Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto Onse Adzatha Posachedwapa

Mavuto Onse Adzatha Posachedwapa

Mavuto Onse Adzatha Posachedwapa

“Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro.”​—DEUTERONOMO 32:4.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani inuyo mumayembekezera kwambiri kudzakhala ndi moyo wosatha? (b) N’chifukwa chiyani anthu ambiri amalephera kukhulupirira Mulungu ngakhale kuti iye akulonjeza kudzachita zinthu zosangalatsa kwambiri m’tsogolo?

KODI mumakonda kuganizira za moyo wa m’Paradaiso? Mwina mumadziona mukupita m’madera osiyanasiyana padzikoli n’kumaona zinthu zamoyo zochuluka zedi zimene simunkazidziwa. Mwinanso mumadziona mukusangalala ndi anzanu pogwira ntchito yosamalira ndi kusintha dzikoli kuti likhale munda wokongola. Kapena mumadziona muli ndi luso la zojambulajambula, lojambula mapulani a nyumba, loimba ndiponso maluso ena koma nthawi yoti muchite zimenezi imasowa. Zonsezi zikungosonyeza kuti muli ndi chiyembekezo chodzakhala moyo womwe Baibulo limati ndi “moyo weniweniwo” umene Yehova akufuna kuti tidzasangalale nawo kosatha.​—1 Timoteyo 6:19.

2 Kodi sizosangalatsa ndiponso mwayi wamtengo wapatali kuuza ena chiyembekezo chopezeka m’Baibulo chimenechi? Komatu anthu ambiri amaona kuti zimenezi sizoona ayi. Iwo amati ndi nkhambakamwa chabe kapena zolakalaka za anthu amene sachedwa kutengeka ndi zilizonse zimene amva. Anthuwa mwinanso zimawavuta kukhulupirira Mulungu amene amalonjeza kuti adzapatsa anthu moyo wosatha m’Paradaiso. N’chifukwa chiyani zimawavuta? Ena n’chifukwa choti samvetsa chifukwa chake zoipa zimachitika. Iwo amaona kuti ngati Mulungu alikodi ndipo ngati alidi wamphamvuyonse ndiponso wachikondi, sipangakhale chifukwa chomveka choti padzikoli pazichitika zoipa anthu n’kumavutika. Amaganiza kuti ngati Mulungu alikodi sipangachitike zoipa. Motero amati ngati alikodi ndiye kuti mwina si wamphamvuyonse kapena saganizirako n’komwe za anthu. Kwa anthu ena maganizo amenewa n’ngomveka ndithu. Satanatu wasonyeza luso lalikulu zedi pochititsa anthu khungu.​—2 Akorinto 4:4.

3. Kodi anthu amavutika ndi funso liti limene ifeyo tingathe kuwayankha, ndipo n’chifukwa chiyani ifeyo tili ndi mwayi wapadera wochita zimenezi?

3 Poti ndife Mboni za Yehova, tili ndi mwayi wapadera kwambiri wothandiza anthu amene akusocheretsedwa ndi Satana komanso nzeru za dzikoli. (1 Akorinto 1:20; 3:19) Timamvetsa chifukwa chimene anthu ambiri sakhulupirira malonjezo a m’Baibulo. Mwachidule tingati n’chifukwa choti sadziwa Yehova. N’kutheka kuti sadziwa n’komwe dzinali ndiponso tanthauzo lake. Mwinanso samvetsa kapena sadziwa n’komwe makhalidwe ake komanso zakuti iye amasunga malonjezo ake nthawi zonse. Ifetu ndife odala zedi kuti tikudziwa zinthu zonsezi. Ndibwino kuti nthawi ndi nthawi tizionanso mmene tingathandizire anthu amene ali “mu mdima wa maganizo,” kuti apeze mayankho omveka a mafunso ovuta kwambiri, monga lakuti: “N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti zoipa zizichitika ndiponso kuti anthu azivutika?” (Aefeso 4:18) Choyamba tiona mmene tingayalire maziko a yankho logwira mtima. Kenaka tikambirana mmene Yehova amaonetsera makhalidwe ake ndipo titero poona chifukwa chimene iye analolera kuti zoipa zizichitika.

Kupeza Njira Yabwino Yowayankhira

4, 5. Kodi tingafunikire kuchita chiyani munthu akafunsa kuti, n’chifukwa chiyani Mulungu amalola anthu kuvutika? Fotokozani.

