja chija, Eliya anapemphera nthawi zingapo kuti moyo wa mwanayo ubwererenso. Mapeto ake Yehova anamva pempherolo. Taganizirani chimwemwe chimene Eliya anali nacho poona kuti mwanayo wayambiranso kupuma. Mwanayo anatsegula maso, ndipo anayamba kuphethira mosonyezeratu kuti ali moyo. Eliya anatenga mwanayo n’kum’pititsa kwa mayi ake, n’kunena kuti: “Taona, mwana wako ali moyo.” Apatu chimwemwe cha mayiyo chinali chosasimbika. Iye anati: “Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mawu a Yehova ali mkamwa mwanuwo n’ngoona.” (1 Mafumu 17:8-24) Chikhulupiriro chake mwa Yehova ndiponso mwa anthu ake chinakula kwambiri kuposa kale.

13. Kodi nkhani ya Eliya youkitsa mwana wa mayi wamasiye imatilimbikitsa bwanji masiku ano?

13 Kusinkhasinkha nkhani zotere kumalimbikitsa kwambiri. N’zoonekeratu kuti Yehova angathe kugonjetsa mdani wathu imfa. Tangoganizirani tsiku limene chimwemwe cha mayiyu chidzachite kudzadza tsaya panthawi imene anthu onse azidzaukitsidwa. Inde, kumwamba nako kudzakhala kusangalala zedi chifukwatu Yehova akufunitsitsa kuuza Mwana wake kuti adzaukitse anthu padziko lonse. (Yohane 5:28, 29) Kodi pali m’bale wanu kapena mnzanu amene wamwalira? N’zosangalatsa zedi kudziwa kuti Yehova angathe kuukitsa akufa ndipo adzaterodi.

Mmene Chiyembekezochi Chimakhudzira Moyo Wanu Panopo

14. Kodi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chingakhudze bwanji moyo wanu?

14 Kodi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chingakhudze bwanji moyo wanu panopo? Chiyembekezo chimenechi chingakulimbitseni mtima kwambiri mukamakumana ndi zovuta zosiyanasiyana, mukamazunzidwa, kapena moyo wanu ukakhala pangozi. Satana amafuna kuti imfa muziiopa kwambiri moti muzilolera kuchita zosakhulupirika pofuna kukhala otetezeka. Musaiwale kuti Satana anauza Yehova kuti: “Munthu adzapereka zonse ali nazo kuwombola moyo wake.” (Yobu 2:4) Ponena mawu amenewa, Satana anatinamizira anthu tonse, kuphatikizapo inuyo. Kodi n’zoona kuti mungasiye kutumikira Mulungu ngati moyo wanu utakhala pangozi? Posinkhasinkha za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, mungathe kukhala wotsimikiza mtima kupitiriza kuchita chifuniro cha Atate wanu wakumwamba.

15. Kodi mawu a Yesu opezeka pa Mateyo 10:28 angatilimbitse mtima bwanji moyo wathu ukakhala pangozi?

15 Yesu anati: “Ndipo musachite mantha ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo; m’malo mwake, muziopa iye amene angathe kuwononga zonse ziwiri, moyo ndi thupi lomwe m’Gehena.” (Mateyo 10:28) Satana kapenanso anthu ake tisamawaope. N’zoona kuti ena angathe kutivulaza, ngakhale kutipha kumene. Komabe, zimene angatichitezo n’zakanthawi basi. Yehova angathe kukonza choipa chilichonse chimene atumiki ake achitidwa, ngakhale kuphedwa kumene. Ndipotu izi n’zimene Yehova adzachite. Ndi Yehova yekha amene tiyenera kumuopa ndi kumulemekeza kwambiri. Ndi Yehova yekha amene angathe kuchotsa moyo ndi chiyembekezo chilichonse chodzakhala kosatha, chifukwa angathe kuwononga thupi ndi moyo mu Gehena. Koma n’zosangalatsa kuti Yehova safuna kuti zimenezi zidzakuchitikireni inuyo. (2 Petulo 3:9) Chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, atumiki a Mulungufe tisamakayike ngakhale pang’ono kuti ndife otetezeka. Moyo wosatha ukutidikira ngati tikhalebe okhulupirika, ndipo palibe chimene Satana ndi om’tsatira ake angachite kuti aletse zimenezi.​—Salmo 118:6; Aheberi 13:6.

