Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaopa Zam’tsogolo?

Kodi Mumaopa Zam’tsogolo?

Kodi Mumaopa Zam’tsogolo?

ANTHU amaopa zinthu zambirimbiri. Mwachitsanzo, anthu ena akuopa kuti, kodi dzikoli lidzakhala lotani m’tsogolo. Magazini ya Time ya April 3, 2006 inati: “Nyengo ikusokonekera kwambiri padziko lonse. Madera ena akutentha kwadzaoneni, kwina kukuchitika mvula zamkuntho, madzi akusefukira, nkhalango zambiri zikupsa, ndipo madera a madzi oundana akusungunuka.”

Mu May chaka cha 2002, bungwe loona za chilengedwe la United Nations Environment Programme linatulutsa chikalata cholembedwa ndi anthu opitirira 1,000. Malinga ndi zimene atolankhani ananena, chikalatacho chinati: “Tingati dziko lafika pa mphambano pofuna kusankha njira yolowera chifukwa chakuti zimene tikuchita lero zikukhudza kwambiri nkhalango, nyanja, mitsinje, mapiri, zinyama, ndi zinthu zina zachilengedwe zochirikiza moyo, zimene ifeyo ndi ana athu tikudalira.”

Mavuto a zachilengedwe amene alipowa ndi chinthu chimodzi chabe chimene anthu akuda nacho nkhawa. Masiku ano anthu padziko lonse akuopa zigawenga. Wachiwiri kwa mkulu wa bungwe la akadzitape ku Canada anati: “Timagona khutu lili kukhomo kuopa kuti chichitike ndi chiyani.” Timada nkhawa ngakhale kungoonerera nkhani pa TV.

Anthu ambiri, ngakhale amene amalimbikira ntchito, akuopa kuchotsedwa ntchito. Ali ndi nkhawa imeneyi chifukwa cha mchokocho, kutsekedwa kwa makampani, mpikisano pantchito, ndi kuvuta kwa mabwana. Achinyamatanso amaopa kuonedwa ngati otsalira ndi anzawo. Ana aang’ono angamade nkhawa kuti makolo awo sawakonda kwenikweni. Nanga bwanji mmene anawo amaonera zimene zikuchitika m’dzikoli? Mayi wina anadandaula kuti: “Nthawi zina, kwa ana amene amadziwa zochepa, dzikoli liyenera kuti limaoneka loopsa kwambiri.” Ndiponso makolo ambiri akuopa kuti anthu amene amawakonda, makamaka ana awo, angatengere makhalidwe oipa a dzikoli.

Nthawi zambiri, okalamba amaopa kugwa pa masitepe kapena kumenyedwa ndi achifwamba panjira. Zoonadi, ‘amaopa za pamwamba,’ mwinanso kuti ‘panjira pangakhale zoopsa.’ (Mlaliki 12:5) Ambirinso amaopa matenda aakulu. Tikamamva za matenda monga chimfine chakupha, khansa, ndi matenda ena opatsirana, timada nkhawa kuti mwina tingadwale matenda achilendo amene angativulaze kapena kutipha ifeyo ndi banja lathu. Tikaona anthu athanzi ndi amphamvu zawo akudwala ndi kufooka, timada nkhawa kuti mwina ifenso kapena okondedwa athu zingawachitikire. Tikayang’ana nkhope ya munthu amene akudwala kwambiri, timamva chisoni kuona kuti alibiretu chiyembekezo.

Popeza kuti anthufe timaopa zinthu zambiri, kodi tili ndi chifukwa chomveka choyembekezera kuti zinthu zikhala bwino m’tsogolo? Kodi pali chimene chingatithandize kukhala ndi chiyembekezo? Nkhani yotsatira iyankha mafunso amenewa.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

© Jeroen Oerlemans/​Panos Pictures