4 Kodi timayankha bwanji munthu akatifunsa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti anthu azivutika? M’posavuta kumufotokozera nkhani yonseyi mwatsatanetsatane, kuyambira ndi zimene zinachitika m’munda wa Edene. Nthawi zina palibe vuto kutero. Komabe tiyenera kusamala. M’pofunika kuyala kaye maziko a yankho lathu. (Miyambo 25:11; Akolose 4:6) Tiyeni tione mfundo zitatu za m’Malemba zimene tiyenera kuzimvetsa bwino tisanayambe kuyankha funsolo.

5 Mfundo yoyamba n’njakuti ngati munthuyo ali wokhumudwa kwambiri chifukwa cha kuchuluka kwa zoipa m’dzikoli, n’kutheka kuti pali zoipa zinazake zimene zam’chitikira iyeyo kapena abale ake. Motero n’chinthu chanzeru kuyamba kumusonyeza kuti takhudzidwa mtima pomva zimene zam’chitikirazo. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti: “Lirani ndi anthu amene akulira.” (Aroma 12:15) Munthuyo akaona kuti tikumumvera “chisoni” angakhudzidwe mtima kwambiri. (1 Petulo 3:8) Akazindikira kuti tikum’ganizira, m’posavuta kuti amvetsere zimene tikufuna kumuuza.

6, 7. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira munthu amene wafunsa funso limene lakhala likum’vutitsa?

6 Mfundo yachiwiri n’njakuti, tingayambe ndi kuthokoza munthuyo ngati akufunsa funsoli n’cholinga chofuna kudziwa. Anthu ena amaganiza kuti kudzifunsa mafunso amenewa kumasonyeza kuti iwowo alibe chikhulupiriro kapena salemekeza Mulungu. N’kuthekanso kuti anamva zimenezi kwa mbusa. Koma si choncho ayi. Ndipotu ngakhale anthu okhulupirika otchulidwa m’Baibulo anafunsapo mafunso oterewa. Mwachitsanzo, wamasalmo Davide anafunsa kuti: “Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m’nyengo za nsautso?” (Salmo 10:1) Chimodzimodzinso mneneri Habakuku. Naye anafunsa kuti: “Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva inu? Ndifuulira kwa inu za chiwawa, koma simupulumutsa. Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndewu, nauka makani.”​—Habakuku 1:2, 3.

7 Awatu anali anthu okhulupirika amene ankalemekeza Mulungu kwambiri. Ndiye kodi Mulungu anawadzudzula chifukwa chofunsa mafunso omwe ankavutika nawo? Ayi, m’malo mwake Yehova anaona kuti ndibwino kuti mafunsowo alembedwe m’Mawu ake. Masiku ano anthu ena amadzifunsa mafunso otere chifukwa cha zoipa zimene zikuchitika. Anthuwa akumva njala yauzimu ndipo akufuna mayankho ochokera m’Baibulo. Kumbukirani kuti Yesu anayamikira anthu amene akumva njala yauzimu, kapena kuti amene “amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyo 5:3) Ndi mwayi waukulu zedi kuthandiza anthu amenewa kupeza chimwemwe chimene Yesu analonjeza.

8. Kodi n’ziphunzitso zotani zosokoneza zimene zachititsa anthu kukhulupirira kuti Mulungu ndiye amachititsa anthu kuvutika, ndipo kodi tingawathandize bwanji?

8 Mfundo yachitatu n’njakuti tingam’thandize munthuyo kumvetsa kuti si Mulungu amene amachititsa zoipa zimene zafala m’dzikoli. Anthu ambiri amaphunzitsidwa kuti Mulungu ndiye akulamulira dzikoli, ndiponso kuti kalekale iyeyo analemberatu zonse zimene zimatichitikira, ndiponso kuti ali ndi zifukwa zodziwa yekha zimene amapatsira anthu mavuto. Ziphunzitso zimenezi n’zabodza. Sizipatsa Mulungu ulemu ndipo zimachititsa kuti Mulunguyo azioneka kuti ndiye amachititsa zoipazi ndiponso kuvutika. Motero m’pofunika kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kutsutsa ziphunzitsozi. (2 Timoteyo 3:16) Si Yehova amene akulamulira dongosolo la zinthu loipali, koma ndi Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Yehova salemberatu zinthu zonse zimene zidzachitike pamoyo. Koma amapatsa aliyense mwayi ndiponso ufulu wosankha kuchita zabwino kapena zoipa, zolungama kapena zosalungama. (Deuteronomo 30:19) Komanso n’zosatheka kuti Yehova achititse choipa china chilichonse, chifukwa iye amadana ndi zoipa ndipo zimam’khudza kwambiri akamaona anthu osalakwa akuvutika.​—Yobu 34:10; Miyambo 6:16-19; 1 Petulo 5:7.

9. Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka zinthu zotani pothandiza anthu kumvetsa chifukwa chimene Yehova Mulungu walolera kuti tizivutika?

9 Mukayala maziko amenewa munthuyo sangavutike kumvetsa chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azivutika. Pofuna kukuthandizani kutero, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wakonza mabuku angapo ofunikira. (Mateyo 24:45-47) Mwachitsanzo, pa Msonkhano Wachigawo wa chaka cha 2005 ndi 2006 wakuti Kumvera Mulungu, panatuluka kapepala kakuti Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa. Ngati kapepala kameneka kalipo m’chinenero chanu, yesetsani kukadziwa bwino. N’chimodzimodzinso ndi buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lomwe tsopano lili m’zinenero 157. Ndipo bukuli lili ndi mutu wathunthu wofotokoza funso lofunikali. Gwiritsani ntchito bwino zinthu zimenezi. Zimafotokoza momveka bwino zimene Baibulo limanena zokhudza nkhani imene inabuka mu Edene yokayikira mfundo yakuti Mulungu n’ngoyenerera kulamulira chilengedwe chonse. Zimafotokozanso chifukwa chimene Yehova anayendetsera nkhaniyo m’njira imeneyi. Mukam’fotokozera munthuyo zimenezi, m’pofunika kukumbukira kuti, mukum’thandiza kudziwa nkhani yofunika koposa nkhani ina iliyonse. Chifukwatu mukum’thandiza kudziwa Yehova ndi makhalidwe ake apamwamba.

Gogomezerani Makhalidwe a Yehova

10. Kodi anthu ambiri amavutika kumvetsa chiyani pankhani ya chifukwa chimene Mulungu amalolera kuvutika, ndipo n’chiyani chingawathandize?

10 Mukamathandiza ena kumvetsa chifukwa chimene Yehova walolera anthu kudzilamulira okha n’kumamvera Satana, yesetsani kugogomezera makhalidwe apamwamba a Yehova. Anthu ambiri amadziwa kuti Mulungu ndi wamphamvu chifukwa kawirikawiri amamva akutchulidwa kuti Wamphamvuyonse. Komabe, mwina zingawavute kumvetsa chifukwa chimene panopa Mulunguyo sagwiritsira ntchito mphamvu zake zosaneneka pothetseratu kusalungama ndiponso kuvutika konse. N’kutheka kuti iwowa sadziwa bwinobwino za makhalidwe ena a Yehova, monga akuti ndi woyera, wachilungamo, wanzeru ndiponso wachikondi. Yehova amasonyeza makhalidwe onsewa mwangwiro ndiponso moyenerera. Motero Baibulo limati: “Ntchito yake ndi yangwiro.” (Deuteronomo 32:4) Kodi mungagogomezere bwanji makhalidwe amenewa poyankha mafunso amene anthu amafunsa pankhaniyi? Tiyeni tionepo zitsanzo zingapo.

11, 12. (a) N’chifukwa chiyani tchimo la Adamu ndi Hava linali losatheka kukhululukidwa? (b) N’chifukwa chiyani Yehova sangalekerere uchimo mpaka kalekale?

11 Kodi Yehova akanatha kungokhululukira Adamu ndi Hava basi? Iyitu siinali nkhani yotheka kukhululukidwa. Poti Adamu ndi Hava anali anthu angwiro, iwo anachita kusankha mwadala kusamvera ulamuliro wa Yehova n’kumvera Satana. Motero n’zosadabwitsa kuti anthu ogalukira Mulunguwa sanasonyeze kulapa kulikonse. Komabe anthu akamafunsa zoti, n’chifukwa chiyani Mulungu sanakhululuke, n’kutheka kuti kwenikweni amakhala akufunsa kuti bwanji Yehova sanayambe wasiya kaye mfundo zake zolungama n’kungololera kuti anthu azichimwa ndi kum’pandukira? Yankho la funsoli likukhudza khalidwe limodzi lofunika kwambiri la Yehova. Iye ndi woyera.​—Eksodo 28:36; 39:30.