16. Kodi zimene timakhulupirira pa kuuka kwa akufa zimatikhudza bwanji tikamaganizira zinthu zofunikira kwambiri kuzichita pamoyo wathu?

16 Ngati sitikayika n’komwe za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, moyo wathu umakhala wopanda nkhawa. Timadziwa kuti “kaya tikhala ndi moyo kapena tifa, ndife a Yehova.” (Aroma 14:7, 8) Motero, tikamaganizira za zinthu zofunikira kwambiri zoti tichite pamoyo wathu timakumbukira malangizo a Paulo akuti: “Musamatengere nzeru za dongosolo lino la zinthu, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Anthu ambiri mitima yawo imakhala dyokodyoko ndi zinthu zilizonse zimene maso awo adyerera. Chifukwa choti amaona kuti moyo n’ngwaufupi zedi, amalimbana kwambiri ndi kuchita zinthu zosangalatsa, ndipo ngakhale amalambira, satero mogwirizana ndi ‘chifuniro changwiro cha Mulungu.’

17, 18. (a) Kodi Mawu a Yehova amasonyeza bwanji kuti moyo wa munthu n’ngwaufupi zedi, komano kodi Mulungu akufuna kuti tidzakhale ndi moyo wotani? (b) N’chiyani chimatipangitsa kuti tizifuna kutamanda Yehova tsiku lililonse?

17 N’zoonadi kuti moyo n’ngwaufupi. ‘Umapita msanga’ kwambiri, mwina pakangodutsa zaka 70 kapena 80 basi. (Salmo 90:10) Anthu sakhalitsa ayi; ali ngati msipu wobiriwira, kapena ngati mthunzi wosakhalitsa, kapenanso mpweya wotuluka popuma. (Salmo 103:15; 144:3, 4) Koma sichinali cholinga cha Mulungu kuti tizibadwa n’kukhala ndi moyo kwa zaka makumi angapo mpaka kufika pokhala anthu aakulu, anzeru zawo ndiponso odziwa zinthu, koma kenaka zaka makumi angapo zotsalazo tiziyamba kulimbana ndi mavuto a m’thupi mpaka kufika pomwalira. Yehova analenga anthu ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo wosatha. Baibulo limatiuza kuti: “Waika zamuyaya m’mitima yawo.” (Mlaliki 3:11) Kodi Mulungu angachite nkhanza zotipatsa mtima wofuna moyo wosatha komano n’kusatipatsa moyo wotero? Ayi ndithu, chifukwatu “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Iye adzaukitsa anthu akufa kuti athe kukhala ndi moyo wosatha.

18 Chifukwa cha chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, tsogolo lathu n’losakayikitsa. Palibe chifukwa choti panopo tizilimbana ndi kuchita zinthu zilizonse zimene tingathe kuchita pa moyo wathu. Tisalimbane ndi ‘kugwiritsa ntchito mokwanira’ dziko limene likupitali. (1 Akorinto 7:29-31; 1 Yohane 2:17) Sitili ngati anthu opanda chiyembekezo, chifukwa choti tili ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri podziwa kuti tikapitiriza kukhala okhulupirika kwa Yehova Mulungu, tidzakhala tikumutamanda kosatha n’kumasangalala ndi moyo. Motero tiyeni tiyesetse kwambiri kutamanda Yehova tsiku lililonse, chifukwa iyeyu ndiye watheketsa kuti akufa adzauke.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chiyenera kutikhudza motani mumtima mwathu?

• Kodi ndi zifukwa zotani zimene zimatsimikizira kuti chiyembekezo cha kuuka kwa akufa n’chosakayikitsa ngakhale pang’ono?

• Kodi mungalimbikitsidwe bwanji ndi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa?

• Kodi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chingakhudze bwanji zochita zanu pamoyo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 28]

Yobu ankadziwa kuti Yehova amafunitsitsa kudzaukitsa olungama

[Chithunzi patsamba 29]

“Taona, mwana wako ali moyo”