12 Baibulo limagogomezera nthawi zambirimbiri kuti Yehova ndi woyera. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ndi anthu ochepa chabe m’dziko loipa lino amene amamvetsa khalidwe limeneli. Yehova ndi woyera, ndipo n’ngotalikirana zedi ndi uchimo uliwonse. (Yesaya 6:3; 59:2) Yehova sangalekelere kuti uchimo upitirire ndipo anakonza njira yodzauchotsera. Yehova atati alekerere uchimo, sitingakhale ndi chiyembekezo chilichonse. (Miyambo 14:12) Panthawi yake, Yehova adzachititsa kuti chilichonse m’chilengedwechi chidzakhale choyera. Mosakayika, zimenezi zidzatheka chifukwa ndi zimene Woyerayo akufuna.

13, 14. N’chifukwa chiyani Yehova anaganiza zosawonongeratu opanduka aja m’Edene?

13 Kodi Yehova akanatha kungowononga opandukawo n’kulenganso ena? N’zoona kuti Yehova anali ndi mphamvu zochitira zimenezi ndipotu posachedwapa adzagwiritsa ntchito mphamvuzi kuwononga anthu onse oipa. Motero, ena angadzifunse kuti, ‘Nangano n’chifukwa chiyani Mulungu sanachitiretu zimenezi pachiyambi pamene m’chilengedwe chonse munali ochimwa atatu okha?’ Iwo amati, ‘Kodi akanatero sakanathetseratu mavuto onse amene timawaona m’dzikoli?’ Komano n’chifukwa chiyani Yehova sanaganize zochita zimenezi? Lemba la Deuteronomo 32:4 limati: “Ntchito yake ndi yangwiro.” Yehova amaona kuti chilungamo n’chofunika kwambiri. Kwenikweni, ‘Yehova amakonda chiweruzo.’ (Salmo 37:28) Chifukwa cha kukonda chilungamo, Yehova sanafune kuwonongeratu opanduka aja m’Edene. Tiyeni tione chifukwa chake zili choncho.

14 Kupanduka kwa Satana kunachititsa kuti pabuke funso lakuti, kodi Mulungu n’ngoyenerera kulamulira chilengedwe chonse? Chifukwa cha chilungamo chake, Yehova anafuna kuti funso limene Satana anayambitsali liyankhidwe bwinobwino. Kuwonongeratu opandukawo nthawi yomweyo, ngakhale kuti sikunali kuwalakwira, sikukanayankha funsoli. N’zoona kuti kukanapereka umboni wowonjezereka wakuti Yehova alibe mnzake pamphamvu. Komatu nkhani apa siinali yokayikira mphamvu za Yehova. Komanso Yehova anali atanena kale cholinga chake kwa Adamu ndi Hava. Iwowa anayenera kukhala ndi ana ndi kudzaza dziko lapansi, kuligonjetsa ndi kulamulira zamoyo zonse zapadziko lapansi. (Genesis 1:28) Yehova akanangowonongeratu Adamu ndi Hava, ndiye kuti mawu amene ananena potchula cholinga chake polenga anthu akanangopita pachabe. Chifukwa cha chilungamo chake, Yehova sakanalola kuti pachitike zoterezi. Pajatu cholinga cha Yehova sichilephera kukwaniritsidwa.​—Yesaya 55:10, 11.

15, 16. Kodi tingathandize bwanji anthu amene akunena maganizo awo a mmene akanathetsera nkhani ya mu Edene?

15 Kodi alipo aliyense m’chilengedwechi amene akanayendetsa mwanzeru kwambiri nkhaniyi kuposa Yehova? Anthu ena amatchula maganizo awo a momwe akanayendetsera nkhani ya kupanduka komwe kunachitika mu Edene. Komabe potero, kodi iwo sakutanthauza kuti akanapeza njira yabwino koposa yoyendetsera nkhaniyi? N’kutheka kuti iwo satero chifukwa cha zolinga zoipa, koma mwina sadziwa bwinobwino za Yehova ndiponso za kuzama kwa nzeru zake. Polembera kalata Akhristu a ku Roma, mtumwi Paulo anafotokoza kwambiri za nzeru za Mulungu, komanso za “chinsinsi chopatulika” chokhudza cholinga cha Yehova chodzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya kuwombola anthu okhulupirika ndi kuyeretsa dzina lake loyera. Kodi Paulo ankamva bwanji akamaganizira za nzeru za Mulungu amene anakonza cholinga choterechi? Mtumwiyu anamaliza kalata yake ndi mawu akuti: “Kwa Mulungu wanzeru yekhayo, kukhale ulemerero kwamuyaya kudzera mwa Yesu Khristu. Amen.”​—Aroma 11:25; 16:25-27.

16 Paulo ankazindikira kuti Yehova ndiye “wanzeru yekhayo,” kapena kuti ndiye chimake chenicheni cha nzeru m’chilengedwe chonse. Ngati anthu opanda ungwirofe timalephera kuthetsa mavuto ena, kuli bwanji vuto lokhudza nzeru za Mulungu pankhani ya kulamulira moyenerera? Motero tiyenera kuthandiza anthu kuti nawonso aziopa Yehova, yemwe ndi Mulungu “wa mtima wanzeru.” (Yobu 9:4) Tikamamvetsa bwino nzeru za Yehova, sitikayika ngakhale pang’ono kuti amayendetsa zinthu m’njira yabwino kwambiri.​—Miyambo 3:5, 6.

Kumvetsa Khalidwe Lalikulu Kwambiri la Yehova

17. Kodi kumvetsa bwino chikondi cha Yehova kungathandize bwanji anthu amene samvetsa chifukwa chimene iye walolera kuti anthu azivutika?

17 “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Mawu a m’Baibulo ochititsa chidwiwa amatiuza za khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova. Ili ndilo khalidwe la Yehova losangalatsa koposa ndiponso lolimbikitsa kwambiri kwa anthu amene akuvutika chifukwa cha kuchuluka kwa zoipa. Yehova wasonyeza chikondi pa zonse zimene wachita poyendetsa nkhani ya mavuto aakulu amene uchimo wabweretsa m’chilengedwe chake. Chifukwa cha chikondi, Yehova anapereka chiyembekezo kwa mbadwa zochimwa za Adamu ndi Hava, n’kuwapatsa njira yofikira kwa iye kenako n’kukhala naye paubwenzi. Chifukwa cha chikondi, Mulungu anapereka dipo lomwe linatsegula njira yoti anthu akhululukidwe machimo onse n’kukhalanso ndi moyo wangwiro komanso wosatha. (Yohane 3:16) Ndipo chifukwa cha chikondi iye amaleza mtima ndi anthu. Yehova wapatsa anthu ochuluka zedi mwayi wokana Satana n’kusankha kulamulidwa ndi iye.​—2 Petulo 3:9.

18. Kodi ndife odala chifukwa chomvetsa chiyani, ndipo nkhani yotsatira ifotokoza chiyani?

18 M’busa wina ananena mawu otsatirawa kwa anthu amene anasonkhana pokumbukira zauchigawenga zimene zinachitika zaka zam’mbuyomo. Iye anati: “Sitikudziwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu walola zoipa ndiponso kuvutika kuti zipitirire.” N’zomvetsa chisoni bwanji! Komatu ife ndife odala kwambiri pomvetsa bwino nkhani imeneyi. (Deuteronomo 29:29) Popeza Yehova ndi wanzeru, wachilungamo, ndiponso wachikondi, tikudziwa kuti posachedwapa achotsa zinthu zonse zovutitsa anthu. Ndipotu iye analonjeza zimenezi. (Chivumbulutso 21:3, 4) Nanga kodi Yehova anakonza zotani poganizira anthu amene akhala akumwalira zaka zambirimbiri m’mbuyo monsemu? Kodi nkhani ya mu Edene ija anaiyendetsa m’njira yopatsa anthuwa chiyembekezo? Inde, mwachikondi chake Yehova wawaganiziranso anthu amenewa, ndipo watero pokonza zodzawaukitsa. Nkhani yotsatirayi ifotokoza zimenezi.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tingayankhe bwanji munthu akatifunsa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika?

• Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti ndi woyera ndiponso wolungama posawononga opanduka a mu Edene aja?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza anthu kumvetsa bwino chikondi cha Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Yesetsani kuthandiza anthu amene zikuwavuta kumvetsa chifukwa chimene anthu akuvutikira

[Zithunzi patsamba 23]

Davide ndi Habakuku anali anthu okhulupirika koma anafunsa Mulungu mafunso